Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mumalola Kuti Woumba Wamkulu Akuumbeni?

Kodi Mumalola Kuti Woumba Wamkulu Akuumbeni?

“Taonani! Mofanana ndi dongo limene lili m’manja mwa woumba mbiya, ndi mmene inunso mulili kwa ine.”—YEREMIYA 18:6.

NYIMBO: 60, 22

1, 2. N’cifukwa ciani Mulungu anali kuona kuti Danieli ni “munthu wokondedwa kwambili?” Nanga tingakhale bwanji omvela monga Danieli?

PAMENE Ayuda anatengedwa kupita ku Babulo, anali kukhala mumzinda umene munali mafano ambili ndipo anthu anali kulambila mizimu yoipa. Koma Ayuda okhulupilika, monga Danieli ndi anzake atatu, anakana kuumbidwa ndi anthu a ku Babulo kapena kuti kutengela zocita zawo. (Danieli 1:6, 8, 12; 3:16-18) Danieli ndi anzake analola kuti Yehova awaumbe ndipo anali kulambila iye yekha cabe. Ngakhale kuti Danieli anakhala ndi anthu oipa kwa nthawi yaitali, mngelo wa Mulungu anakamba kuti iye anali “munthu wokondedwa kwambili.”—Danieli 10:11, 19.

2 Kale, woumba anali ndi ufulu woumba ciliconse cimene wafuna pogwilitsila nchito dothi. Masiku ano, olambila oona amadziŵa kuti Yehova ni Wolamulila wa cilengedwe conse ndipo ali ndi mphamvu zoumba mitundu ya anthu. (Ŵelengani Yeremiya 18:6.) Mulungu alinso ndi mphamvu zoumba aliyense wa ife. Komabe, Yehova sakakamiza munthu kuti asinthe. Iye amafuna kuti tizimulola kutiumba. M’nkhani ino, tiphunzila zimene zingatithandize kukhala ngati dothi lofewa m’manja mwa Mulungu. Tikambilana mafunso atatu otsatilawa: (1) Tingapewe bwanji makhalidwe amene angaticititse kukana malangizo a Yehova ndi kukhala monga dothi louma? (2) Tingacite ciani kuti tikhale ndi makhalidwe amene angatithandize kukhalabe ololela monga dothi lofewa? (3) Ni mbali ya bwanji imene makolo angacite pamene Mulungu akuumba ana awo?

PEWANI MAKHALIDWE AMENE ANGAUMITSE MTIMA WANU

3. Ni makhalidwe a bwanji amene angaumitse mtima wathu? Pelekani citsanzo.

3 Lemba la Miyambo 4:23 limakamba kuti: “Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenela kutetezedwa, pakuti mumtimamo ndiye muli akasupe a moyo.” Kuti mtima wathu usakhale wouma, tiyenela kupewa mzimu wonyada ndi cizoloŵezi cocita chimo, ndiponso tiyenela kulimbitsa cikhulupililo cathu. Ngati siticita zimenezi, tingakhale osamvela ndi opanduka. (Danieli 5:1, 20; Aheberi 3:13, 18, 19) Izi n’zimene zinacitikila Mfumu Uziya ya Yuda. (Ŵelengani 2 Mbiri 26:3-5, 16-21.) Poyamba, Uziya anali womvela ndiponso anali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Motelo, Mulungu anacititsa kuti akhale wamphamvu. Koma “atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza.” Iye anadzikuza kwambili cakuti anafuna kufukiza nsembe m’kacisi ngakhale kuti nchito imeneyo inali ya ansembe cabe. Pamene ansembe anamuletsa, Uziya anakwiya kwambili. Yehova anamulanga ndipo anakhala ndi khate mpaka tsiku limene anamwalila.—Miyambo 16:18.

4, 5. N’ciani cingacitike ngati sitipewa mzimu wonyada? Pelekani citsanzo.

