Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Musakhumudwe Ndi Zolakwa za Ena

Musakhumudwe Ndi Zolakwa za Ena

“Pitilizani . . . kukhululukilana ndi mtima wonse.”—AKOLOSE 3:13.

NYIMBO: 121, 75

1, 2. Kodi Baibulo inakambilatu ciani ponena za kuculuka kwa anthu a Yehova?

PADZIKO lapansi pali gulu la anthu amene amakonda Yehova ndi kum’tumikila. Anthu amenewa ni Mboni za Yehova. Ngakhale kuti a Mboni ali ndi zofooka ndipo amalakwitsa zinthu zina, Yehova amawatsogolela ndi mzimu woyela. Tiyeni tione mmene Mulungu wawadalitsila.

2 Mu 1914, ni anthu ocepa amene anali kulambila Yehova. Koma Yehova watidalitsa pa nchito yolalikila. Zotsatila zake n’zakuti anthu mamiliyoni ambili aphunzila coonadi ca m’Baibulo ndi kukhala Mboni zake. Yehova anakambilatu za kupita patsogolo kumeneku. Iye anati, “Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wocepa adzasanduka mtundu wamphamvu. Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.” (Yesaya 60:22) N’zoonekelatu kuti ulosi umenewu ukukwanilitsika masiku ano. Anthu a Yehova ali ngati mtundu waukulu. Ndipo padzikoli pali maiko ambili amene ciŵelengelo ca anthu m’dziko lililonse palokha n’cocepa poyelekezela ndi ciŵelengelo ca anthu onse a Yehova.

3. Kodi atumiki a Mulungu aonetsa bwanji kuti amakondana?

3 M’masiku ano otsiliza, Yehova waphunzitsa anthu ake kukhala okondana kwambili. Iwo amatengela citsanzo cake cifukwa “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:8) Yesu analamula otsatila ake kuti ‘azikondana.’ Iye anawauzanso kuti: “Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.” (Yohane 13:34, 35) M’zaka za posacedwapa, atumiki a Yehova aonetsa kuti amakondana ngakhale pa nthawi ya nkhondo. Mwacitsanzo, pa nkhondo yaciŵili ya pa dziko lonse, anthu pafupifupi 55 miliyoni anaphedwa. Koma anthu a Yehova sanapheko munthu aliyense. (Ŵelengani Mika 4:1, 3.) Izi zawathandiza kuti akhale “oyela pa mlandu wa magazi a anthu onse.”—Machitidwe 20:26.

4. N’cifukwa ciani n’zocititsa cidwi kuti gulu la Yehova likukulilakulila?

4 Anthu a Mulungu akupitilizabe kuculuka ngakhale kuti ali ndi mdani wamphamvu, Satana. Iye ni “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akorinto 4:4) Satana ndiye amalamulila magulu andale ndi ofalitsa nkhani, ndipo amawaseŵenzetsa kuti aletse nchito yolalikila uthenga wabwino. Koma sangakwanitse kulepheletsa nchito imeneyi. Iye adziŵa kuti watsala ndi kanthawi kocepa. Conco amayesabe kutiletsa kulambila Yehova.—Chivumbulutso 12:12.

KODI MUDZAKHALABE WOKHULUPILIKA ANTHU ENA AKALAKWITSA?

5. N’cifukwa ciani nthawi zina anthu ena amatikhumudwitsa? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

5 Atumiki a Mulungu amadziŵa kuti afunika kukonda Mulungu ndi anthu ena. Yesu anati: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambili komanso loyamba. Laciŵili lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.’” (Mateyu 22:35-39) Komabe, Baibulo imakamba kuti anthu onse amabadwa opanda ungwilo cifukwa ca ucimo wa Adamu. (Ŵelengani Aroma 5:12, 19.) Motelo, nthawi zina ena mumpingo angakambe kapena kucita zinthu zimene zingatikhumudwitse. Kodi mudzacita ciani ngati zotelo zakucitikilani? Kodi mudzapitilizabe kukonda Yehova ndi mtima wonse? Kodi mudzakhalabe wokhulupilika kwa iye ndi kwa anthu ake? Baibulo imakamba za atumiki ena a Mulungu amene anakamba kapena kucita zinthu zimene zinakhumudwitsa ena. Tiyeni tikambilane zimene zinacitika ndiponso zimene tingaphunzilepo.

