Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 26

Kodi Mungathandize pa Nchito Yopanga Ophunzila?

Kodi Mungathandize pa Nchito Yopanga Ophunzila?

“Mulungu. . . amalimbitsa zolakalaka zanu [na kukupatsani mphamvu] kuti mucite zinthu zonse zimene iye amakonda.”—AFIL. 2:13.

NYIMBO 64 Timasangalala Kuthandizila pa Nchito Yokolola

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Yehova wakucitilani zotani?

KODI munakhala bwanji Mboni ya Yehova? Coyamba, munamva “uthenga wabwino”—mwina kwa makolo anu, mnzanu wa ku nchito kapena wa ku sukulu, kapenanso kupitila m’nchito yolalikila khomo na khomo. (Maliko 13:10) Ndiyeno, wina wake anacita khama pothela nthawi yoculuka kuphunzila namwe Baibo. Ndipo pamene munali kuphunzila Baibo, munayamba kum’konda Yehova, ndipo munadziŵa kuti iyenso amakukondani. Yehova anakukokelani ku coonadi. Ndipo popeza tsopano ndimwe wophunzila wa Yesu Khristu, muli na ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya. (Yoh. 6:44) Mosakayikila, mumayamikila Yehova kuti anasonkhezela wina wake kukuphunzitsani coonadi, ndipo Iye anakulandilani monga mmodzi wa atumiki ake.

2. Tikambilana ciani m’nkhani ino?

2 Lomba popeza tadziŵa coonadi, tili na mwayi wothandizako ena kuyenda nafe pa njila ya kumoyo. Cingakhale copepuka kwa ife kulalikila khomo na khomo. Koma mwina kuyambitsa phunzilo la Baibo kungakhale kovuta. Kodi ni mmene zilili kwa inu? Ngati n’telo, mwina mudzaona kuti ena mwa malingalilo a m’nkhani ino ni othandiza. Tikambilane cimene cimatisonkhezela kupanga ophunzila. Tikambilanenso zopinga zimene zingatilepheletse kutsogoza phunzilo la Baibo. Coyamba, tiyeni tikambilane cifukwa cake tiyenela kulalikila anthu na kuwaphunzitsa uthenga wabwino.

YESU ANATIPATSA NCHITO YOLALIKILA ANTHU NA KUŴAPHUNZITSA

3. N’cifukwa ciani timalalikila?

3 Yesu ali padziko lapansi, anapatsa otsatila ake nchito ya mbali ziŵili. Mbali yoyamba, anawauza kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu, ndipo anawaonetsa mocitila mwake. (Mat. 10:7; Luka 8:1) Mwacitsanzo, Yesu anauza ophunzila ake zimene anayenela kucita kaya anthu alandile uthenga wa Ufumu, kapena kuukana. (Luka 9:2-5) Iye anafotokozela otsatila ake za kukula kwa nchito yawo yolalikila, powauka kuti adzacitila “umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14; Mac. 1:8) Mosasamala kanthu za mmene anthu akanalandilila uthengawo, ophunzilawo anafunika kuuza anthu za Ufumu wa Mulungu na zimene udzakwanilitsa.

4. Malinga na Mateyu 28:18-20, kodi tiyenela kucitanso ciani kuwonjezela pa kulalikila za Ufumu?

4 Kodi mbali yaciŵili ya nchito imene Yesu analamula ophunzila ake ni iti? Iye anauza otsatila ake kuti aphunzitse anthu oyenelela kusunga zinthu zonse zimene iye anawalamula. Kodi nchito yolalikila na kupanga ophunzila inayenela kugwilidwa cabe na Akhristu a m’zaka za zana loyamba, monga mmene anthu ena amakambila? Ayi, Yesu anaonetsa kuti nchito yofunika imeneyi inali kudzapitilizabe “mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Ŵelengani Mateyu 28:18-20.) Yesu ayenela kuti anapeleka nchitoyo pamene anaonekela kwa ophunzila ake oposa 500. (1 Akor. 15:6) Ndipo m’masomphenya amene anaonetsa Yohane, Yesu anaonetsa bwino kuti ophunzila ake onse ayenela kuthandiza ena kuphunzila za Yehova.—Chiv. 22:17.

