Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 31

“Khalani Olimba, Osasunthika”

“Khalani Olimba, Osasunthika”

“Abale anga okondedwa, khalani olimba, osasunthika.”—1 AKOR. 15:58.

NYIMBO 122 Cilimikani, Musasunthike!

ZIMENE TIKAMBILANE a

1-2. Kodi Mkhristu ali ngati nyumba ija ya nsanjika motani? (1 Akorinto 15:58)

 MU 1978, nyumba yaitali ya nsanjika 60 inamangidwa mu mzinda wa Tokyo, ku Japan. Anthu anali kudzifunsa ngati nyumbayo idzapilila zivomezi zimene zinali kucitika pafupi-pafupi mu mzindawo. Kodi cinsinsi cake cinali ciyani? Akatswili anaimanga m’njila yakuti ikhale yolimba, koma panthawi imodzimodzi kuti ikhale yofeŵa kukacitika civomezi. Akhristu ali monga nyumba ya nsanjika imeneyo. Motani?

2 Mkhristu ayenela kukhala wosasunthika. Koma ayenelanso kukhala wofeŵa kapena kuti wokonzeka kusintha. Ayenela kukhala wolimba komanso wosasunthika pa kumvela malamulo na miyeso ya Yehova. (Ŵelengani 1 Akorinto 15:58.) Iye ni ‘wokonzeka kumvela’ nthawi zonse. Kumbali ina, ayenela kukhala ‘wololela’ kapena kuti wokonzeka kusintha pakafunika kutelo. (Yak. 3:17) Mkhristu amene amaona zinthu mwa njila imeneyi amapewa kukhwimitsa kwambili zinthu, kapena kukhala wololela mopitilila malile. M’nkhani ino, tikambilane zimene tingacite kuti tisasunthike. Tikambilanenso misampha isanu imene Satana amagwilitsa nchito kuti tisunthike, na mmene tingakanizile misamphayo.

ZIMENE TINGACITE KUTI TIKHALE OLIMBA

3. Ni malamulo otani a Mulungu amene ali pa Machitidwe 15:28, 29?

3 Pokhala wopeleka Malamulo Wamkulu, Yehova nthawi zonse wakhala akupatsa anthu ake malamulo. (Yes. 33:22) Mwacitsanzo, bungwe lolamulila la m’zaka za zana loyamba linachula zinthu zitatu zimene Akhristu anayenela kucita kuti akhale olimba: (1) kupewa mafano na kulambila Yehova yekha basi, (2) kuona magazi kukhala opatulika, komanso (3) kutsatila kwambili malamulo a m’Baibo. (Ŵelengani Machitidwe 15:28, 29.) Kodi Akhristu masiku ano angakhale bwanji osasunthika pa mbali zitatu zimenezi?

4. Kodi timalambila Yehova yekhayo motani? (Chivumbulutso 4:11)

4 Sitipembedza mafano, koma timalambila Yehova yekha basi. Mulungu analamula Aisiraeli kuti azilambila iye yekha basi. (Deut. 5:6-10) Ndipo pamene Yesu anayesedwa na Mdyerekezi, anaonetsa bwino kuti tiyenela kulambila Yehova yekhayo. (Mat. 4:8-10) Pa cifukwa cimeneci, sitilambila mafano. Cina, sitilambila anthu—kaya akhale atsogoleli acipembedzo, andale, kapena akatswili a zamaseŵela komanso a zoimba-imba. Timaimabe nji kwa Yehova, na kulambila yekhayo amene ‘analenga zinthu zonse.’—Ŵelengani Chivumbulutso 4:11.

