Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Kuonetsa Ena Cidwi Kumabweletsa Madalitso Okhalitsa

Kuonetsa Ena Cidwi Kumabweletsa Madalitso Okhalitsa

Ine, amayi, na mlongosi wanga Pat, mu 1948

“CHALICHI ca Anglican siciphunzitsa coonadi. Pitiliza kufuna-funa coonadi.” Ambuye ŵanga amene anali m’chalichi ca Anglican atanena zimenezi, amayi anayamba kufuna-funa cipembedzo coona. Komabe, iwo anali kupewa Mboni za Yehova, ndipo anali kuniuza kuti nibisale akabwela pa nyumba pathu ku Toronto, ku Canada. Koma amayi aang’ono atayamba kuphunzila Baibo na Mboni mu 1950, amayi anga nawonso anayamba kuphunzila. Iwo anali kuphunzilila kunyumba kwa amayi aang’onowo. Ndipo patapita nthawi anabatizika.

Atate anali na m’busa m’chalichi ca United Church of Canada. Conco, m’mawa uliwonse pa Sondo, anali kutumiza ine na mng’ono wanga wamkazi ku Sande sukulu. Ndiyeno ku ma 11:00, tinali kuloŵa na atate m’chalichi kukacita nawo mapemphelo. Koma masana, amayi anali kupita nafe ku Nyumba ya Ufumu. Tinatha kuona kuti zipembedzo ziŵilizi n’zosiyana kwambili.

Pa msonkhano wamaiko mu 1958, pamodzi na banja la a Hutcheson

Amayi anali kuuzako mabwenzi awo a Bob Hutcheson na akazi awo a Marion zimene anali kuphunzila. Ndipo m’kupita kwa nthawi nawonso anakhala Mboni. Mu 1958 banjali pamodzi na ana awo atatu, linapita nane ku msonkhano wa maiko wa masiku 8 mu mzinda wa New York. Tsopano, nimaona kuti sicinali copepuka kuti apite nane ku msonkhano umenewo. Koma msonkhanowo unali wosaiŵalika kwa ine.

CIDWI CIMENE ANANIONETSA CINANILIMBIKITSA KUCITA ZAMBILI

Nili wacinyamata tinali kukhala pa famu, ndipo n’nali kusangalala kusamalila nyama. Conco, n’nayamba kuganizila kwambili zodzakhala dokotala wa zinyama. Amayi anauzako mkulu wina mu mpingo za colinga canga cimeneco. Mokoma mtima mkuluyo ananikumbutsa kuti tikukhala ‘m’masiku otsiliza.’ Ndipo ananifunsa mmene kucita maphunzilo a ku yuniveziti kwa zaka zambili kungakhudzile ubale wanga na Yehova. (2 Tim. 3:1) Conco, n’nasankha kusacita maphunzilo a ku yuniveziti.

Koma n’nali kuganizilabe zimene nizikacita nikatsiliza sukulu. Ngakhale kuti n’nali kulalikila kumapeto kwa mlungu uliwonse, sin’nali kusangalala nawo ulaliki. Ndipo zokhala mpainiya, munalibiletu m’maganizo mwanga. Pa nthawiyo, atate na ang’ono awo amene sanali Mboni anali kunilimbikitsa kugwila nchito ya nthawi zonse pa kampani yaikulu ya za inshuwalansi ku Toronto. Atate aang’ono anali na udindo waukulu pa kampaniyo, conco n’navomela nchitoyo.

Cifukwa cogwila nchito ma ovataimu, komanso kugwilizana na anthu osalambila Mulungu, sin’nali wokangalika pa zinthu zauzimu. Poyamba, n’nali kukhala na ambuye amuna amene sanali Mboni. Koma atamwalila, n’nafunika kupeza malo okhala.

Banja la a Hutcheson amene anapita nane ku msonkhano mu 1958 anali ngati makolo anga. Iwo ananitenga kuti nidzikhala nawo, ndipo ananithandiza kukula kuuzimu. Mu 1960, ine na mwana wawo John tinabatizika. John anayamba upainiya. Izi zinanilimbikitsa kuyamba kulalikila kwambili. Abale mu mpingo anaona kupita kwanga patsogolo. Conco, ananiika kukhala mtumiki wa Sukulu ya Ulaliki. a

KUPEZA MNZANGA WA MU UKWATI NA KUYAMBA UPAINIYA

Pa tsiku la cikwati cathu mu 1966

Mu 1966, n’nakwatila mpainiya wokangalika dzina lake Randi Berge. Iye anali wofunitsitsa kutumikila kumalo osoŵa. Woyang’anila dela anationetsa cidwi, na kutilimbikitsa kuti tikathandizile mpingo wa Orillia ku Ontario. Nthawi yomweyo tinasamuka.

