“Yehova Mulungu Wathu Ndi Yehova Mmodzi”
“Tamvelani, Aisiraeli inu: Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.” —DEUTERONOMO 6:4.
NYIMBO: 138, 112
1, 2. (a) N’cifukwa ciani mau a pa Deuteronomo 6:4 ndi odziŵika kwambili? (b) N’cifukwa ciani Mose anakamba mau amenewo?
KWA zaka zambili, Ayuda popeleka pemphelo lawo lapadela, akhala akuchula mau amene ali pa Deuteronomo 6:4. Pemphelo limenelo limachedwa Shema. Shema ni liu loyambilila pa vesi imeneyi m’Ciheberi. Ayuda ambili amapeleka pempheloli tsiku lililonse m’maŵa ndi m’madzulo pofuna kuonetsa kudzipeleka kwawo kwa Mulungu.
2 Mose anakamba mau amenewa pamene anali kukamba nkhani yake yotsiliza ku mtundu wa Aisiraeli. Mu 1473, Khiristu asanabwele, mtunduwo unali m’dziko la Mowabu, ndipo unali wokonzeka kuoloka Mtsinje wa Yorodano ndi kulanda Dziko Lolonjezedwa. (Deuteronomo 6:1) Mose anali atatsogolela anthuwo kwa zaka 40, ndipo anali kufuna kuti iwo akhale olimba mtima kuti akakwanitse kulimbana ndi mavuto amene angakumane nawo mtsogolo. Anafunika kudalila Mulungu wawo, Yehova, ndi kukhala okhulupilika kwa iye. Conco, mau otsiliza a Mose analimbikitsa Aisiraeli kucita zimenezo. Pambuyo pochula Malamulo 10, ndi ena amene Yehova anapeleka, Mose anawakumbutsa mfundo yofunika kwambili imene ili pa Deuteronomo 6:4, 5. (Ŵelengani.)
3. Ni mafunso ati amene tikambilana m’nkhani ino?
3 Aisiraeli anali kudziŵa kuti Yehova Mulungu wawo ni “Yehova mmodzi.” Aisiraeli okhulupilika anali kulambila Mulungu mmodzi, amene anali Mulungu wa makolo awo. Nanga n’cifukwa ciani Mose anawakumbutsa kuti Yehova Mulungu wawo ni “Yehova mmodzi”? Kodi mfundo imeneyi igwilizana bwanji ndi mfundo yakuti tiyenela kukonda Mulungu ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, ndi mphamvu zathu zonse? Nanga mau a pa Deuteronomo 6:4, 5 amatikhudza bwanji masiku ano?
MULUNGU WATHU NI “YEHOVA MMODZI”
4, 5. (a) Kodi mau akuti “Yehova mmodzi” atanthauza ciani? (b) Nanga Yehova amasiyana bwanji ndi milungu ya mitundu ina?
4 Ni wapadela. Mau akuti “Yehova mmodzi” atanthauza kuti Yehova ni wapadela, palibe wolingana naye. N’cifukwa ciani Mose anakamba mau amenewa? Pamene Mose anakamba mau amenewa sanali kukamba za ciphunzitso cabodza ca utatu. Yehova ndiye anapanga kumwamba ndi dziko lapansi ndipo ndiye Wolamulila cilengedwe conse. Iye yekha ndiye Mulungu woona, ndipo palibe mulungu wina wolingana naye. (2 Samueli 7:22) Cotelo, mau a Mose anali kukumbutsa Aisiraeli kuti afunika kulambila Yehova yekha. Iwo sanafunike kutengela anthu olambila milungu yonama amene anali kukhala nawo pafupi. Anthu amenewo anali kukhulupilila kuti milungu yawo ingalamulile zinthu zina zacilengedwe.
5 Mwacitsanzo, Aiguputo anali kulambila mulungu wa dzuŵa Ra, wa makumbi Nut, wa dziko lapansi Geb, wa mtsinje wa Nailo Hapi, kuphatikizapo nyama zosiyanasiyana. Yehova anaonetsa kuti ni wapamwamba kwambili kuposa milungu yonama imeneyo pamene anabweletsa Milili 10. Akanani ambili anali kulambila Baala, mulungu wonama amene iwo anali kukhulupilila kuti ndiye anapanga moyo ndi kuti ndiye mulungu wa makumbi, mvula, ndi mphepo. M’madela ambili, anthu anali kudalila Baala kuti awateteze. (Numeri 25:3) Aisiraeli anafunika kumakumbukila kuti Mulungu wawo, “Mulungu woona,” ni wapadela. Iye ni “Yehova mmodzi.”—Deuteronomo 4:35, 39.