5. N’cifukwa ciyani timatsatila lamulo la Yehova lokhudza kupatulila kwa moyo na magazi?

5 Timatsatila lamulo la Yehova lokhudza kupatulila kwa moyo na magazi. Cifukwa ciyani? Cifukwa Yehova amati magazi amaimila moyo, umene ni mphatso yamtengo wapatali. (Lev. 17:14) Yehova atalola anthu kudya nyama, anawalamula kuti sayenela kudyanso magazi ake. (Gen. 9:4) Lamulo limeneli analibwelezanso m’Cilamulo ca Mose kwa Aisiraeli. (Lev. 17:10) Ndipo anatsogolela bungwe lolamulila la m’zaka za zana loyamba kugamula kuti Mkhristu aliyense ayenela “kupitiliza kupewa . . . magazi.” (Mac. 15:28, 29) Timatsatila lamulo limeneli mosasunthika popanga zisankho zokhudza cithandizo ca mankhwala. b

6. Kodi timayesetsa kucita ciyani kuti tizitsatila malamulo a Yehova?

6 Timatsatila kwambili malamulo a Yehova. (Aheb. 13:4) Mophiphilitsa, mtumwi Paulo anati tiyenela kucititsa ziwalo za thupi lathu kukhala “zakufa.” Izi zitanthauza kuti tiyenela kuthetselatu zilakolako zoipa. Timapewa kuyang’ana kapena kucita ciliconse cimene cingatipangitse kucita ciwelewele. (Akol. 3:5; Yobu 31:1) Tikakumana na mayeselo, nthawi yomweyo timapewa kuganizila zoipa, kapena kucita zinthu zimene zidzawononga ubwenzi wathu na Mulungu.

7. Kodi tiyenela kutsimikiza mtima kucita ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani?

7 Yehova amafuna kuti ‘tizimumvela mocokela pansi pa mtima.’ (Aroma 6:17) Zonse zimene amatiuza kucita n’zabwino kwa ife, ndipo malamulo ake sasintha. (Yes. 48:17, 18; 1 Akor. 6:9, 10) Timayesetsa kukondweletsa Yehova, na kuonetsa mzimu umene wamasalimo anaonetsa pamene anati: “Ndatsimikiza mtima kutsatila malangizo anu, mpaka kale-kale, ndithu kwa moyo wanga wonse.” (Sal. 119:112) Komabe, Satana amayesa kutipangitsa kuti tilephele kuimabe nji. Kodi amaseŵenzetsa zinthu ziti?

ZIMENE SATANA AMAGWILITSA NCHITO KUTI ATIFOOKETSE

8. Kodi Satana amacita ciyani pofuna kutifooketsa?

8 Mazunzo. Mdyerekezi amagwilitsa nchito anthu ena kuti atizunze pofuna kutifooketsa. Colinga cake ni ‘kutimeza,’ kuwononga ubale wathu na Yehova. (1 Pet. 5:8) Akhristu a m’zaka za zana loyamba anaopsezedwa, kumenyedwa, na kuphedwa cifukwa ca kusasunthika kwawo. (Mac. 5:27, 28, 40; 7:54-60) Satana akali kugwilitsa nchito mazunzo masiku ano. Umboni wa zimenezi ni nkhanza zimene zikucitikila abale na alongo athu ku Russia na kumaiko ena.

9. Fotokozani citsanzo coonetsa kufunika kokhala osamala na mayeso ovuta kuwazindikila.

9 Mayeso ovuta kuwazindikila. Kuwonjezela pa mazunzo, Satana amagwilitsanso nchito “zocita zacinyengo.” (Aef. 6:11) Ganizilani zimene zinacitika kwa m’bale wina dzina lake Bob, amene anali m’cipatala poyembekezela kucitidwa opaleshoni yaikulu. Iye anauza madokotala kuti sadzalola kuikidwa magazi zivute zitani. Madokotalawo anati adzalemekeza cisankho cake. Komabe, usiku wakuti maŵa acitidwa opaleshoni, dokotala wina anapita kukalankhula na m’bale Bob banja lake litapita kunyumba. Iye anamuuza kuti sadzamuika magazi, koma adzasunga magaziwo pambali kuti mwina angafunikile. N’kutheka kuti dokotalayo anaganiza kuti m’bale Bob adzasintha maganizo ake poona kuti palibe a m’banja lake. Koma m’baleyu sanasunthike, ndipo anati sangalole kuikidwa magazi zivute zitani.