Titangosamukila ku Orillia, n’nayamba upainiya wa nthawi zonse. Tonse aŵili tinali okondwela kwambili! N’taika maganizo anga onse pa upainiya, n’napeza cimwemwe cifukwa coseŵenzetsa Baibo, komanso poona kuti anthu akulandila coonadi. Ndipo zinali zosangalatsa kwambili kuthandiza banja lina ku Orillia kupanga masinthidwe mu umoyo wawo na kukhala atumiki a Yehova.

KUPHUNZILA CINENELO CATSOPANO KOMANSO KUSINTHA KAGANIZIDWE KATHU

Titapita kukaceza ku Toronto, n’nakumana na m’bale Arnold MacNamara. Iye anali mmodzi mwa abale otsogolela pa Beteli. Ananifunsa ngati tingakonde kukhala apainiya apadela. Nthawi yomweyo n’namuyankha kuti: “Inde! Tingatumikile kulikonse kupatulapo ku Quebec.” Sin’nafuneko cifukwa n’nali n’tatengela maganizo olakwika amene anthu okamba Cizungu ku Canada anali nawo ponena za anthu okamba ci French ku Quebec. Pa nthawiyo, magulu a ndale ku Quebec anali kucita zionetselo kuti boma ilole mzinda wa Quebec kukhala dziko lodziimila palokha.

M’bale MacNamara anati, “Pakali pano, Quebec ndiwo mzinda umene ofesi ya nthambi ikutumiza apainiya apadela.” Nthawi yomweyo n’navomela. N’nadziŵa kuti mkazi wanga anali wofunitsitsa kutumikila kumeneko. M’kupita kwa nthawi, n’nazindikila kuti ici cinali cimodzi mwa zisankho zabwino koposa.

Pambuyo pophunzila ci French kwa milungu isanu, ine na mkazi wanga pamodzi na banja lina, tinapita m’tauni ya Rimouski, imene inali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 540 kucokela ku Montreal. Ci French sitinali kucidziŵa bwino, ndipo izi zinaonekelatu pamene n’naŵelenga zilengezo pa msonkhano. M’malo monena kuti pa msonkhano wacigawo umene ukubwelawo tidzakhala na alendo ambili “a ku Austria,” n’nanena kuti “a ku ostrich,” mawu otanthauza nthiwatiwa.

Nyumba imene tinali kukhalamo ku Rimouski

Pamene anayife tinali kutumikila ku Rimouski, kunabwelanso alongo anayi okangalika amene anali mbeta. Kunabwelanso m’bale na mlongo Huberdeau na ana awo aŵili aakazi. Banjali linali kucita lendi nyumba yaikulu imene tonsefe apainiya tinali kukhalamo, ndipo tinali kuthandizila kulipila lendi. M’nyumbamo, nthawi zambili tinali kukhalamo anthu 12 kapena 14. Pokhala apainiya apadela, ine na mkazi wanga tinali kulalikila m’maŵa, masana, na m’madzulo. Ndipo tinali kuyamikila kwambili kuti nthawi zonse tinali kukhala na wina wopita naye mu ulaliki, ngakhale m’madzulo kukazizila.

Ubale wathu unalimba kwambili na apainiya omwe tinali kukhala nawo, moti anakhala ngati banja kwa ife. Masiku ena, tinali kuphikila pamodzi cakudya, na kuwotha moto capamodzi. M’bale wina anali na luso loimba na zipangizo zoimbila. Conco, pa Ciŵelu ciliconse madzulo tinali kuimba na kuvina.

Anthu ambili ku Rimouski anali acidwi. Pa zaka zisanu cabe, tinaona ophunzila Baibo angapo akupita patsogolo mpaka kubatizika. Mpingo unakula kufika pafupifupi ofalitsa 35. Izi zinatikondweletsa ngako.

