Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 29

Kodi Mwacikonzekela Cisautso Cacikulu?

Kodi Mwacikonzekela Cisautso Cacikulu?

“Khalani okonzeka.”—MAT. 24:44.

NYIMBO 150 Funani Cipulumutso ca Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. N’cifukwa ciyani ni canzelu kukonzekela matsoka?

 KUKONZEKELA kumapulumutsa miyoyo. Mwacitsanzo, tsoka la zacilengedwe likacitika, anthu amene analikonzekela tsokalo kambili ndiwo amapulumuka na kuthandizako anthu ena. Bungwe lina ku Europe lothandiza anthu linati: “Munthu akakonzekela, zimamuyendelako bwino.”

2. N’cifukwa ciyani tiyenela kucikonzekela cisautso cacikulu? (Mateyu 24:44)

2 “Cisautso cacikulu” cidzayamba mwadzidzidzi. (Mat. 24:21) Mosiyana na matsoka ena, kwa ife atumiki a Mulungu cisautso cacikulu sicidzatidzidzimutsa ayi. Tikutelo cifukwa zaka pafupi-fupi 2,000 zapitazo, Yesu anauza otsatila ake kuti akhale okonzeka za tsikulo. (Ŵelengani Mateyu 24:44.) Tikakhala okonzeka, cidzakhala capafupi kuipilila nthawi yovuta kwambili imeneyo, komanso kuthandizako ena kucita cimodzimodzi.—Luka 21:36.

3. Kodi kupilila, cifundo, na cikondi, zingatithandize bwanji kukonzekela cisautso cacikulu?

3 Kuti ticikonzekele cisautso cacikulu, pali makhalidwe atatu amene tiyenela kukhala nawo. Kodi tidzacita motani akadzatipempha kuti tiyambe kulengeza uthenga woŵaŵa wa ciweluzo, ndipo anthu akutitsutsa? (Chiv. 16:21) Tidzafunikila khalidwe la kupilila kuti tikamvele Yehova, na kum’khulupilila kuti adzatiteteza. Kodi tidzacita ciyani abale athu akadzataikilidwa zina mwa zinthu zawo zakuthupi kapena zonse? (Hab. 3:17, 18) Tidzafunikila khalidwe la cifundo limene lidzatilimbikitsa kukapeleka thandizo lofunikila kwa iwo. Kodi tidzacita bwanji tikadzafunika kukhalila pamodzi na abale na alongo athu cifukwa coukilidwa na mgwilizano wa mitundu? (Ezek. 38:10-12) Tidzafunikila cikondi cacikulu kuti tikawathandize kupilila nthawi yovuta imeneyo.

4. Kodi Baibo imaonetsa bwanji kuti sitiyenela kuleka kukulitsa makhalidwe a kupilila, cifundo, na cikondi?

4 Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kusaleka kukulitsa makhalidwe a kupilila, cifundo, na cikondi. Luka 21:19 imati: “Ngati inu mudzapilile, mudzapeza moyo.” Akolose 3:12 nayonso imati: “Valani . . . cifundo cacikulu.” Ndipo 1 Atesalonika 4:9, 10 imati: “Mulungu amakuphunzitsani kukondana. . . . Koma tikukudandaulilani abale kuti mupitilize kutelo mowonjezeleka.” Malembawa analembela ophunzila omwe anali kuonetsa kale kupilila, cifundo, na cikondi. Komabe, anayenela kupitiliza kukulitsa makhalidwe amenewa. Nafenso tiyenela kucita cimodzimodzi. Tiyeni tsopano tikambilane mmene Akhristu oyambilila anaonetsela makhalidwewa. Kenaka, tiona mmene tingatengele citsanzo cawo, kuti tionetse kuti tacikonzekela cisautso cacikulu.

