Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kudziletsa—N’kofunika Kuti Tikondweletse Yehova

Kudziletsa—N’kofunika Kuti Tikondweletse Yehova

“Khazeni wanga atayamba kukangana nane, n’namugwila pakhosi n’kuyamba kum’kanyanga. N’nali kufuna kumupha,” anatelo Paul.

“Nikakhala kunyumba, n’nali kukwiya msanga kwambili ngakhale pa zifukwa zocepa. Nikakwiya, n’nali kuphwanya mipando, tukadoli, na ciliconse cimene napeza pafupi,” anatelo Marco.

Mwina ife sitingacite kufika pamenepa. Olo n’telo, tonsefe timalephela kudziletsa nthawi zina. Zili conco, maka-maka cifukwa cakuti tinatengela ucimo kwa kholo lathu loyambilila, Adamu. (Aroma 5:12) Mofanana na Paul komanso Marco, ena amalephela kulamulila mkwiyo wawo. Ena cimawavuta kulamulila maganizo awo. Amangokhalila kuganizila zinthu zimene zimawacititsa mantha kapena zimene zimawafooketsa. Enanso amalephela kudziletsa pa makhalidwe monga ciwelewele, kumwa moŵa mwaucidakwa, kapena kuseŵenzetsa amkolabongo.

Anthu amene amalephela kulamulila maganizo awo, zilakolako zawo, ndiponso zocita zawo, amadzibweletsela mavuto ambili pa umoyo wawo. Koma n’zotheka kupewa zimenezi. Motani? Mwa kukhala odziletsa. Kuti tikulitse khalidwe limeneli, tiyeni tikambilane mafunso atatu awa: (1) Kodi kudziletsa n’kutani? (2) N’cifukwa ciani n’kofunika kwambili? (3) Kodi tingacite ciani kuti tikhale na khalidwe limeneli, lomwe ni limodzi mwa “makhalidwe amene mzimu woyela” umabala? (Agal. 5:22, 23) Pambuyo pake, tikambilana zimene tingacite ngati nthawi zina timalephela kudziletsa.

KODI KUDZILETSA N’KUTANI?

Munthu wodziletsa amatha kulamulila maganizo na mtima wake. Iye amayesetsa kupewa kukamba kapena kucita zinthu zimene Mulungu sakondwela nazo.

Yesu anaonetsa bwino kwambili khalidwe la kudziletsa

Mwa zocita zake, Yesu anaonetsa bwino tanthauzo la kudziletsa. Baibo imati: “Pamene anali kunenedwa zacipongwe, sanabwezele zacipongwe. Pamene anali kuvutika, sanawopseze, koma anali kudzipeleka kwa iye amene amaweluza molungama.” (1 Pet. 2:23) Mwacitsanzo, Yesu anakhala wodziletsa pamene anthu otsutsa anali kumunyodola ali pa mtengo wozunzilapo. (Mat. 27:39-44) Izi zisanacitike, iye anaonetsanso kudziletsa pamene atsogoleli acipembedzo anayesa kum’peza cifukwa. (Mat. 22:15-22) Komanso tangoganizilani citsanzo cabwino ca kudziletsa cimene iye anaonetsa pamene Ayuda okwiya anatola miyala kuti am’teme nayo! M’malo mowabwezela, “Yesu anabisala ndi kutuluka m’kacisimo.”—Yoh. 8:57-59.

Kodi tingakwanitse kutengela citsanzo ca Yesu? Inde, tingakwanitse pa mlingo winawake. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Khristu anavutika cifukwa ca inu, ndipo anakusiyilani citsanzo kuti mutsatile mapazi ake mosamala kwambili.” (1 Pet. 2:21) Olo kuti ndise opanda ungwilo, n’zotheka kutengela mosamala kwambili citsanzo ca Yesu ca kudziletsa. N’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika kwambili?

N’CIFUKWA CIANI KUDZILETSA N’KOFUNIKA KWAMBILI?

Tiyenela kukhala odziletsa kuti Yehova azikondwela nafe. Ngakhale kuti mwina tatumikila Yehova mokhulupilika kwa nthawi yaitali, tikhoza kuwononga ubwenzi wathu na iye ngati sitidziletsa m’zocita na m’zokamba zathu.

Ganizilani za Mose, amene anali “munthu wofatsa kwambili kuposa anthu onse amene anali padziko lapansi” panthawiyo. (Num. 12:3) Kwa zaka zambili, Mose anapilila moleza mtima madandaulo a Aisiraeli. Koma tsiku lina, analephela kudziletsa. Iye anakwiya pamene Aisiraeli anadandaulanso za vuto la kusoŵa kwa madzi. Anakamba mwaukali kwa iwo, amvekele: “Tsopano tamvelani anthu opanduka inu! Kodi ticite kukutulutsilani madzi m’thanthweli?”—Num. 20:2-11.

Apa Mose analephela kulamulila mkwiyo wake. Iye sanapeleke ulemu kwa Yehova amene anapatsa madzi Aisiraeli mozizwitsa. (Sal. 106:32, 33) Zotulukapo zake n’zakuti, Yehova sanamulole Mose kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 20:12) Mpaka pa tsiku limene anamwalila, Mose ayenela kuti anali kudziimbabe mlandu cifukwa cakuti analephela kudziletsa panthawiyo.—Deut. 3:23-27.

