Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 28

Pewani Kuyambitsa Mzimu Wampikisano—Limbikitsani Mtendele

Pewani Kuyambitsa Mzimu Wampikisano—Limbikitsani Mtendele

“Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu, ndi ocitilana kaduka.”—AGAL. 5:26.

NYIMBO 101 Tisunge Umodzi Wathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’ciani cingacitike ngati anthu ena ali na mzimu wampikisano?

MASIKU ano, anthu ambili amacita zinthu mosonkhezeledwa na mzimu wampikisano. Mwacitsanzo, munthu wamalonda angacite zilizonse zowononga malonda a anzake kuti zake ziyende. Wocita maseŵela angavulaze mnzake mwadala pofuna kuti iye apambane maseŵelawo. Mwana wa sukulu angabele mayeso n’colinga cakuti apite ku yunivesiti. Pokhala Akhristu, timadziŵa kuti khalidwe limeneli n’loipa; lili m’gulu la “nchito za thupi.” (Agal. 5:19-21) Komabe, kodi zingatheke atumiki ena a Yehova kuyambitsa mzimu wampikisano mu mpingo mosazindikila? Limeneli ni funso lofunika kwambili cifukwa mzimu wampikisano ungasokoneze mgwilizano wa mpingo.

2. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

2 M’nkhani ino, tikambilana makhalidwe oipa amene angatipangitse kuyamba mpikisano na abale athu. Tikambilananso zitsanzo za amuna na akazi okhulupilika a nthawi za m’Baibo amene anapewa mzimu wampikisano. Koma coyamba, tiyeni tikambilane mmene tingapendele zolinga zathu.

PENDANI ZOLINGA ZANU

3. Kodi tiyenela kudzifunsa mafunso ati?

3 Nthawi na nthawi, ni bwino kumapenda zolinga zathu. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi nimadziona kuti nimaposa ena? Kodi nimagwila nchito molimbika mu mpingo cifukwa cofuna kukhala woposa ena? Kapena nimagwila nchito molimbika cifukwa cofuna kupatsa Yehova zabwino koposa?’ N’cifukwa ciani tiyenela kudzifunsa mafunso amenewa? Onani zimene Mawu a Mulungu amakamba.

4. Malinga na Agalatiya 6:3, 4, n’cifukwa ciani sitiyenela kudziyelekezela na ena?

4 Baibo imatiuza kuti sitiyenela kudziyelekezela na ena. (Ŵelengani Agalatiya 6:3, 4.) Cifukwa ciani? Cifukwa ngati timaona kuti ndife oposa abale athu tingakhale onyada. Ndipo ngati timakonda kudziyelekezela na ena, tingalefuke. Conco, kudziyelekezela na ena kungatilepheletse kukhala oganiza bwino. (Aroma 12:3) Mlongo wina wa ku Greece dzina lake Katerina, * anati: “N’nali kukonda kudziyelekezela na ena amene anali kuoneka okongola, aluso mu ulaliki, komanso amene anali kukondedwa na anthu ambili. Zotulukapo zake n’zakuti n’nali kudziona wacabecabe.” Tizikumbukila kuti Yehova anatikokela kwa iye, osati cifukwa cakuti ndife okongola, odziŵa kulankhula bwino, kapena cifukwa cokondedwa na anthu ambili, koma cifukwa timam’konda komanso kumvela Mwana wake.—Yoh. 6:44; 1 Akor. 1:26-31.

5. Kodi mwaphunzilapo ciani pa citsanzo ca m’bale Hyun?

5 Tingadzifunsenso kuti: ‘Kodi nimadziŵika kukhala munthu wokonda mtendele, kapena nthawi zambili nimakangana na ena?’ Ganizilani citsanzo ca m’bale wina dzina lake Hyun, amene amakhala ku South Korea. Panthawi ina, iye anali kuona ena amene anali na maudindo mu mpingo monga adani ake. Anati: “N’nali kuwapezela zifukwa abalewo, ndipo nthawi zambili sin’nali kugwilizana na zokamba zawo.” Kodi panakhala zotulukapo zotani? Iye anati: “Khalidwe langa limeneli linasokoneza mgwilizano mu mpingo.” Mabwenzi ena a Hyun anam’thandiza kuzindikila khalidwe lake loipali. M’bale Hyun anapanga masinthidwe ofunikila, ndipo tsopano ni mkulu wocita bwino. Ngati taona kuti tili na mzimu wokonda kuyambitsa mpikisano m’malo molimbikitsa mtendele, tiyenela kusintha mwamsanga.