Kodi mukanakhala ku Isiraeli m’nthawi ya Eli ndi ana ake, sembe munacita ciani? (Onani ndime 6)

6. Kodi Eli analephela bwanji kulanga ana ake?

6 Mwacitsanzo, Eli anali mkulu wa ansembe ku Isiraeli, koma ana ake aŵili aamuna anali kuphwanya malamulo a Yehova. Baibulo imati: “Ana aamuna a Eli anali anthu opanda pake. Iwo anali kunyalanyaza Yehova.” (1 Samueli 2:12) Eli anali kudziŵa kuti ana ake akucita zinthu zoipa kwambili. Koma sanali kuwalangiza mwamphamvu. Kenako Yehova analanga Eli ndi ana ake aŵiliwo. Pambuyo pake, Mulungu sanalolenso mbadwa iliyonse ya Eli kutumikila monga mkulu wa ansembe. (1 Samueli 3:10-14) Mukanakhalapo m’nthawi ya Eli ndi kumuona akulekelela ana ake kucita zinthu zonyansa, kodi sembe munakhumudwa? Kodi mukanalola zimenezi kufooketsa cikhulupililo canu mpaka kuleka kutumikila Yehova?

7. Ni macimo aakulu ati amene Davide anacita? Nanga Mulungu anacita ciani?

7 Davide anali ndi makhalidwe abwino kwambili. Ndiye cifukwa cake Yehova anali kumukonda kwambili. (1 Samueli 13:13, 14; Machitidwe 13:22) Koma nthawi ina Davide anacita zinthu zoipa kwambili. Pamene Uriya anali kunkhondo, Davide anacita cigololo ndi mkazi wa Uriya, Bati-seba, ndipo anakhala ndi pakati. Davide sanafune kuti anthu adziŵe zimene anacitazo. Cotelo anaitanitsa Uriya ndi kumunyengelela kuti apite kunyumba kwake. Davide anali kuganiza kuti Uriya akapita kunyumba kwake ndi kugona ndi mkazi wake, Bati-seba, anthu adzayamba kuona kuti mwana ni wa Uriya. Koma Uriya anakana kupita kunyumba kwake. Conco, Davide anam’konzela ciwembu kuti akaphedwe ku nkhondo. Cifukwa ca macimo amenewa, Davide ndi banja lake anakumana ndi mavuto aakulu. (2 Samueli 12:9-12) Koma Yehova anamucitila cifundo ndi kumukhululukila. Iye anadziŵa kuti Davide anali ndi mtima wabwino. (1 Mafumu 9:4) Mukanakhalapo nthawi imeneyo, kodi mukanamvela bwanji ndi zimene Davide anacita? Kodi mukanaleka kutumikila Yehova?

8. (a) Kodi mtumwi Petulo analephela bwanji kusunga lonjezo lake? (b) N’cifukwa ciani Yehova anapitiliza kugwilitsila nchito Petulo pambuyo pakuti wacimwa?

8 Citsanzo cina ca m’Baibulo ni ca mtumwi Petulo. Yesu anamusankha kuti akhale mtumwi. Ngakhale zinali conco, Petulo nthawi ina anakamba ndi kucita zinthu zolakwika. Mwacitsanzo, Petulo anakamba kuti sangamusiye Yesu ngakhale anzake ena onse atathawa. (Maliko 14:27-31, 50) Koma Yesu atagwidwa, atumwi onse anamuthaŵa, kuphatikizapo Petulo. Kenako, Petulo anakana Yesu katatu. (Maliko 14:53, 54, 66-72) Pambuyo pake, Petulo anamva cisoni kwambili ndi zimene anacitazo. Conco, Yehova anamukhululukila ndipo anapitiliza kumuseŵenzetsa. Mukanakhala kuti ndinu wophunzila wa Yesu ndipo mwadziŵa zimene Petulo wacita, kodi sembe munapitiliza kukhulupilila Yehova?

Sitiyenela kukaikila kuti Yehova nthawi zonse amacita zinthu zoyenela ndi zacilungamo

9. Kodi mumakhulupilila kuti Mulungu nthawi zonse amacita zinthu mwacilungamo? Cifukwa ciani?

9 Zitsanzo zimenezi zionetsa kuti atumiki ena a Yehova anacitapo zolakwa zimene zinakhumudwitsa kwambili anthu ena. Kodi mungacite ciani ngati zotele zacitika masiku ano? Kodi mungaleke kusonkhana kapena mungasiye Yehova ndi gulu lake? Kapena mungakumbukile kuti Yehova ni wacifundo ndipo amayembekezela kuti munthu alape? Koma nthawi zina, munthu amene wacita chimo lalikulu angaonetse mzimu wosalapa. Kodi mudzakhalabe ndi cikhulupililo cakuti Yehova adziŵa zimenezi ndipo adzacitapo kanthu panthawi yoyenela? Iye angacotse munthuyo mumpingo ngati waona kuti afunika kucita zimenezo. Kodi mumakhulupilila kuti Yehova nthawi zonse amacita zinthu zoyenela ndi zacilungamo?

