Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 25

“Inetu Ndidzafunafuna Nkhosa Zanga”

“Inetu Ndidzafunafuna Nkhosa Zanga”

“Inetu ndidzafunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalila.”—EZEK. 34:11.

NYIMBO 105 “Mulungu Ndiye Cikondi”

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’cifukwa ciani Yehova anadziyelekezela na mayi woyamwitsa?

“KODI mayi angaiŵale mwana wake woyamwa”? Yehova anafunsa funso limeneli m’masiku a mneneli Yesaya. Mulungu anauza anthu ake kuti, “Ngakhale amayi amenewa akhoza kuiwala, koma ine sindidzakuiwala.” (Yes. 49:15) Si kaŵili-kaŵili Yehova kudziyelekezela na mayi. Koma izi n’zimene anacita panthawiyo. Mulungu anayelekezela cikondi camphamvu cimene cimakhalapo pakati pa mayi na mwana wake pofotokoza cikondi camphamvu cimene iye ali naco pa atumiki ake. Amayi ambili angavomeleze zimene mlongo wina dzina lake Jasmin anakamba. Iye anati: “Ukamayamwitsa mwana, cikondi pakati iwe na mwanayo cimakula kwambili moti cimakhalapo kwa moyo wonse.”

2. Kodi Yehova amamvela bwanji akaona kuti mmodzi wa ana ake wazilala?

2 Yehova amadziŵa ngakhale pamene mmodzi cabe wa ana ake waleka kulalikila na kusonkhana. Conco tangoganizilani mmene iye amamvelela poona atumiki ake masauzande akuzilala * caka ciliconse.

3. N’ciani cimene Yehova amafuna?

3 Ambili mwa abale na alongo athu ozilala amenewa m’kupita kwa nthawi amabwelelanso mu mpingo, ndipo timawalandila na manja aŵili. Yehova amafuna kuti iwo abwelele. Ifenso n’zimene timafuna. (1 Pet. 2:25) Kodi tingawathandize bwanji? Tisanayankhe funsoli, coyamba tiyenela kudziŵa cifukwa cake ena amaleka kusonkhana na kulalikila.

N’CIFUKWA CIANI ENA AMALEKA KUTUMIKILA YEHOVA?

4. N’ciani cacitikila Akhristu ena cifukwa ca nchito yakuthupi?

4 Ena amazilala cifukwa cotangwanika kwambili na nchito yawo yakuthupi. M’bale wina wa ku Southeast Asia, dzina lake Hung, * anati: “N’nali kutaila nthawi yoculuka pa nchito yanga yakuthupi. N’nali kudzinamiza poganiza kuti nikakhala na ndalama zambili, m’pamene nidzakwanitsa kutumikila bwino Yehova. Motelo, n’nali kuseŵenza kwa maola ambili patsiku. N’nayamba kuphonya-phonya misonkhano cakuti pamapeto pake n’nalekelatu kusonkhana. Zioneka kuti Satana amaseŵenzetsa dzikoli popatutsa anthu pang’ono-pang’ono kuti aleke kutumikila Mulungu.”

5. Kodi mlongo Anne anakhudzidwa bwanji na mavuto amene anakumana nawo?

5 Abale na alongo ena amazilala cifukwa colefulidwa na mavuto. Mwacitsanzo, mlongo wina wa ku Britain, dzina lake Anne, ali ndi ana 5. Iye anati: “Mwana wanga wina anabadwa wolemala kwambili. Patapita nthawi, mwana wanga wina wamkazi anacotsedwa mu mpingo, ndipo winanso wamwamuna anayamba kudwala matenda a maganizo. Izi zinanilefula kwambili. N’naleka kusonkhana na kulalikila, moti m’kupita kwa nthawi n’nakhala wofalitsa wozilala.” Kukamba zoona, timumvelela cifundo kwambili mlongo Anne na banja lake, komanso Akhristu ena amene akukumana na mavuto otelo.

6. Kodi kusagwilitsila nchito malangizo a pa Akolose 3:13 kungapangitse bwanji munthu kuleka kugwilizana ndi anthu a Yehova?

6 Ŵelengani Akolose 3:13. Atumiki ena a Yehova anazilala cifukwa cokhumudwa na zimene Mkhristu mnzawo anakamba kapena kuwacitila. Mtumwi Paulo anavomeleza kuti nthawi zina tingakhale na “cifukwa” comveka “codandaulila” za m’bale kapena mlongo wathu. N’kutheka kuti tinacitilidwa zinthu mopanda cilungamo. Ngati sitingasamale, tingakhumudwe na zimenezo. Ndipo kukhumudwa kumeneko, m’kupita kwa nthawi kungatipangitse kuleka kugwilizana ndi anthu a Yehova. Izi n’zimene zinacitikila m’bale wina wa ku South America, dzina lake Pablo. Ena anamunamizila kuti anacita colakwa cinacake. Ndipo zotsatila zake analandidwa mwayi wautumiki umene anali nawo mu mpingo. Kodi iye anacita ciani? “N’nakwiya kwambili,” anatelo Pablo, “ndipo pang’ono m’pang’ono n’naleka kugwilizana na mpingo.”