KULITSANI KHALIDWE LA KUPILILA

5. Kodi Akhristu oyambilila anacita ciyani kuti apilile mayeso?

5 Akhristu oyambilila anafunikila kupilila. (Aheb. 10:36) Kuwonjezela pa kukumana na mavuto amene amagwela anthu onse, iwo anakumananso na mavuto ena. Ambili a iwo anazunzidwa na atsogoleli acipembedzo aciyuda mu ulamulilo wa Aroma. Anazunzidwanso na mabanja awo enieni. (Mat. 10:21) Cina, anayenela kuonetsetsa kuti akupewa ziphunzitso zabodza za ampatuko, amene anali kufuna kubweletsa magaŵano mu mpingo. (Mac. 20:29, 30) Akhristuwo anapilila zinthu zonsezi mokhulupilika. (Chiv. 2:3) Motani? Iwo anasinkhasinkha zitsanzo za m’Malemba za anthu amene anapilila, monga Yobu. (Yak. 5:10, 11) Anapemphelanso kwa Mulungu kuti awalimbitse mtima. (Mac. 4:29-31) Cina, iwo anaganizila madalitso omwe adzapeza akakhalabe opilila.—Mac. 5:41.

6. Kodi muphunzilapo ciyani pa zimene mlongo Merita anacita kuti apilile citsutso?

6 Nafenso tingakulitse khalidwe la kupilila, tikamaŵelenga na kusinkhasinkha zitsanzo za kupilila zopezeka m’Baibo, komanso m’zofalitsa zathu. Mwa kutelo, mlongo Merita wa ku Albania anakwanitsa kupilila pamene acibale ake anali kumutsutsa kwambili. Iye anati: “Kuŵelenga nkhani ya Yobu kunanilimbikitsa zedi. Yobu anavutika kwadzaoneni, olo kuti sanadziŵe cimene cinali kucititsa mayeso ake. Ngakhale n’telo, iye anakamba kuti: “Mpaka ine kumwalila, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika!” (Yobu 27:5) N’naona kuti mayeso a Yobu anali aakulu kuposa anga. Ndipo mosiyana na Yobu, ine n’namudziŵa wocititsa mavuto anga.”

7. Ngakhale kuti pali pano sitikukumana na mavuto aakulu, kodi tiyenela kucitabe ciyani?

7 Cina cimene tingacite kuti tikhale opilila, ni kupemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima nthawi zonse, na kumuuza nkhawa zathu. (Afil. 4:6; 1 Ates. 5:17) N’kutheka kuti pali pano simukukumana na mayeso aakulu. Ngakhale n’telo, muyenela kupemphabe citsogozo kwa Yehova mukakhumudwa kapena kuthedwa nzelu. Ngati pali pano mumatembenukila kwa Mulungu kuti akuthandizeni pa zovuta za tsiku na tsiku, simudzazengeleza kukacita zimenezo mukadzakumana na mavuto aakulu m’tsogolomu. Ndipo mudzakhala wotsimikiza kuti iye amadziŵa nthawi yabwino yokuthandizani, komanso mmene angacitile zimenezo.—Sal. 27:1, 3.

KUPILILA

Kupilila mayeso pali pano kumatikonzekeletsa kudzapilila mayeso m’tsogolomu (Onani ndime 8)

8. Kodi citsanzo ca mlongo Mira cionetsa bwanji kuti kupilila mayeso pali pano, kungatithandize kudzapililanso mayeso m’tsogolomu? (Yakobo 1:2-4) (Onaninso cithunzi.)

8 Tikamapilila mavuto pali pano, tingadzapililenso cisautso cacikulu m’tsogolomu. (Aroma 5:3) N’cifukwa ciyani tikutelo? Abale na alongo athu ambili aona kuti akapilila mayeso oyesa cikhulupililo cawo, amatha kupililanso ena. Kupilila kumawayenga na kulimbitsa cidalilo cawo cakuti Yehova ni wokonzeka komanso wofunitsitsa kuwathandiza. Ndipo cidaliloco cimawathandiza kupilila mayeso alionse. (Ŵelengani Yakobo 1:2-4.) Mlongo Mira wa ku Albania, amene ni mpainiya, waona kuti kupilila mavuto kumene anacita kumbuyoku kwam’thandiza kupitilizabe kupilila. Iye anati nthawi zina amaona ngati ndiye yekha amene ali na mavuto ambili. Koma akakumbukila zimene Yehova wam’citila pa zaka 20 zapitazo, amadziuza kuti: ‘Pitiliza kukhala wokhulupilika. Usalole kuti kupilila kumene wacita pa zaka zonsezo mwa thandizo la Yehova kupite pacabe.’ Inunso mungaganizile mmene Yehova wakuthandizilani kuti mupilile. Ndipo dziŵani kuti mukapilila vuto lililonse, iye amaona ndipo adzakufupani. (Mat. 5:10-12) Ndiyeno cisautso cacikulu cikadzayamba, mudzakhala mutaphunzila kupilila, ndipo mudzakhala wofunitsitsa kupililabe.

