Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 32

Khalani Ololela Potengela Yehova

Khalani Ololela Potengela Yehova

“Anthu onse adziŵe kuti ndinu ololela.”—AFIL. 4:5.

NYIMBO 89 Mvela Udalitsike

ZIMENE TIKAMBILANE a

Kodi mungakonde kukhala mtengo uti apa? (Onani ndime 1)

1. Kodi Akhristu ayenela kukhala monga mtengo m’njila iti? (Onaninso cithunzi.)

 “CIMPHEMPO sicingathyole mtengo umene umapindika.” Mwambiwu uonetsa kuti kupindika kwa mitengo ina kumaithandiza kupitiliza kukula. Nafenso Akhristu kuti tipitilize kukula kuuzimu tiyenela kukhala ololela, okonzeka kusintha. Tingatelo mwa kusintha nafenso zinthu zikasintha pa umoyo wathu, komanso mwa kulemekeza kapenyedwe ka ena na zisankho zawo.

2. Zinthu zikasintha pa umoyo wathu, ni makhalidwe ati angatithandize kusintha nafenso? Nanga tiphunzilenji m’nkhani ino?

2 Ife atumiki a Yehova, timafuna kukhala ololela. Timafunanso kukhala odzicepetsa komanso acifundo. M’nkhani ino, tiona mmene makhalidwewa anathandizila Akhristu ena kusintha nawonso pamene mikhalidwe inasintha pa umoyo wawo. Tionenso mmene makhalidwewa angatithandizile. Koma coyamba, tiyeni tiphunzile kwa Yehova na Yesu, amene ni zitsanzo zabwino koposa pa nkhani yoonetsa kulolela.

YEHOVA NA YESU NI OLOLELA

3. Tili na umboni wotani woonetsa kuti Yehova ni wololela?

3 Yehova amachedwa “Thanthwe” cifukwa ni wolimba komanso wosasunthika. (Deut. 32:4) Ngakhale n’telo, alinso wololela. Pomwe zocitika m’dzikoli zikusintha, Mulungu wathu akupitiliza kusintha kuti akwanilitse colinga cake. Yehova analenga anthu m’cifanizilo cake kuti iwonso azitha kusintha pamene zinthu zasintha mu moyo wawo. Kupitila m’Baibo, iye anapeleka mfundo zomveka bwino zimene zingatithandize kupanga zisankho zanzelu, kaya tikumane na zopinga zotani. Citsanzo cake na mfundo zimene watipatsazo ni umboni wakuti ngakhale kuti iye ni “Thanthwe,” Yehova ni wololela.

4. Pelekani citsanzo coonetsa kuti Yehova ni wololela. (Levitiko 5:7, 11)

4 Mmene Yehova amacitila zinthu zimaonetsa kuti ni wololela. Saumitsa zinthu pocita zinthu na anthu. Mwacitsanzo, ganizilani mmene Yehova anaonetsela kulolela pocita zinthu na Aisiraeli. Iye sanalamule kuti onse azipeleka nsembe zofanana, kaya munthu ni wosauka kapena wolemela. Nthawi zina, anali kulola kuti munthu aliyense payekha apeleke nsembe mogwilizana na mikhalidwe yake.—Ŵelengani Levitiko 5:7, 11.

5. Fotokozani citsanzo ca kudzicepetsa kwa Yehova na cifundo cake.

5 Kudzicepetsa kwa Yehova na cifundo cake, zimamulimbikitsa kukhala wololela. Mwacitsanzo, kudzicepetsa kwa Yehova kuonaonekela bwino atatsala pang’ono kuwononga anthu oipa a mu Sodomu. Kupitila mwa angelo ake, Yehova anauza munthu wolungama Loti kuti athaŵile kumapili. Koma Loti anaopa kupita kumeneko. Conco, anacondelela Mulungu kuti amulole pamodzi na banja lake kuti athaŵile mu mzinda waung’ono wa Zowari, umene unayenelanso kuwonongedwa. Yehova akanafuna akanaumilila ndithu kuti Loti angotsatila malangizowo ndendende. Koma m’malo mwake, iye anamva pempho la Loti, ngakhale kuti izi zinatanthauza kusawononga mzinda wa Zowari. (Gen. 19:18-22) Patapita zaka mahandiledi, Yehova anaonetsa cifundo kwa anthu a ku Nineve. Anatuma mneneli Yona kukalengeza kuti mzindawo pamodzi na anthu oipa okhala mmenemo adzawonongedwa. Koma anthu a ku Nineve atalapa, Yehova anawamvela cisoni, ndipo sanauwononge mzindawo.—Yona 3:1, 10; 4:10, 11.

