Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu
Ikani Patsogolo Zinthu Zofunika Kwambili
N’zoona kuti tonsefe timakhala na nthawi yocepa yocita phunzilo la munthu mwini. Koma kodi tingaiseŵenzetse motani kuti tizipindula kwambili? Coyamba, musamathamange. Mudzapindula kwambili mukamaŵelenga mfundo zocepa modekha, kuposa kuŵelenga mfundo zambili mothamanga.
Kenako, ikani patsogolo zinthu zofunika kwambili. (Aef. 5:15, 16) Onankoni malingalilo otsatilawa:
Muziŵelenga Baibo tsiku lililonse. (Sal. 1:2) Poyambila pabwino ni kuŵelenga macaputala a kuŵelenga Baibo kwa mlungu na mlungu pa msonkhano wa mkati mwa mlungu.
Muzikonzekela Phunzilo la Nsanja ya Mlonda, na msonkhano wa mkati mwa mlungu, ndipo muzipelekapo ndemanga.—Sal. 22:22.
Malinga na nthawi imene muli nayo, muziyesetsa kudya cakudya cina zauzimu, monga kuonenela mavidiyo, kuŵelenga magazini ogaŵila, na zofalitsa zina za pa jw.org.
Muziŵelenga nkhani zimene muli nazo cidwi. Mungafufuze nkhani yokhudza vuto limene mukukumana nalo, funso limene muli nalo, kapena nkhani ya m’Baibo imene mufuna kumvetsetsa. Kuti mupeze malingalilo ena, pitani pa jw.org pa mbali yakuti “Bible Study Activities.”