ONETSANI CIFUNDO

9. Kodi mpingo wa ku Antiyokeya unaonetsa bwanji cifundo?

9 Onani zinacitika pamene Akhristu ku Yudeya anali pa njala yadzaoneni. Mpingo wa ku Antiokeya wa ku Siriya utamva za njalayo, mwacionekele anawamvela cifundo abale awo ku Yudeya. Conco, anacitapo kanthu kuti awathandize. Iwo “anatsimikiza mtima kutumiza thandizo lililonse limene akanatha kwa abale okhala ku Yudeya.” (Mac. 11:27-30) Ngakhale kuti okhudzidwa na njala anali kukhala kutali kwambili na ku Antiyokeya, Akhristu a ku Antiyokeya anapelekabe thandizo kwa abale awo.—1 Yoh. 3:17, 18.

CIFUNDO

Matsoka a zacilengedwe amatipatsa mpata woonetsa cifundo (Onani ndime 10)

10. Kodi tingawaonetse motani cifundo alambili anzathu tsoka likawagwela? (Onaninso cithunzi.)

10 Nafenso tingawacitile cifundo alambili anzathu tikamva kuti tsoka lawagwela. Timacitapo kanthu mwamsanga, mwina mwa kufunsa akulu ngati tingadzipeleke kukathandizila. Cina, timapanga zopeleka pa nchito ya padziko lonse, kapena timapemphelela omwe akumana na tsokalo. b (Miy. 17:17) Mwacitsanzo, mu 2020, Makomiti Othandizila Pakagwa Tsoka opitilila 950 anakhazikitsidwa padziko lonse kuti asamalile okhudzidwa na mlili wa COVID-19. Timawayamikila kwambili abale na alongo athu amene amagwila nchito yopeleka thandizo imeneyo. Cifundo n’cimene cimawasonkhezela kukapeleka thandizo lakuthupi, lauzimu, komanso nthawi zina kumanga kapena kukonzanso nyumba zawo, kuphatikizapo malo awo olambilila.—Yelekezelani na 2 Akorinto 8:1-4.

11. Kodi nchito za cifundo zimalemekeza bwanji Atate wathu wakumwamba?

11 Tikaonetsa cifundo abale pa nthawi ya tsoka, anthu ena amaona kudzimana kwathu. Mwacitsanzo, mu 2019, namondwe wa Dorian unawononga Nyumba ya Ufumu ku Bahamas. Pamene abale athu anali kumanganso Nyumba ya Ufumuyo, anafunsa mwini kampani ina ya zomanga-manga, kuti awauze ndalama zimene angamulipile kuti awathandize pa nchito inayake. Munthuyo anati: “Nidzangokupatsani . . . zipangizo, katundu wogwilitsa nchito, ndipo n’zakugwililani ulele nchitoyo. . . . Ningofuna kuthandiza gulu lanu. Nakhudzika mtima na cikondi cimene mwaonetsa mabwenzi anu.” Anthu oculuka m’dzikoli sam’dziŵa Yehova. Koma ambili a iwo amaona zocita za Mboni za Yehova. N’zokondweletsa kwambili kudziŵa kuti nchito zathu za cifundo, zimakokela anthu kwa Yehova, amene ni “wacifundo coculuka.”—Aef. 2:4.