6. Fotokozani zitsanzo zoonetsa mmene Yesu anatengela citsanzo ca Yehova ca kulolela.

6 Yesu anatengela citsanzo ca Yehova ca kulolela. Iye anatumidwa padziko lapansi kudzalalikila “kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.” Koma anaonetsa kulolela pocita utumiki wakewo. Panthawi ina, mayi wina amene sanali Mwisiraeli anam’condelela kuti acilitse mwana wake wamkazi, amene anali ‘atagwidwa ndi ciwanda mocititsa mantha.’ Mwacifundo, Yesu anacita zimene mayiyo anam’pempha ndipo anam’cilitsa mwanayo. (Mat. 15:21-28) Naci citsanzo cina. Ca kumayambililo kwa utumiki wake, Yesu ananena kuti: “Aliyense wondikana . . . , inenso ndidzamukana.” (Mat. 10:33) Iye anakanidwa katatu na Petulo. Koma kodi Yesu anam’kana Petulo? Ayi. Yesu anaona kulapa na cikhulupililo ca Petulo. Pambuyo poukitsidwa, Yesu anaonekela kwa Petulo. Ndipo mwacionekele, anam’tsimikizila kuti anam’khululukila komanso kuti anali kum’kondabe.—Luka 24:33, 34.

7. Mogwilizana na Afilipi 4:5, kodi timafuna kukhala na mbili yotani?

7 Pofika pano, taona kuti Yehova Mulungu na Yesu Khristu ni ololela. Nanga bwanji ife? Afilipi 4:5 imaonetsa kuti Yehova amafuna kuti nafenso tikhale ololela. (Ŵelengani.) Baibo ina inamasulila vesiyi kuti: “Khalani na mbili yoti ndinu munthu wololela.” Tingadzifunse kuti: ‘Kodi anthu amanidziŵa kuti ndine munthu wololela? Kapena amanidziŵa kuti ndine woumitsa zinthu, wokhwimitsa zinthu, kapena wa zimene ndanena-ndanena? Kodi nimaumiliza ena kucita ndendende zimene ine niona kuti ndiye zoyenela? Kapena nimamvako za ena na kulolela kuti zinthu zicitike mmene iwo afunila ngati n’kotheka?’ Tikamaonetsa kwambili kulolela, timaonetsanso kuti tikutengela kwambili Yehova na Yesu. Tiyeni tikambilane mbali ziŵili zimene zimafuna kulolela. Yoyamba, zinthu zikasintha pa umoyo wathu. Yaciŵili, malingalilo komanso zisankho za ena zikasiyana na zathu.

KHALANI WOLOLELA MIKHALIDWE IKASINTHA

8. N’ciyani cingatithandize kukhala ololela mikhalidwe ikasintha? (Onaninso mawu a m’munsi.)

8 Munthu wololela amakhala wokonzeka kusintha pamene mikhalidwe yasintha. Zinthu zikasintha, tingakumane na mavuto amene sitinawayembekezele. Mwacitsanzo, tingadwale mwadzidzidzi. Mwina kusintha mosayembekezela kwa zacuma kapena zandale, kungapangitse umoyo wathu kukhala wovuta kwadzaoneni. (Mlal. 9:11; 1 Akor. 7:31) Ngakhale kusinthidwa pa udindo, utumiki, kapena malo otumikilako kungatiike pa mayeso. Mosasamala kanthu za copinga cathu, tikhoza kusintha mogwilizana na mikhalidwe yathu yatsopano ngati tatsatila masitepe anayi otsatilawa: (1) civomelezeni kuti zinthu zasintha, (2) yang’anani kutsogolo, (3) muziika maganizo anu pa zinthu zolimbikitsa, komanso (4) muzithandiza ena. b Tiyeni tioneko mmene ena mwa abale na alongo athu apindulila potsatila masitepe amenewa.

