Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani Yophunzila 24

Gubuduzani Maganizo Aliwonse Otsutsana ndi Kudziŵa Mulungu!

Gubuduzani Maganizo Aliwonse Otsutsana ndi Kudziŵa Mulungu!

“Tikugubuduza maganizo komanso cochinga ciliconse cotsutsana ndi kudziŵa Mulungu.”—2 AKOR. 10:5.

NYIMBO 124 Tikhale Okhulupilika Nthawi Zonse

ZA M’NKHANI INO *

1. Ni cenjezo lotani limene mtumwi Paulo anapeleka kwa Akhristu odzozedwa?

MTUMWI Paulo anacenjeza Akhristu a m’nthawi yake kuti: “Musamatengele nzelu za nthawi ino.” (Aroma 12:2) N’cifukwa ciani Paulo anapeleka cenjezo limeneli kwa anthu amene anali kale Akhristu odzipeleka kwa Mulungu komanso odzozedwa na mzimu woyela?—Aroma 1:7.

2-3. Kodi Satana amacita ciani pofuna kuwononga ubwenzi wathu na Yehova? Nanga tingathetse bwanji maganizo oipa amene ‘anazikika molimba’ mu mtima mwathu?

2 Paulo anali kuwadela nkhawa Akhristuwo cifukwa zioneka kuti ena mwa iwo anali atayamba kuyendela maganizo na nzelu za m’dziko la Satana. (Aef. 4:17-19) Zaconco zingacitikilenso aliyense wa ife masiku ano. Satana, amene ni mulungu wa nthawi ino, amaseŵenzetsa misampha yosiyana-siyana kuti awononge ubale wathu na Yehova. Mwacitsanzo, ngati tili na mtima wodzikuza kapena wofuna kuchuka, iye angatengelepo mwayi kuti atipangitse kusokoneza ubwenzi wathu na Yehova. Satana angaseŵenzetsanso zinthu zina zimene tinaphunzila pa nyumba, ku sukulu, kapena kwa anthu okhala nawo pafupi, pofuna kutipangitsa kutengela maganizo ake.

3 Kodi n’zotheka kuthetsa maganizo oipa amene ‘anazikika molimba’ mumtima mwathu? (2 Akor. 10:4) Yankho ili m’mawu amene Paulo anakamba, akuti: “Tikugubuduza maganizo komanso cochinga ciliconse cotsutsana ndi kudziwa Mulungu, ndipo tikugonjetsa ganizo lililonse n’kulimanga ngati mkaidi kuti lizimvela Khristu.” (2 Akor. 10:5) Conco, ndi thandizo la Yehova, n’zotheka kuthetsa maganizo oipa. Monga mmene mankhwala amathetsela mphamvu ya poizoni, Mawu a Mulungu angatithandize kuthetsa maganizo oipa amene tingakhale nawo cifukwa cokhala m’dziko la Satanali.

“KUSINTHA MAGANIZO ANU”

4. Ni masinthidwe otani amene ambili a ife tinapanga pamene tinayamba kuphunzila coonadi?

4 Kodi n’zinthu ziti zimene munasintha mu umoyo wanu pamene munayamba kuphunzila coonadi ca m’Baibo na kutumikila Yehova? Mosakayikila, ambili a ife tinaleka makhalidwe oipa. (1 Akor. 6:9-11) Ndipo timayamikila kwambili kuti Yehova anatithandiza kucita zimenezi.

5. N’zinthu ziŵili ziti zochulidwa pa Aroma 12:2 zimene tiyenela kucita?

5 Koma tifunika kukhalabe osamala. Olo kuti tinaleka kucita macimo akulu-akulu amene tinali kucita tisanabatizike, tiyenela kuyesetsa kupewa ciliconse cimene cingatisonkhezele kuyambanso makhalidwe amenewo. Kodi tingacite bwanji zimenezi? Paulo anati: “Musamatengele nzelu za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu.” (Aroma 12:2) Conco, pali zinthu ziŵili zimene tiyenela kucita. Coyamba, tifunika kupewa ‘kutengela’ nzelu za dzikoli. Caciŵili, tifunika ‘kusandulika’ mwa kusintha maganizo athu.