12. Kodi kukulitsa khalidwe la cifundo pali pano kumatikonzekeletsa bwanji cisautso cacikulu? (Chivumbulutso 13:16, 17)

12 N’cifukwa ciyani tidzafunika kuonetsa cifundo pa cisautso cacikulu? Baibo imaonetsa kuti amene sakhalila mbali m’zandale, adzakumana na zovuta panthawi ino, komanso pa cisautso cacikulu. (Ŵelengani Chivumbulutso 13:16, 17.) Abale na alongo athu angadzafunikile thandizo kuti apeze zofunikila pa umoyo. Mfumu yathu Khristu Yesu akadzabwela kudzaweluza anthu, tikufuna adzatipeze tikuonetsa cifundo, na kutiuza kuti “loŵani mu Ufumu.”—Mat. 25:34-40.

KULITSANI CIKONDI CANU

13. Malinga na Aroma 15:7, kodi Akhristu oyambilila anakulitsa bwanji cikondi pakati pawo?

13 Akhristu oyambilila anali kudziŵika na khalidwe la cikondi. Koma kodi cinali capafupi kuonetsa cikondi? Akhristu mu mpingo wa ku Roma anali osiyana mitundu na zikhalidwe. Munali Ayuda amene anali kutsatila Cilamulo ca Mose cibadwileni. Munalinso anthu amitundu ina amene cikhalidwe cawo cinali cosiyana kwambili na ca Ayuda. N’kutheka kuti Akhristu ena anali akapolo, pomwe ena anali mfulu. Mwinanso ena anali na akapolo owatumikila. Kodi Akhristuwo akanatani kuti akulitse cikondi pakati pawo mosasamala kanthu za kusiyana zikhalidwe? Mtumwi Paulo anawalimbikitsa kuti: “Landilanani.” (Ŵelengani Aroma 15:7.) Kodi anatanthauzanji? Liwu lomasulidwa kuti “kulandila” litanthauza kuceleza munthu mokoma mtima, monga kum’landila m’nyumba mwathu kapena pakati pa mabwenzi athu. Mwacitsanzo, Paulo anauza Filimoni mmene ayenela kulandilila Onesimo, kapolo amene anamuthaŵa. Anamuuza kuti: “Umulandile ndi manja awili.” (Filim. 17) Komanso, Purisikila na Akula analandila Apolo, amene sanali kudziŵa zambili zokhudza Cikhristu, pom’tenga n’kukhala naye. (Mac. 18:26) Akhristuwo sanalole kuti kusiyana zikhalidwe kuwagaŵanitse. M’malo mwake, anali kulandilana.

CIKONDI

Tifunikila cikondi ca abale na alongo athu onse (Onani ndime 15)

14. Kodi mlongo Anna na mwamuna wake anaonetsa bwanji cikondi?

14 Nafenso tingawaonetse cikondi abale na alongo athu pokhala nawo pa ubwenzi. Tikatelo, nawonso adzationetsa cikondi. (2 Akor. 6:11-13) Citsanzo ni mlongo Anna na mwamuna wake. Atasamukila kum’mwela kwa Africa monga amishonale, mlili wa COVID-19 unabuka. Sanathe kuonana na abale komanso alongo pamasom’pamaso kuti adziŵane bwino. Koma kodi banjali likanatha bwanji kuonetsa cikondi? Kupitila pa vidiyokonfalensi, anali kuceza na abale na alongo, na kuwauza kuti anali kufunitsitsa kudziŵana nawo bwino. Mabanja analimbikitsidwa na cikondi ca amishonalewo, moti kambili anali kuwatumila foni na kuwalembela mauthenga. Nanga n’cifukwa ciyani amishonalewo anayesetsa kudziŵana nawo abale na alongo? Mlongo Anna anati, “Sinidzaiŵala cikondi cimene abale na alongo anationetsa panthawi zovuta komanso zabwino. Citsanzo cawo cimanilimbikitsa kuonetsa cikondi.”