PEWANI KUDZIKUZA KOMANSO KADUKA

6. Malinga na Agalatiya 5:26, ni makhalidwe ati osayenela amene angatipangitse kuyambitsa mzimu wampikisano?

6 Ŵelengani Agalatiya 5:26. Ni makhalidwe ati osayenela amene angatipangitse kuyambitsa mzimu wampikisano? Limodzi mwa iwo ni kudzikuza. Munthu wodzikuza amakhala wonyada komanso wodzikonda. Khalidwe lina losayenela ni kaduka. Munthu wakaduka samangolakalaka zinthu zimene wina ali nazo, koma amafunanso kuti zimene munthuyo ali nazo zikhale zake. Kukamba zoona, kaduka ni khalidwe loipa kwambili. Conco, tiyenela kupewa makhalidwe oipa amenewa monga mmene tingapewele poizoni!

7. N’citsanzo citi cimene cionetsa kuti khalidwe la kudzikuza komanso kaduka n’loipa?

7 Kudzikuza komanso kaduka tingaziyelekezele na ciswe cimene cimadya mtengo pang’ono-pang’ono. Ngakhale mtengowo ungaoneke wolimba, m’kupita kwa nthawi umagwa. Mofananamo, munthu angatumikile Yehova kwa nthawi yaitali. Koma ngati amam’tumikila mosonkhezeledwa na mzimu wonyada komanso kaduka sangapite patali. (Miy. 16:18) Iye adzaleka kutumikila Yehova ndipo angadzipweteke na kupweteketsa ena. Ndiye, tingapewe bwanji kudzikuza na kaduka?

8. Kodi tingapewe bwanji kudzikuza?

8 Tingapewe kudzikuza mwa kutsatila uphungu wa mtumwi Paulo wopita kwa Afilipi wakuti: “Musacite ciliconse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzicepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.” (Afil. 2:3) Ngati timaona ena kukhala otiposa, tidzapewa kupikisana na abale athu amene ali na maluso kuposa ife. M’malo mopikisana nawo, tidzasangalalila nawo limodzi, maka-maka ngati akuseŵenzetsa maluso awo potumikila Yehova. Ndipo ngati abale na alongo amene ali na maluso amenewa amatsatila uphungu wa Paulo, nawonso aziona zabwino mwa ife. Tikatelo, tonsefe tidzalimbikitsa mtendele na mgwilizano mu mpingo.

9. Kodi tingathetse bwanji kaduka?

9 Ngati tikhala odzicepetsa mwa kuzindikila kuti pali zina zimene sitingakwanitse kucita, tidzakwanitsa kuthetsa kaduka. Ngati ndife odzicepetsa, sitidzadziona kuti timacita bwino kuposa ena. M’malo mwake, tidzayesetsa kuphunzilako kwa ena amene acita bwino kuposa ife. Mwacitsanzo, tinene kuti m’bale mu mpingo amapeleka nkhani zotentha za anthu onse. Tingam’funse mmene amakonzekelela nkhani zake. Ngati mlongo amadziŵa kuphika bwino, tingam’funse kuti atiuzeko mophikila bwino. Ngati Mkhristu wacicepele amavutika kupanga mabwenzi, angafunsileko kwa ena amene amapanga mabwenzi mosavuta. Tikacita zimenezi, tidzakulitsa maluso athu na kupewa kaduka.

PHUNZILANI PA ZITSANZO ZA M’BAIBO

Gidiyoni anasungitsa mtendele na a Efuraimu cifukwa ca kudzicepetsa (Onani ndime 10-12)

10. Kodi Gidiyoni anakumana na vuto lotani?

10 Ganizilani zimene zinacitikila Gidiyoni, wa fuko la Manase, na amuna a fuko la Efuraimu. Yehova anathandiza Gidiyoni na asilikali ake 300 kupambana nkhondo. Ndipo izi zikanapangitsa iwo kukhala onyada. Amuna a fuko la Efuraimu anapita kwa Gidiyoni, osati kuti akamuyamikile, koma kuti akakangane naye. Zioneka kuti iwo anakhumudwa cifukwa Gidiyoni sanaŵaitane pokamenya nkhondo na adani a Mulungu. Koma colinga cawo cinali cakuti anthu azilemekeza mtundu wawo. Iwo analephela kuona zabwino zimene Gidiyoni anacita polemekeza dzina la Yehova na kuteteza anthu Ake.—Ower. 8:1.