4 Kunyada kungatipangitse kudziona kuti ndife apamwamba kwambili kuposa ena cakuti tingakane kutsatila malangizo ocokela m’Baibulo amene tingapatsidwe. (Miyambo 29:1; Aroma 12:3) Izi n’zimene zinacitikila mkulu wina dzina lake Jim. Iye anasiyana maganizo ndi akulu anzake pankhani inayake mumpingo. Jim anati, “Ndinauza abalewo kuti alibe cikondi, kenako ndinacokapo pa miting’i ya akulu.” Patapita miyezi 6, anasamukila mumpingo wina, koma kumeneko sanaikidwe kukhala mkulu. Jim anakhumudwa kwambili. Iye anali kuona kuti maganizo ake si olakwika cakuti analeka kutumikila Yehova ndipo anakhala wozilala kwa zaka 10. Iye amakamba kuti anali wonyada cakuti anayamba kuimba mlandu Yehova cifukwa ca zimene zinali kucitika. Kwa zaka zambili, abale anali kumuyendela kuti amuthandize, koma Jim sanasinthe maganizo ake.

5 Jim anati, “Nthawi zonse n’nali kuganizila zimene n’nali kuona kuti abalewo akulakwitsa.” Citsanzo cimeneci cionetsa kuti kunyada kungatipangitse kudzikhululukila tikalakwitsa. Tikatelo, timakhala ngati dothi louma. (Yeremiya 17:9) Kodi m’bale kapena mlongo anakukhumudwitsamponi? Kodi munakhumudwapo cifukwa cocotsedwa pa udindo? Ngati n’conco, kodi munacita ciani? Kodi munakhala ndi mzimu wonyada, kapena munazindikila kuti cofunika kwambili ni kukhala pamtendele ndi ena ndiponso kukhalabe okhulupilika kwa Yehova?—Ŵelengani Salimo 119:165; Akolose 3:13.

6. N’ciani cingacitike ngati tili ndi cizoloŵezi cocita chimo?

6 Ngati munthu amacita chimo ndipo amabisa, angayambe kukana malangizo a Mulungu. Zimenezi zingapangitse kuti afike pozoloŵela kwambili kucita chimo. M’bale wina anakamba kuti anafika pozoloŵela kwambili kucita zinthu zinazake zoipa cakuti cikumbumtima cake sicinali kumutsutsa. (Mlaliki 8:11) M’bale wina amene anali ndi cizoloŵezi cotamba zamalisece anati, “Ndinayamba kunena akulu kuti ndi oipa.” Cizoloŵezi cakeco cinawononga ubwenzi wake ndi Yehova. Pamene zinadziŵika kuti amatamba zamalisece, akulu anayenda kukamuthandiza. N’zoona kuti tonse ndife opanda ungwilo. Koma ngati timanena anthu amene amatipatsa uphungu kapena kupeza zifukwa zodzikhululukila tikalakwa m’malo mopempha Mulungu kuti atikhululukile ndi kutithandiza, tingaumitse mtima wathu.

Aisiraeli osamvela anafela m’cipululu cifukwa cakuti anaumitsa mitima yawo ndiponso analibe cikhulupililo

7, 8. (a) Kodi citsanzo ca Aisiraeli cionetsa bwanji kuti kusoŵa cikhulupililo kungaumitse mitima yathu? (b) Kodi ife tiphunzilapo ciani?

7 Aisiraeli anaona zozizwitsa zambili zimene Yehova anacita atawatulutsa mu Iguputo. Koma pamene anatsala pang’ono kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, anaumitsa mitima yawo. N’ciani cinacititsa kuti aumitse mitima yawo? Analibe cikhulupililo mwa Mulungu. M’malo modalila Yehova, anayamba kucita mantha cakuti anayamba kudandaula za Mose. Iwo anafika pokamba kuti cili bwino kubwelela ku Iguputo kumene anali akapolo. Izi zinamuŵaŵa kwambili Yehova cakuti anafunsa kuti: “Kodi anthu awa apitiliza kundinyoza kufikila liti?” (Numeri 14:1-4, 11; Salimo 78:40, 41) Aisiraeliwo anafela m’cipululu cifukwa anaumitsa mitima yawo ndiponso analibe cikhulupililo.