7. N’ciani cingacitike ngati munthu akuvutika na cikumbumtima?

7 Ena cikumbumtima cimawavutitsa kwambili cifukwa ca chimo limene anacita kumbuyoko, moti amayamba kuona kuti Mulungu sawakondanso. Olo kuti analapa ndiponso anacitilidwa cifundo, akhoza kumadziona kuti si woyenelela kukhala mmodzi wa atumiki a Mulungu. Umu ni mmene m’bale Francisco anamvelela. Iye anati: “N’nadzudzulidwa cifukwa ca chimo la dama limene n’nacita. Olo kuti n’napitiliza kusonkhana, n’nali kuvutika maganizo komanso kudziona wosayenelela kukhala pakati pa anthu a Yehova. Cikumbumtima cinali kunivutitsa kwambili, ndipo n’nali kuona kuti Yehova sananikhululukile. M’kupita kwa nthawi, n’naleka kusonkhana na kulalikila.” Kodi mumamvela bwanji mukaganizila za abale na alongo amene amakumana na mavuto monga amene tawachula m’nkhani ino? Kodi mumawamvelela cifundo? Komanso funso lofunika kwambili n’lakuti, kodi Yehova amawaona bwanji?

YEHOVA AMAKONDA NKHOSA ZAKE

M’busa waciisiraeli anali kuidela nkhawa kwambili nkhosa yosocela (Onani ndime 8-9) *

8. Kodi Yehova amawaiŵala atumiki ake amene anazilala? Fotokozani.

8 Yehova saiŵala atumiki ake amene kwa kanthawi analeka kusonkhana komanso kulalikila. Saiŵalanso nchito zimene iwo anacita pom’tumikila. (Aheb. 6:10) Mneneli Yesaya analemba mawu ocititsa cidwi oonetsa mmene Yehova amakondela anthu ake na kuwasamalila. Yesaya anati: “Iye adzaweta gulu lake lankhosa ngati m’busa. Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi dzanja lake, ndipo adzawanyamulila pacifuwa pake.” (Yes. 40:11) Kodi M’busa Wamkulu Yehova amamvela bwanji ngati imodzi mwa nkhosa zake yasocela? Yesu anaonetsa bwino mmene Yehova amamvelela pamene anafunsa ophunzila ake kuti: “Mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi mwa nkhosazo n’kusocela, kodi sangasiye nkhosa 99 zija m’phili ndi kupita kukafunafuna yosocelayo? Akaipeza, ndithu ndikunenetsa, amakondwela kwambili ndi nkhosa imeneyo kusiyana ndi nkhosa 99 zosasocela zija.”—Mat. 18:12, 13.

9. Kodi m’busa wabwino m’nthawi yakale anali kusamalila bwanji nkhosa zake? (Onani cithunzi pacikuto.)

9 N’cifukwa ciani m’poyenela kuyelekezela Yehova na m’busa? Cifukwa m’nthawi yakale, m’busa wabwino anali kusamalila bwino kwambili nkhosa zake. Citsanzo ni Davide. Iye anali kuzikonda kwambili nkhosa zake, cakuti anapha mkango na cimbalangondo pofuna kuteteza nkhosazo. (1 Sam. 17:34, 35) M’busa wabwino anali kuzidziŵa bwino nkhosa zake, kotelo kuti olo imodzi yasowa, iye anali kudziŵa. (Yoh. 10:3, 14) M’busa wotelo anali kulolela kusiya nkhosa zake 99 m’khola kapena m’manja mwa m’busa mnzake na kupita kukafuna-funa nkhosa yosocelayo. Yesu anaseŵenzetsa citsanzo cimeneci pofuna kutiphunzitsa mfundo ya coonadi yofunika kwambili yakuti: “Atate [wathu] wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.”—Mat. 18:14.