11. Kodi Gidiyoni anawauza ciani amuna a ku Efuraimu?

11 Gidiyoni modzicepetsa anauza amuna a ku Efuraimu kuti: “Kodi ine ndacita ciani poyelekeza ndi inu?” Ndiyeno anawakumbutsa mmene Yehova anawathandizila kumbuyoku. Amunawo atamvela zimenezi, “mkwiyo wawo unaphwa.” (Ower. 8:2, 3) Gidiyoni anadzicepetsa kuti asungitse mtendele pakati pa anthu a Mulungu.

12. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca a Efuraimu komanso Gidiyoni?

12 Kodi tiphunzilapo ciani pa cocitikaci? Pa citsanzo ca a Efuraimu, tiphunzilapo kuti tiyenela kupewa kudzifunila ulemelelo m’malo molemekeza Yehova. Mitu ya mabanja komanso akulu, tingatengepo phunzilo pa citsanzo ca Gidiyoni. Ngati wina wakhumudwa cifukwa ca zimene tacita, tiyenela kudziŵa cifukwa cake munthuyo wakhumudwa. Cina, tingamuyamikile pa zimene wacita bwino. Koma kuti ticite zimenezi, tiyenela kukhala odzicepetsa, maka-maka ngati n’zoonekelatu kuti munthuyo ndiye wolakwa. Kukhazikitsa mtendele kuli bwino kuposa kufuna kuonetsa ena kuti ni olakwa.

Hana anakhalanso na mtendele wa maganizo cifukwa codalila Yehova kuti adzakonza zinthu (Onani ndime 13-14 13-14)

13. Kodi Hana anakumana na vuto lotani? Nanga analigonjetsa bwanji?

13 Ganizilaninso citsanzo ca Hana. Iye anakwatiwa na Mlevi wina dzina lake Elikana, amene anali kum’konda ngako. Koma Elikana anali na mkazi wina dzina lake Penina. Elikana anali kukonda kwambili Hana kuposa Penina. Komabe, “Penina anabeleka ana koma Hana analibe ana.” Pa cifukwa cimeneci, Penina anali kusautsa Hana kwambili “n’colinga coti amukhumudwitse.” Kodi Hana anali kumvela bwanji? Cinali kumuŵaŵa kwambili! “Anali kulila ndiponso sankadya.” (1 Sam. 1:2, 6, 7) Olo n’conco, m’Baibo palibe paliponse paonetsa kuti Hana anabwezela. M’malo mwake, anakhuthula za mu mtima mwake kwa Yehova ali na cidalilo cakuti iye adzakonza zinthu. Kodi Penina anasintha khalidwe lake? Baibo siikambapo. Koma cimene tidziŵa n’cakuti Hana anakhalanso na mtendele wa maganizo, “ndipo sanakhalenso ndi nkhawa.”—1 Sam. 1:10, 18.

14. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Hana?

14 Kodi tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Hana? Ngati wina akuyesa kupikisana namwe pewani kubwezela. M’malo mobwezela coipa pa coipa, yesani kukhazikitsa mtendele. (Aroma 12:17-21) Olo kuti munthuyo sasintha, inuyo mudzakhalabe na mtendele wa maganizo.

Apolo na Paulo sanali kucitilana kaduka cifukwa anali kudziŵa kuti Yehova ndiye anali kudalitsa nchito yawo (Onani ndime 15-18)

15. Kodi Apolo na Paulo anali kufanana motani?

15 Cotsilizila, ganizilani zimene tingaphunzilepo pa citsanzo ca wophunzila Apolo na mtumwi Paulo. Amuna aŵiliwa anali na cidziŵitso cokwana ca m’Malemba. Onse anali odziŵika komanso aphunzitsi aluso. Ndipo onse aŵili anapanga ophunzila ambili. Koma sanali kucitilana kaduka.