8 Tsopano, tatsala pang’ono kuloŵa m’dziko latsopano, ndipo cikhulupililo cathu cikuyesedwa. Cotelo tiyenela kudzipenda ngati tili ndi cikhulupililo colimba. N’ciani cingatithandize kulimbitsa cikhulupililo cathu? Tiyenela kuganizila mau a Yesu a pa Mateyu 6:33 ndi kudzifunsa kuti: ‘Kodi zolinga zanga ndi zinthu zimene nimasankha zimaonetsa kuti nimakhulupililadi mau a Yesu amenewa? Kodi nimaphonya misonkhano kapena kulephela kupita muulaliki n’colinga cakuti nipange ndalama zambili? Ningacite ciani ngati nchito yanga imanidyela nthawi ndi mphamvu zoculuka? Kodi nimalola dzikoli kuniumba kapena kunilepheletsa kutumikila Yehova?’

9. N’cifukwa ciani tiyenela ‘kupitiliza kudziyesa’ kuti tione ngati tikali olimba m’cikhulupililo? Nanga tingacite bwanji zimenezi?

9 Ngati sitimvela malangizo a m’Baibulo pa nkhani ya anthu oceza nawo, mmene tiyenela kucitila zinthu ndi ocotsedwa, ndi posankha zosangulutsa, mitima yathu ingaume. Mungacite ciani ngati mwayamba kunyalanyaza malangizo pankhani zimenezi? Mwamsanga muyenela kudziyesa kuti muone ngati cikhulupililo canu cayamba kufooka. Baibulo imakamba kuti: “Pitilizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali olimba m’cikhulupililo. Pitilizani kudziyesa kuti mudziŵe kuti ndinu munthu wotani.” (2 Akorinto 13:5) Muzidziyesa moona mtima ndi kuseŵenzetsa Mau a Mulungu kuti muwongolele maganizo anu.

MUZIKHALA MONGA DOTHI LOFEWA

10. N’ciani cingatithandize kukhala ngati dothi lofewa m’manja mwa Yehova?

10 Pofuna kutithandiza kukhalabe monga dothi lofewa, Mulungu watipatsa Mau ake, mpingo wacikristu, ndi nchito yolalikila. Kuŵelenga m’Baibulo ndi kusinkhasinkha zimene taŵelenga tsiku lililonse, kungatithandize kukhala monga dothi lofewa m’manja mwa Yehova cakuti iye adzatiumba mosavuta. Yehova analamula mafumu a Isiraeli kuti azikopela buku la Cilamulo ca Mulungu ndi kumaliŵelenga tsiku lililonse. (Deuteronomo 17:18, 19) Atumwi nawonso anali kudziŵa kuti kuŵelenga Malemba ndi kuwasinkhasinkha n’kofunika kwambili pa utumiki wao. Iwo anagwila mau mbali zina za Malemba Aciheberi polemba Malemba Acigiriki, ndipo polalikila anali kulimbikitsa anthu kuphunzila Malemba. (Machitidwe 17:11) Ifenso timaona kuti kuŵelenga ndi kusinkhasinkha Mau a Mulungu tsiku lililonse n’kofunika. (1 Timoteyo 4:15) Kucita zimenezi kumatithandiza kukhalabe odzicepetsa ndipo Yehova amakwanitsa kutiumba.

Mudziseŵenzetsa zinthu zimene Mulungu wapeleka kuti mukhale ngati dothi lofewa (Onani ndime 10-13)

11, 12. Kodi Yehova angaseŵenzetse bwanji mpingo kuti atiumbe mogwilizana ndi zofooka zathu? Pelekani citsanzo.