6. Kodi tiphunzilapo ciani pa mawu amene Yesu anakamba pa Mateyu 12:43-45?

6 Kusandulika kumene Paulo anakamba kumatanthauza zambili, osati kusintha cabe maonekedwe athu. Kumatanthauza kusintha mbali iliyonse ya umoyo wathu. (Onani bokosi yakuti “ Kusandulika Kapena Ciphamaso Cabe?”) Tifunika kusandulika kothelatu, kutathauza kusintha zimene timaganiza mkatikati mwa mtima wathu, zolinga zathu, na zolakalaka zathu. Conco, aliyense wa ife afunika kudzifunsa kuti, ‘Kodi masinthidwe amene nikupanga mu umoyo wanga wacikhristu ni aciphamaso, kapena ni ocokeladi pansi pa mtima?’ Funso limeneli n’lofunika kwamibili. Mawu a Yesu pa Mateyu 12:43-45, amatithandiza kuona zimene tiyenela kucita kuti tisandulike. (Ŵelengani.) Zimene Yesu anakamba pa lembali zimatiphunzitsa mfundo yofunika kwambili yakuti: Kucotsa maganizo oipa mu mtima mwathu sikokwanila. Koma tifunikanso kuloŵetsamo maganizo abwino amene amakondweletsa Mulungu.

“MUKHALE ATSOPANO MU MPHAMVU YOYENDETSA MAGANIZO ANU”

7. Tingacite ciani kuti tisinthe umunthu wathu wamkati?

7 Kodi n’zotheka kusintha umunthu wathu wamkati kapena mphamvu yoyendetsa maganizo athu? Mawu a Mulungu amati: “Munaphunzitsidwa kuti mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu, ndi kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu ndipo umatsatila zofunika pa cilungamo ceniceni ndi pa kukhulupilika.” (Aef. 4:23, 24) Conco, n’zotheka kusintha umunthu wathu wamkati. Koma pamafunika khama. Tiyenela kuyesetsa kupondeleza zilakolako zoipa na kupewa makhalidwe oipa. Koma tiyenela kucita zoposa pamenepo. Tiyenelanso kusintha “mphamvu yoyendetsa maganizo” athu. Kucita izi kumaphatikizapo kusintha zolakalaka zathu, zizoloŵezi, na zolinga zathu. Kuti izi zitheke, timafunika kucita khama nthawi zonse.

8-9. Kodi citsanzo ca m’bale wina cionetsa bwanji kufunika kosintha umunthu wathu wamkati?

8 Ganizilani za m’bale wina amene anali wa ndewu asanakhale Mboni. Ataleka ndewu na kumwa moŵa, anabatizika. Zimenezi zinapeleka umboni wabwino kwa anthu a m’dela limene iye anali kukhala. Atangobatizika kumene, tsiku lina madzulo anakumana na ciyeso. Munthu wina wokolewa anafika ku nyumba kwa m’baleyo na kumuwopseza kuti amumenya. Poyamba, m’baleyo anayesetsa kuugwila mtima. Koma pamene mwamunayo anakamba mawu onyoza dzina la Yehova, m’baleyo anakwiya kwambili. Iye anatuluka m’nyumba na kumenya mwamunayo. Kodi m’baleyu anali na vuto lanji? Ngakhale kuti kuphunzila Baibo kunamuthandiza kuti aleke kukonda ndewu, m’baleyu anali asanasinthe mphamvu yoyendetsa maganizo ake. M’mawu ena, tingakambe kuti iye anali asanasinthe umunthu wake wamkati.

9 Koma m’baleyo sanabwelele m’mbuyo. (Miy. 24:16) Mothandizidwa na akulu, anapitiliza kukula mwauzimu. Ndipo m’kupita kwa nthawi, anakhala mkulu. Patapita zaka, iye anakumananso na ciyeso cina cofanana ndi ca poyamba cija. Tsiku lina madzulo ali pa Nyumba ya Ufumu, kunabwela munthu wina wokolewa amene anafuna kumenya mmodzi wa akulu. Kodi m’baleyo anacita ciani? Modekha komanso modzicepetsa, anakambilana na munthu wokolewayo na kum’pelekeza ku nyumba kwake. N’ciani cinathandiza m’baleyo kucita zinthu mosiyana na mmene anacitila poyamba paja? Iye anali atasintha mphamvu yoyendetsa maganizo ake. Anali atasintha umunthu wake wamkati na kukhala munthu wamtendele ndiponso wodzicepetsa. Izi zinacititsa kuti Yehova atamandike.