M’busa m’nthawi ya Aisiraeli akusamalila nkhosa yosocela (Onani ndime 9)

YEHOVA AMAFUNA-FUNA NKHOSA ZAKE

10. Mogwilizana na Ezekieli 34:11-16, kodi Yehova analonjeza ciani ponena za nkhosa zake zosocela?

10 Yehova amakonda aliyense wa ife, kuphatikizapo ana ake osocela. Kupitila mwa mneneli Ezekieli, Mulungu analonjeza kuti adzafuna-funa nkhosa zake zosocela na kuzithandiza kuti zikhalenso zolimba mwauzimu. Iye anafotokoza mwacindunji zimene adzacita pothandiza nkhosazo. Zinthu zimenezo, n’zimenenso m’busa waciisiraeli anali kucita ngati nkhosa yasocela. (Ŵelengani Ezekieli 34:11-16.) Coyamba, m’busa anali kufuna-funa nkhosa yosocelayo, ndipo izi zinali kufuna nthawi yoculuka na khama. Ndiyeno akaipeza, anali kuitenga na kukaiika pa gulu la nkhosa zinzake. Cinanso, ngati nkhosayo yavulala kapena ili na njala, m’busayo anali kuisamalila mwacikondi. Anali kumanga mabalawo, kuinyamula, na kuipatsa cakudya. Akulu amene ni abusa a “nkhosa za Mulungu” afunika kucitanso zimenezi pothandiza aliyense amene analeka kugwilizana na mpingo. (1 Pet. 5:2, 3) Akulu amafuna-funa nkhosa zosocela, kuzithandiza kuti zibwelele ku gulu la nkhosa, komanso kuzionetsa cikondi mwa kupeleka thandizo lauzimu lofunikila. *

11. Kodi m’busa wabwino anali kudziŵa ciani?

11 M’busa wabwino anali kudziŵa kuti nthawi zina nkhosa zingasocele. Ngati nkhosa yasocela, m’busa sanali kucita nayo zinthu mwankhanza. Ganizilani citsanzo cimene Yehova anapeleka pothandiza atumiki ake amene anayamba kufooka pom’tumikila.

12. Kodi Yehova anacita naye zinthu motani Yona?

12 Panthawi ina, mneneli Yona anathaŵa utumiki umene Yehova anamupatsa. Olo zinali conco, Yehova sanamusiye Yona. Monga m’busa wabwino, Yehova anapulumutsa Yona na kum’thandiza kupeza mphamvu zofunikila kuti akwanilitse utumiki wake. (Yona 2:7; 3:1, 2) Pambuyo pake, Mulungu anagwilitsila nchito comela ca mtundu wa mphonda pomuthandiza kuona kuti moyo wa munthu aliyense ni wofunika kwambili. (Yona 4:10, 11) Kodi tiphunzilapo ciani? Akulu afunika kupitilizabe kuthandiza Akhristu amene anazilala. Iwo ayenela kuyesetsa kumvetsetsa cimene cinapangitsa nkhosa kusocela. Ndipo nkhosayo ikabwelela kwa Yehova, akulu ayenela kupitiliza kuonetsa kuti amaikonda na kuidela nkhawa.

13. Kodi tiphunzilapo ciani tikaganizila mmene Yehova anacitila zinthu na wolemba Salimo 73?

13 Wolemba Salimo 73 analefulidwa kwambili cifukwa coona ngati kuti anthu oipa zinthu zinali kuwayendela bwino. Iye anafika pokayikila zakuti kucita cifunilo ca Mulungu n’kwaphindu. (Sal. 73:12, 13, 16) Kodi Yehova anacita ciani? Sanamuimbe mlandu. Koma analola kuti mawu a wamasalimoyo alembedwe m’Baibo. M’kupita kwa nthawi, iye anazindikila kuti kukhala pa ubale wabwino na Yehova ndiye cinthu cabwino kwambili mu umoyo kuposa cina ciliconse. (Sal. 73:23, 24, 26, 28) Kodi tiphunzilapo ciani? Akulu sayenela kuthamangila kuimba mlandu Mkhristu amene wayamba kukamba na kucita zinthu zoonetsa kuti akukayikila zoti kutumikila Yehova kuli na phindu. M’malomwake, afunika kuyesetsa kumvetsetsa cifukwa cake iye amakamba na kucita zinthu mwa njila imeneyo. Akatelo, m’pamene angakwanitse kuseŵenzetsa bwino Malemba pom’limbikitsa.