5. Malinga na 1 Akorinto 3:6-9, kodi Paulo anaseŵenzetsa fanizo lotani poonetsa kugwilizana pakati pa kulalikila na kuphunzitsa?

5 Mtumwi Paulo anayelekezela nchito yopanga ophunzila na kubzala mbewu, kuonetsa kuti tiyenela kucita zambili kuposa cabe pa kubzala mbewu. Iye anakumbutsa Akorinto kuti: “Ineyo ndinabzala, Apolo anathilila. . . Inuyo ndinu munda wa Mulungu umene ukulimidwa.” (Ŵelengani 1 Akorinto 3:6-9.) Monga anchito ‘m’munda wa Mulungu,’ sitimangobzala, komanso timathilila na kuona mmene mbewuzo zikukulila. (Yoh. 4:35) Koma timadziŵa kuti Mulungu ndiye amakulitsa mbewuzo.

6. Kodi nchito yathu monga aphunzitsi imaphatikizapo ciani?

6 Timafunafuna awo ‘amene anali ndi maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’ (Mac. 13:48) Kuti tithandize anthu amenewo kukhala ophunzila a Yesu, tiyenela kuŵathandiza (1) kumvetsa, (2) kuvomeleza, komanso (3) kuseŵenzetsa zimene akuphunzila m’Baibo. (Yoh. 17:3; Akol. 2:6, 7; 1 Ates. 2:13) Onse mu mpingo angathandize ophunzila Baibo atsopano amenewa mwa kuwaonetsa cikondi, komanso kuwalandila mwacimwemwe akabwela ku misonkhano. (Yoh. 13:35) Mphunzitsi wa Baibo angafunikenso kuthela nthawi yoculuka komanso kucita khama pothandiza wophunzila kusiya zikhulupililo kapena miyambo ‘yozikika molimba.’ (2 Akor. 10:4, 5) Zingatenga miyezi yambili kuti muthandize munthu kupanga masinthidwe amenewo kuti akakwanilitse colinga cake ca kubatizika. Ndipo m’pake kupanga masinthidwe amenewa.

CIKONDI CIMATILIMBIKITSA KUPANGA OPHUNZILA

7. N’ciani cimatilimbikitsa kulalikila na kupanga ophunzila?

7 N’cifukwa ciani timagwila nchito yolalikila na kupanga ophunzila? Coyamba, timam’konda Yehova. Pamene mucita zonse zotheka pomvela lamulo la kulalikila na kupanga ophunzila, mumaonetsa cikondi canu pa Mulungu. (1 Yoh. 5:3) Ganizilani izi: Cikondi canu pa Yehova cinakusonkhezelani kuyamba kulalikila nyumba na nyumba. Kodi lamulo limeneli linali lopepuka kulitsatila? Osati kwenikweni. Mutafika pa khomo la munthu kwa ulendo woyamba kuti mulalikile, kodi munacita mantha? Mosakayikila munacitadi mantha! Koma podziŵa kuti iyi ni nchito imene Yesu afuna kuti muigwile, munamvelabe lamulo limeneli. Mwacionekele, m’kupita kwa nthawi, cinakhala copepuka kwa imwe kugwila nchito yolalikila. Nanga bwanji zotsogoza phunzilo la Baibo? Kodi mumacita mantha mukaiganizila nkhani imeneyi? Mwina. Komabe, mukapempha Yehova kuti akuthandizeni kugonjetsa mantha, kenako na kulimba mtima kuti muyambe kutsogoza phunzilo la Baibo, Yehova adzakuthandizani kukulitsa cikhumbo canu ca kupanga ophunzila.