11 Yehova amadziŵa zofooka za aliyense wa ife, ndipo amatiumba pogwilitsila nchito mpingo wacikristu. Jim, amene tamuchula poyamba paja, anayamba kusintha maganizo ake pamene mkulu wina anamuonetsa cidwi. Jim anati: “Mkuluyo sananiimbepo mlandu cifukwa ca vuto langa kapena kunidzudzula. Koma anali ndi cikhulupililo cakuti ningasinthe ndipo anaonetsa kuti afunadi kunithandiza.” Patapita miyezi itatu, mkuluyo anaitanila Jim ku msonkhano. Jim anakamba kuti abale ndi alongo mumpingo anamulandila bwino. Anakambanso kuti cikondi cimene anamuonetsa cinamuthandiza kusintha maganizo ake. Iye anayamba kuona kuti cofunika kwambili si mmene anali kumvelela. Akulu a mumpingo ndi mkazi wake anamulimbikitsa cakuti m’kupita kwa nthawi, anayambanso kutumikila Yehova. Cina cimene cinathandiza Jim ni kuŵelenga nkhani yakuti “Yehova Sayenela Kuimbidwa Mlandu” ndi yakuti “Tumikilani Yehova Mokhulupilika,” zimene zili mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1992.

12 M’kupita kwa nthawi, Jim anaikidwanso kukhala mkulu. Iye tsopano amathandiza abale ena kulimbitsa cikhulupililo cawo ndi kuthetsa mavuto ofanana ndi amene iye anakumana nawo. Jim amakamba kuti ubwenzi wake ndi Yehova sunali wolimba ngakhale kuti iye anali kuona kuti unali wolimba. Iye amakamba kuti sanacite bwino kulola mzimu wonyada kumupangitsa kumangoganizila zolakwa za ena m’malo moganizila zinthu zofunika kwambili.—1 Akorinto 10:12.

Ngati titengela makhalidwe a Khiristu, anthu adzayamba kukopeka ndi uthenga wathu ndipo angasinthe mmene amationela

13. Kodi nchito yolalikila imatithandiza kukhala ndi makhalidwe ya bwanji? Nanga pamakhala zotulukapo za bwanji?

13 Kulalikila kungatiumbe ndi kutithandiza kukhala anthu abwino. Takamba zimenezi cifukwa pamene tilalikila uthenga wabwino, timafunika kukhala odzicepetsa ndi kuonetsa makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umatulutsa. (Agalatiya 5:22, 23) Ganizilani makhalidwe abwino amene mwakhala nawo cifukwa cogwila nchito yolalikila. Ngati titengela makhalidwe a Khiristu, anthu adzakopeka ndi uthenga wathu ndipo adzasintha mmene amationela. Mwacitsanzo, Mboni za Yehova ziŵili ku dziko la Australia zinafika pa nyumba ya mayi wina ndi kuyamba kumulalikila, koma iye anakwiya kwambili ndi kuwakalipila. Komabe, Mbonizo zinamvetsela mwaulemu pamene iye anali kukamba. Patapita nthawi, mayiyo anacita manyazi ndi zimene anacita ndipo analembela kalata ofesi ya nthambi. M’kalatamo, iye anapepesa cifukwa ca zimene anacita. Anakamba kuti, “Niona kuti ndine wopusa kwambili. Sin’nafunike kukalipila anthu amene anasiya zocita zawo ndi kubwela kudzaniphunzitsa Mau a Mulungu.” Malinga ndi citsanzoci tikhoza kuona kuti kukhala oleza mtima pamene tilalikila n’kofunika. N’zoona kuti timagwila nchito yolalikila kuti tithandize ena koma nchitoyi imatithandizanso kuongolela umunthu wathu.

