NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA June 2020

Magazini ino ili na nkhani zophunzila kuyambila pa August 3-30, 2020.

“Dzina Lanu Liyeletsedwe”

Nkhani yophunzila 23: Wiki ya August 3-9, 2020. Kodi ni nkhani yofunika kwambili iti imene ikhudza anthu onse na angelo? N’cifukwa ciani nkhani imeneyo ni yofunika kwambili? Nanga ise tingacite ciani pothandiza kuthetsa nkhani imeneyo? Kudziŵa mayankho pa mafunso amenewa ndi ena okhudzana na nkhaniyo kungatithandize kulimbitsa ubale wathu na Yehova.

“Ndipatseni Mtima Wosagawanika Kuti Ndiope Dzina Lanu”

Nkhani yophunzila 24: Wiki ya August 10-16, 2020. M’nkhani ino, tikambilana mbali ya pemphelo la Mfumu Davide yopezeka pa Salimo 86:11, 12. Kodi kuopa dzina la Yehova kutanthauza ciani? N’zinthu ziti zimene zimatisonkhezela kuopa dzina lalikulu limeneli? Nanga kuopa Mulungu kungatiteteze bwanji tikayesedwa kuti ticite zoipa?

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi makhalidwe ochulidwa pa Agalatiya 5:22, 23 ndiwo okha “amene mzimu woyela umatulutsa”?

“Inetu Ndidzafunafuna Nkhosa Zanga”

Nkhani yophunzila 25: Wiki ya August 17-23, 2020. N’cifukwa ciani Akhristu ena amene atumikila Yehova mokhulupilika kwa zaka amazilala? Kodi Mulungu amawaona bwanji Akhristu amenewo? M’nkhani ino, tikambilana mayankho pa mafunso amenewa. Tikambilananso mmene Yehova anathandizila atumiki ake akale amene anayamba kufooka pom’tumikila, ndipo tiona zimene tingaphunzilepo.

“Bwelelani kwa Ine”

Nkhani yophunzila 26: Wiki ya August 24-30, 2020. Yehova amafuna kuti Akhristu amene analeka kusonkhana na kulalikila abwelela kwa iye. Pali zambili zimene tingacite kuti tithandize ozilala amene amafuna kulabadila ciitano ca Yehova cakuti: ‘Bwelelani kwa ine.’ M’nkhani ino, tikambilana mmene tingawathandizile kubwelela kwa Yehova.