8. Malinga na Maliko 6:34, n’ciani cina cingatilimbikitse kuphunzitsa ena?

8 Caciŵili, cikondi pa anansi athu cimatisonkhezela kuŵaphunzitsa coonadi. Panthawi ina, Yesu na ophunzila ake anali wolema kwambili pambuyo pogwila nchito yolalikila. Iwo anali kufuna malo kuti apumuleko, koma cikhamu ca anthu cinawatsatila. Atawamvela cifundo, Yesu anayamba kuwaphunzitsa “zinthu zambili.(Ŵelengani Maliko 6:34.) Ngakhale kuti iye anali wolema, analimbikila kugwila nchitoyi. Cifukwa ciani? Yesu anali kudziŵa mmene anthu a m’khamulo anali kumvelela. Iye anaona mmene iwo anali kuvutikila. Anali kufunikila ciyembekezo, ndipo iye anali kufuna kuwathandiza. Ni mmenenso anthu alili masiku ano. Musatengele maonekedwe awo a kunja. Ali monga nkhosa zopanda m’busa wozitsogolela. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti anthu otelo sadziŵa Mulungu ndipo alibe ciyembekezo. (Aef. 2:12) Iwo ali ‘panjila yopita kuciwonongeko’ (Mat. 7:13) Tikaganizila mmene umoyo wauzimu wa anthu ulili m’gawo lathu, cikondi na cifundo zimatilimbikitsa kuwathandiza. Ndipo njila yabwino yowathandizila ni kuwapempha kuti tiziphunzila nawo Baibo.

9. Malinga na Afilipi 2:13, kodi Yehova angakuthandizeni bwanji?

9 Mwina mumadodoma kuti muyambitse phunzilo la Baibo cifukwa mudziŵa kuti kutsogoza phunzilo kumafuna nthawi. Ngati ni mmene zilili kwa inu, muuzeni Yehova mmene mumvelela. M’pempheni kuti akuthandizeni kukulitsa cikhumbo canu cofuna kupeza munthu wofuna kuphunzila naye Baibo. (Ŵelengani Afilipi 2:13.) Mtumwi Yohane anatitsimikizila kuti Mulungu amayankha mapemphelo athu ogwilizana na cifunilo cake. (1 Yoh. 5:14, 15) Conco, mungakhale na cidalilo cakuti Yehova adzakuthandizani kukulitsa cikhumbo canu cofuna kupanga ophunzila.

KUGONJETSA ZOPINGA ZINA

10-11. Kodi n’ciani cingatilepheletse kutsogoza phunzilo la Baibo?

10 Sitiona mopepuka nchito yathu yophunzitsa, ngakhale kuti timakumana na zopinga zimene zingatilepheletse kutengako mbali mmene tifunila m’nchito yopanga ophunzila. Tiyeni tione zina mwa zopinga zimenezo na kuona mmene tingazigonjetsele.

11 Mwina timaona kuti sitingakwanitse kucita zambili cifukwa ca mmene zinthu zilili kwa ife. Mwacitsanzo, ofalitsa ena ni okalamba kapena ali na thanzi lofooka. Kodi ndiye mmene zinthu zilili kwa inu? Ngati n’telo, onani maphunzilo ena amene tatengapo pa nthawi ino ya mlili wa kolona. Taphunzila kuti tingatsogoze maphunzilo a Baibo kupitila pa zipangizo zamakono! Conco mungayambitse phunzilo la Baibo na kulitsogoza muli m’nyumba mwanu. Koma palinso phindu lina pamenepa. Ena amafuna kuphunzila Baibo, koma sapezeka pa nyumba pa nthawi imene abale athu anapatula kuti azilalikila. Komabe, ena amapezeka pa nyumba m’mawa kwambili kapena m’madzulo kwambili. Kodi mungakonze zakuti muziphunzila Baibo na munthu wina pa nthawi ngati zimenezi? Yesu anaphunzitsa Nikodemo usiku, nthawi imene Nikodemo anaona kuti inali bwino kwa iye.—Yoh. 3:1, 2.