10. Kodi tifunika kucita ciani kuti tisinthe umunthu wathu wamkati?

10 Kusintha kumeneku sikucitika tsiku limodzi, ndipo kumafuna khama. Tingafunike ‘kuyesetsa mwakhama’ kwa zaka zambili kuti tisinthe. (2 Pet. 1:5) Kungokhala “m’coonadi” kwa nthawi yaitali, pakokha sikokwanila. Timafunika kucita zonse zimene tingathe kuti tisinthe umunthu wathu. Lomba tiyeni tikambilane zinthu zingapo zofunika kwambili zimene zingatithandize kupanga masinthidwe amenewa.

ZIMENE TINGACITE KUTI TISINTHE MPHAMVU YOYENDETSA MAGANIZO ATHU

11. Kodi pemphelo limatithandiza bwanji kusintha mphamvu yoyendetsa maganizo athu?

11 Cinthu coyamba cofunika kwambili cimene tiyenela kucita ni kupemphela. Tifunika kupemphela monga mmene wamasalimo anacitila. Iye anati: “Lengani mtima wolungama mkati mwanga, ndipo ikani maganizo atsopano ndi okhazikika mwa ine.” (Sal. 51:10) Tiyenela kuzindikila kuti tifunika kusintha mphamvu yoyendetsa maganizo athu na kupempha Yehova kuti atithandize. N’cifukwa ciani ndife otsimikiza kuti Yehova angatithandize kusintha? Ganizilani zimene Yehova anakamba ponena za Aisiraeli ouma mtima a m’nthawi ya Ezekieli. Iye anati: “Ndidzawapatsa mtima umodzi ndipo ndidzaika mzimu watsopano mwa iwo . . . n’kuwapatsa mtima wamnofu,” [kutanthauza mtima womvela Mulungu.] (Ezek. 11:19) Yehova anali wokonzeka kuthandiza Aisiraeli ouma mtimawo kusintha. Ndipo ni wokonzekanso kutithandiza.

12-13. (a) Malinga na Salimo 119:59, kodi tiyenela kusinkha-sinkha za ciani? (b) Nanga tiyenela kudzifunsa mafunso ati?

12 Cinthu caciŵili cofunika kwambili ni kusinkha-sinkha. Pamene tiŵelenga mosamala Mawu a Mulungu tsiku lililonse, tiyenela kupatula nthawi yosinkha-sinkha, kapena kuti kuganizila mozama pa zimene tawelengazo, n’colinga cakuti tizindikile maganizo oipa na zilakolako zosayenela zimene tifunika kusintha. (Ŵelengani Salimo 119:59; Aheb. 4:12; Yak. 1:25) Tiyenela kudzipenda kuti tione ngati tayamba kutengeka na nzelu za dzikoli. Tiyenelanso kuvomeleza modzicepetsa zofooka zathu na kugwililapo nchito zolimba kuti tiwongolele.

13 Mwacitsanzo, dzifunseni kuti: ‘Kodi niliko na kamtima ka nsanje kapena kaduka? (1 Pet. 2:1) ‘Kodi nimadziona kuti ndine wapamwamba kuposa ena cifukwa ca maphunzilo amene n’nacita, cuma cimene nili naco, kapena cifukwa ca kumene n’nakulila?’ (Miy. 16:5) ‘Kodi nimaona ena kukhala osanunkha kanthu cifukwa cakuti alibe zinthu zofanana ndi zimene ine nili nazo, kapena cifukwa ni a mtundu wina?’ (Yak. 2:2-4) ‘Kodi nimakopeka na zinthu za m’dziko la Satanali?’ (1 Yoh. 2:15-17) ‘Kodi nimakopeka na zosangalatsa zaciwelewele kapena zaciwawa?’ (Sal. 97:10; 101:3; Amosi 5:15) Kuganizila mafunso amenewa, kudzatithandiza kuzindikila mbali zimene tifunika kugwililapo nchito. Ngati tiyesetsa kuthetsa maganizo oipa amene ‘anazikika molimba’ mumtima mwathu, tidzakondweletsa Atate wathu wakumwamba.—Sal. 19:14.