9. Kodi banja lina la amishonale linakwanitsa bwanji kupilila, mikhalidwe itasintha mwadzidzidzi?

9 Civomelezeni kuti zinthu zasintha. M’bale Emanuele na mkazi wake Francesca anatumidwa ku dziko lina monga amishonale. Atangoyamba kukhazikika mu mpingo wawo watsopano na kuphunzila cinenelo, mlili wa COVID-19 unabuka ndipo anafunika kukhala kwa okha. Mwatsoka lanji, amayi ake Francesca anamwalila mwadzidzidzi. Iye anafunitsitsa kukhala pamodzi na banja lawo, koma mlili unamulepheletsa kupita kwawo. Kodi anazipilila motani zocitika zolefula zimenezi? Coyamba, iwo monga banja, anapempha nzelu kwa Mulungu kuti iwathandize kusada nkhawa na za maŵa, koma azingothana na nkhawa za tsiku limodzi. Yehova anayankha mapemphelo awo mwa kupeleka thandizo la pa nthawi yake kupitila m’gulu lake. Mwacitsanzo, iwo analimbikitsidwa kwambili na zimene m’bale wina ananena mu vidiyo ina kuti: “Tikavomeleza msanga kuti zinthu zasintha pa umoyo wathu, mwamsanga timakhalanso acimwemwe. Ndipo timapeza mipata yokhalila umoyo wopindulitsa m’mikhalidwe yatsopano.” c Caciŵili, iwo analimbikitsidwa kuyamba kunola maluso awo pa ulaliki wa pafoni, ndipo anafika poyambitsa phunzilo la Baibo. Cacitatu, iwo anavomela kulandila thandizo na cilimbikitso kucokela kwa abale na alongo a m’dziko limene anali kukhala. Mlongo wina woganizila ena anali kuwatumizila kauthenga kacidule tsiku lililonse kwa caka, kokhala na vesi ya m’Baibo. Nafenso tikavomeleza kuti zinthu zasintha, tidzatha kupeza cimwemwe pa zilizonse zimene takwanitsa kucita.

10. Kodi mlongo wina anasintha motani atakumana na masinthidwe aakulu?

10 Yang’anani kutsogolo, ndipo ikani maganizo anu pa zinthu zolimbikitsa. Mlongo Christina wocokela ku Romania amene akhala ku Japan anakhumudwa mpingo wawo wa Cizungu utathetsedwa. Komabe, sanangokhalila kuganizila zinacitikazo. M’malo mwake, anacita zonse zotheka kuti apite patsogolo mu mpingo wa kumeneko wolankhula ci Japanese, mwa kutengako mbali mokwanila m’nchito yolalikila m’gawo limenelo. Anapempha mayi wina amene anali kugwila naye nchito kumbuyoko, kuti am’thandize kucidziŵa bwino ci Japanese. Mayiyo analola kugwilitsa nchito Baibo na kabuku kakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! pom’phunzitsa. Mlongo Christina anayamba kucidziŵa bwino ci Japanese, ndipo mayiyo anayamba kuonetsa cidwi pa coonadi. Tikamayang’ana kutsogolo na kuganizila zinthu zolimbikitsa, masinthidwe a mwadzidzidzi angatibweletsele madalitso amene sitinawayembekezele.

11. Kodi banja lina linathana nawo bwanji mavuto a zacuma?

11 Thandizani ena. Banja lina ku dziko limene nchito yathu inatsekedwa, linayamba kuvuta kupeza ndalama cuma ca dzikolo citaloŵa pansi. Kodi anapanga masinthidwe otani? Iwo anayamba kukhala umoyo wosalila zambili. Cina, m’malo moika maganizo pa mavuto awo, anayamba kuganizila kwambili mmene angathandizile ena, mwa kutangwanika na nchito yolalikila. (Mac. 20:35) Mutu wa banjalo anati, “Kuthela nthawi yoculuka mu ulaliki kunatithandiza kuika maganizo athu pa kucita cifunilo ca Mulungu, m’malo moganizila zinthu zofooketsa.” Zinthu zikasintha pa umoyo wathu, kuthandizabe ena n’kofunika kwambili, maka-maka mwa kulalikila.