15. Kodi mwaphunzila ciyani kwa mlongo Vanessa pa nkhani yokonda abale na alongo athu onse? (Onaninso cithunzi.)

15 Ambili tili m’mipingo muli abale na alongo a zikhalidwe zosiyana-siyana, komanso zibadwa zosiyana-siyana. Tingakulitse cikondi cathu kwa onsewo mwa kuyang’ana kwambili pa makhalidwe awo abwino. Mlongo Vanessa wa ku New Zealand, cinali kumuvuta kugwilizana na anthu ena mu mpingo mwawo. M’malo mowapewa anthu amene umunthu wawo sunali kum’kondweletsa, anayamba kuceza nawo kwambili. Kucita izi kunam’thandiza kuona zimene Yehova amakonda mwa anthuwo. Iye anati: “Mwamuna wanga cikhalileni woyang’anila dela, takhala tikucita zinthu na abale komanso alongo a zibadwa zosiyana-siyana, ndipo sinimavutika kugwilizana nawo. Tsopano nimasangalala na anthu a zikhalidwe zosiyana-siyana. Mwacionekele, Yehova nayenso amasangalala, cifukwa ndiye anatikokela m’gulu la anthu a zikhalidwe zosiyana-siyana limeneli.” Tikamaona ena mmene Yehova amawaonela, timaonetsa kuti timawakonda.—2 Akor. 8:24.

Pa cisautso cacikulu, Yehova adzatiteteza tikapitilizabe kum’lambila pamodzi na Akhristu anzathu (Onani ndime 16)

16. N’cifukwa ciyani cikondi cidzakhala cofunika kwambili pa cisautso cacikulu? (Onaninso cithunzi.)

16 Pa cisautso cacikulu, cikondi cidzakhala cofunika kwambili. Kodi n’kuti kumene tidzapeza citetezo cisautsoco cikadzayamba? Onani malangizo amene Yehova anauza atumiki ake Babulo wakale ataukilidwa. Iye anawauza kuti: “Inu anthu anga, pitani mukaloŵe m’zipinda zanu zamkati ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Zioneka kuti malangizo amenewa adzagwilanso nchito kwa ife pa cisautso cacikulu. “Zipinda zamkati” zingaimile mipingo yathu. Pa cisautso cacikulu, Yehova adzatiteteza tikapitilizabe kum’lambila pamodzi na Akhristu anzathu. Cotelo, tiyenela kuyesetsa pali pano kukulitsa cikondi pa abale na alongo athu. Cipulumutso cathu cingadzadalile cikondi cathu pa iwo.

KONZEKELANI PALI PANO

17. Tikakonzekela pali pano, kodi tidzatha kucita ciyani pa cisautso cacikulu?

17 “Tsiku lalikulu la Yehova” lidzakhala nthawi yovuta kwa anthu. (Zef. 1:14, 15) Nawonso atumiki a Yehova adzakumana na mavuto. Koma tikakonzekela pali pano, tidzakhalabe odekha na kuthandiza anthu ena. Tidzatha kupilila mavuto alionse amene tingadzakumane nawo. Okhulupilila anzathu akadzakumana na mavuto, tidzawaonetsa cifundo popeleka thandizo lofunikila kwa iwo. Ndipo tikaphunzila kuonetsa cikondi abale na alongo athu pali pano, cidzakhala capafupi kudzagwilizana nawo kwambili pa nthawi zovuta m’tsogolomu. Pamapeto pake, Yehova adzatifupa potipatsa moyo wosatha m’dziko limene matsoka na masautso adzakhala mbili yakale.—Yes. 65:17.

NYIMBO 144 Yang’ana pa Mphoto

a Cisautso cacikulu cidzayamba posacedwa. Makhalidwe monga kupilila, cifundo, na cikondi, adzatithandiza kukonzekela nthawi yovuta kwambili imeneyo m’mbili yonse ya anthu. Tiona mmene Akhristu oyambilila anakulitsila makhalidwe amenewa, mmene tingatengele citsanzo cawo, komanso mmene makhalidwewa angatithandizile kukonzekela cisautso cacikulu.

b Amene afuna kugwilako nchito yothandizila pakagwa tsoka, ayenela kulemba Fomu Yofunsila Kucilikiza Nchito za Cimango (DC-50) kapena Fomu Yofunsila Utumiki Wodzipeleka (A-19). Ayenela kuyembekezela kufikila ataitanidwa.