Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 30

Muzikulabe m’Cikondi Canu

Muzikulabe m’Cikondi Canu

“Tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzela m’cikondi.”—AEF. 4:15.

NYIMBO 2 Dzina Lanu Ndimwe Yehova

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi munadziŵa zotani mutayamba kuphunzila Baibo?

 KODI mukumbukila pamene munayamba kuphunzila Baibo? Mwina munadabwa mutadziŵa kuti Mulungu ali na dzina. Kapena munamva bwino mutadziŵa kuti Mulungu sazunza anthu m’moto wa helo. Ndipo n’kutheka kuti munakondwela mutaphunzila kuti okondedwa anu amene anamwalila, mudzawaonanso na kukhala nawo m’paradaiso padziko lapansi.

2. Kuwonjezela pa kuphunzila coonadi ca m’Baibo, ni masinthidwe ena ati amene munapanga? (Aefeso 5:1, 2)

2 Pamene munapitiliza kuphunzila Mawu a Mulungu, cikondi canu pa iye cinali kukulilakulila. Cikondico cinakulimbikitsani kuseŵenzetsa zimene munali kuphunzila. Pogwilitsa nchito mfundo za m’Baibo, munayamba kupanga zisankho zabwino. Munasintha kaganizidwe kanu na khalidwe lanu kuti mukondweletse Mulungu. Munayamba kutengela citsanzo ca Atate wanu wakumwamba, monga mmene mwana amatengela kholo lake lacikondi.—Ŵelengani Aefeso 5:1, 2.

3. Kodi tingadzifunse mafunso otani?

3 Tingadzifunse kuti: ‘Kodi Yehova nimam’konda kwambili pali pano, kuposa pamene n’nangokhala Mkhristu? Cibatizikileni, kodi napita patsogolo, maka-maka pa nkhani yokonda abale na alongo potengela citsanzo ca Yehova?’ Ngati ‘cikondi cimene munali naco poyamba’ cazilala, musalefuke. Izi n’zimene zinacitikila Akhristu oyambilila. Yesu sanawakane Akhristuwo cikondi cawo citazilala, ndipo nafenso sadzatikana. (Chiv. 2:4, 7) Iye adziŵa kuti tingacikulitsenso cikondi cathu ca poyamba.

4. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

4 M’nkhani ino, tikambilane mmene tingapitilizile kukula m’cikondi cathu pa Yehova komanso pa anthu ena. Kenaka, tikambilane mapindu amene timapeza tikakulitsa cikondi cathu pa Yehova, komanso pa abale na alongo.

KULANI M’CIKONDI CANU PA YEHOVA

5-6. Ni zokhoma zotani zimene Paulo anakumana nazo pa utumiki wake? Nanga n’ciyani cinam’limbikitsa kuti asaleke kutumikila Yehova?

5 Mtumwi Paulo anali kusangalala potumikila Yehova. Koma anakumana na zokhoma zambili. Kambili, anali kuyenda maulendo atali-atali, ndipo mayendedwe anali ovuta kwambili masiku amenewo. Pa maulendowo, nthawi zina anali kukumana na “zoopsa za m’mitsinje,” komanso “zoopsa za acifwamba.” Nthawi zinanso anali kumenyedwa na anthu otsutsa. (2 Akor. 11:23-27) Ndipo ngakhale Akhristu anzake si nthawi zonse pamene anayamikila pa zimene anali kucita kuti awathandize.—2 Akor. 10:10; Afil. 4:15.

6 N’ciyani cinathandiza Paulo kuti asaleke kutumikila Yehova? Iye anaphunzila zambili zokhudza makhalidwe a Yehova m’Malemba, komanso pa zimene iye mwini anapitamo. Izi zinam’tsimikizila kuti Yehova anali kum’konda kwambili. (Aroma 8:38, 39; Aef. 2:4, 5) Ndipo nayenso anakulitsa cikondi cake pa Yehova. Anaonetsa cikondico ‘potumikila oyela na kupitiliza kuwatumikila.’—Aheb. 6:10.

