Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 26

Thandizani Ena Kulimbana na Nkhawa

Thandizani Ena Kulimbana na Nkhawa

“Nonsenu mukhale amaganizo amodzi, omvelana cisoni, okonda abale, acifundo cacikulu, ndiponso amaganizo odzicepetsa.”—1 PET. 3:8.

NYIMBO 107 Cikondi ca Umulungu

ZA M’NKHANI INO *

1. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Atate wathu wacikondi Yehova?

YEHOVA amatikonda kwambili. (Yoh. 3:16) Ndipo timafuna kutengela citsanzo cake. Ndiye cifukwa cake timayesetsa kukhala “omvelana cisoni, okonda abale, [ndi] acifundo cacikulu.” Timacita izi makamaka kwa “abale ndi alongo athu m’cikhulupililo.” (1 Pet. 3:8; Agal. 6:10) Ngati ena m’banja lathu lauzimu akumana na mavuto, timafuna kuwathandiza.

2. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

2 Aliyense amene wasankha kukhala m’banja lauzimu la Yehova, adzakumana na mavuto. (Maliko 10:29, 30) Ndipo n’zacidziwikile kuti pamene mapeto akuyandikila, mavuto aziculukila-culukila. Kodi tingalimbikitsane bwanji pa nthawi ya mavuto? Tiyeni tikambilane zimene tingaphunzilepo pa nkhani za m’Baibo zokhudza Loti, Yobu, ndi Naomi. Tidzakambilananso mavuto amene abale na alongo athu akukumana nawo masiku ano, komanso mmene tingawathandizile kupilila.

KHALANI OLEZA MTIMA

3. Malinga na 2 Petulo 2:7, 8, kodi Loti anapanga cosankha colakwika citi? Nanga panakhala zotulukapo zanji?

3 Loti anapanga cosankha colakwika cokakhala mu mzinda wa Sodomu, mmene munali anthu a khalidwe lonyansa laciwelewele. (Ŵelengani 2 Petulo 2:7, 8) Mzinda wa Sodomu unali wolemela. Koma Loti anakumana na mavuto ambili cifukwa cokhala mumzinda umenewo. (Gen. 13:8-13; 14:12) Mwacitsanzo, mkazi wake ayenela kuti anaukonda kwambili umoyo wa mumzindawo. Ayenelanso kuti anali kugwilizana kwambili ndi anthu ena a mumzindawo. Izi zinapangitsa kuti asamvele Yehova. Ndipo pa mapeto pake, anawonongedwa pamene Mulungu anagwetsa moto na sulufule mu Sodomu. Ganizilaninso za ana aŵili a Loti. Amuna aŵili amene anawatomela, anaphedwa pamene mzindawo unawonongedwa. Loti anataikilidwa mkazi wake wokondedwa, katundu, na nyumba. (Gen. 19:12-14, 17, 26) Kodi Yehova anamulekelela Loti panthawi yovuta imeneyi cifukwa cakuti anapanga cosankha colakwika? Iyai.

Mwacifundo, Yehova anatumiza angelo kuti akapulumutse Loti na banja lake (Onani ndime 4)

4. Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuleza mtima pocita zinthu na Loti? (Onani cithunzi pacikuto.)

4 Ngakhale kuti Loti anasankha kukakhala mumzinda woipa wa Sodomu, mwacifundo cake, Yehova anatumiza angelo kuti akam’pulumutse pamodzi na banja lake. Angelowo anamuuza kuti atuluke mwamsanga mumzinda wa Sodomu. Koma iye “anali kuzengeleza.” Angelowo anacita kugwila dzanja la Loti, ana ake, na mkazi wake n’kuwatulutsa mumzindawo. (Gen. 19:15, 16) Kenako, anawauza kuti athaŵile ku mapili. Koma m’malo momvela Yehova, Loti anapempha kuti athaŵile ku mzinda wina wa pafupi. (Gen. 19:17-20) Yehova anamvetsela moleza mtima, na kuvomeleza kuti Loti athaŵile ku mzinda umene anapempha. Pambuyo pake, iye anacita mantha kukhala mumzindawo, ndipo anapita kukhala kudela la kumapili, kumene Yehova anamuuza kuti athaŵileko poyamba. (Gen. 19:30) Apa, Yehova anaonetsa kuleza mtima kwakukulu. Kodi tingatengele bwanji citsanzo cake?