12. Kodi citsanzo ca mtumwi Paulo cingatithandize bwanji kukhala okhoza kusintha ulaliki?

12 Tizikhala ololela pa utumiki wathu. Timakumana na anthu a zikhulupililo na maganizo osiyana-siyana, komanso ocokela kosiyana-siyana. Mtumwi Paulo anali wololela, ndipo tingatengeleko citsanzo cake. Yesu anaika Paulo kukhala ‘mtumwi wotumidwa kwa mitundu ina.’ (Aroma 11:13) Pa utumiki wake umenewo, Paulo analalikila kwa Ayuda, Agiriki, anthu ophunzila, alimi osauka, anyanchito a boma, komanso mafumu. Kuti awafike pa mtima anthu onsewo, Paulo ‘anakhala zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana.’ (1 Akor. 9:19-23) Poganizila cikhalidwe na zikhulupililo za anthu amene anali kuwalalikila, mtumwi Paulo anasintha njila yolalikila. Nafenso tingakhale alaliki ogwila mtima tikamakhala okonzeka kusintha ulaliki wathu kuti ugwilizane na munthu amene tapeza.

MUZILEMEKEZA MAGANIZO A ANTHU ENA

Tikakhala ololela timalemekeza maganizo a ena (Onani ndime 13)

13. Malinga na 1 Akorinto 8:9, kodi tidzapewa ciyani tikamalemekeza maganizo a ena?

13 Kukhala wololela kumatithandiza kulemekeza maganizo a anthu ena. Mwacitsanzo, alongo athu ena amakonda kuphauda pamene ena satelo. Akhristu ena amamwako moŵa mwacikatikati pamene ena amaupewelatu. Akhristu onse amafuna kukhala na thanzi labwino, koma amasankha njila zosiyana za cithandizo ca mankhwala. Ngati timaona kuti kapenyedwe kathu ndiye kabwino nthawi zonse, ndipo timalimbikitsa ena kutengela kapenyedwe kathuko, tingakhale copunthwitsa kwa ena, ndipo tingabweletse magaŵano mu mpingo. Sitifuna ngakhale pang’ono kucita zimenezi! (Ŵelengani 1 Akorinto 8:9; 10:23, 24) Tiyeni tsopano tikambilane zitsanzo ziŵili zimene zionetsa kuti kutsatila mfundo za m’Baibo kungatithandize kukhala ololela na kukhazikitsa mtendele.

Tikakhala ololela timalemekeza maganizo a ena (Onani ndime 14)

14. Ni mfundo ziti za m’Baibo zimene ziyenela kutitsogolela pa nkhani ya mavalidwe na kudzikongoletsa?

14 Mavalidwe na kudzikongoletsa. Yehova sanacite kutichulila kuti tizivala zakuti-zakuti. M’malo mwake, anangotipatsa mfundo zoyenela kutsatila. Tiyenela kuvala m’njila yoyenela atumiki a Mulungu, yoonetsa kuti ndife oganiza bwino, aulemu komanso ‘anzelu.’ (1 Tim. 2:9, 10; 1 Pet. 3:3) Cotelo, sitivala m’njila yoti anthu ena azingoti maso dwii pa ife. Mfundo za m’Baibo zingathandizenso akulu kupewa kuika malamulo awo-awo pa nkhani ya mavalidwe na kudzikongoletsa. Mwacitsanzo, mu mpingo wina, akulu anafuna kuthandiza acinyamata omwe anatengela kakonzedwe ka tsitsi kofala. Amakhala na tsitsi lalifupi koma losapesa. Kodi akulu akanawathandiza motani anyamatawo popanda kuwaikila malamulo? Woyang’anila dela anauza akulu kuti akakambilane na abalewo mfundo iyi, “Ngati muli pa pulatifomu ndipo omvetsela akuganizila kwambili za maonekedwe anu m’malo mwa zimene mukunena, ndiye kuti kavalidwe kanu na kudzikongoletsa kwanu n’kolakwika.” Kafotokozedwe kacidule kameneka kanathetsa nkhani imeneyo popanda kuika lamulo. d

Tikakhala ololela timalemekeza maganizo a ena (Onani ndime 15)

