Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 30

Pitilizani Kuyenda m’Coonadi

Pitilizani Kuyenda m’Coonadi

“Palibe cimene cimandisangalatsa kwambili kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’coonadi.”—3 YOH. 4.

NYIMBO 54 “Njila ni Iyi”

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Malinga na 3 Yohane 3, 4, n’ciani cimatikondweletsa?

TANGOGANIZILANI cimwemwe cimene mtumwi Yohane anali naco, pamene anamvela kuti anthu amene anawaphunzitsa coonadi akutumikilabe Yehova mokhulupilika. Akhristu okhulupilika amenewo anali kukumana na mavuto ambili. Ndipo Yohane anayesetsa kuwathandiza kulimbitsa cikhulupililo cawo monga ana ake auzimu. Mofanana na Yohane, nafenso timakondwela ngati ana athu kapena anthu amene timaphunzila nawo Baibo adzipatulila kwa Yehova, ndipo akupitiliza kum’tumikila.—Ŵelengani 3 Yohane 3, 4.

2. Kodi colinga ca Yohane polembela Akhristu anzake makalata cinali ciani?

2 Mu 98 C.E., Yohane ayenela kuti anali kukhala ku Efeso kapena ku dela lapafupi na mzindawo. Iye ayenela kuti anapita kukakhala kumeneko atacoka pa cisumbu ca Patimo pamene anali kukhala monga mkaidi. Ca panthawi imeneyo, m’pamene mzimu woyela wa Yehova unamutsogolela kulemba makalata ake atatu. Iye analemba makalatawo pofuna kulimbikitsa Akhristu okhulupilika kuti apitilize kukhulupilila Yesu na kuyendabe m’coonadi.

3. Kodi tikambilana mafunso ati?

3 Yohane ndiye anali mtumwi wotsilizila kumwalila. Iye anali na nkhawa cifukwa ca zimene aphunzitsi onyenga anali kucita mumpingo wacikhristu. * (1 Yoh. 2:18, 19, 26) Anthu ampatuko amenewo anali kukamba kuti amam’dziŵa Mulungu, koma sanali kumvela malamulo ake. Tsopano tiyeni tikambilane malangizo ouzilidwa amene Yohane anapeleka. Pokambilana, tidzayankha mafunso atatu awa: Kodi kuyenda m’coonadi kumatanthauza ciani? Ni zinthu ziti zimene zingatilepheletse kuyendabe m’coonadi? Nanga tingathandizane bwanji kuti tonse tipitilize kuyenda m’coonadi?

KODI KUYENDA M’COONADI KUMATANTHAUZA CIANI?

4. Kulingana na 1 Yohane 2:3-6 na 2 Yohane 4, 6, kodi tiyenela kucita ciani kuti tiziyenda m’coonadi?

4 Kuti tiyende m’coonadi, tifunika kudziŵa coonadi copezeka m’Mawu a Mulungu, Baibo. Kuwonjezela apo, tifunika “kusunga malamulo [a Yehova],” kapena kuti kumumvela. (Ŵelengani 1 Yohane 2:3-6; 2 Yohane 4, 6.) Yesu anatipatsa citsanzo cabwino kwambili pa nkhani yomvela Yehova. Conco, njila imodzi yofunika kwambili imene timaonetsela kuti timamvela Yehova ni mwa kutsatila citsanzo ca Yesu mosamala kwambili.—Yoh. 8:29; 1 Pet. 2:21.

