Kuŵelenga Mpukutu Wamakedzana Wakupsa na Moto
Zinali zosatheka kuŵelenga mawu a mu mpukutu wakupsa na moto, umene unapezeka ku Ein Gedi mu 1970. Koma poseŵenzetsa makina amakono ounikila zinthu, akatswili akwanitsa kuuŵelenga, ndipo apeza kuti mu mpukutuwo muli mavesi ena a m’buku la Levitiko, kuphatikizapo dzina la Mulungu
MU 1970, akatswili ofukula zinthu zakale, anapeza mpukutu wakupsa na moto ku Ein Gedi, m’dziko la Israel, ca kumadzulo kwa Nyanja Yakufa. Anapeza mpukutuwo pamene anali kufukula matongwe a sunagoge wa m’mudzi winawake. Sunagogeyo anatenthedwa na moto pamene mudziwo unawonongedwa. Izi ziyenela kuti zinacitika ca m’ma 500 C.E. Popeza kuti mpukutuwo unali wakupsa, cinali covuta kuufunyulula kuti auŵelenge. Koma poseŵenzetsa makina amakono ounikila zinthu, akatswili akwanitsa kuŵelenga zimene zili mu mpukutuwo. Zili ngati kuti akwanitsa kuufunyulula.
Kodi n’ciani cimene anapeza pambuyo poŵelenga mpukutuwo? Anapeza kuti mpukutuwo ni mbali ya Baibo. Mbali yotsala ya mpukutuwo ili na mavesi oyambilila a m’buku la Levitiko. M’mavesi amenewo muli dzina la Mulungu, lolembedwa m’zilembo zinayi za Ciheberi. Cioneka kuti mpukutuwo ni wa m’zaka za pakati pa 50 C.E na 400 C.E. Ngati n’telodi, ndiye kuti umenewu ni mpukutu wakale kwambili umene akatswili apeza kucokela pamene anapeza mipukutu ya ku Nyanja Yakufa. M’nyuzipepa yochedwa The Jerusalem Post, Gil Zohari analemba kuti: “Cidutswa ca ku Ein Gedi ca mpukutu wa Levitiko cisanapezeke, panali nyengo ya zaka 1000 pakati pa mipukutu ya ku Nyanja Yakufa, yolembedwa ca m’ma 100 B.C.E, zaka 2000 zapitazo, na mipukutu ya Aleppo Codex, yolembedwa ca m’ma 930 C.E. Akatswili a Baibo amakamba kuti mawu a mu mpukutuwo aonetsa kuti Malemba acimasorete a m’mabuku asanu oyambilila a Baibo, “anasungidwa mokhulupilika kwa zaka zoposa 1000, komanso kuti okopolola Malemba, anakopolola molondola kwambili.”