Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 28

NYIMBO 123 Gonjelani Dongosolo la Mulungu

Kodi Mumacizindikila Coonadi?

Kodi Mumacizindikila Coonadi?

“Khalani olimba, mutamanga kwambili coonadi mʼciuno mwanu ngati lamba.”AEF. 6:14.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Mmene tingadziŵile kusiyanitsa coonadi cimene tinaphunzila kwa Yehova na mabodza amene Satana komanso otitsutsa amalimbikitsa.

1. Kodi mumaciona bwanji coonadi?

 ANTHU a Yehova amakonda coonadi copezeka m’Mawu a Mulungu. Ndipo cikhulupililo cathu n’cozikika m’Mawu a Mulungu. (Aroma 10:17) Pofika pano tinazindikila kuti Yehova ndiye anakhazikitsa mpingo wa Cikhristu kuti ‘ulimbikitse ndi kuteteza coonadi.’ (1 Tim. 3:15) Ndipo timagonjela mofunitsitsa ‘amene akutsogolela’ pakati pathu akamatifotokozela coonadi ca m’Baibo, na kutipatsa citsogozo mogwilizana na cifunilo ca Mulungu.—Aheb. 13:17.

2. Malinga na Yakobo 5:​19, pamakhalabe ciopsezo cotani pambuyo pophunzila coonadi?

2 Komabe, ngakhale pambuyo pakuti talandila coonadi na kuvomeleza kuti gulu la Mulungu n’limene limatipatsa citsogozo codalilika, n’zothekabe kusoceletsedwa. (Ŵelengani Yakobo 5:19.) Satana angakondwele ngako atatileketsa kukhulupilila Baibo na citsogozo cimene timalandila kucokela ku gulu la Mulungu.—Aef. 4:14.

3. N’cifukwa ciyani tiyenela kucigwila zolimba coonadi? (Aefeso 6:​13, 14)

3 Ŵelengani Aefeso 6:​13, 14. Posacedwa Mdyelekezi adzagwilitsa nchito mauthenga abodza amphamvu posoceletsa mitundu ya anthu kuti itsutsane na Yehova. (Chiv. 16:​13, 14) Ndiponso n’zosakaikitsa kuti Satana adzawonjezela zoyesetsa zake kuti asoceletse anthu a Yehova. (Chiv. 12:9) Ndiye cifukwa cake m’pofunika kuti tizidziŵa bwino kusiyanitsa coonadi na mabodza, komanso kuti tizilabadila coonadi. (Aroma 6:17; 1 Pet. 1:22) Kupanda kutelo, sitingapulumuke pa cisautso cacikulu!

4. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

4 M’nkhani ino, tiona makhalidwe aŵili omwe angatithandize kuzindikila coonadi cocokela m’Baibo, na kuvomeleza citsogozo cocokela ku gulu la Mulungu. Kenako tikambilane zinthu zitatu zimene tiyenela kucita kuti tipitilize kugwilitsitsa coonadi.

MAKHALIDWE OTITHANDIZA KUZINDIKILA COONADI

5. Kodi kuopa Yehova kumatithandiza motani kuzindikila coonadi?

5 Kuopa Yehova. Tikakulitsa mantha oyenelela pa Yehova, timamukonda ngako, ndipo timapewa kucita ciliconse com’khumudwitsa. Ndife ofunitsitsa kudziŵa kusiyana pakati pa cabwino na coipa, komanso pakati pa coonadi na mabodza. Timafuna kucita izi kuti tikhale ovomelezeka kwa Yehova. (Miy. 2:​3-6; Aheb. 5:14) Tisalole mantha oopa anthu kukhala aakulu kuposa cikondi cathu pa Yehova. Zili conco cifukwa nthawi zambili zimene anthu amakondwela nazo, n’zimene zimakhumudwitsa Yehova.