5-6. Kodi tingaseŵenzetse bwanji malangizo a pa 1 Atesalonika 5:14 potengela citsanzo ca Mulungu?

5 Mofanana ndi Loti, nthawi zina wina m’banja lathu lauzimu angapange cosankha colakwika, cimene cingam’bweletsele mavuto aakulu. Ngati zaconco zacitika, kodi tingacite ciani? Mwina tingaganize zongomuuza kuti akukolola zimene anafesa. Ndipo zimenezo zingakhale zoona. (Agal. 6:7) Koma kukamba conco, sikungam’thandize. Tingacite bwino kutengela citsanzo ca mmene Yehova anathandizila Loti. Kodi tingacite bwanji zimenezi?

6 Yehova anatumiza angelo kuti akacenjeze Loti, komanso kuti akam’thandize mwa kum’tulutsa mumzinda wa Sodomu, umene unali pafupi kuwonongedwa. N’cimodzi-modzi na ife. Ngati taona kuti m’bale wathu wayamba kuyenda njila yolakwika, tingafunike kum’cenjeza. Koma tingafunikenso kum’thandiza. Ngakhale atacedwa kuseŵenzetsa uphungu wa m’Baibo umene tam’patsa, tiyenela kuleza naye mtima. Tifunika kutengela citsanzo ca angelo aŵili aja. M’malo mongom’siya, tiyenela kupitiliza kum’thandiza, osati mwa mawu cabe, koma mwa zocita zathu. (1 Yoh. 3:18) Tingafunike kum’gwila dzanja, titelo kukamba kwake, mwa kum’thandiza kuseŵenzetsa uphungu wabwino umene tam’patsa.—Ŵelengani 1 Atesalonika 5:14.

7. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova ca mmene anali kuonela Loti?

7 Yehova sanayang’ane pa zolakwa za Loti. Ndiye cifukwa cake iye anauzila mtumwi Petulo kulemba kuti Loti anali munthu wolungama. N’zolimbikitsa kwambili kuona kuti Yehova amatikhululukila zolakwa zathu. (Sal. 130:3) Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova? Tiziyang’ana kwambili pa makhalidwe abwino amene abale na alongo athu ali nawo. Tikatelo, tidzayamba kucita nawo zinthu moleza mtima kwambili. Ndipo izi zidzapangitsa kuti cikhale cosavuta kwa iwo kulandila thandizo limene tingawapatse.

KHALANI ACIFUNDO

8. Kodi cifundo cimatilimbikitsa kucita ciani?

8 Mosiyana na Loti, Yobu sanapange zosankha molakwika. Koma anakumana na mavuto aakulu mosayembekezeleka. Mwacitsanzo, cuma cake cinawonongeka, anthu m’dela lake analeka kum’lemekeza, komanso anadwala matenda oopsa. Kuwonjezela apo, ana ake onse anafa. Cinanso, anzake atatu acinyengo anayamba kumuimba mlandu. Koma kodi n’cifukwa ciani anzakewo sanam’citile cifundo? Cifukwa cimodzi n’cakuti sanayese kumvetsetsa mavuto amene Yobu anali kukumana nawo. Conco, anangothamangila kumuweluza molakwa na kum’dzudzula mopanda cifundo. Kodi tingapewe bwanji kucita colakwa ngati cimeneci? Tizikumbukila kuti Yehova yekha ndiye amadziŵa zonse zokhudza mavuto amene munthu akukumana nawo. Tizimvetsela mosamala pamene munthu akufotokoza vuto lake. Tiziyesetsanso kuganizila mmene iye akumvelela cifukwa ca vutolo. Tikatelo, m’pamene tidzaonetsadi cifundo ceni-ceni kwa m’bale kapena mlongo wathu.

