NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA June 2016

Magazini ino ili ndi nkhani zophunzila kuyambila mlungu wa August 1 mpaka 28, 2016.

Yehova Amatiumba

Kodi Mulungu amasankha bwanji anthu amene amawaumba? N’cifukwa ciani amawaumba? Nanga amawaumba bwanji?

Kodi Mumalola Kuti Woumba Wamkulu Akuumbeni?

Ni makhalidwe a bwanji amene angacititse kuti Mulungu akuumbeni mosavuta?

“Yehova Mulungu Wathu Ndi Yehova Mmodzi”

Kodi Mulungu ni “mmodzi” m’njila ya bwanji? Nanga tifunika kumulambila bwanji?

Musakhumudwe Ndi Zolakwa za Ena

Kale, atumiki okhulupilika a Mulungu anakamba kapena kucita zinthu zimene zinaŵaŵa ena. Kodi tingaphunzilepo ciani pa zitsanzo za m’Baibulo zimenezi?

Khalidwe Labwino Kwambili Kuposa Dayamondi

Kukhala woona mtima n’kofunika kwambili.

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

M’masophenya a Ezekieli, kodi mwamuna amene anali ndi kacikwama ka mlembi, konyamulilamo inki ndi zolembela ndiponso amuna 6 onyamula zida zophwanyila amaimila ndani?