7. Tiyenela kucita ciyani kuti tikule m’cikondi cathu pa Yehova?

7 Tingakule m’cikondi cathu pa Mulungu mwa kuŵelenga Baibo mwakhama. Mukamaŵelenga, muziona zimene muphunzilapo za Yehova. Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi nkhaniyi ionetsa bwanji kuti Yehova amanikonda? Kodi ikuonetsa zifukwa zotani zom’kondela Yehova?’

8. Kodi pemphelo lingatithandize bwanji kukulitsa cikondi cathu pa Mulungu?

8 Cina cimene tingacite kuti tikule m’cikondi cathu pa Yehova, ni kupemphela kwa iye nthawi zonse. (Sal. 25:4, 5) Tikamapemphela, iye azitiyankha. (1 Yoh. 3:21, 22) Mlongo Khanh wa ku Asia anati: “Poyamba, n’nali kukonda Yehova cifukwa ca zimene n’naphunzila zokhudza iye. Koma pomwe anali kuyankha mapemphelo anga, cikondi canga cinakulilako. Izi zinanilimbikitsa kucita zinthu zom’kondweletsa.” b

KULANI M’CIKONDI CANU PA ANTHU ENA

9. Kodi Timoteyo anaonetsa bwanji kuti anali kupita patsogolo pa nkhani yoonetsa cikondi?

9 Patapita zaka zingapo Paulo atakhala Mkhristu, anakumana na Timoteyo. Timoteyo anali kukonda kwambili Yehova komanso anthu. Paulo anauza Akhristu ku Filipi kuti: “Ndilibe wina wamtima ngati [Timoteyo], amene angasamaledi za inu moona mtima.” (Afil. 2:20) Apa Paulo sanali kuyamikila Timoteyo cifukwa ca luso lake lolinganiza bwino zinthu, kapena cifukwa cokhala mphunzitsi waluso. Koma iye anacita cidwi poona cikondi cimene Timoteyo anali naco pa abale na alongo. Mosakayikila, mipingo imene Timoteyo anali kucezela inali kuyembekezela mwacidwi kufika kwake.—1 Akor. 4:17.

10. Kodi mlongo Anna na mwamuna wake anaonetsa bwanji cikondi kwa abale na alongo?

10 Nafenso timafuna-funa mipata kuti tithandize abale na alongo. (Aheb. 13:16) Ganizilani citsanzo ca mlongo Anna, amene tinam’chula m’nkhani yapita. Pambuyo pa cimphepo camkuntho, iye na mwamuna wake anapita kukaona banja lina la Mboni. Atafika, anapeza kuti mtenje wa nyumba unawonongeka na cimphepoco, ndipo zovala zonse za banjalo zinali zitada. Mlongo Anna anati: “Tinatenga zovalazo kuti tikazicape, ndipo tinazibweza zili zochisa komanso zopeteka bwino. Zimene tinacitazo zinali zocepa, koma zinalimbitsa ubwenzi wathu mpaka pano.” Cifukwa cokonda abale na alongo awo, mlongo Anna na mwamuna wake anapeleka thandizo lofunikila kwa iwo.—1 Yoh. 3:17, 18.

11. (a) Kodi anthu ena amacita motani akaona kuti timawakonda? (b) Malinga na Miyambo 19:17, kodi Yehova adzacitapo ciyani ngati tionetsa ena cikondi?