9. Kodi cifundo cidzatithandiza kupewa kucita ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

9 Ngati tili na cifundo, tidzapewa kukamba mijedo yovulaza ponena za mavuto amene anthu ena akukumana nawo. Munthu wojeda anzake sagwilizanitsa mpingo. Koma amaugaŵanitsa. (Miy. 20: 19; Aroma 14:19) Iye sakamba ndi anthu mokoma mtima, kapena mowaganizila. Ndipo mawu ake angavulaze munthu amene ali kale na mavuto. (Miy. 12:18; Aef. 4:31, 32) Conco, ni bwino kuyang’ana pa makhalidwe abwino amene munthu ali nawo, na kuganizila mmene tingam’thandizile kupilila mavuto ake.

Mvetselani moleza mtima ngakhale pamene Mkhristu mnzanu wayamba kukamba zinthu “zopanda pake,” ndiyeno kambani mawu oyenelela om’limbikitsa (Onani ndime 10-11) *

10. Kodi mawu a pa Yobu 6:2, 3, atiphunzitsa ciani?

10 Ŵelengani Yobu 6:2, 3Pa nthawi yovuta imeneyi, Yobu analankhula “zopanda pake.” Ndipo pambuyo pake, anavomeleza kuti zinthu zina zimene anakamba zinali zolakwika. (Yobu 42:6) Mofanana na Yobu, munthu amene akukumana na mavuto, nthawi zina angakambe zinthu zopanda pake, zimene pambuyo pake angadziimbe nazo mlandu. Kodi tiyenela kucita ciani zikakhala conco? M’malo mom’dzudzula, tiyenela kumumvelela cifundo. Kumbukilani kuti sicinali cifunilo ca Yehova kuti anthufe tizikumana na mavuto kapena zinthu zina zothetsa nzelu. Conco, n’zosadabwitsa kuti nthawi zina mtumiki wokhulupilika wa Yehova, angakambe zinthu mosaganizila cifukwa ca nkhawa yaikulu imene ali nayo. Ngakhale atakamba zinthu zimene si zoona ponena za Yehova kapena za ife, tisafulumile kum’kwiyila kapena kum’dzudzula.—Miy. 19:11.

11. Kodi akulu angatengele bwanji citsanzo ca Elihu pamene apeleka uphungu?

11 Nthawi zina, ngakhale munthu amene akukumana na mavuto aakulu, angafunike kupatsidwa uphungu. (Agal. 6:1) Kodi akulu angacite bwanji zimenezi? Iwo afunika kutengela citsanzo ca Elihu, amene anamvetsela mwacifundo kwambili pamene Yobu anali kufotokoza mavuto ake. (Yobu 33:6, 7) Elihu anapeleka uphungu kwa Yobu pambuyo pomvetsetsa maganizo ake. Mofananamo, akulu amene amatengela citsanzo ca Elihu, amamvetsela mosamala na kuyesa kumvetsetsa mmene zinthu zilili mu umoyo wa munthu amene afuna kum’patsa uphungu. Ndiyeno, pamene apeleka uphungu kwa munthuyo, cimakhala cosavuta kumufika pa mtima.

LANKHULANI MOLIMBIKITSA

12. Kodi imfa ya mwamuna wake ndi ana ake aŵili inam’khudza bwanji Naomi?

12 Naomi anali mkazi wokhulupilika amene anali kukonda Yehova. Koma mwamuna wake ndi ana ake aŵili atamwalila, anafuna kusintha dzina lake lakuti Naomi kuti likhale “Mara,” kutanthauza “Kuwawa.” (Rute 1:3, 5, 20, ftn., 21) Rute, mtengwa wa Naomi, anakhalabe naye nthawi yonse ya mavuto ake. Rute anali kuthandiza Naomi kupeza zinthu zofunikila mu umoyo. Kuwonjezela apo, anali kulankhula naye molimbikitsa. Iye anaonetsa kuti anali kum’konda Naomi na kum’cilikiza mwa kukamba mawu acidule, koma ocokela pansi pamtima.—Rute 1:16, 17.