10. Kodi maganizo a dzikoli ni oopsa motani? (1 Akorinto 3:19, 20)

10 Nzelu za anthu. Tikamaona zinthu potengela maganizo a anthu, tinganyanyale Yehova na miyeso yake. (Ŵelengani 1 Akorinto 3:19, 20.) “Nzelu za m’dzikoli” nthawi zambili zimapangitsa anthu kusamvela Mulungu. Akhristu angapo a mu mzinda wa Pegamo komanso Tiyatira, anatengela kapenyedwe ka anthu owazungulila pa nkhani ya kulambila mafano, ndiponso zaciwelewele. Yesu anapeleka uphungu wamphamvu kwa Akhristu a m’mizindayi cifukwa colekelela zaciwelewele. (Chiv. 2:14, 20) Masiku anonso, timayesedwa kuti titengele maganizo oipa a dzikoli. Acibale athu na anansi athu, angamatinyengelele kuti tiphwanye malamulo a Yehova. Mwacitsanzo, angamatiuze kuti kutsatila zilakolako za thupi si nkhani yaikulu, komanso kuti malamulo a m’Baibo ni acikalekale.

11. Poyesetsa kukhala osasunthika, kodi tiyenela kupewanji?

11 Nthawi zina, tingaganize kuti malangizo amene Yehova amatipatsa si okwanila. Tingafike pofuna ‘kupitilila zinthu zolembedwa.’ (1 Akor. 4:6) Atsogoleli acipembedzo m’nthawi ya Yesu anali na mlandu wocita zimenezi. Cifukwa cowonjezela malamulo awo-awo pa Cilamulo, anali kusenzetsa anthu wamba mtolo wolemetsa. (Mat. 23:4) Yehova amatipatsa malangizo omveka bwino kudzela m’Mawu ake na gulu lake. Sitiyenela kuwonjezelapo pa malangizo amene iye amatipatsa. (Miy. 3:5-7) Conco, sitipitilila pa zimene zinalembedwa m’Baibo, kapena kuikila malamulo alambili anzathu pa nkhani za munthu mwini.

12. Kodi Satana amagwilitsa nchito bwanji “cinyengo”?

12 Cinyengo. Satana amagwilitsanso nchito “cinyengo copanda pake,” komanso “mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli” kuti asoceletse anthu na kuwagaŵanitsa. (Akol. 2:8) M’nthawi ya atumwi, izi zinaphatikizapo maganizo a anthu, ziphunzitso zaciyuda zosemphana na Malemba, komanso ciphunzitso cakuti Akhristu ayenela kutsatila Cilamulo ca Mose. Maganizo amenewo anasoceletsa anthu cifukwa anawakanganula kwa Yehova, Gwelo la nzelu zenizeni. Masiku ano, Satana amaseŵenzetsa TV, wailesi, manyuzipepala, komanso soshomidiya pofalitsa mphekesela na malipoti abodza ocokela kwa atsogoleli andale. Tinaona zimenezi panthawi ya mlili wa COVID-19. c Mboni za Yehova zimene zinatsatila malangizo a gulu lathu, sizinakhale na nkhawa zopambanitsa zimene anthu osocoletsedwa na nkhani zabodza anali nazo.—Mat. 24:45.

13. N’cifukwa ciyani tiyenela kupewa zoceutsa?

13 Zoceutsa. Tiyenela kuika maganizo athu pa “zinthu zofunika kwambili.” (Afil. 1:9, 10) Zoceutsa zingatidyele nthawi yathu, na kutilanda mphamvu yocita zinthu zotipindulila kwambili. Zinthu zimene timacita tsiku na tsiku monga kudya, kumwa, zosangulutsa, komanso nchito yakuthupi, zingaticeutse ngati tiziika patsogolo. (Luka 21:34, 35) Kuwonjezela apo, tsiku lililonse timamva na kuŵelenga nkhani zokhudza zionetselo komanso mikangano ya ndale. Conde, tisalole zimenezo kuticeutsa, cifukwa ngati tingatelo tidzayamba kukhalila mbali pa nkhani zimenezo m’mitima yathu. Colinga ca Satana pogwilitsa nchito misampha imene tachulayi, ni kufuna kutilepheletsa kucita zoyenela. Tiyeni tsopano tikambilane mmene tingakanizile misampha ya Satana imeneyi.