5. Kodi tifunika kukhulupilila ciani?

5 Kuti tipitilize kuyenda m’coonadi, tifunika kukhulupilila kuti Yehova ni Mulungu wa coonadi, ndipo ciliconse cimene amatiuza m’Mawu ake, Baibo, ni coonadi. Tifunikanso kukhulupilila kuti Yesu ni Mesiya wolonjezedwa. Anthu ambili masiku ano amakayikila zakuti Yesu anadzozedwa monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Yohane anacenjeza Akhristu anzake kuti panali “anthu onyenga ambili,” amene akanasoceletsa Akhristu amene anali na cikhulupililo cocepa mwa Yehova na Yesu. (2 Yoh. 7-11) Yohane analemba kuti: “Kodi wabodza angakhalenso ndani, kuposa amene amatsutsa kuti Yesu ndiye Khristu?” (1 Yoh. 2:22) Kuti tisasoceletsedwe, palibenso cina cimene tingacite kuposa kuphunzila Mawu a Mulungu. Ngati tacita zimenezi, m’pamene tingadziŵe bwino Yehova na Yesu. (Yoh. 17:3) Ndipo tikatelo, tidzafika pokhutila kuti cimene tili naco ni coonadi.

ZIMENE ZINGATILEPHELETSE KUPITILIZA KUYENDA M’COONADI

6. N’ciani cingalepheletse Akhristu acinyamata kuyendabe m’coonadi?

6 Akhristu tonse tifunika kukhala osamala kuti tisasoceletsedwe na nzelu za anthu. (1 Yoh. 2:26) Maka-maka Akhristu acicepele ni amene afunika kusamala kwambili na msampha umenewu. Mlongo wina wa ku France, dzina lake Alexia, * amene ali na zaka 25, anati: “Pamene n’nali pa sukulu, n’naphunzila za cisanduliko na ziphunzitso zina za anthu. Ziphunzitso zimenezo zinanipangitsa kuyamba kukayikila coonadi. Nthawi zina, n’nali kuona ngati ziphunzitso zimenezo n’zoona. Koma n’naona kuti kungakhale kulakwitsa kunyalanyaza zimene Yehova amatiphunzitsa kupitila m’Baibo, n’kumangokhulupilila zilizonse zimene nimaphunzila ku sukulu.” Alexia anayamba kuŵelenga buku lakuti, Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Patapita mawiki ocepa cabe, maganizo ake okayikila anathelatu. Iye anati: “N’nadzionela nekha kuti m’Baibo muli coonadi. Komanso n’nazindikila kuti kutsatila mfundo zake kunganithandize kukhala na umoyo wacimwemwe ndiponso wamtendele.”

7. Kodi tiyenela kuyesetsa kupewa ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

7 Akhristu tonse, kaya ndife acinyamata kapena acikulile, tifunika kuyesetsa kupewa kukhala na umoyo wapaŵili. Yohane anaonetsa kuti n’zosatheka kuyenda m’coonadi, pa nthawi imodzi-modziyo n’kumacita makhalidwe oipa. (1 Yoh. 1:6) Ngati tifuna kuti Yehova azikondwela nafe, nthawi zonse tiyenela kucita zinthu monga kuti aliyense akutiona. Ndipo kukamba zoona, kulibe chimo lobisika, cifukwa Yehova amaona zonse zimene timacita. —Aheb. 4:13.

8. Kodi tiyenela kupewa ciani?

8 Tiyenela kupewa kuona chimo mmene anthu a m’dzikoli amalionela. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Tikanena kuti: ‘Tilibe ucimo,’ ndiye kuti tikudzinamiza.” (1 Yoh. 1:8) M’nthawi ya Yohane, anthu ampatuko anali kukamba kuti n’zotheka munthu kukhalabe pa ubale na Mulungu olo kuti amacita chimo mwadala. Masiku ano, anthu m’dzikoli alinso na maganizo aconco. Ambili amakamba kuti amakhulupilila Mulungu. Koma saona chimo mmene Yehova amalionela, maka-maka pa nkhani ya kugonana. Zimene Yehova amaziona kuti ni chimo, iwo amati ni cosankha ca munthu kapena ni ufulu wake.