Ku Quebec tinalandila maphunzilo abwino kwambili monga alengezi. Tinaona Yehova akutithandiza pa utumiki wathu komanso pa zofunikila za kuthupi. Kuwonjezela apo, tinayamba kukonda anthu okamba ci French, komanso cinenelo cawo na cikhalidwe cawo. izi zinapangitsa kuti tizikondanso anthu azikhalidwe zina.—2 Akor. 6: 13.

Mosayembekezela, ofesi ya nthambi inatipempha kuti tisamukile ku Tracadie, ca kum’mawa kwa New Brunswick. Izi zinali zovuta cifukwa tinali titangosaina kalata ya pangano yokhudza kucita lendi nyumba, komanso n’nali kugwila nchito ya ganyu pa sukulu inayake. Cinanso, maphunzilo athu ena a Baibo anali atangokhala kumene ofalitsa, komanso tinali mkati momanga Nyumba ya Ufumu.

Nkhani yosamukayi tinaipemphelela kwambili. Kenako, tinapita kukayendela tauni ya Tracadie imene inali yosiyana kwambili na Rimouski. Popeza n’kumene Yehova anali kufuna kuti tipite, tinaganiza zongopita. Tinamuyesa Yehova pa nkhaniyi, ndipo tinaona akutithandiza kugonjetsa zopinga. (Mal. 3:10) Popeza mkazi wanga anali wauzimu kwambili, wodzipeleka, komanso wansangala, sizinali zovuta kudzoloŵela umoyo watsopano.

M’bale Robert Ross ndiye mkulu yekha amene tinapeza mu mpingo. Iye na mkazi wake Linda anali kucita upainiya kumeneko. Koma mwana wawo woyamba atabadwa, anasankha kukhalabe kumeneko. Ngakhale kuti anali kusamalila mwana wamng’ono, iwo anatilimbikitsa kwambili cifukwa anali oceleza, komanso okangalika mu ulaliki.

TAPEZA MADALITSO CIFUKWA COTUMIKILA KULIKONSE KOFUNIKILA THANDIZO

Nyengo yozizila pa ulendo wathu woyamba m’nchito yadela

Titatumikila monga apainiya kwa zaka ziŵili ku Tracadie, mosayembekezelanso tinalandila utumiki wina. Anatipempha kuti tiyambe nchito ya m’dela. Tinatumikila m’madela a Cizungu kwa zaka 7. Pambuyo pake, anatitumiza m’dela la ci French ku Quebec. M’bale Léonce Crépeault, amene anali woyang’anila cigawo, nthawi zonse anali kuniyamikila nikakamba nkhani. Kenako anali kunifunsa kuti, “Kodi ungacite ciyani kuti uzikamba nkhani mogwila mtima kwambilil?” b Cidwi cimene ananionetsa cinanithandiza kuti nikulitse luso la nanga la kuphunzitsa.

Imodzi mwa nchito zimene sinimaiŵala, ni kutumikila ku kafiteliya pa msonkhano wa maiko mu 1978 ku Montreal. Tinali kuyembekezela anthu 80,000, ndipo panapangidwa makonzedwe atsopano a mopelekela cakudya. Ziwiya zophikila, zakudya, komanso mophikila mwake, zonse zinali za tsopano. Tinali na mafiliji akuluakulu pafupifupi 20, koma nthawi zina sanali kugwila bwino nchito. Cifukwa cakuti mu sitediyamu munali kucitika maseŵela tsiku lakuti maŵa ni msonkhano, sitinathe kuloŵa kuti tiike zinthu m’malo mpaka pakati pa usiku. Tinali kuuka mbandakuca kuti tikonze cakudya ca m’mawa. Tinali kukhala olema, koma n’naphunzila zambili kwa anchito anzanga olimbika pa nchito, okhwima mwauzimu, komanso ansangala amenewo. Tinapanga ubwenzi wathithithi, ndipo ukalipo mpaka pano. Zinali zokondweletsa ngako kupezeka ku msonkhano wosaiŵalika ku Quebec, mzinda umene munali mazunzo m’zaka zapakati pa 1940 komanso 1960!

Ine na mkazi wanga tikugwila nchito yokonzekela msonkhano ku Montreal mu 1985

N’naphunzila zambili kwa oyang’anila ena pa misonkhano ikulu-ikulu ku Montreal. Caka cina, m’bale David Splane, amene tsopano ni ciwalo ca Bungwe Lolamulila, anali woyang’anila msonkhano. Koma pa msonkhano wotsatila, n’nasankhidwa kukhala woyang’anila msonkhano, ndipo m’bale Splane anayanja zimenezo na mtima wonse.