14. N’cifukwa ciani Eliya anafunika thandizo? Nanga Yehova anamuthandiza bwanji?

14 Mneneli Eliya anathaŵa Mfumukazi Yezebeli. (1 Maf. 19:1-3) Panthawiyo, iye anaganiza kuti panalibe aliyense amene anali kutumikila monga mneneli wa Yehova. Ndiponso anayamba kuona ngati kuti nchito yake ya uneneli inalibe phindu. Iye analefuka kwambili cakuti analaka-laka kuti afe cabe. (1 Maf. 19:4, 10) Yehova sanamuimbe mlandu Eliya, koma anamutsimikizila kuti sanali yekha, komanso anamuuza kuti ayenela kudalila mphamvu za Mulungu. Anamuuzanso kuti panali nchito yaikulu imene iye anafunika kucita. Yehova anamvetsela mokoma mtima pamene Eliya anali kufotokoza nkhawa zake, ndipo anamupatsa nchito zina zakuti acite. (1 Maf. 19:11-16, 18) Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa? Tonsefe, maka-maka akulu, tiyenela kucita zinthu mokoma mtima na nkhosa za Yehova. Ngati wina mumpingo akukamba kuti ni wokhumudwa kapena akuona kuti Yehova sangamukhululukile, akulu ayenela kumumvetsela pamene akufotokoza nkhawa zake mocokela pansi pamtima. Ndiyeno, ayenela kutsimikizila munthuyo, amene ali ngati nkhosa yotaika, kuti Yehova amam’konda.

KODI TIYENELA KUZIONA BWANJI NKHOSA ZA MULUNGU ZOSOCELA?

15. Malinga na Yohane 6:39, kodi Yesu anali kuziona bwanji nkhosa za Atate wake?

15 Kodi Yehova amafuna kuti tiziziona bwanji nkhosa zake zosocela? Yesu anatipatsa citsanzo pa nkhani imeneyi. Iye anali kudziŵa kuti nkhosa iliyonse ya Yehova ni yamtengo wapatali pamaso pa Mulungu. Conco, anacita zonse zotheka kuti athandize “nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli” kubwelela kwa Yehova. (Mat. 15:24; Luka 19:9, 10) Komanso, Yesu pokhala m’busa wabwino, anayesetsa kuteteza nkhosa za Yehova kuti pasatayike iliyonse.—Ŵelengani Yohane 6:39.

16-17. Kodi akulu ayenela kuiona bwanji nchito yothandiza nkhosa zosocela? (Onani bokosi yakuti, “ Mmene Nkhosa Yosocela Ingamvelele.”)

16 Mtumwi Paulo analimbikitsa akulu mumpingo wa ku Efeso kuti azitengela citsanzo ca Yesu. Anati: “Muthandize ofookawo, ndipo muzikumbukila mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, ‘Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.’” (Mac. 20:17, 35) N’zoonekelatu kuti akulu masiku ano ali na udindo waukulu wosamalila anthu a Yehova. M’bale Salvador amene ni mkulu mumpingo ku Spain anati: “Nikaganizila cikondi cacikulu cimene Yehova amaonetsa posamalila nkhosa zake zosocela, nimalimbikitsidwa kucita zonse zotheka pothandiza nkhosazo. Pokhala m’busa wauzimu, nidziŵa kuti Yehova amafuna kuti nizisamalila nkhosa zake.”

17 Abale na alongo onse amene achulidwa m’nkhani ino, amene panthawi ina analeka kugwilizana na mpingo, anathandizidwa kubwelela kwa Yehova. Pano tikamba, pali Akhristu ambili ozilala amene amafuna kubwelela kwa Yehova. Nkhani yotsatila idzafotokoza zina zimene tingacite kuti tiwathandize kubwelela kwa Yehova.

NYIMBO 139 Yelekeza Uli M’dziko Latsopano

^ ndime 5 N’cifukwa ciani Akhristu ena amene atumikila Yehova mokhulupilika kwa zaka amazilala? Kodi Mulungu amawaona bwanji Akhristu amenewo? M’nkhani ino, tikambilana mayankho pa mafunso amenewa. Tikambilananso mmene Yehova anathandizila atumiki ake akale amene anayamba kufooka pom’tumikila, ndipo tiona zimene tingaphunzilepo.

^ ndime 2 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Wofalitsa wozilala ni uja amene sanapeleke lipoti lililonse pa nchito yolalikila na kuphunzitsa kwa miyezi 6 kapena kuposapo. Ngakhale n’telo, ofalitsa ozilala ni abale na alongo athu ndithu, ndipo timawakonda.

^ ndime 4 Maina ena asinthidwa.

^ ndime 10 Nkhani yotsatila idzafotokoza mmene akulu angacitile zinthu zitatu zimenezi.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’busa waciisiraeli anali kudela nkhawa nkhosa yosocela. Anali kuisakila, ndipo akaipeza anali kuitenga n’kuibweletsa pa gulu la nkhosa zinzake. N’zimenenso abusa auzimu amacita masiku ano.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pamene mlongo wozilala akuyembekezela kuti basi imene wakwela inyamuke, akuona Mboni ziŵili zikucita ulaliki wapoyela mosangalala.