TINGACITE CIYANI KUTI TISAGWEDEZEKE?

Kuti mukhalebe osasunthika, muziganizila cifukwa cake munadzipatulila na kubatizika, muziŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkhasinkha, khalani na mtima wosasunthika, komanso mukhulupilileni Yehova (Onani ndime 14-18)

14. N’ciyani cingatithandize kukhalabe kumbali ya Yehova?

14 Ganizilani cifukwa cake munadzipatulila na kubatizika. Munatenga masitepe amenewa pofuna kukhala kumbali ya Yehova. Kumbukilani cimene cinakukhutilitsani kuti mwapeza coonadi. Munaphunzila coonadi ponena za Yehova, ndipo munayamba kukonda Atate wanu wakumwamba, na kum’lemekeza. Cina, munakhala na cikhulupililo ndipo cinakusonkhezelani kulapa. Kenako, munaleka makhalidwe oipa, n’kuyamba kucita zinthu zokondweletsa Mulungu. Mtima wanu unakhala m’malo mutazindikila kuti Mulungu wakukhululukilani. (Sal. 32:1, 2) Kuwonjezela apo, munayamba kupezeka pa misonkhano yacikhristu, na kuuzako ena zinthu zosangalatsa zimene munali kuphunzila. Tsopano monga Mkhristu wobatizika, mukuyenda pa msewu wopita kumoyo, ndipo ndinu wofunitsitsa kuyendabe pa msewuwo.—Mat. 7:13, 14.

15. N’cifukwa ciyani kuŵelenga na kusinkhasinkha n’kopindulitsa?

15 Muziŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkhasinkha. Mtengo umakhala wolimba ngati mizu yake inazikika pansi mozama. Mofananamo, tingakhalebe olimba ngati cikhulupililo cathu n’cozikika mozama m’Mawu a Mulungu. Mtengo ukamakula, mizu yake imaloŵa pansi kwambili na kutambalala. Tikamaŵelenga Baibo na kusinkhasinkha, timalimbitsa cikhulupililo cathu, komanso timakhala otsimikiza kothelatu kuti mfundo za Yehova ndizo zabwino koposa. (Akol. 2:6, 7) Ganizilani mmene malangizo a Yehova, citsogozo, na citetezo cake, cinathandila atumiki ake akale. Mwacitsanzo, Ezekieli anayang’anitsitsa pamene mngelo anali kuyesa kacisi m’masomphenya. Masomphenya amenewo anam’limbikitsa Ezekieli. Ndipo amatiphunzitsa mmene tingatsatilile miyeso ya Yehova pa nkhani ya kulambila koyela. d (Ezek. 40:1-4; 43:10-12) Nafenso timapindula tikamapatula nthawi yoŵelenga na kusinkhasinkha zinthu zozama za m’Mawu a Mulungu.

16. Kodi mtima wosasunthika unam’teteza bwanji m’bale Bob? (Salimo 112:7)

16 Khalani na mtima wosasunthika. Mfumu Davide anaonetsa kuti sadzaleka kukonda Mulungu pamene anaimba kuti: “Mtima wanga wakhazikika, Inu Mulungu.” (Sal. 57:7) Nafenso tingakhale na mtima wosasunthika, na kudalila Yehova na mtima wonse. (Ŵelengani Salimo 112:7.) Izi n’zimene zinathandiza m’bale Bob amene tam’chula uja. Atamuuza kuti adzasunga magazi ena pambali kuti mwina angafunikile, nthawi yomweyo iye anauza dokotalayo kuti ngati akonza zokamuika magazi, sadzacitila mwina koma kutuluka m’cipatala nthawi yomweyo. Patapita nthawi iye anati: “N’natsimikiza mtima kucitadi zimenezo, ndipo sin’nade nkhawa na zimene zinganicitikile.”