12. Ni zinthu ziti zimene zimatipatsa cidalilo cakuti tingakhale aphunzitsi aluso?

12 Tingamaone kuti tilibe luso lotsogoza phunzilo la Baibo. Mwina timaona kuti tifunika kukhala na cidziŵitso cacikulu kapena kukhala mphunzitsi waluso tisanayambe kutsogoza phunzilo.Ngati umu ni mmene mumamvelela, onani zinthu zitatu izi zimene zingakuthandizeni kukulitsa cidalilo canu. Coyamba, Yehova amakuona kukhala woyenelela kuphunzitsa ena. (2 Akor. 3:5) Caciŵili, Yesu, amene ali na ‘ulamulilo wonse kumwamba ndi padziko lapansi,’ wakulamulani kuti muziphunzitsa. (Mat. 28:18) Ndipo cacitatu, mungadalile ena kukuthandizani. Yesu anali kudalila zimene Atate wake anam’phunzitsa kukamba, ndipo nanunso mungacite zimenezo. (Yoh. 8:28; 12:49) Kuwonjezela apo, mungapemphe woyang’anila kagulu kanu ka ulaliki, mpainiya wocita bwino, kapena wofalitsa waluso kuti akuthandizeni kuyambitsa phunzilo la Baibo na kulitsogoza. Njila imodzi imene mungakulitsile cidalilo canu, ni kupezekapo pamene ofalitsa amenewa akutsogoza maphunzilo awo a Baibo.

13. N’cifukwa ciani tiyenela kukhala okonzeka kusintha?

13 Cingakhale covuta kuseŵenzetsa njila na zida zatsopano za ulaliki. Pakhala kusintha mmene timatsogozela maphunzilo a Baibo. Cofalitsa cacikulu cophunzitsila Baibo lomba, ni buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Bukuli limafuna kukonzekela phunzilo na kulitsogoza mosiyana na mmene timacitila kumbuyoku. Timaŵelenga ndime zocepa na kukhala na nthawi yoculuka ya kukambilana na wophunzila. Ndipo pophunzitsa, timaseŵenzetsa kwambili mavidiyo na zida zamakono monga JW Laibulali®. Ngati simudziŵa moseŵenzetsela zida zimenezi, pemphani wina kuti akuthandizeni kudziŵa moziseŵenzetsela. Anthufe timakonda kucita zinthu m’njila imene tinazoloŵela. Ndipo si copepuka kuzolowela kucita zinthu m’njila yatsopano. Koma mwa thandizo la Yehova na anthu ena, cidzakhala cosavuta kwa imwe kusintha ndipo mudzakondwela kuphunzila Baibo na anthu. Monga mmene mpainiya wina anakambila, kuphunzila Baibo mwa njila imeneyi ni “kosangalatsa kwambili kwa ophunzila na mphunzitsi wake.”

14. Kodi tiyenela kukumbukila ciani ngati timalalikila m’gawo lovuta? Nanga 1 Akorinto 3:6, 7 ingatilimbikitse bwanji?

14 Mwina tikhala m’gawo lovuta kuyambitsa maphunzilo a Baibo. Mwina anthu angakhale alibe cidwi na uthenga wathu kapena kuukana kumene. N’ciani cingatithandize kukhala na maganizo olimbikitsa m’gawo lotelo? Kumbukilani kuti zinthu mu umoyo wa anthu zimasintha mofulumila kwambili m’dziko lodzala na mavutoli, ndipo aja amene poyamba analibe cidwi angazindikile zosoŵa zawo zauzimu. (Mat. 5:3) Ena amene kumbuyoku anali kukana mabuku athu, m’kupita kwa nthawi anavomela kuphunzila Baibo. Ndipo tidziŵa kuti Yehova ndiye Mbuye wa zokolola. (Mat. 9:38) Afuna kuti tipitilize kubzala na kuthilila mbewu, koma iye ndiye amakulitsa. (1 Akor. 3:6, 7) N’zolimbikitsa kudziŵa kuti ngakhale sititsogoza phunzilo la Baibo pali pano, Yehova amatidalitsa cifukwa ca kuyesayesa kwathu, osati cifukwa ca kuculuka kwa zimene timacita! *

PEZANI CIMWEMWE CIMENE CIMABWELA PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA

Onani mmene nchito yathu yolalikila na kuphunzitsa ingathandizile munthu (Onani ndime 15-17) *