11 Tikamacita nawo mwacikondi komanso mokoma mtima anthu ena, iwo amaona kuti tikuyesetsa kutengela Yehova. Ndipo angatiyamikile koposa cifukwa cowakomela mtima. Mlongo Khanh amene tam’chula uja, saiŵala anthu amene anam’thandiza. Iye anakamba kuti: “Niwayamikila ngako alongo onse amene anali kupita nane mu ulaliki. Anali kubwela kudzanitenga, kuniitanila ku cakudya, komanso kunibweletsa pa nyumba. Tsopano nazindikila kuti imeneyo inali nchito yaikulu. Anali kucita zimenezo cifukwa conikonda.” N’zoona kuti si onse angatiyamikile pa zimene timawacitila. Ponena za amene anam’thandiza, mlongo Khanh anati: “Nimafuna kuwabwezela pa kukoma mtima kumene ananionetsa, kungoti sinidziŵa kumene amakhala. Koma Yehova adziŵako, ndipo nimam’pempha kuti awabwezele m’malo mwa ine.” Zimenezi n’zoona. Yehova amaona ngakhale zocepa zimene timacitila anthu ena. Iye amaziona kuti ni nsembe zamtengo wapatali, komanso nkhongole imene adzatibwezela.—Ŵelengani Miyambo 19:17.

Munthu akamapita patsogolo mwauzimu, amafuna-funa mipata kuti athandize ena (Onani ndime 12)

12. Kodi abale angaonetse bwanji kuti amakonda mpingo? (Onaninso zithunzi.)

12 Ngati ndinu m’bale, kodi mungaonetse bwanji cikondi kwa anthu ena? M’bale wacicepele dzina lake Jordan anafunsa mkulu zimene angacite kuti azithandiza kwambili mu mpingo. Mkuluyo anamuyamikila pa kupita kwake patsogolo, ndipo anamuuza zimene angacite monga kufika mofulumila pa Nyumba ya Ufumu kuti azipatsa ena moni, kupelekapo ndemanga pa misonkhano, kulalikila nthawi zonse na kagulu kake ka ulaliki, komanso kufuna-funa mipata yothandizila ena. Jordan atayamba kuseŵenzetsa malangizowa, sanali kungophunzila nchito zatsopano, koma anali kukulitsanso cikondi pa abale na alongo ake. Iye anaphunzila kuti m’bale akakhala mtumiki wothandiza sikuti m’pamene amayamba kuthandiza ena. Koma amapitiliza kuwathandiza.—1 Tim. 3:8-10, 13.

13. Kodi cikondi cinam’limbikitsa bwanji m’bale Christian kuti ayenelele kutumikilanso monga mkulu?

13 Bwanji ngati kale munali mkulu kapena mtumiki wothandiza? Dziŵani kuti Yehova amakumbukila nchito zanu, komanso cikondi cimene cinakulimbikitsani kucita zimenezo. (1 Akor. 15:58) Amaonanso cikondi cimene mwakhala mukucionetsa mpaka pano. M’bale wina dzina lake Christian anakhumudwa atatsitsidwa pa udindo monga mkulu. Komabe, iye anati: “N’nacita zonse zotheka kuti nizitumikila Yehova cifukwa com’konda, osati kuyang’ana pa udindo.” M’kupita kwa nthawi, anakhalanso mkulu. M’bale Christian anati: “N’nali kucita mantha pang’ono nikaganizila za kuyambanso kutumikila monga mkulu. Koma n’nadziuza kuti, ngati Yehova mwa cisomo cake akunilola kutumikilanso, nidzacita zimenezo cifukwa com’konda, komanso cifukwa cokonda abale na alongo.”

14. Kodi mwaphunzila ciyani pa ndemanga ya mlongo wa ku Georgia?

14 Atumiki a Yehova amaonetsanso cikondi kwa anthu ena. (Mat. 22:37-39) Mwacitsanzo, mlongo Elena wa ku Georgia anati: “Poyamba, cimene cinali kunilimbikitsa kulalikila ni cikondi canga pa Yehova basi. Koma pamene cikondi pa Atate wanga wakumwamba cinali kukula, n’nayamba kukondanso kwambili anthu ena. N’nayamba kuganizila mavuto amene anali kukumana nawo, komanso nkhani zimene zingawafike pa mtima. Kuganizila kwambili za iwo kunanipangitsa kukhala wofunitsitsa kuwathandiza.”—Aroma 10:13-15.