6. Kodi mantha anapangitsa bwanji azondi 10 Aciisiraeli kupotoza coonadi?

6 Tikamaopa kwambili anthu kuposa mmene timaopela Mulungu, tingapatuke pa njila ya coonadi. Ganizilani citsanzo ca azondi 12 amene anapita kukazonda dziko limene Yehova analonjeza kupatsa Aisiraeli. Azondi 10 aja, mantha awo pa Akanani anali aakulu kuposa cikondi cawo pa Yehova. Iwo anauza Aisiraeli anzawo kuti: “Sitingathe kukalimbana nawo anthuwo, cifukwa ndi amphamvu kuposa ifeyo.” (Num. 13:​27-31) M’kapenyedwe kaumunthu, Akanani anaonekadi amphamvu kuposa Aisiraeli. Koma aliyense amene anakamba kuti Aisiraeli sakanatha kugonjetsa adani awo anali atamuiŵala Yehova. Azondi 10 amenewo anafunikila kuika maganizo awo pa zimene Yehova anauza Aisiraeli kuti acite. Anayenelanso kuganizila zimene Yehova anawacitila m’mbuyomo. Izi zikanawathandiza kuzindikila kuti mphamvu za Akanani sizinali kanthu poyelekezela na mphamvu zazikulu za Yehova. Mosiyana na azondi opanda cikhulupililo amenewo, Yoswa na Kalebe anafuna kukondweletsa Yehova. Iwo anauza anthuwo kuti: “Ngati Yehova akusangalala nafe, adzatilowetsadi mʼdzikolo nʼkulipeleka kwa ife.”—Num. 14:​6-9.

7. Tiyenela kutani kuti tikulitse mantha athu pa Yehova? (Onaninso cithunzi.)

7 Kuti tikulitse mantha athu pa Yehova, tiyenela kuika mtima wathu pa kukondweletsa Yehova popanga cisankho ciliconse. (Sal. 16:8) Poŵelenga zitsanzo za m’Baibo, dzifunseni kuti, ‘Nikanakhala ine, nikanapanga cisankho cotani?’ Mwa citsanzo, yelekezani kuti munalipo pamene azondi 10 Aciisiraeli anali kupeleka lipoti loipalo. Kodi mukanalikhulupilila lipotilo na kukhala na mantha? Kapena mukanalola cikondi canu pa Yehova na cikhumbo cofuna kum’kondweletsa kugonjetsa mantha amenewo? Mtundu wonse wa Isiraeli unalephela kuzindikila coonadi cimene Yoswa na Kalebe anawauza. Zotulukapo zake, Aisiraeli amene sanakhulupilile anataya mwayi woloŵa m’Dziko Lolonjezedwa.—Num. 14:​10, 22, 23.

Kodi mukanakhulupilila ndani? (Onani ndime 7)


8. Kodi tiyenela kucita khama kuti tikulitse khalidwe liti? Ndipo cifukwa ciyani?

8 Kudzicepetsa. Yehova amaunikila coonadi anthu odzicepetsa. (Mat. 11:25) Modzicepetsa tinalandila thandizo kuti tiphunzile coonadi. (Mac. 8:​30, 31) Komabe, tiyenela kukhala osamala kuti tisakhale onyada. Kunyada kungatipangitse kuyamba kuona malingalilo athu kukhala ofunika molingana na mfundo za m’Malemba komanso citsogozo cocokela ku gulu la Yehova.

9. Tiyenela kutani kuti tikhalebe odzicepetsa?

9 Kuti tikhalebe odzicepetsa, tiyenela kukumbukila kuti ndife aang’ono kwambili poyelekezela na ukulu wa Yehova. (Sal. 8:​3, 4) Tingapemphelenso kuti tikhale odzicepetsa komanso na mzimu wophunzitsika. M’malo moyendela maganizo athu, Yehova adzatithandiza kuti tiziyendela maganizo ake, amene amapeleka kupitila m’Mawu ake na gulu lake. Pamene muŵelenga Baibo, pezani mfundo zoonetsa kuti Yehova amakonda munthu wodzicepetsa. Koma amadana na munthu wodzikuza komanso wonyanda. Ndipo yesetsani kukhala wodzicepetsa maka-maka mukalandila utumiki wapadela umene umakupatsani ulamulilo winawake.