14. N’cifukwa ciani kusankha mabwenzi abwino n’kofunika kwambili?

14 Kusankha mabwenzi abwino ni mbali yacitatu yofunika kwambili. Mwacibadwa, anthufe timakonda kutengela zocita za anzathu. (Miy. 13:20) Kaya tili ku nchito kapena ku sukulu, nthawi zambili timakhala ndi anthu amene sangatilimbikitse kukhala na maganizo okondweletsa Mulungu. Komabe, tingapeze mabwenzi abwino ku misonkhano yathu. Kumeneko, n’kumene timalimbikitsidwa pa “cikondi ndi nchito zabwino.”—Aheb. 10:24, 25.

KHALANI ‘OKHAZIKIKA M’CIKHULUPILILO’

15-16. Kodi Satana amayesa bwanji kusintha maganizo athu?

15 Kumbukilani kuti Satana amacita zonse zotheka kuti asinthe kaganizidwe kathu. Iye amaseŵenzetsa njila zosiyana-siyana pofuna kutipangitsa kukayikila coonadi ca m’Baibo.

16 Satana akupitilizabe kufunsa mafunso ofanana ndi limene anafunsa Hava m’munda wa Edeni. Iye anafunsa kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati . . . ?” (Gen. 3:1) M’dziko la Satanali, nthawi zambili timafunsidwa mafunso amene angatipangitse kukayikila zimene timakhulupilila. Timafunsidwa mafunso monga akuti: ‘Kodi n’zoona kuti Mulungu amaletsa kukwatila cipali? Kodi n’zoona kuti Mulungu amaletsa kukondwelela Khrisimasi kapena masiku akubadwa? Kodi n’zoona kuti Mulungu amaletsa kuikidwa magazi? Kodi n’zoona kuti Mulungu wacikondi amakuletsani kuyanjana na acibululu komanso mabwenzi anu ocotsedwa mu mpingo?’

17. Kodi tifunika kucita ciani ngati munthu winawake watifunsa mafunso otipangitsa kukayikila zimene timakhulupilila? Nanga Akolose 2:6, 7 ionetsa kuti pangakhale zotulukapo zotani?

17 Tifunika kukhala okhutila na zimene timakhulupilila. Ngati sitiyesetsa kupeza mayankho pa mafunso ofunika kwambili okhudza cikhulupililo cathu, tingayambe kukayikila zimene timakhulupilila. M’kupita kwa nthawi, izi zingapotoze maganizo athu na kuwononga cikhulupililo cathu. Nanga tiyenela kucita ciani? Mawu a Mulungu amati tifunika kusintha maganizo athu, kuti tizindikile cimene cili “cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka ndi cangwilo.” (Aroma 12:2) Conco, ngati tiŵelenga Baibo na mabuku athu nthawi zonse, tidzafika pokhutila kuti zimene timaphunzila m’Baibo ni coonadi. Tidzafikanso pokhulupilila na mtima wonse kuti miyezo ya Yehova ni yolungama. Pamapeto pake, monga mtengo wa mizu yolimba, tidzakhala ozikika molimba komanso ‘okhazikika m’cikhulupililo.’—Ŵelengani Akolose 2:6, 7.

18. N’ciani cingatithandize kudziteteza ku cisonkhezelo coipa ca dziko la Satanali?

18 Kulimbitsa cikhulupililo ni udindo wa aliyense payekha. Conco, pitilizani kukhala atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu. Muzipemphela nthawi zonse kwa Yehova. Muzim’condelela kuti akuthandizeni na mzimu wake. Muzisinkha-sinkha mozama pa zimene mwaŵelenga. Ndipo pitilizani kupenda maganizo anu na zolakalaka zanu. Pezani mabwenzi abwino amene angakuthandizeni kusintha maganizo anu. Mukatelo, mudzadziteteza ku cisonkhezelo coipa ca dziko la Satanali. Kuwonjezela apo, mudzakwanitsa “kugubuduza maganizo komanso cochinga ciliconse cotsutsana ndi kudziwa Mulungu.”—2 Akor. 10:5.

NYIMBO 50 Pemphelo Yanga Yodzipelekela kwa Mulungu

^ ndime 5 Maganizo athu nthawi zonse amasonkhezeledwa na cikhalidwe cathu, maphunzilo, na zokumana nazo mu umoyo. Nanga bwanji ngati taona kuti zizolowezi zina zoipa zinazika mizu mwa ife? M’nkhani ino, tidzaphunzila zimene tingacite kuti tithetse zizolowezi zoipa zilizonse zimene tingakhale nazo.