Acinyamata, yesetsani kumvetsetsa mfundo za m’Baibo za makhalidwe abwino na kuzikhulupilila kwambili. Mukatelo, mudzakwanitsa kuteteza cikhulupililo canu (Onani ndime 9) *

9. Kodi acinyamata amapindula bwanji akamayesetsa kutsatila mfundo za m’Baibo?

9 Nthawi zina, Akhristu acinyamata amakakamizika kutengela maganizo olakwika amene anzawo kunchito kapena kusukulu ali nawo pa nkhani ya kugonana. Izi n’zimene zinacitikila Aleksandar. Iye anati: “Atsikana ena kusukulu anali kuninyengelela kuti nigone nawo. Popeza n’nalibe cisumbali, iwo anali kuninena kuti ndine wamathanyula, kapena kuti nimagonana na amuna anzanga.” Mukakumana na mayeselo ngati amenewa, musasunthike potsatila mfundo za m’Baibo. Mukatelo, mudzadzisungila ulemu, mudzakhala na thanzi labwino, mudzakhala na cikumbumtima coyela, komanso mudzakhalabe pa ubale wabwino na Yehova. Nthawi iliyonse mukakana kugonja ku mayeselo, zimakhala zopepukilako kucita coyenela. Kumbukilaninso kuti maganizo olakwika amene anthu a m’dzikoli ali nawo pa nkhani ya kugonana ni ocokela kwa Satana. Ngati mupewa kutsatila maganizo a dziko, ndiye kuti ‘mukugonjetsa woipayo.’—1 Yoh. 2:14.

10. Kodi lemba la 1 Yohane 1:9 limatilimbikitsa bwanji kutumikila Yehova na cikumbumtima coyela?

10 Timadziŵa kuti Yehova ndiye ali na udindo wotiuza kuti kucita zakuti-zakuti ni chimo. Ndipo timayesetsa kupewa kucita chimo. Koma tikacimwa, timavomeleza colakwa cathu kwa Yehova m’pemphelo. (Ŵelengani 1 Yohane 1:9.) Tikacita chimo lalikulu, timapempha thandizo kwa akulu, amene Yehova anawaika kuti azitisamalila. (Yak. 5:14-16) Komabe, sitiyenela kumangodziimba mlandu cifukwa ca macimo akale. Cifukwa ciani? Cifukwa Atate wathu wacikondi anapeleka nsembe ya dipo la Mwana wake n’colinga cakuti macimo athu azikhululukidwa. Yehova akakhululukila munthu wolapa, amakhululukadi na mtima wonse. Conco, palibe cimene cingatilepheletse kutumikila Yehova na cikumbumtima coyela.—1 Yoh. 2:1, 2, 12; 3:19, 20.

11. Tingacite ciani kuti tisasoceletsedwe na ziphunzitso zimene zingafooketse cikhulupililo cathu?

11 Tifunika kupewa ziphunzitso za anthu ampatuko. Kungocokela pamene mpingo wacikhristu unayamba, Mdyelekezi wakhala akuseŵenzetsa aphunzitsi onyenga pocititsa atumiki a Mulungu okhulupilika kuyamba kukayikila zimene amaphunzila. Pa cifukwa cimeneci, tifunika kuphunzila kusiyanitsa pakati pa zoona na mabodza. * Adani athu angaseŵenzetse mawebusaiti kapena malo ocezela pa intaneti pofuna kufooketsa cikhulupililo cathu mwa Yehova, kapena pofuna kutipangitsa kuti tisamakondane na Akhristu anzathu. Koma musakhulupilile mabodza awo. Kumbukilani kuti ni ocokela kwa Satana.—1 Yoh. 4:1, 6; Chiv. 12:9.