PITILIZANI KUKHALA WOKHULUPILIKA

10. Kodi Yesu anazindikila ciani pa zolakwa za Yudasi Isikariyoti ndi Petulo?

10 Baibulo imakamba za anthu ambili amene anakhalabe okhulupilika kwa Yehova ngakhale kuti anthu amene anali kukhala nao anacita zolakwa zazikulu. Yesu n’citsanzo cabwino kwambili pankhani imeneyi. Iye anapemphela usiku wonse kwa Atate wake kuti amuthandize kusankha atumwi. Kenako anasankha atumwi ake 12. Koma mmodzi wa iwo, “Yudasi Isikariyoti,” anam’peleka kwa adani ake. Ndiponso mtumwi Petulo anakana Yesu. (Luka 6:12-16; 22:2-6, 31, 32) Pamene ophunzila ake ena anamukhumudwitsa, Yesu sanaimbe mlandu Yehova kapena ophunzila ena osalakwa. Koma anakhalabe pa ubwenzi wabwino ndi Atate wake ndipo anapitilizabe kuwatumikila mokhulupilika. Pa cifukwa cimeneci, Yehova anamudalitsa mwa kumuukitsa ndi kumuika kukhala Mfumu ya Ufumu wakumwamba.—Mateyu 28:7, 18-20.

11. Kodi Baibulo inakamba ciani ponena za atumiki a Yehova a masiku ano?

11 Citsanzo ca Yesu citiphunzitsa kuti tifunika kukhala okhulupilika kwa Yehova ndi kwa anthu ake. Pali zifukwa zambili zimene tiyenela kucitila zimenezi. Taona kuti Yehova akutsogolela atumiki ake masiku ano otsiliza. Akuwathandiza kulalikila coonadi padziko lonse, ndipo ni iwo okha amene akugwila nchito imeneyi. Iwo ni ogwilizana ndiponso osangalala cifukwa ca zimene Yehova amawaphunzitsa. Yehova anafotokoza zimenezi pamene anati: “Atumiki anga adzafuula mokondwa cifukwa cokhala ndi cimwemwe mumtima.”—Yesaya 65:14.

Kungakhale kupanda nzelu ndiponso kulakwa kusiya Yehova ndi anthu ake cifukwa cakuti munthu winawake watilakwila

12. Kodi tiyenela kucita ciani ena akatilakwila?

12 Timakhala acimwemwe cifukwa cakuti Yehova amatitsogolela ndi kutithandiza kucita zinthu zambili zabwino. Koma anthu m’dziko la Satanali si osangalala ndipo alibe ciyembekezo codalilika. Kungakhale kupanda nzelu ndiponso kulakwa kusiya Yehova ndi anthu ake cifukwa cakuti munthu winawake mumpingo watilakwila kapena wakamba mau oipa. M’malomwake, tifunika kukhalabe okhulupilika kwa Yehova ndi kutsatila malangizo ake. Tifunikanso kuphunzila zimene tiyenela kucita ena akatilakwila.

KODI MUYENELA KUCITA BWANJI WINA AKAKULAKWILANI?

13, 14. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kukhala oleza mtima ndi abale athu? (b) Ni lonjezo liti limene tiyenela kumakumbukila?

13 Kodi tiyenela kucita bwanji ngati m’bale wathu wakamba mau oipa kapena wacita zinthu zimene zatikhumudwitsa? Baibulo imatilangiza kuti: “Usamafulumile kukwiya mumtima mwako, pakuti anthu opusa ndi amene sacedwa kupsa mtima.” (Mlaliki 7:9) Tonse ndife ocimwa ndipo timalakwitsa. Conco, sitingayembekezele kuti abale athu azikamba kapena kucita zinthu zabwino zokhazokha. Ndipo si bwino kumangoganizila zolakwa zawo. Ngati ticita zimenezo, sitingakhale acimwemwe potumikila Yehova. Coipa kwambili kuposa pamenepo n’cakuti cikhulupililo cathu cingafooke, ndipo tingaleke kugwilizana ndi gulu la Yehova. Pamapeto pake, tingaleke kutumikila Yehova ndi kutaya mwai wodzakhala m’dziko latsopano.