Yehova Mulungu sasinthasintha. Iye ni wokhulupilika, wodalilika, ndipo sanama.
6, 7. Kodi mau akuti “mmodzi,” amatanthauzanso ciani? Nanga Yehova anaonetsa bwanji kuti ni “mmodzi”?
6 Sasintha Ndipo ni Wokhulupilika. Liu lakuti “mmodzi” m’mau akuti “Yehova mmodzi” limatanthauzanso kuti colinga cake ndi zocita zake n’zodalilika nthawi zonse. Yehova Mulungu sasinthasintha. Iye ni wokhulupilika, wodalilika, ndipo sanama. Mwacitsanzo, analonjeza Abulahamu kuti mbadwa zake zidzakhala m’Dziko Lolonjezedwa. Ndipo Yehova anacita zozizwitsa zambili kuti akwanilitse lonjezo limenelo. Ngakhale patapita zaka 430 pambuyo popeleka lonjezolo, Genesis 12:1, 2, 7; Ekisodo 12:40, 41.
Yehova sanasinthe colinga cake.—7 Patapita zaka zambili, Yehova anacha Aisiraeli kuti ni Mboni zake ndipo anawauza kuti: “Ine sindinasinthe. Ine ndisanakhaleko kunalibe Mulungu amene anapangidwa, ndipo pambuyo panga palibenso wina.” Kuonjezela apo, Yehova anakamba kuti cifunilo cake sicisintha. Iye anati: “Nthawi zonse ine sindisintha.” (Yesaya 43:10, 13; 44:6; 48:12) Kukamba zoona, Aisiraeli anali ndi mwayi. Anali kutumikila Mulungu amene sasintha, ndiponso amene ni wokhulupilika nthawi zonse. Ifenso tili ndi mwayi umenewo.—Malaki 3:6; Yakobo 1:17.
8, 9. (a) Kodi Yehova amafuna kuti amene amamulambila azicita ciani? (b) Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti mau a Mose ni ofunika kwambili?
8 Mose anakumbutsa Aisiraeli kuti Yehova sadzasintha, ndipo adzapitiliza kuwakonda ndi kuwasamalila. Yehova anali kufuna kuti iwo akhale odzipeleka kwa iye yekha ndi kuti azimukonda ndi mtima wawo wonse, moyo wawo wonse, ndi mphamvu zawo zonse. Makolo anafunika kuphunzitsa ana awo pa mpata uliwonse umene apeza kuti naonso azitumikila Yehova yekha.—Deuteronomo 6:6-9.
9 Yehova sasintha colinga cake, conco sadzasintha zimene amayembekezela olambila ake kucita. Ngati tifuna kuti Yehova azikondwela pamene tim’tumikila, tiyenela kudzipeleka kwa iye yekha ndi kum’konda ndi mtima wathu wonse, maganizo athu onse, ndi mphamvu zathu zonse. Yesu anakamba kuti limeneli ndilo lamulo lofunika kwambili. (Ŵelengani Maliko 12:28-31.) Tiyeni tione mmene tingaonetsele mwa zocita zathu kuti timakhulupilila kuti “Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.”
KHALANI ODZIPELEKA KWA YEHOVA YEKHA
10, 11. (a) Tingaonetse bwanji kuti timalambila Yehova yekha? (b) Kodi acicepele aciheberi anaonetsa bwanji kuti anali odzipeleka kwa Yehova yekha?
10 Yehova yekha ndiye Mulungu wathu. Timaonetsa kuti ndife odzipeleka kwa Mulungu mwa kulambila iye yekha cabe. Sitiyenela kutumikila Yehova uku tikutumikilanso milungu ina kapena kukhulupilila zinthu zina zabodza. Sikuti iye ali cabe mulungu wamphamvu kuposa milungu ina. Yehova ndiye Mulungu woona, ndipo tifunika kulambila Iye yekha cabe.—Ŵelengani Chivumbulutso 4:11.
11 M’buku la Danieli, timaŵelenga za acicepele anai aciheberi awa; Danieli, Hananiya, Misayeli ndi Azariya. Iwo anaonetsa kuti anali odzipeleka kwa Yehova yekha mwa kukana kudya zakudya zodetsedwa zimene olambila Yehova anayenela kupewa. Kuonjezela pamenepo, anzake atatu a Danieli anakana kugwadila fano la golide limene Nebukadinezara anapanga. Iwo anaona kuti kumvela Yehova ndiye kofunika kwambili. Anali okhulupilika kwa Iye ndi mtima wonse.—Danieli 2:1–3:30.