12. N’cifukwa ciani tiyenela kulimbitsa cikhulupililo cathu pa coonadi cimene tinaphunzila?

12 Kuti Satana asatigonjetse, tifunika kukhulupilila kwambili Yesu na udindo umene Mulungu anam’patsa pokwanilitsa colinga cake. Tiyenelanso kukhulupilila cabe kapolo wokhulupilika ndi wanzelu amene Yehova akumugwilitsila nchito potsogolela gulu lake masiku ano. (Mat. 24:45-47) Timalimbitsa cikhulupililo cathu mwa kuŵelenga Mawu a Mulungu nthawi zonse. Tikatelo, cikhulupililo cathu cidzakhala ngati mtengo umene uli na mizu yopita patali. Paulo anakamba mfundo yofanana na imeneyi polembela kalata mpingo wa Akolose. Anati: “Popeza mwalandila Khristu Yesu Ambuye wathu, yendanibe mogwilizana naye. Khalanibe ozikika mozama mwa iye, ndipo monga mmene munaphunzitsidwila, pitilizani kukula pamene mukumuona iye monga maziko anu, ndi kukhazikika m’cikhulupililo.” (Akol. 2:6, 7) Tikalimbitsa cikhulupililo cathu, palibe cimene Satana na onse amene ali ku mbali yake angacite, comwe cingatilepheletse kuyendabe m’coonadi.—2 Yoh. 8, 9.

13. Kodi tiyenela kuyembekezela ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

13 Tifunika kuyembekezela kuzondewa na dzikoli. (1 Yoh. 3:13) Yohane anatikumbutsa kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yoh. 5:19) Pamene tikuyandikila mapeto a dzikoli, mkwiyo wa Satana ukukulila-kulila. (Chiv. 12:12) Kuwonjezela potiukila mwacinyengo, monga kutikopa kuti ticite ciwelewele kapena kufalitsa mabodza kupitila mwa anthu ampatuko, Satana amatiukilanso mwacindunji. Mwacitsanzo, amasonkhezela adani athu kuti azitizunza mwankhanza. Iye adziŵa kuti wangotsala na nthawi yocepa yoti aletse nchito yathu yolalikila, kapena yoti awononge cikhulupililo cathu. Telo n’zosadabwitsa kuti m’maiko ena, nchito yathu ni yoletsedwa, ndipo m’maiko enanso abale athu alibe ufulu wokwanila wa kulambila. Ngakhale n’conco, abale na alongo athu m’maiko amenewo akupilila. Uwu ni umboni wakuti olo Satana atayesa bwanji kulimbana nafe, tingakwanitse kukhalabe okhulupilika.

MUZITHANDIZANA KUTI MUKHALEBE M’COONADI

14. Ni njila imodzi iti imene tingathandizile abale na alongo athu kukhalabe m’coonadi?

14 Kuti tithandize abale na alongo athu kukhalabe m’coonadi, tifunika kuwaonetsa cifundo. (1 Yoh. 3:10, 11, 16-18) Tifunika kukondana osati cabe pamene zinthu zili bwino, koma ngakhalenso pamene kwabuka mavuto. Mwacitsanzo, kodi mudziŵako winawake amene m’bululu wake anamwalila ndipo afunika kutonthozedwa kapena kuthandizidwa m’njila zina? Kapena kodi pali Akhristu anzanu ena amene zinthu zawo zinawonongeka cifukwa ca tsoka la zacilengedwe, ndipo afunika thandizo kuti amangenso Nyumba za Ufumu kapena nyumba zawo? Timaonetsa kuti timawakonda kwambili abale na alongo athu na kuwamvelela cifundo, osati mwa zokamba cabe, koma maka-maka mwa zocita zathu.