15. Kodi m’Baibo muli malamulo na mfundo zotani zotithandiza posankha mankhwala? (Aroma 14:5)

15 Cithandizo camankhwala. Mkhristu aliyense ayenela kusankha mmene angasamalile thanzi lake. (Agal. 6:5) Pali malamulo ocepa cabe okhudza cithandizo camankhwala amene Mkhristu ayenela kutsatila, monga kupewa magazi na zamizimu. (Mac. 15:20; Agal. 5:19, 20) Koma mbali zina zonse ni nkhani ya munthu mwini. Anthu ena amavomela thandizo lacipatala cabe, pomwe ena amasankha njila zina osati zakucipatala. Ngakhale titaona kuti cithandizo cinacake camankhwala ndico cabwino koposa, tiyenela kulemekeza ufulu wa ena wodzisankhila pa nkhani imeneyi. Cotelo, tiyenela kukumbukila mfundo zinayi izi: (1) Ni Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetselatu matenda. (Yes. 33:24) (2) Mkhristu aliyense ayenela kukhala “wotsimikiza ndi mtima wonse” zimene zili zothandiza kwa iye. (Ŵelengani Aroma 14:5) (3) Sitiyenela kuweluza ena kapena kuwaikila copunthwitsa. (Aroma 14:15, 19, 20) (4) Akhristu ayenela kuonetsana cikondi, ndipo amaona mgwilizano wa mu mpingo kukhala wofunika kwambili kuposa ufulu wawo wodzisankhila pa nkhani za munthu mwini. (Aroma 14:15, 19, 20) Tikamakumbukila mfundozi, timakhala ogwilizana kwambili na abale na alongo athu, ndipo timalimbikitsa mtendele mu mpingo.

Tikakhala ololela timalemekeza maganizo a ena (Onani ndime 16)

16. Kodi mkulu angaonetse bwanji kulolela pocita zinthu na akulu anzake? (Onaninso zithunzi.)

16 Akulu ayenela kukhala citsanzo cabwino pa nkhani yololela. (1 Tim. 3:2, 3) Mkulu sayenela kuganiza kuti nthawi zonse malingalilo ake ayenela kutsatilidwa cabe cifukwa ni wamkulu msinkhu kuposa akulu ena. Iye amazindikila kuti mzimu wa Yehova ungatsogolele mkulu aliyense kupeleka lingalilo limene lingathandize kupanga cigamulo canzelu. Ndipo ngati palibe mfundo iliyonse ya m’Baibo imene yanyalanyazidwa, mkulu wololela amavomeleza na mtima wonse cigamulo ca ambili pa bungwepo, ngakhale kuti anali na lingalilo losiyana.

MAPINDU A KUKHALA WOLOLELA

17. Kodi Akhristu ololela amapeza madalitso otani?

17 Akhristufe timapeza madalitso ambili tikakhala ololela. Mwacitsanzo, timakhala nawo pa ubale wabwino abale na alongo athu, ndipo mu mpingo mumakhala mtendele. Cina, n’kosangalatsa kukhala na maumunthu osiyana-siyana, komanso zikhalidwe zosiyana-siyana pakati pa alambili a Yehova ogwilizana. Ndipo koposa zonse, timakhala acimwemwe podziŵa kuti tikutengela Yehova, Mulungu wathu wololela.

NYIMBO 90 Tilimbikitsane Wina na Mnzake

a Yehova na Yesu ni ololela, ndipo iwo amafuna kuti nafenso tikulitse khalidwe limeneli. Tikatelo, cidzakhala cosavuta ifenso kusintha pamene zinthu zasintha pa umoyo wathu, monga tikayamba kudwala kapena zacuma zikavuta. Tikakhala ololela tingalimbikitsenso mtendele na mgwilizano mu mpingo.

b Onani nkhani yakuti “Zimene Mungachite Zinthu Zikasintha” mu Galamukani! ya Na. 4 2016.

c Onelelani vidiyo yakuti Kufunsa Mafunso M’bale Dmitriy Mikhaylov imene inali m’nkhani yakuti “Yehova Amasintha Cizunzo Kukhala Njila Yocitila Umboni” mu Kabuku ka Misonkhano ka Umoyo na Utumiki Wathu wa Cikhristu ka March-April 2021.

d Kuti mudziŵe zambili zokhudza mavalidwe na kudzikongoletsa, onani phunzilo 52 mu buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!