Mu 2011, pambuyo pogwila nchito ya m’dela zaka 36, ananipempha kuti nikhale mlangizi wa Sukulu ya Akulu a Mpingo. Pa zaka ziŵili, tinagona m’nyumba zosiyanasina zokwana 75. Koma tinapindula kwambili pa kudzimana kwathu kumeneko. Kumapeto kwa mlungu uliwonse, akulu anali kuyamikila kwambili poona kuti Bungwe Lolamulila limasamala kwambili za umoyo wawo wauzimu.

Patapita nthawi, n’nakhala mlangizi wa Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Tsiku lililonse, ophunzila anali kuthela maola 7 m’kalasi. Ndipo m’madzulo anali kuthela maola atatu kulemba mahomuweki awo. Cina, mlungu uliwonse anali kusamalila mbali zinayi kapena zisanu zimene agaŵilidwa. Mwa ici, anali kukhala otopa kwambili. Ine na mlangizi mnzanga tinali kuwauza kuti adzakwanitsa kokha na thandizo la Yehova. Sinidzaiŵala cimwemwe cimene ophunzilawo anali kukhala naco poona kuti cifukwa codalila Yehova, akwanitsa kucita zambili zimene anali kuona kuti sangakwanitse.

KUONETSA ENA CIDWI KUMATIPINDULILA NTHAWI ZONSE

Cidwi cimene amayi anali kuonetsa kwa ena cinathandiza maphunzilo awo a Baibo kupita patsogolo. Cinathandizanso atate kusintha mmene anali kuonela coonadi. Patapita masiku atatu amayi atamwalila, tinadabwa kuti atate anasonkhana nafe ku Nyumba ya Ufumu. Ndipo anapitiliza kucita zimenezo kwa zaka 26. Olo kuti atate sanabatizike, akulu ananiuza kuti nthawi zonse iwo anali kukhala oyamba kufika ku misonkhano mlungu uliwonse.

Amayi anali citsanzo cabwino kwa ine na azilongosi anga. Alongosi anga onse atatu na amuna awo akutumikila Yehova mokhulupilika. Aŵili mwa alongosi angawo atumikila pa ofesi ya nthambi—wina ku Portugal, wina ku Haiti.

Palipano, ine na mkazi wanga ndife apainiya apadela ku Hamilton, ku Ontario. M’nchito yadela, tinali kukonda kupita na abale komanso alongo ku maulendo awo obwelelako na ku maphunzilo awo a Baibo. Koma lomba timakondwela kuti tili na maphunzilo athu-athu a Baibo opita patsogolo mwauzimu. Ndipo pamene tikupanga mabwenzi mu mpingo wathu watsopano, zimatilimbitsa tikaona mmene Yehova amawathandizila panthawi zabwino komanso zovuta.

Tikayang’ana kumbuyo, timayamikila ngako kuti anthu ambili anationetsa cidwi. Ndipo nafenso tayesetsa ‘kudela nkhawa’ anthu ena kapena kuti kuwaonetsa cidwi, mwa kuwalimbikitsa kutumikila Yehova mmene angathele. (2 Akor. 7:6, 7) Mwacitsanzo, mlongo wina, mwana wake wamwamuna, komanso wamkazi, anali apainiya. N’nafunsa mwamuna wa mlongoyo ngati anaganizilapo zoyamba upainiya. Iye anati anali kusamalila apainiya atatu amenewo. Conco, n’namufunsa kuti, “Kodi inu mungawasamalile bwino kupambana Yehova?” N’namulimbikitsa kuti alaŵeko cimwemwe cimene a m’banja mwake anali naco cifukwa cocita upainiya. Patapita miyezi 6, anakhala mpainiya.

Ine na mkazi wanga Randi sitidzaleka kufotokozela “m’badwo wotsatila” zokhudza “nchito [za Yehova] zodabwitsa.” Ndipo tikukhulupilila kuti nawonso adzasangalala kutumikila Yehova monga ife tacitila.—Sal. 71:17, 18.

a Tsopano amachedwa woyang’anila Umoyo na Utumiki.

b Onani mbili ya m’bale Léonce Crépeault mu Nsanja ya Mlonda ya February 2020 masa. 26-30.