16. Kodi Apolo anali munthu wa bwanji?

16 Apolo anali “mbadwa ya ku Alekizandiriya,” mzinda umene unali cimake ca maphunzilo m’nthawi ya atumwi. Iye anali na mphatso ya kulankhula, komanso anali “kuwadziŵa bwino Malemba.” (Mac. 18:24) Pamene Apolo anali ku Korinto, abale ena mu mpingo anaonetsa poyela kuti anali kum’konda kwambili kuposa abale ena, kuphatikizapo Paulo. (1 Akor. 1:12, 13) Kodi Apolo analimbikitsa magaŵano amenewo? Sitingamuganizile n’komwe kuti anacita zimenezi. Tikutelo cifukwa patapita nthawi pambuyo pakuti Apolo wacokako ku Korinto, Paulo anam’limbikitsa kubwelela kumeneko. (1 Akor. 16:12) Paulo sakanacita zimenezo ngati Apolo anali kulimbikitsa magaŵano mu mpingo. N’zoonekelatu kuti Apolo anaseŵenzetsa maluso ake m’njila yabwino—polengeza uthenga wabwino na kulimbikitsa abale. Tingakhalenso otsimikiza kuti Apolo anali wodzicepetsa. Mwacitsanzo, Baibo siionetsa kuti Apolo anakhumudwa pamene Akula na Purisikila “anamufotokozela njila ya Mulungu molondola.”—Mac. 18:24-28

17. Kodi Paulo analimbikitsa bwanji mtendele?

17 Mtumwi Paulo anali kudziŵa za nchito yabwino imene Apolo anali kucita. Koma Paulo sanade nkhawa kuti anthu adzayamba kuona Apolo kukhala womuposa. Uphungu umene anapatsa mpingo wa ku Korinto, umaonetsa kuti Paulo anali wodzicepetsa ndi wololela. M’malo mokondwela na zimene anthu anali kukamba kuti “Ine ndine wa Paulo,” anapeleka ulemelelo kwa Yehova Mulungu na Yesu Khristu.—1 Akor. 3:3-6.

18. Malinga na 1 Akorinto 4:6, 7, tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Apolo komanso Paulo?

18 Kodi tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Apolo komanso Paulo? Tingamatumikile Yehova mwakhama na kuthandiza anthu ambili kupita patsogolo mpaka kukabatizika. Koma timadziŵa kuti zonsezi zimatheka cifukwa ca thandizo la Yehova. Citsanzo ca Apolo komanso Paulo citiphunzitsanso kuti ngati tili na maudindo ambili mu mpingo, tingacite zambili polimbikitsa mtendele. Timayamikila kwambili ngati amuna apaudindo amalimbikitsa mtendele na mgwilizano mwa kuseŵenzetsa Mawu a Mulungu popeleka uphungu, komanso ngati amayesetsa kutengela citsanzo ca Yesu Khristu m’malo modzifunila ulemelelo!—Ŵelengani 1 Akorinto 4:6, 7.

19. Kodi aliyense wa ife ayenela kucita ciani? (Onani bokosi lakuti “ Pewani Kuyambitsa Mzimu Wampikisano.”)

19 Aliyense wa ife ali na maluso amene Mulungu anam’patsa. Malusowo tiyenela kuwaseŵenzetsa “potumikilana.” (1 Pet. 4:10) Tingaone monga timacita mbali yocepa kwambili. Koma zinthu zing’ono-zing’ono zimene tingacite polimbikitsa mgwilizano, zili monga nchelwa iliyonse imene imakhala yofunikila kuti nyumba imangidwe. Tiyeni tonsefe tiyesetse kuthetselatu mzimu wampikisano. Tiyeni tionetsetse kuti tikucita zonse zotheka kuti tilimbikitse mtendele na mgwilizano mu mpingo.—Aef. 4:⁠3.

NYIMBO 80 ‘Talaŵani, Muone Kuti Yehova ni Wabwino’

^ ndime 5 Monga mmene mbiya ya ming’alu siikhala yolimba, mpingonso umakhala wagwede-gwede ngati muli mzimu wampikisano. Ngati mpingo si wogwilizana, sungakhale malo a mtendele olambililapo Mulungu. M’nkhani ino, tikambilane cifukwa cake tifunika kupewa kuyambitsa mzimu wampikisano, komanso zimene tingacite kuti tilimbikitse mtendele mu mpingo.

^ ndime 4 Maina ena asinthidwa.