Kodi titengapo phunzilo lanji? Olo kuti takhala m’coonadi kwa nthawi yaitali, tiyenela kupewelatu kukamba mopanda ulemu kwa anthu amene atikhumudwitsa kapena amene afunikila uphungu. (Aef. 4:32; Akol. 3:12) N’zoona kuti pamene munthu akukalamba, nthawi zina zimavuta kucita zinthu moleza mtima. Koma tiyenela kukumbukila zimene zinacitikila Mose. Ndipo tisalole kuti mbili yabwino imene tapanga potumikila Yehova mokhulupilika kwa nthawi yaitali, iwonongeke cifukwa colephela kudziletsa. Kodi tingacite ciani kuti tikulitse khalidwe lofunika kwambili limeneli?

MMENE TINGAKULITSILE KHALIDWE LA KUDZILETSA

Pemphani mzimu woyela. Cifukwa ciani? Cifukwa kudziletsa ni limodzi mwa makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umabala, ndipo Yehova amapeleka mzimu wake kwa anthu amene amaupempha. (Luka 11:13) Kupitila mwa mzimu wake, Yehova angatipatse mphamvu kuti tikwanitse kukhala odziletsa. (Afil. 4:13) Angatithandizenso kukhala na makhalidwe ena amene mzimu umabala, monga cikondi, cimene cimatithandiza kukulitsa khalidwe la kudziletsa.—1 Akor. 13:5.

Pewani ciliconse cimene cingapangitse kuti muzivutika kudziletsa

Pewani ciliconse cimene cingapangitse kuti muzivutika kudziletsa. Mwacitsanzo, muzipewa mawebusaiti na zosangalatsa zimene zimaonetsa zinthu zoipa. (Aef. 5:3, 4) Tiyenela kupewa ciliconse cimene cingatiyese kuti ticite zinthu zoipa. (Miy. 22:3; 1 Akor. 6:12) Mwacitsanzo, munthu amene amacita makhalidwe odetsa a za kugonana cifukwa colephela kulamulila cilakolako cake, angacite bwino kupewelatu kuŵelenga mabuku a zacikondi kapena kutamba mafilimu otelo.

Mwina tingaone kuti n’covuta kutsatila malangizo amenewa. Koma ngati ticita khama, Yehova adzatipatsa mphamvu zotithandiza kukhala odziletsa. (2 Pet. 1:5-8) Adzatithandiza kuti tizikwanitsa kulamulila maganizo athu, zokamba, na zocita zathu. Citsanzo ca zimenezi ni Paul na Marco, amene tawachula kuciyambi kwa nkhani ino. Aliyense wa iwo anaphunzila kulamulila mkwiyo wake. Ganizilaninso za m’bale wina amene anali kukonda kukwiya komanso kukangana na madilaiva ena poyendetsa motoka pa msewu. Kodi iye anacita ciani pofuna kuthetsa vutolo? M’baleyo anati: “N’nali kupemphela kwa Yehova mocondelela tsiku lililonse. N’nali kuŵelenga nkhani zofotokoza khalidwe la kudziletsa, komanso n’naloŵeza pamtima mavesi ena othandiza pa nkhaniyi. Ngakhale kuti nakhala nikulimbana na vutoli kwa zaka zambili, tsiku lililonse kukaca nimadziikila colinga cakuti niyesetse kukhala wodekha. Nikakhala na ulendo, nimanyamuka mwamsanga kuti nisakakamizike kuyenda mothamanga.”

KODI TINGACITE CIANI TIKALEPHELA KUDZILETSA?

Nthawi zina, tingalephele kukhala odziletsa. Ngati zaconco zacitika, tingamvele manyazi kwambili kupemphela kwa Yehova. Koma iyi ndiyo nthawi yofunika kupemphela kwambili. Conco mukalephela kudziletsa, nthawi yomweyo pemphelani kwa Yehova. M’pempheni kuti akukhululukileni na kukuthandizani, ndiponso tsimikizani mtima kusabwelezanso colakwaco. (Sal. 51:9-11) Musaganize kuti Yehova sangamvetsele pempho lanu locokela pansi pa mtima lopempha cikhululukilo. (Sal. 102:17) Kumbukilani kuti mtumwi Yohane anakamba kuti magazi a Mwana wa Mulungu ‘amatiyeletsa ku ucimo wonse.’ (1 Yoh. 1:7; 2:1; Sal. 86:5) Kumbukilaninso kuti Yehova amalangiza atumiki ake kuti ayenela kukhululukilana mobweleza-bweleza. Conco, tingakhale otsimikiza kuti iye adzacitanso cimodzi-modzi kwa ife.—Mat. 18:21, 22; Akol. 3:13.

Yehova sanakondwele pamene Mose analephela kudziletsa pa nthawi ina m’cipululu. Olo zinali telo, iye anamukhululukila Mose. Ndipo Mawu a Mulungu amakamba kuti Mose anali munthu wacikhulupililo cosagwedela, cimene tingatengeleko. (Deut. 34:10; Aheb. 11:24-28) Ngakhale kuti Yehova sanamulole Mose kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, m’tsogolo adzamuukitsa na kum’patsa mwayi wokhala na moyo wosatha m’Paladaiso pano pa dziko lapansi. Nafenso tingakhale na mwayi umenewu ngati tipitilizabe kuyesetsa kukulitsa khalidwe lofunika kwambili limeneli la kudziletsa.—1 Akor. 9:25.