Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi Mboni za Yehova ziyenela kuseŵenzetsa mawebusaiti opezelapo zibwenzi kuti apeze womanga naye banja?

Yehova amafuna kuti anthu aŵili akakwatilana azikhala acimwemwe, komanso kuti akhale ogwilizana kwa moyo wawo wonse. (Mat. 19:4-6) Ngati mufuna kukwatila, kodi mungam’peze kuti munthu woyenelela womanga naye banja? Pokhala Mlengi wathu, Yehova adziŵa zimene tifunika kucita kuti tikhale na cikwati ca cimwemwe. Conco, mukaseŵenzetsa mfundo zimene watipatsa zinthu zidzakuyendelani bwino. Onani zina mwa mfundo zimenezo.

Coyamba, tiyenela kudziŵa mfundo iyi: “Mtima ndi wonyenga kwambili kuposa cina ciliconse ndipo ungathe kucita cina ciliconse coipa.” (Yer. 17:9) Anthu aŵili amene afuna kukwatilana akayamba cibwenzi, mwamsanga amayamba kuonetsana cikondi kwambili cakuti zimakhala zovuta kwa iwo kupanga cisankho canzelu. Anthu akasankha kuti akwatilane, cabe cifukwa ca mmene akumvelela, zotulukapo zake n’zakuti amagwilitsidwa mwala. (Miy. 28:26) Ndiye cifukwa cake si cinthu canzelu kwa anthu aŵili ali pa cibwenzi kuonetsana cikondi kwambili, kapena kulonjezana kuti adzakwatilana asanafike podziŵana bwino.

Miyambo 22:3 imati: “Wocenjela ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.” Kodi pali kuopsa kotani ngati tiseŵenzetsa mawebusaiti opezelapo zibwenzi? N’zacisoni kuti ena apeza anthu amene sawadziŵa pa intaneti, n’kuyamba nawo cibwenzi, pambuyo pake n’kuzindikila kuti anthuwo anali kuwanamiza. Komanso, anthu ena osaona mtima apanga maakaunti abodza pa intaneti n’colinga cofuna kupusitsa anthu kuti awabele ndalama. Ndipo nthawi zina, anthu amene amacita zacinyengo zimenezi amanamizila kukhala a Mboni.

Onani kuopsa kwina kumene kumakhalapo. Mawebusaiti ena opezelapo zibwenzi, amaseŵenzetsa masamu a mtundu winawake kuti aone anthu amene angayenelelane kukhala pacibwenzi. Komabe, palibe umboni woonetsa kuti njila zimenezi n’zothandizadi. Kodi n’canzelu kukhulupilila njila zokhazikitsidwa na anthu popanga cisankho pa nkhani yofunika kwambili monga cikwati? Mfundo za m’Baibo n’zodalilika kuposa masamu amene anthu amaseŵenzetsa kuti apeze munthu womanga naye banja.—Miy. 1:7; 3:5-7.

Mfundo ya pa Miyambo 14:15 imati: “Munthu amene sadziŵa zinthu amakhulupilila mawu alionse, koma wocenjela amaganizila za mmene akuyendela.” Musanatsimikize ngati munthu amene mufuna kumanga naye banja ni wokuyenelelani, mudziŵeni bwino coyamba. Koma n’zosatheka kumudziŵa bwino munthu kupitila pa intaneti. Olo kuti mumaona mfundo zokhudza munthuyo pa intaneti na kuceza naye kwa nthawi yaitali, kodi mungati mum’dziŵadi bwino munthuyo? Ena amene anali kuganiza kuti apeza wacikondi wawo, anagwilitsidwa mwala ataonana na munthuyo pamasom’pamaso.

Wamasalimo anati: “Sindinakhale pansi pamodzi ndi anthu acinyengo. Ndipo sindinayanjane ndi anthu obisa umunthu wawo.”(Sal. 26:4) Anthu ambili amakonda kunamiza anthu pa intaneti kuti aoneke ngati ni anthu abwino. Iwo amabisa umunthu wawo kapena makhalidwe awo oipa pamene akutumiza mauthenga kwa ena pa intaneti. Ngakhale kuti ena anganene kuti ni Mboni za Yehova, kodi ni obatizika? Kodi ni okhwima mwauzimu? Kodi ali paubale wabwino na Yehova? Kodi anthu mu mpingo amawalemekeza? Kodi ni zitsanzo zoipa, kapena kodi ni anthu osafunika “kugwilizana” nawo? (1 Akor. 15:33; 2 Tim. 2:20, 21) Kodi ni omasuka mwa Malemba kukwatila kapena kukwatiwanso? Muyenela kudziŵa mayankho pa mafunso amenewa. Koma cingakhale covuta kudziŵa zenizeni zokhudza munthuyo popanda kufunsilako kwa Mboni zina zimene zimamudziŵa bwino munthuyo. (Miy. 15:22) Ndiiko komwe, mtumiki wa Yehova wokhulupilika sangayese olo pang’ono ‘kumangidwa m’goli’ na osakhulupilila.—2 Akor.6:14; 1 Akor. 7:39.

Popeza kuti kugwilitsila nchito mawebusaiti opezelapo zibwenzi n’koopsa, pali njila zabwino zimene tingapezele munthu womanga naye banja na kum’dziŵa bwino. Kodi mungam’peze kuti munthu woyenelela womanga naye banja? Ngati n’kololeka kusonkhana pamodzi, Mboni za Yehova zimadziŵana na ena pa misonkhano ya mpingo, yadela, yacigawo, komanso pa zocitika zina.

Pamene mupatula nthawi yoceza pamodzi, mudzaona ngati muli na zolinga zofanana, komanso ngati ndinu oyenelelana

Ngati n’zosatheka kusonkhana pamodzi, monga panthawi ino ya mlili wa COVID-19, timaseŵenzetsa zipangizo zamakono pocita misonkhano ya mpingo, ndipo timakhala na mpata wodziŵana na abale na alongo amene ni mbeta. Timaona mmene akutengelako mbali pa misonkhano, komanso mmene akupelekela ndemanga poonetsa cikhulupililo cawo. (1 Tim. 6:11, 12) Ngati misonkhano yanu mumacitila pa zoom, mungamaceze inu aŵili misonkhano ikatha mwa kuseŵenzetsa breakout room. Maceza abwino acikhristu, angakuthandizeni kuona mmene munthu amene mwakopeka naye amacitila zinthu na ena. Izi zimaonetsa umunthu wake weniweni. (1 Pet. 3:4) M’kupita kwa nthawi, mukafika podziŵana bwino, mungaone ngati muli na zolinga zofanana, komanso ngati ndinu oyenelelana.

Ngati anthu amene ni mbeta aseŵenzetsa mfundo za m’Baibo posakila munthu woyenelela womanga naye banja, mosakaikila adzakhala na banja lacimwemwe. Paja Baibo imati: “Kodi munthu wapeza mkazi [kapena mwamuna] wabwino? Ndiye kuti wapeza cinthu cabwino, ndipo Yehova amakondwela naye.”—Miy. 18:22.