Kodi Mudziŵa?
Kodi nchelwa zimene anapeza pa matongwe a Babulo wakale komanso mmene anaziumbila, zionetsa bwanji kuti Baibo ni yolondola?
AKATSWILI ofukula zinthu zakale anapeza nchelwa zowocha mamiliyoni pa matongwe a Babulo, zimene anaseŵenzetsa pomanga mzindawo. Malinga na katswili wina dzina lake Robert Koldewey, nchelwa zimenezo anali kuzipangila m’ng’anjo zimene zinali “kunja kwa mzindawo, kumene kunali dothi yabwino komanso nkhuni zambili.”
Akatswiliwo apezanso umboni woonetsa kuti nduna za boma ku Babulo, zinali kuseŵenzetsa ng’anjo zimenezi kucita zinthu zoipa kwambili. Pulofesa wina wa mbili yakale, komanso wa cinenelo ca Asiriya wa pa yunivesiti ya ku Toronto, dzina lake Paul-Alain Beaulieu, anati: “Zolemba za ku Babulo zionetsa kuti mfumu inaika lamulo lakuti anthu osamvela mfumu, komanso osalemekeza zinthu zopatulika, aziwatentha mwa kuwaponya m’ng’anjo. Mwacitsanzo, mawu ena omwe analembedwa m’nthawi ya mfumu Nebukadinezara anali akuti: “Awonongeni, atentheni, akazingeni, . . . utsi wawo upite kumwamba, apheni mwa kuwaponya m’ng’anjo ya moto.”
Izi zitikumbutsa cocitika ca m’Baibo m’buku la Danieli caputala 3. Malinga na caputalaci, Mfumu Nebukadinezara anapanga fano lalikulu la golide m’cigwa ca Dura, kunja kwa mzinda wa Babulo. Anyamata atatu aciheberi—Sadirake, Mesake, na Abedinego—atakana kuŵelamila fanolo, Nebukadinezara anapsa mtima kwambili, na kulamula kuti akolezele ng’anjo “kuwilikiza ka 7 kuposa mmene anali kucitila nthawi zonse.” Ndipo analamula kuti anyamata atatuwo ‘aponyedwe m’ng’anjo yoyaka motoyo.’ Koma mngelo wa mphamvu anawapulumutsa ku imfa.—Dan. 3:1-6, 19-28.
Nazonso nchelwa za ku Babulo pazokha zimatsimikizila kuti Baibo ni yolondola. Pa nchelwa zambili panalembedwa mawu otamanda mfumu. Mwacitsanzo, zina zinali zolembedwa mawu ngati awa: “Nebukadinezara, Mfumu ya Babulo . . . Malo amene ine Mfumu Yaikulu namanga . . . Mbadwa zanga zam’tsogolo zidzilamulila mmenemo kwamuyaya.” Mawu amenewa afanana kwambili na mawu apa Danieli 4:30, pamene Nebukadinezara anadzikweza ponena kuti: “Kodi uyu si Babulo Wamkulu amene ine ndamanga ndi mphamvu zanga zazikulu ndiponso ndi ulemelelo wanga waukulu ndi colinga cakuti kukhale nyumba yacifumu?”