Tikakhala na cikhulupililo colimba, tidzakhalabe osasunthika kaya tikumane na mayeso otani (Onani ndime 17)

17. Kodi tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca m’bale Bob? (Onaninso cithunzi.)

17 M’bale Bob sanasunthike cifukwa anali atapangilatu cisankho asanagonekedwe m’cipatala. Coyamba, anali kufuna kukondweletsa Yehova. Caciŵili, anafufuza m’Baibo komanso m’zofalitsa zozikika pa Baibo pa nkhani ya kupatulika kwa moyo na magazi. Ndipo cacitatu, anali wotsimikiza kuti kutsatila citsogozo ca Yehova kumapindulila nthawi zonse. Nafenso tingakhale na mtima wosasunthika mosasamala kanthu na zimene zingaticikile.

Baraki na anthu ake molimba mtima anathamangitsa gulu la asilikali la Sisera (Onani ndime 18)

18. Kodi citsanzo ca Baraki citiphunzitsa ciyani pa nkhani yokhulupilila Yehova? (Onani cithunzi pacikuto.)

18 Muzim’khulupilila Yehova. Baraki anapeza cipambano cifukwa cokhulupilila citsogozo ca Yehova. Mu Isiraeli munalibe zida zomenyela nkhondo. Koma Yehova anauza Baraki kuti akamenye nkhondo na gulu la asilikali acikanani lotsogoleledwa na Sisera, lokhala na zida zankhondo. (Ower. 5:8) Mneneli wamkazi Debora anauza Baraki kuti atsike m’phili, kuti akayang’anizane na Sisera na magaleta ake 900 m’cidikha. Olo kuti Baraki anadziŵa kuti angagonjetsedwe mosavuta pamalo a cidikha amenewo, iye anamvelabe. Pamene Baraki na asilikali ake anali kutsika m’phiri la Tabori, Yehova anagwetsa cimvula. Magaleta a Sisera anatitimila m’matope, ndipo Yehova anapeleka cipambano kwa Baraki. (Ower. 4:1-7, 10, 13-16) Nafenso Yehova adzatipatsa cipambano tikam’khulupilila, na kutsatila citsogozo cimene amapeleka kudzela mwa anthu omuimilako.—Deut. 31:6.

KHALANIBE OLIMBA

19. N’cifukwa ciyani mufuna kukhalabe olimba, osasunthika?

19 Malinga ngati tikukhala m’dziko loipali, tidzapitiliza kumenya nkhondo kuti tikhalabe osasunthika. (1 Tim. 6:11, 12; 2 Pet. 3:17) Conde, tisalole mazunzo, mayeso ovuta kuwazindikila, nzelu za anthu, cinyengo, komanso zoceutsa, kuti zitifooketse. (Aef. 4:14) M’malo mwake, tiyeni tikhalebe olimba pa kudzipeleka kwathu kwa Yehova, komanso osasunthika pomvela malamulo ake. Koma panthawi imodzimodzi, tiyeni tikhale ololela. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana citsanzo cabwino ngako ca Yehova na Yesu pa nkhani ya kukhala ololela.

NYIMBO 129 Tidzapilila Mosalekeza

a Kungocokela m’nthawi ya Adamu na Hava, Satana wakhala akulimbikitsa mfundo yakuti anthu ayenela kusankha okha cabwino kapena coipa. Amafuna kuti tiziyendela mfundo imeneyi ponena za malamulo a Yehova, komanso malangizo a gulu amene timalandila. Nkhani ino itithandiza kupewa mzimu wofala umenewu wa dziko la Satanali. Itithandizanso kukhala otsimikiza mtima kuimabe zolimba ku mbali ya Yehova.

b Kuti mudziŵe zambili za mmene Akhristu angatsatilile lamulo la Mulungu lokhudza magazi, onani phunzilo 39 m’buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!

c Onani nkhani yakuti “Dzitetezeni Kuti Musamapusitsidwe ndi Nkhani Zabodza.” Nkhaniyi ili pa jw.org ku Chichewa.