15. Kodi Yehova amamvela bwanji ngati munthu wayamba kuphunzila Baibo na kuseŵenzetsa zimene akuphunzilazo?

15 Yehova amakondwela kwambili ngati munthu walandila coonadi ca m’Baibo, ndipo amauzako ena zimene amaphunzilazo. (Miy. 23:15, 16) Iye ayenela kuti amakondwela kwambili akaona anthu ake akulalikila na kuphunzitsa mwakhama masiku ano! Mwacitsanzo, olo kuti m’caka ca utumiki ca 2020 panali mlili wa dziko lonse, tinatha kutsogoza maphunzilo a Baibo okwana 7,705,765, ndipo izi zinathandiza kuti anthu okwana 241,994 adzipatulile kwa Yehova na kubatizika. Ndipo nawonso ophunzila a Yesu atsopano amenewa, azitsogoza maphunzilo a Baibo na kupanga ophunzila ambili. (Luka 6:40) Mosakayika konse, timakondweletsa Yehova ngati titengako mbali m’nchito yopanga ophunzila.

16. Kodi tingadziikile colinga cabwino citi?

16 Kupanga ophunzila si nchito yopepuka, koma na thandizo la Yehova tingathe kutengapo gawo kuphunzitsa acatsopano kukonda Atate wathu wakumwamba. Kodi tingadziikile colinga coyambitsa phunzilo la Baibo olo limodzi cabe na kumalitsogoza? Tingadabwe na zimene zingacitike ngati tiseŵenzetsa mpata uliwonse kufunsa amene timakumana nawo ngati angakonde kuphunzila nawo Baibo. Tingakhale na cidalilo cakuti Yehova adzadalitsa khama lathu.

17. Kodi tidzamvela bwanji ngati timatsogoza phunzilo la Baibo?

17 Ha, ni mwayi waukulu cotani nanga umene tili nawo wa kulalikila na kuphunzitsa ena coonadi! Nchito imeneyi imatipatsa cimwemwe ceniceni. Mtumwi Paulo, amene anathandiza anthu a ku Tesalonika kukhala ophunzila a Yesu, anafotokoza mmene anali kumvelela, mwanjila iyi: “Ciyembekezo cathu, kapena cimwemwe cathu n’ciani? Inde, mphoto yathu yoinyadila pamaso pa Ambuye wathu Yesu, pa nthawi ya kukhalapo kwake n’ciani? Si inu amene kodi? Ndithudi, inu ndinudi ulemelelo wathu ndi cimwemwe cathu.” (1 Ates. 2:19, 20; Mac. 17:1-4) Umu ndi mmene ambili amamvelela masiku ano. Mlongo wina dzina lake Stéphanie, pamodzi na mwamuna wake, amene athandiza anthu ambili kufika mpaka kubatizika anati: “Palibe cimene cimabweletsa cimwemwe cacikulu kuposa kuthandiza anthu kudzipatulila kwa Yehova.”

NYIMBO 57 Tilalikile kwa Anthu a Makhalidwe Onse

^ ndime 5 Yehova watipatsa nchito yolalikila anthu, komanso kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene Yesu anatilamula. Kodi n’ciani cimatilimbikitsa kuphunzitsa ena? Timakumana na zopinga zotani pa nchito yolalikila na kupanga ophunzila? Nanga tingazigonjetse bwanji zopinga zimenezo? Nkhani ino, iyankha mafunso amenewa.

^ ndime 14 Kunena za mbali imene timacita pa nchito yopanga ophunzila, onani nkhani yakuti “Monga Mpingo, Thandizani Maphunzilo a Baibo Kupita Patsogolo Kuti Akabatizike,” mu Nsanja ya Mlonda ya March 2021.

^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Onani mmene kuphunzila Baibo na munthu kungam’thandizile kupanga masinthidwe mu umoyo wake: Poyamba munthu uyu aoneka kuti moyo wake ulibe colinga, ndipo sadziŵa Yehova. Ndiyeno Mboni za Yehova zakumana naye pamene zikulalikila, ndipo wavomela kuphunzila Baibo. Zimene waphunzilazo zam’thandiza kuti adzipatulile na kubatizika. M’kupita kwanthawi, iyenso wayamba kuthandiza ena kukhala ophunzila a Yesu. Pamapeto pake, onse akukondwela na moyo m’paradaiso.