13. N’cifukwa ciani tiyenela kulimbikitsa anthu amene anafedwa mnzawo wa m’cikwati?

13 Pamene wina m’banja lathu lauzimu wataikilidwa wokondedwa wake mu imfa, amafunikila cilimbikitso cathu. Mwamuna na mkazi okwatilana, tingawayelekeze na mitengo iŵili imene inamela na kukulila pa malo amodzi. M’kupita kwa zaka, mizu ya mitengoyo imaloŵana-loŵana. Ndipo mtengo umodzi ukazulidwa, mtengo wotsalawo umakhudzidwa kwambili. Mofananamo, munthu akafedwa mkazi kapena mwamuna wake, amakhala na cisoni cacikulu, ndipo cingatenge nthawi yaitali. Mwacitsanzo, mlongo Paula, * amene mwamuna wake anamwalila mwadzidzidzi, anati: “Umoyo wanga unasinthilatu, ndipo n’nasoŵelatu mtengo wogwila. Mwamuna wanga anali bwenzi langa lapamtima. N’nali kumuuza zilizonse za mu mtima mwanga. Anali kusangalala nane pamodzi, komanso anali kunicilikiza pa nthawi ya mavuto. Nthawi zonse, anali kunimvetsela pamene nikum’fotokozela mavuto anga. Atamwalila, n’namvela monga anidula pakati n’kucotsako mbali imodzi.”

Kodi anthu amene anafedwa mnzawo wa m’cikwati tingawalimbikitse bwanji? (Onani ndime 14-15) *

14-15. Tingam’tonthoze bwanji munthu amene anafedwa mnzake wa m’cikwati?

14 Kodi tingam’tonthoze bwanji munthu amene anafedwa mnzake wa m’cikwati? Coyamba, tifunika kukamba naye. Kucita izi n’kofunika, ngakhale kuti mwina tingakhale omangika, kapena tingasoŵe mawu abwino okamba naye. Mlongo Paula, amene tam’chula m’ndime yapita, anati: “Nidziŵa kuti imfa imapangitsa anthu kukhala omangika. Iwo amaopa kuti angakambe zinthu zokhumudwitsa ena. Koma zimakhala zolimbikitsa ngati wina wakambako mawu, kusiyana n’kungokhala cete.” Nthawi zina zimakhala kuti munthu wofedwayo sakudelanso nkhawa za mawu amene tingakambe naye. Mlongo Paula anati: “N’nali kulimbikitsidwa kwambili anzanga akabwela na kukamba cabe kuti: ‘Pepani, cinaipa kwambili.’”

15 M’bale William, amene anafedwa mkazi wake zaka zingapo zapitazo, anati: “Zimanilimbikitsa kwambili anthu akamakamba zabwino zimene mkazi wanga anali kucita. Zimanithandiza kuona kuti anali kum’konda na kum’lemekeza. Zimanitonthoza kwambili, cifukwa n’nali kum’konda ngako mkazi wanga, ndipo anali kunithandiza m’zambili.” Mlongo wina wofedwa, dzina lake Bianca, anati: “Nimalimbikitsidwa kwambili ngati ena apemphela nane na kuŵelenga nane lemba limodzi kapena aŵili. Nimatonthozedwa akamakamba za mwamuna wanga, kapena kunimvetsela pamene nifotokoza za iye.”

16. (a) N’cifukwa ciani tifunika kupitiliza kulimbikitsa munthu amene anataikilidwa wokondedwa wake mu imfa? (b) Malinga na Yakobo 1:27, kodi tili na udindo wotani?

16 Rute anapitilizabe kulimbikitsa Naomi, mkazi wa masiye. Nafenso tifunika kupitiliza kulimbikitsa anthu amene anataikilidwa okondedwa awo mu imfa. Paula, amene tam’chulapo kale m’nkhani ino, anati: “Amuna ŵanga atangomwalila, anthu ambili anali kunilimbikitsa na kunithandiza. Koma pamene masiku anali kupita, analeka kunilimbikitsa cifukwa cotangwanika na zocitika za tsiku na tsiku. Komabe panthawiyi, umoyo wanga unali utasintha kwambili. Conco, ni bwino kuzindikila kuti munthu wofedwa, amafunika kulimbikitsidwa kwa miyezi, ngakhale zaka kumene.” Tiyenela kukumbukila kuti anthu amasiyana-siyana. Ena amajaila mwamsanga pamene zinthu zasintha mu umoyo wawo. Koma ena sajaila mwamsanga, cakuti nthawi zonse ngati acita zinthu zimene anali kucita na wokondedwa wawo, zimawakumbutsa imfa yake. Zili telo cifukwa anthu amaonetsa cisoni m’njila zosiyana-siyana. Conco, tizikumbukila kuti Yehova anatipatsa mwayi na udindo wosamalila anthu amene anafedwa mnzawo wa m’cikwati.—Ŵelengani Yakobo 1:27.