MMENE TINGACIGWILILE ZOLIMBA COONADI

10. Kodi Yehova wakhala akuseŵenzetsa ndani popeleka citsogozo na malangizo kwa anthu ake?

10 Musaleke kudalila citsogozo ca gulu la Yehova. M’nthawi ya Aisiraeli, Yehova anagwilitsa nchito Mose, kenako Yoswa kupeleka malangizo kwa anthu ake. (Yos. 1:​16, 17) Aisiraeli anali kudalitsidwa poona amuna amenewa kukhala oimilako Yehova. Zaka zambili pambuyo pake, mpingo wa Cikhristu utangokhazikitsidwa, atumwi 12 ndiwo anali kutsogolela. (Mac. 8:​14, 15) Kenako, kagulu kameneka kanadzaphatikizapo akulu ena a ku Yerusalemu. Cifukwa cotsatila citsogozo ca amuna okhulupilika amenewa, “anthu m’mipingo anapitiliza kukhala ndi cikhulupililo colimba ndipo ciŵelengelo cinkawonjezeka tsiku ndi tsiku.” (Mac.16:​4, 5) Nafenso timadalitsidwa tikatsatila citsogozo ca gulu la Yehova. Kodi Yehova angamve bwanji ngati takana kutsatila citsogozo ca omwe waasankha kuti azititsogolela? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tiganizile zimene zinacitikila Aisiraeli paulendo wawo wopita ku Dziko Lolonjezedwa.

11. N’ciyani cinacitikila Aisiraeli amene anatsutsa Mose monga wosankhidwa wa Yehova? (Onaninso cithunzi.)

11 Pa nthawi inayake pamene Aisiraeli anali paulendo wopita ku Dziko Lolonjezedwa, amuna a maudindo anatsutsa Mose, na kudelela udindo umene Yehova anamupatsa. Iwo anati: “Gulu lonseli [osati cabe Mose] ndi loyela, ndipo Yehova ali pakati pawo.” (Num. 16:​1-3) N’zoona kuti m’maso mwa Yehova ‘gulu lonselo’ linali loyela, koma Yehova anali atasankha Mose kuti azitsogolela anthu ake. (Num. 16:28) Potsutsana na Mose, oukilawo anali kutsutsana na Yehova. Iwo anaika maganizo awo pa zofuna zawo, zomwe ni kuchuka komanso mphamvu zowonjezeleka, m’malo moika maganizo pa zimene Yehova anali kufuna. Yehova anakantha atsogoleli a cipanduko cimeneci, komanso anthu masauzande amene anagwilizana nawo. (Num. 16:​30-35, 41, 49) Mosakaika konse, masiku anonso Yehova amadana nawo onse osalemekeza citsogozo ca gulu lake.

Kodi mukanakhala kumbali ya ndani? (Onani ndime 11)


12. N’cifukwa ciyani tiyenela kudalila gulu la Yehova?

12 N’zotheka kudalilabe gulu la Yehova. Zikacita kuonekelatu kuti m’pofunika kusintha kamvedwe ka mfundo inayake ya m’Baibo, kapena kusintha mmene gulu limacitila zinthu, abale amene amatitsogolela sazengeleza kupanga masinthidwe. (Miy. 4:18) Cimene iwo amacitila zimenezi si cina ayi, koma kufuna kukondweletsa Yehova. Amaonetsetsanso kuti zigamulo zawo zimazikika m’Mawu a Mulungu, amene ndiwo muyeso umene mtumiki wa Mulungu aliyense ayenela kuutsatila.

13. Kodi “mawu olondola” n’ciyani? Nanga tiyenela kucita nawo ciyani?

13 ‘Gwilitsitsanibe. . .mawu olondola.’ (2 Tim. 1:13) “Mawu olondola” aimila ziphunzitso za Cikhristu zopezeka m’Baibo. (Yoh. 17:17) Ziphunzitso zimenezo ndizo maziko a zonse zimene timakhulupilila. Gulu la Yehova latiphunzitsa kukangamila ku mawu olondola amenewo. Tikacita zimenezi tidzadalitsidwa.

