Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi
M’masophenya a Ezekieli, kodi mwamuna amene anali ndi kacikwama ka mlembi, konyamulilamo inki ndi zolembela ndiponso amuna 6 onyamula zida zophwanyila amaimila ndani?
Iwo amaimila zolengedwa zamphamvu zakumwamba zimene zinawononga mzinda wa Yerusalemu ndipo zidzawononganso dziko loipa la Satanali pa Aramagedo. Aka n’kamvedwe katsopano. N’cifukwa ciani tasintha kamvedwe kathu?
Caka ca 607 B.C.E. cisanafike, Yehova anaonetsa Ezekieli masomphenya a zimene zidzacitika m’Yerusalemu, mzindawo utatsala pang’ono kuonongeka. M’masophenya amenewo, Ezekieli anaona zinthu zambili zoipa zikucitika mumzindawo. Kenako anaona amuna 6, aliyense wa iwo atanyamula “cida cake cophwanyila.” Pakati pawo panalinso munthu mmodzi “atavala zovala zansalu” ndipo anali ndi “kacikwama ka mlembi, konyamulilamo inki ndi zolembela.” (Ezekieli 8:6-12; 9:2, 3) Munthu ameneyo anauzidwa kuti apite mumzinda ‘kukalemba cizindikilo pamphumi za anthu amene anali kuusa moyo ndi kubuula cifukwa ca zonyansa zonse zimene zinali kucitika mumzindawo.’ Ndipo amuna 6 onyamula zida zophwanyila anauzidwa kuti aphe anthu onse a mumzinda amene sanaikidwe cizindikilo. (Ezekieli 9:4-7) Kodi tiphunzilapo ciani pa masomphenya amenewa? Nanga munthu amene ananyamula kacikwama ka mlembi konyamulilamo inki ndi zolembela ndani?
Ezekieli anaona masomphenya amenewa mu 612 B.C.E. Masomphenya amenewa ni ulosi umene unakwanilitsika koyamba patapita zaka 5, panthawi imene Yehova analola asilikali a Babulo kuwononga mzinda wa Yerusalemu. Mwakutelo, Yehova analola Ababulo kulanga anthu ake osamvela. (Yeremiya 25:9, 15-18) N’ciani cinacitikila Ayuda osalakwa amene sanali kucitako zoipa mumzindawo? Yehova anawapulumutsa.
M’masophenyawo, Ezekieli si amene anali kuika cizindikilo kapena kupha anthu a mumzindawo. Angelo ni amene anawononga mzinda wa Yerusalemu. Conco, ulosi umenewu umatipatsa mwayi wodziŵa zimene zinacitika kumwamba. Yehova analamula magulu ankhondo a kumwamba kuti awononge anthu oipa ndi kupulumutsa anthu olungama. *
Ulosi umenewu udzakwanilitsikanso mtsogolo. Kale tinali kukamba kuti munthu amene ananyamula kacikwama ka mlembi konyamulilamo inki amaimila odzozedwa amene akali padziko. Tinali kukambanso kuti anthu akalandila uthenga wabwino umene tawalalikila, ndiye kuti aikidwa cizindikilo. Koma posacedwapa, tinaona kuti m’poyenela kusintha mmene timafotokozela ulosi umenewu. Pa Mateyu 25:31-33 tinaphunzila kuti Yesu ni amene adzaweluza anthu. Iye adzacita zimenezi mtsogolo pa nthawi ya cisautso cacikulu. Pa nthawi imeneyo, onse amene adzaweluzidwa monga nkhosa adzapulumuka, ndipo amene adzaweluzidwa monga mbuzi adzawonongedwa.
Kodi tiphunzilapo ciani pa masomphenya a Ezekieli amenewa? Tiphunzilapo mfundo zisanu izi:
-
Mzinda wa Yerusalemu usanawonongedwe, Ezekieli, Yeremiya, ndi Yesaya anacenjeza anthu kuti mzindawo udzawonongedwa. Iwo anali ngati alonda. Masiku ano, Yehova akuseŵenzetsa kagulu ka odzozedwa pophunzitsa anthu ake ndi kucenjeza anthu ena cisautso cacikulu cisanafike. Atumiki onse a Mulungu amene ni anchito a pakhomo a Khiristu, akugwila nchito yocenjeza anthu imeneyi.—Mateyu 24:45-47.
-
Ezekieli sanaike cizindikilo anthu amene anafunika kupulumuka. Nawonso anthu a Yehova masiku ano saika cizindikilo anthu amene adzapulumuka. Amangolalikila ena ndi kuwacenjeza za zinthu zimene zidzacitika mtsogolo. Nchito yolalikila imeneyi ikucitika padziko lonse lapansi mothandizidwa ndi angelo.—Chivumbulutso 14:6.
-
Anthu amene anapulumuka m’nthawi ya Ezekieli sanaikidwe cizindikilo ceniceni pamphumi zawo. Mofananamo, anthu amene adzapulumuka sadzaikidwa cizindikilo ceniceni. Kodi anthu ayenela kucita ciani kuti adzapulumuke cisautso cacikulu? Iwo afunika kumvela cenjezo, kutengela Khiristu, kudzipeleka kwa Mulungu, ndi kucilikiza abale a Khiristu pa nchito yolalikila uthenga wabwino. (Mateyu 25:35-40) Pa cisautso cacikulu, iwo adzaikidwa cizindikilo, kutanthauza kuti adzapulumutsidwa.
-
Munthu amene ananyamula kacikwama konyamulilamo inki akuimila Yesu. Pa cisautso cacikulu, iye adzaika cizindikilo a khamu lalikulu pamene adzawaweluza kuti ni nkhosa. Iwo adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha padziko lapansi.—Mateyu 25:34, 46. *
-
Masiku ano, amuna 6 onyamula zida zophwanyila aimila gulu la angelo lotsogoleledwa ndi Yesu. Posacedwa, iwo adzawononga mitundu ya anthu ndi kuthetsa kuipa konse.—Ezekieli 10:2, 6, 7; Chivumbulutso 19:11-21.
Zimene taphunzila m’masophenya amenewa zatithandiza kukhulupilila kuti Yehova sadzawononga anthu olungama pamodzi ndi oipa. (2 Petulo 2:9; 3:9) Zatithandizanso kuona kuti nchito yolalikila ni yofunika kwambili masiku ano. Munthu aliyense afunika kucenjezedwa mapeto asanafike.—Mateyu 24:14.
^ par. 6 Anthu amene anapulumuka, monga Baruki (mlembi wa Yeremiya), Ebedi-meleki Mwiitiyopiya, ndi Arekabu, sanali ndi cizindikilo ceniceni pamphumi pawo. (Yeremiya 35:1-19; 39:15-18; 45:1-5) Cizindikilo cimene anaikidwa cinali cophiphilitsa, ndipo cinali kutanthauza cabe kuti adzapulumuka.
^ par. 12 Odzozedwa amene ni okhulupilika sadzafunikila cizindikilo cimeneci kuti apulumuke. Koma adzalandila cidindo comaliza akalibe kufa kapena cisautso cacikulu cisanayambe.—Chivumbulutso 7:1, 3.