14 Ngati ena akukhumudwitsani, kodi n’ciani cingakuthandizeni kukhalabe wacimwemwe potumikila Yehova? Nthawi zonse muzikumbukila lonjezo lolimbikitsa ili la Mulungu: “Ndikulenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zinthu zakale sizidzakumbukilidwanso ndipo sizidzabwelanso mumtima.” (Yesaya 65:17; 2 Petulo 3:13) Yehova adzakupatsani madalitso amenewa ngati mukhalabe okhulupilika kwa iye.

15. Kodi Yesu anakamba kuti tiyenela kucita ciani ena akatilakwila?

15 Tikalibe kuloŵa m’dziko latsopano. Conco, ngati munthu wina watikhumudwitsa, tiyenela kuganizila zimene Yehova amafuna. Mwacitsanzo, Yesu anati: “Mukamakhululukila anthu macimo awo, inunso Atate wanu wakumwamba adzakukhululukilani. Koma ngati simukhululukila anthu macimo awo, Atate wanu sadzakukhululukilani macimo anu.” Nthawi ina Petulo anafunsa Yesu ngati tifunika kukhululukila ena “mpaka nthawi 7.” Yesu anamuyankha kuti “Ndikukuuza kuti, osati nthawi 7 zokha ayi, koma, mpaka nthawi 77.” Yesu anatiphunzitsa kuti nthawi zonse tiyenela kukhala okonzeka kukhululukila ena.—Mateyu 6:14, 15; 18:21, 22.

16. N’citsanzo cabwino citi cimene Yosefe anapeleka?

16 Kuganizila citsanzo ca Yosefe kungatithandize kudziŵa zimene tiyenela kucita ngati ena atikhumudwitsa. Yosefe ndi mng’ono wake anali ana aŵili okhawo amene Rakele anabelekela Yakobo. Yakobo anali ndi ana ena 10 aamuna, koma anali kukonda kwambili Yosefe. Zimenezi zinapangitsa kuti abale ake azimucitila nsanje. Iwo anali kumuzonda kwambili cakuti anamugulitsa monga kapolo, ndipo anthu amene am’gulawo anapita naye ku Iguputo. Patapita zaka zambili, mfumu ya ku Iguputo inaika Yosefe kukhala munthu waciŵili wapamwamba kwambili m’dzikolo cifukwa cakuti inacita cidwi ndi luso lake pa nchito. Pambuyo pake, abale a Yosefe anapita ku Iguputo kukagula cakudya cifukwa cakuti kwawo kunali njala. Ataona Yosefe, sanamudziŵe, koma iye anawadziŵa. Ngakhale kuti abale akewo anamucitila nkhanza, iye sanawakhaulitse koma anawayesa kuti aone ngati anasinthadi. Yosefe atadziŵa kuti anasintha, anadziulula kuti ni m’bale wawo. Pambuyo pake anawalimbikitsa ndi mau akuti: “Musacite mantha. Ine ndipitiliza kukugaŵilani cakudya limodzi ndi ana anu.”—Genesis 50:21.

17. Kodi inu mudzacita ciani ngati ena akulakwilani?

17 Tiyenelanso kukumbukila kuti popeza tonse tili ndi zofooka, ifenso nthawi zina tingakhumudwitse ena. Cotelo ngati mwakhumudwitsa munthu wina, muyenela kutsatila malangizo a m’Baibulo. M’pempheni kuti akukhululukileni, ndipo yesetsani kubwezeletsa mtendele. (Ŵelengani Mateyu 5:23, 24.) Timasangalala ngati ena atikhululukila. Ndiye cifukwa cake ifenso tiyenela kukhululukila ena. Lemba la Akolose 3:13 limati: “Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake. Monga Yehova anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso teloni.” Ngati timakondadi abale athu, tidzapewa kuwasungila zifukwa akatilakwila. (1 Akorinto 13:5) Komanso ngati tikhululukila ena, Yehova nayenso adzatikhululukila. Conco, ena akatilakwila, tiyeni tiziwacitila cifundo, monga mmene Atate wathu, Yehova, amacitila kwa ife.—Ŵelengani Salimo 103:12-14.