Tiyenela kuika Yehova patsogolo mu umoyo wathu
12. Ngati tifuna kudzipeleka kwa Yehova yekha, kodi tiyenela kusamala ndi ciani?
12 Yehova ayenela kukhala patsogolo mu umoyo wathu. Ngati tifuna kukhala odzipeleka kwa iye yekha tiyenela kusamala kuti zinthu zina zisakhale patsogolo mu umoyo wathu. Kodi zinthu zimenezo Deuteronomo 5:6-10) Masiku ano, pali mitundu yambili ya kulambila mafano, ndipo ina sitingaidziŵe mwamsanga. Yehova sanasinthe zofuna zake. Iye akali “Yehova mmodzi.” Tiyeni tikambilane mmene tingapewele kulambila mafano masiku ano.
n’ziti? M’malamulo 10, Yehova anapeleka lamulo lakuti anthu ake sayenela kulambila milungu ina. Iwo sayenela kucita cinthu ciliconse cokhudzana ndi kulambila mafano. (13. N’zinthu ziti zimene tingayambe kukonda kwambili kuposa Yehova?
13 Lemba la Akolose 3:5. (Ŵelengani.) limafotokoza zinthu zina zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Taona kuti kusilila kwa nsanje n’kulambila mafano. N’cifukwa ciani zili telo? Ngati tifunitsitsa kwambili cinthu cina cake, monga ndalama zambili kapena zinthu zina zapamwamba, zinthuzo zingayambe kulamulila moyo wathu ndi kukhala mulungu wathu. Macimo onse amene achulidwa pa Akolose 3:5 amagwilizana ndi kusilila kwa nsanje kumene n’kulambila mafano. Ngati tifunitsitsa zinthu zimenezi, tingayambe kuzikonda kwambili kuposa mmene timakondela Mulungu. Ngati tacita zimenezo, Yehova sangakhale “Yehova mmodzi” kwa ife. Palibe amene angafune kucita zimenezo.
14. N’cenjezo liti limene Yohane anapeleka la mmene tiyenela kukondela Mulungu?
14 Mtumwi Yohane anakambapo mfundo yofanana ndi imeneyi. Anacenjeza kuti ngati munthu akonda kwambili zinthu za m’dzikoli “monga cilakolako ca thupi, cilakolako ca maso ndi kudzionetsela ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake” ndiye kuti “sakonda Atate.” (1 Yohane 2:15, 16) Conco aliyense wa ife ayenela kudzifufuza nthawi zonse ndi kuona ngati amakonda zinthu za m’dzikoli. Mwina tingazindikile kuti tayamba kukonda zosangulutsa, anthu, zovala, ndiponso kudzikongoletsa kwa m’dzikoli. Kapena tingafune kupeza “zinthu zazikulu” mwa kucita maphunzilo apamwamba. (Yeremiya 45:4, 5) Dziko latsopano lili pafupi kwambili. Motelo, tiyenela kumakumbukila mau a mphamvu a Mose. Ngati timamvetsetsa zimene mau akuti “Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi” amatanthauza, tidzam’konda ndi mtima wonse ndi kum’tumikila m’njila imene afuna.—Aheberi 12:28, 29.
TIZIKHALA OGWILIZANA MONGA AKHIRISTU
15. N’cifukwa ciani Paulo anakumbutsa Akhiristu kuti Mulungu ni “Yehova mmodzi”?
15 Mau akuti “Yehova mmodzi” amatithandiza kumvetsetsa kuti Yehova afuna kuti atumiki ake azigwilizana ndi kukhala ndi colinga cimodzi. Mumpingo wacikhiristu woyambilila, munali Ayuda, Agiriki, Aroma ndi anthu a mitundu ina. Iwo anali ocokela ku malo osiyanasiyana, anali ndi zikhalidwe zosiyana ndipo anali kukonda zinthu zosiyana. Cifukwa ca ici, cinali covuta kwa ena kuvomeleza njila yatsopano yolambilila kapena kuleka zinthu zosayenela zimene anali kucita. Conco, Paulo 1 Akorinto 8:5, 6.
anafunika kuwakumbutsa kuti Akhiristu ali ndi Mulungu mmodzi, Yehova.—ŴelenganiYehova afuna kuti atumiki ake azigwilizana ndi kukhala ndi colinga cimodzi
16, 17. (a) Ni ulosi wa bwanji umene ukukwanilitsika masiku ano? Nanga ukukwanilitsika bwanji? (b) N’ciani cingawononge mgwilizano wathu?