MAPINDU AMENE TIMAPEZA TIKAMAKONDA ANTHU ENA

Kuonetsa cikondi kamodzi kokha kungapindulile anthu ambili (Onani ndime 15-16)

15-16. Monga tikuonela pa zithunzi, kodi timapindula motani tikamaonetsa cikondi anthu ena?

15 Tikamakonda abale na alongo, nafenso timapindula. Pamene mlili wa COVID-19 unabuka, m’bale wina dzina lake Paolo na mkazi wake, anathandiza alongo ambili okalamba moseŵenzetsela zipangizo zamakono polalikila. Mwacitsanzo, mlongo wina anadziŵa moseŵenzetsela cipangizo cake, moti anakwanitsa kuitanila acibale ake ku Cikumbutso pogwilitsa nchito cipangizoco. Acibale ake 6 anapezekapo kudzela pa vidiyokonfalensi. Mlongoyo na acibale ake anapindula na thandizo la m’bale Paolo na mkazi wake. Patapita nthawi, mlongoyo analembela m’bale Paolo kuti: “Zikomo ngako potiphunzitsa okalambafe. Sinidzaiŵala cikondi ca Yehova komanso khama lanu potithandiza.”

16 M’bale Paolo anatengapo phunzilo pa zocitika ngati zimenezi. Iye anaphunzila kuti cikondi ndiye cofunika kwambili kupambana cidziŵitso kapena maluso athu. Iye anakamba kuti: “N’nali woyang’anila dela. Ngakhale kuti abale na alongo mwina anaiŵala nkhani zimene n’nali kukamba ku mipingo, iwo amakumbukilabe thandizo langa.”

17. Ndaninso amapindula tikamaonetsa cikondi?

17 Tikamaonetsa cikondi anthu ena, timapindula m’njila zimene sitinayembekezele. M’bale Jonathan wa ku New Zealand, anatsimikizila mfundo imeneyi. Tsiku lina pa Ciŵelu masana pamene kunatentha kwambili, anaona mpainiya wina akulalikila yekha-yekha m’mbali mwa msewu. M’bale Jonathan anaganiza zoyamba kulalikila na mpainiya ameneyo Ciŵelu ciliconse masana. Pa nthawiyo, sanadziŵe mmene iye mwini adzapindulila akaonetsa cikondi cotelo. Iye anati: “Pa nthawiyo, sin’nali kusangalala nawo ulaliki. Koma n’taona mmene mpainiyayo anali kuphunzitsila, komanso zotulukapo zabwino, ulaliki n’nayamba kuukonda ngako. Cina, mpainiyayo anakhala mnzanga wapamtima amene ananithandiza kukula mwauzimu, kumasangalala nawo ulaliki, komanso kulimbitsa ubale wanga na Yehova.”

18. Kodi Yehova amafuna kuti ticite ciyani?

18 Yehova amafuna kuti tonsefe tikule m’cikondi pa iye komanso pa anthu anzathu. Monga taonela, tingakule m’cikondi cathu pa Yehova mwa kuŵelenga Mawu ake na kuwasinkhasinkha, komanso kumakamba naye m’pemphelo. Tingakulitse cikondi cathu pa abale na alongo, mwa kupeleka thandizo lofunikila kwa iwo. Cikondi cathu cikamakula, tidzamuyandikila kwambili Yehova na banja lathu lauzimu mpaka muyaya.

NYIMBO 109 Tizikondana ndi Mtima Wonse

a Kaya ndife acatsopano m’coonadi kapena tatumikila Yehova kwa zaka zambili, tonsefe tiyenela kupitabe patsogolo. Tingacite zimenezo mwa kukula m’cikondi cathu pa Yehova komanso pa anthu ena. Ndipo izi n’zimene tikambilane m’nkhani ino. Posinkhasinkha mfundo za m’nkhani ino, ganizilani mmene mwapitila kale patsogolo, na mmene mungawonjezele kucita zimenezo.

b Maina ena asinthidwa.