MUZICITA MBALI YANU PAMENE MULUNGU AKUUMBA ANA ANU

14. Kodi makolo ayenela kucita ciani kuti akwanitse kuumba ana awo?

14 Ana ambili ni odzicepetsa ndipo amafuna kuphunzila zinthu zatsopano. (Mateyu 18:1-4) Conco makolo angacite bwino kuphunzitsa ana awo kukonda coonadi akali ang’ono. (2 Timoteyo 3:14, 15) Koma kuti akwanitse kucita zimenezi, makolo ayenela kukonda coonadi ndi kutsatila zimene Baibulo imakamba. Ngati makolo acita izi, cidzakhala cosavuta kwa ana awo kukonda coonadi. Cina, anawo adzadziŵa kuti cilango cimene makolo awo amawapatsa cimaonetsa kuti amawakonda ndi kuti Yehova naye amawakonda.

15, 16. Kodi makolo angaonetse bwanji kuti amakonda Yehova ngati mwana wawo wacotsedwa mumpingo?

15 Nthawi zina makolo amaphunzitsa ana awo coonadi bwinobwino. Koma ana ena amasiya Yehova kapena kucotsedwa mumpingo. Izi zikacitika, banja lonse limakhudzidwa kwambili. Mlongo wina wa ku South Africa anakamba kuti: “Pamene mlongosi wanga anacotsedwa mumpingo, n’namvela monga wamwalila.” Cinaniŵaŵa kwambili!” Koma kodi mlongoyo ndi makolo ake anacita ciani? Iwo anamvela malangizo a m’Baibulo. (Ŵelengani 1 Akorinto 5:11, 13.) Makolowo anadziŵa kuti kumvela malangizo a Mulungu kudzapindulitsa onse m’banjalo. Anadziŵanso kuti makonzedwe akuti ocimwa azicotsedwa mumpingo ni njila imene Yehova amatilangila mwacikondi. Conco, anali kukambilana ndi mnyamatayo pokhapo ngati pali zinthu zofunika kwambili za pabanja zimene ayenela kukambilana.

16 Kodi mwanayo anali kumvela bwanji? Patapita nthawi, anakamba kuti, “N’nali kudziŵa kuti anthu a pabanja langa sanizonda, koma amafuna kumvela malangizo a Yehova ndi gulu lake.” Anakambanso kuti, “Ukakamizika kupempha Yehova kuti akukhululukile ndi kukuthandiza, m’pamene umadziŵa kuti umafunikila citsogozo cake.” Mwacionekele, banjalo linasangalala kwambili pamene mnyamatayo anabwelela kwa Yehova. Kukamba zoona, tingakhale osangalala pokhapo ngati timvela Mulungu nthawi zonse.Miyambo 3:5, 6; 28:26.

Ngati ndife odzicepetsa ndipo timamvela Yehova nthawi zonse, iye adzatikonda kwambili

17. N’cifukwa ciani tiyenela kumvela Yehova nthawi zonse? Nanga tikacita zimenezo tidzapindula bwanji?

17 Mneneli Yesaya anakambilatu kuti Ayuda a ku Babulo adzalapa ndi kukamba kuti: “Inu Yehova, inu ndinu Atate wathu. Ife ndife dothi ndipo inu ndinu Wotiumba. Tonsefe ndife nchito ya manja anu.” Iwo adzacondelela Yehova mwa kukamba kuti: “Musakumbukile zolakwa zathu kwamuyaya. Conde, kumbukilani kuti tonsefe ndife anthu anu.” (Yesaya 64:8, 9) Ngati tikhala odzicepetsa ndi kumvela Yehova nthawi zonse, iye adzatikonda kwambili monga mmene anakondela Danieli. Yehova adzapitiliza kutiumba pogwilitsila nchito Mau ake, mzimu wake, ndi gulu lake n’colinga cakuti mtsogolo tidzakhale “ana a Mulungu” angwilo.—Aroma 8:21.