17. N’cifukwa ciani anthu amene anasiyidwa na anzawo a m’cikwati tifunika kuwalimbikitsa?

17 Pali abale na alongo ena amene anasiyidwa na mnzawo wa m’cikwati. Izi zimacititsa kuti azikhala opsinjika maganizo kwambili. Mwacitsanzo, mlongo Joyce, amene mwamuna wake anam’sudzula na kukatenga mkazi wina, anati: “Mwamuna wanga atanisudzula, cinaniŵaŵa kwambili mwina kuposa mmene nikanamvela iye akanakhala kuti wamwalila. Akanamwalila pangozi kapena cifukwa ca matenda, nikanadziŵa kuti zangocitika, sanacite kufuna. Koma apa, iye anacita kusankha kuti anisudzule. N’naona kuti wanipeputsa na kunicotsela ulemu.”

18. Tingacite ciani kuti tithandize anthu amene anasiyidwa na anzawo a m’cikwati?

18 Tizicita zinthu zoonetsa kukoma mtima kwa anthu amene anasiyidwa na anzawo a m’cikwati. Tingawacitile zinthu ngakhale zooneka zocepa. Tikatelo, iwo amaona kuti timawakondadi. Popeza ali okha tsopano, amafunikila mabwenzi abwino. (Miy. 17:17) Mungaonetse bwanji kuti ndimwe bwenzi lawo? Mungawaitanileko ku nyumba kwanu kuti mudzadye nawo cakudya. Kapena mungawapemphe kuti mukacite nawo zosangalatsa zinazake kapena kupita nawo mu ulaliki. Komanso, nthawi na nthawi mungawaphemphe kuti azikhala nanu pa kulambila kwa pabanja. Mukatelo, mudzakondweletsa Yehova, cifukwa iye “ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka,” ndiponso “ndi woweluzila akazi amasiye milandu.”—Sal. 34:18; 68:5.

19. Malinga n’zimene 1 Petulo 3:8 imakamba, kodi mwatsimikiza mtima kucita ciani?

19 Posacedwa, Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulila dziko, ndipo “masautso akale adzaiwalika.” Tiyembekezela mwacidwi nthawi pamene “zinthu zakale sizidzakumbukilidwanso ndipo sizidzabwelanso mumtima.” (Yes. 65:16, 17) Conco, pamene tiyembekezela nthawi imeneyo, tiyeni tizilimbikitsana komanso kukamba na kucita zinthu zoonetsa kuti timakonda aliyense m’banja lathu lauzimu.—Ŵelengani 1 Petulo 3:8.

NYIMBO 111 Zifukwa Zokhalila Acimwemwe

^ ndime 5 Loti, Yobu, ndi Naomi, anakumana na mavuto osiyana-siyana mu umoyo wawo. Koma anatumikila Yehova mokhulupilika. M’nkhani ino, tikambilana zimene tingaphunzilepo pa zimene zinawacitikila. Tikambilananso cifukwa cake tifunika kulankhula molimbikitsa kwa abale na alongo amene akukumana na mavuto, ndiponso kucita nawo zinthu moleza mtima ndi mwacifundo.

^ ndime 13 Maina m’nkhani ino asinthidwa.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: M’bale wakwiya kwambili, ndipo wayamba “kukamba zopanda pake.” Koma mkulu akumvetsela moleza mtima. Pa nthawi ina, m’baleyo atakhazika mtima pansi, mkulu akum’patsa uphungu mokoma mtima.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: M’bale na mlongo amene angoloŵa kumene m’banja akuceza na m’bale amene anafedwa mkazi camanje-manje. Iwo akukumbukila nthawi pamene anali kusangalala pamodzi na malemuyo.