14. Ni motani mmene Akhristu ena anasiyila kugwilitsitsa “mawu olondola”?

14 N’ciyani cingacitike tikapatuka pa “mawu olondola”? Ganizilani citsanzo ici. M’zaka za zana loyamba, Akhristu ena anali kufalitsa nkhani yakuti tsiku la Yehova linali litafika kale. Zioneka kuti anthu anakhala na maganizo amenewo cifukwa ca kalata inayake, imene iwo anaganiza kuti mtumwi Paulo ndiye anailemba. M’malo mofufuza kuti adziŵe zoona za nkhaniyo, Akhristu ena ku Tesalonika anaikhulupilila nkhaniyo, na kuyamba kuifalitsanso kwa Akhristu anzawo. Iwo sakanapusitsidwa akanakumbukila zimene mtumwi Paulo anawaphunzitsa pamene anali pakati pawo. (2 Ates. 2:​1-5) Mtumwi Paulo anacenjeza abale ake kuti asamakhulupilile nkhani iliyonse imene amva. Pofuna kuwathandiza kuti asadzapusitsidwenso m’tsogolo, mtumwi Paulo anamaliza kalata yake yaciŵili kwa Atesolonika na mawu akuti: “Landilani moni wanga, amene ineyo Paulo ndalemba ndi dzanja langa. Nthawi zonse ndimalemba conci mʼmakalata anga onse, kuti mudziwe kuti ndine amene ndalemba. Umu ndi mmene ndimalembela.”—2 Ates. 3:17.

15. Tingadziteteze bwanji ku nkhani zabodza zooneka ngati zoona? Fotokozani citsanzo. (Onaninso zithunzi.)

15 Tiphunzilapo ciyani pa mawu amene mtumwi Paulo analembela Atesalonika? Tikamva nkhani inayake imene sigwilizana na zimene tinaphunzila m’Baibo, kapena tikamva nkhani inayake yocititsa cidwi koma yodabwitsa, tiyenela kukhala osamala. Mu ulamulilo wakale wa Soviet Union, adani athu anapatsa abale kalata yooneka ngati yacokela ku likulu lathu. Kalata imeneyo inalimbikitsa abale na alongo kuti adzipatule ku gulu la Yehova na kupanga gulu lawo lodziimila palokha. Kalata imeneyo inali kuoneka ngati yacokeladi kulikulu lathu. Koma abale na alongo okhulupilika sanapusitsidwe. Iwo anazindikila kuti zimene kalatayo inakamba zinali zosiyana na zimene anaphunzila. Masiku anonso, adani a coonadi amaseŵenzetsa njila zamakono na colinga cakuti atisokoneze na kubweletsa magaŵano pakati pathu. M’malo molola “kuti wina aliyense asinthe maganizo” athu mosavuta, tiyeni tidziteteze mwa kuganizilapo mozama ngati zimene tamva kapena kuŵelengazo zigwilizana na coonadi cimene tinaphunzila kale.—2 Ates. 2:2; 1 Yoh. 4:1.

Musapusitsike na nkhani zabodza zooneka ngati zoona (Onani ndime 15) a


16. Malinga na Aroma 16:​17, 18, tiyenela kucita ciyani ngati ena apatuka pa njila ya coonadi?

16 Khalanibe ogwilizana nawo anthu okhulupilika kwa Yehova. Mulungu afuna kuti tizimulambila mogwilizana. Tidzakhalabe ogwilizana malinga ngati tikangamilabe ku coonadi. Aliyense amene amafalitsa nkhani zotsutsana na coonadi, amabweletsa magaŵano mu mpingo, ndipo Mulungu amatiuza kuti ‘tiziwapewa.’ Tikapanda kuwapewa, angatikanganule ku coonadi.—Ŵelengani Aroma 16:​17, 18.

17. Timapeza mapindu anji tikazindikila coonadi na kucigwila zolimba?

17 Tikazindikila coonadi na kucigwila zolimba tidzakhala athanzi komanso otetezeka kuuzimu. (Aef. 4:​15, 16) Tidzakhalanso otetezeka ku ziphunzitso zonama, komanso mauthenga abodza osonkhezeledwa na Satana. Tidzakhalabe otetezeka m’manja mwa Yehova panthawi ya cisautso cacikulu. Motelo, pitilizani kucigwilitsitsa mwamphamvu coonadi, “ndipo Mulungu wamtendele adzakhala nanu.”—Afil. 4:​8, 9.

NYIMBO 122 Cilimikani, Musasunthike!

a MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Cithunzi coyelekezela abale athu mu ulamulilo wakale wa Soviet Union, atalandila kalata yooneka ngati yacokela kulikulu lathu, pomwe m’ceniceni inacokela kwa adani athu. Masiku anonso, adani athu angaseŵenzetse intaneti pofalitsa nkhani zabodza zokhudza gulu la Yehova.