15. Kulingana na zimene 1 Yohane 4:7, 8 imakamba, kodi tiyenela kucita ciani?

15 Tikamakondana, ndiye kuti tikutengela Atate wathu wacikondi wakumwamba. (Ŵelengani 1 Yohane 4:7, 8.) Njila imodzi yofunika kwambili imene timaonetsela cikondi ni kukhululukilana. Mwacitsanzo, m’bale kapena mlongo wathu angatikhumudwitse, koma pambuyo pake n’kutipepesa. Zikakhala conco, tingaonetse cikondi mwa kumukhululukila na kuiŵalako colakwaco. (Akol. 3:13) M’bale wina, dzina lake Aldo anakhumudwa pamene m’bale amene iye anali kumukhulupilila anakamba mawu oipa ponena za anthu a mtundu wake. M’bale Aldo anati: “N’napemphela kwa Yehova mobweleza-bweleza kuti anithandize kusam’sungila cakukhosi m’baleyo.” Koma palinso zina zimene Aldo anacita. Anapempha m’baleyo kuti ayende naye limodzi mu ulaliki. Pamene anali mu ulaliki, Aldo anafotokozela m’baleyo kuti mawu amene anakamba anamuŵaŵa kwambili. Aldo anati: “M’baleyo atamvela kuti zimene anakamba zinanikhumudwitsa, anapepesa. Mawu ake anali kucita kuonetselatu kuti anadzimvela cisoni cifukwa ca zimene anakamba. Pambuyo pake, tinakhalanso mabwenzi, ndipo tinaiŵalako za nkhaniyo.”

16-17. Kodi tiyenela kutsimikiza mtima kucita ciani?

16 Mtumwi Yohane anali kuwakonda kwambili abale ake auzimu ndiponso anali kudela nkhawa umoyo wawo wauzimu. Cikondi cake cimeneco cimaonekela bwino tikaganizila malangizo amene iye anawapatsa m’makalata ake atatu ouzilidwa. Ndithudi, n’zolimbikitsa ngako kudziŵa kuti amuna na akazi odzozedwa amene adzalamulila na Khristu, nawonso ni acikondi ndipo amadela nkhawa ena mofanana na Yohane.—1 Yoh. 2:27.

17 Tiyeni tiyesetse kutsatila malangizo amene takambilana m’nkhani ino. Tiyeni titsimikize mtima kuyendabe m’coonadi, kutanthauza kumvela Yehova pa zilizonse zimene timacita pa umoyo wathu. Tiziŵelenga Mawu ake na kuwadalila. Tiyenelanso kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa Yesu. Tizikana kutsatila nzelu za anthu komanso ziphunzitso za ampatuko. Tiyeni tizipewa kukhala na umoyo wapaŵili komanso tisalole ena kutinyengelela kuti ticite chimo. Tizitsatila mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. Cinanso, tizithandiza abale athu kukhalabe olimba kuuzimu mwa kuwakhululukila akatilakwila, komanso mwa kuthandiza amene afunika thandizo. Tikatelo, ndiye kuti olo tikumane na mavuto otani, tidzapitilizabe kuyenda m’coonadi.

NYIMBO 49 Tikondweletse Mtima wa Yehova

^ ndime 5 Tikukhala m’dziko lolamulidwa na Satana, tate wake wa bodza. Conco zingakhale zovuta kwambili kuyenda m’coonadi. Umu ni mmenenso zinalili kwa Akhristu a m’nthawi ya atumwi. Pofuna kuthandiza Akhristu amenewo na ife masiku ano, Yehova anauzila mtumwi Yohane kulemba makalata atatu. Mfundo za m’makalata amenewa zingatithandize kudziŵa zinthu zimene zingatilepheletse kuyendabe m’coonadi. Komanso zingatithandize kudziŵa zimene tingacite kuti tisagonje ku zinthu zimenezo.

^ ndime 6 Maina ena asinthidwa.

^ ndime 11 Onani nkhani yophunzila yakuti “Kodi Mudziŵa Bwino Zoona Zake?” mu Nsanja ya Mlonda ya August 2018.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pamene mlongo wacitsikana ali ku sukulu, akumvela na kuona zinthu zambili zopangitsa munthu kuona ngati khalidwe la mathanyula n’labwino. (M’zikhalidwe zina, mitundu yosiyana-siyana ya pa utawaleza amaiseŵenzetsa monga cizindikilo ca mcitidwe wa mathanyula.) Pambuyo pake, mlongoyo wapatula nthawi yofufuza kuti alimbitse cikhulupililo cake pa zimene Baibo imaphunzitsa. Izi zam’thandiza kupanga cosankha cabwino.