16 Nanga bwanji za mpingo wacikhiristu masiku ano? Mneneli Yesaya anakamba kuti “m’masiku otsiliza,” anthu ocokela ku mitundu yosiyanasiyana adzabwela pamodzi kuti alambile Yehova. Iwo adzakamba kuti: “Iye akatiphunzitsa njila zake, ndipo ife tidzayenda m’njila zakezo.” (Yesaya 2:2, 3) Ndife osangalala kwambili kuona ulosi umenewu ukukwanilitsika masiku ano. Abale ndi alongo athu amacoka ku malo osiyanasiyana, amakamba zitundu zosiyanasiyana, ndipo zikhalidwe zawo n’zosiyanasiyana. Koma ndife ogwilizana polambila Yehova. Komabe, cifukwa cakuti ndife osiyana, nthawi zina timasemphana maganizo.
17 Mwacitsanzo, kodi abale ndi alongo amene ali ndi cikhalidwe cosiyana ndi canu mumawaona bwanji? Kakambidwe kawo, kavalidwe kawo, ndi zakudya zawo, zingakhale zosiyana kwambili ndi zanu. Kodi mumawapewa ndi kuceza kwambili ndi aja amene amafanana ndi inu? Kodi akulu
amene ali m’dela lanu amene ni aang’ono pali inu mumawaona bwanji? Nanga amene anacokela ku mtundu kapena cikhalidwe cina mumawaona bwanji? Ngati sitisamala, tingalole kuti kusiyana kumeneko kuwononge mgwilizano pakati pathu.18, 19. (a) Ni malangizo otani amene ali pa Aefeso 4:1-3? (b) Tingacite ciani kuti tithandize mpingo kukhala wogwilizana?
18 Tingacite ciani kuti zimenezo zisacitike? Paulo anapeleka malangizo othandiza kwambili kwa Akhiristu amene anali kukhala ku Aefeso, mzinda umenewu unali wolemela ndipo unali ndi anthu ocokela ku malo osiyanasiyana. (Ŵelengani Aefeso 4:1-3.) Paulo anachula makhalidwe monga kudzicepetsa, kufatsa, kuleza mtima, ndi cikondi. Makhalidwe amenewa ali monga mizati yolimba imene imagwila nyumba. Koma kuti nyumba ikhalebe yolimba, khama n’lofunika. Paulo anali kufuna kuti Akhiristu a ku Efeso aziyesetsa ‘kusunga umodzi mwa mzimu.’
19 Tonse tiyenela kucita zimene tingathe kuti mpingo ukhalebe wogwilizana. Kodi tingacite bwanji zimenezo? Coyamba, tiyenela kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene Paulo anakamba amene ni kudzicepetsa, kufatsa, kuleza mtima, ndi cikondi. Caciŵili, tiyenela kuyesetsa “kusunga umodzi wathu mwa mzimuwo.” Monga nyumba imene nthawi zina imang’ambika, kusemphana maganizo kuli monga ming’alu ing’onoing’ono imene ingawononge mgwilizano wathu. Conco tiyenela kucita zimene tingathe kuti tithetse kusamvana kulikonse kumene kuli pakati pathu kuti tikhalebe ogwilizana ndiponso amtendele.
20. Tingaonetse bwanji kuti timamvetsetsa tanthauzo la mau akuti “Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi”?
20 “Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.” Mau amenewa ni a mphamvu kwambili. Analimbikitsa Aisiraeli kupilila mavuto amene anali kukumana nawo pamene analoŵa m’dziko Lolonjezedwa. Mauwa angatilimbikitse kwambili kuti tikapulumuke cisautso cacikulu, ndiponso angatithandize kukonzekela kudzakhala m’Paradaiso. Tiyeni tipitilize kutumikila Yehova ndi mtima wonse. Tiyenela kum’konda ndi mtima wonse ndi kum’tumikila ndi mtima wathu wonse, maganizo athu onse ndi mphamvu zathu zonse. Kuwonjezela pamenepo, tiyenela kucita zimene tingathe kuti pakati pathu pakhalebe mtendele ndi mgwilizano. Ngati tipitiliza kucita zimenezi, Yesu adzatiweluza monga nkhosa ndipo tidzaona kukwanilitsika kwa mau ake akuti: “Bwelani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate wanga. Loŵani mu ufumu umene anakonzela inu kucokela pa kukhazikitsidwa kwa dziko.”—Mateyu 25:34.