Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kulabadila Kulila kwa Lipenga Masiku Ano

Kulabadila Kulila kwa Lipenga Masiku Ano

TONSE timakhulupilila kuti Yehova akutsogolela anthu ake na kuwadyetsa mwauzimu ‘m’masiku otsiliza’ ano. (2 Tim. 3:1) Koma aliyense payekha ali na udindo womvela malangizo amene Yehova amatipatsa. Mmene zinthu zilili kwa ife masiku ano zifanana na mmene zinalili kwa Aisiraeli m’cipululu. Iwo anafunika kulabadila kulila kwa malipenga.

Yehova analamula Mose kuti apange malipenga aŵili asiliva kuti ‘aziwagwilitsa nchito poitanitsa msonkhano ndi posamutsa msasa.’ (Num. 10:2) Ansembe anali kuliza malipengawo m’njila zosiyana-siyana podziŵitsa anthuwo zoyenela kucita. (Num. 10:3-8) Lelolino, anthu a Mulungu amalandila malangizo m’njila zambili. Tsopano tiyeni tioneko njila zitatu cabe za mmene timalandilila malangizo na kuziyelekezela na kulila kosiyana-siyana kwa malipenga m’nthawi ya Aisiraeli. Masiku ano, timalandila malangizo tikaitanidwa ku misonkhano ikulu-ikulu, akulu akaitanidwa kuti akaloŵe sukulu, ndiponso pamene mipingo yonse yalandila malangizo atsopano.

KULILA KWA LIPENGA KOITANILA ANTHU KU MISONKHANO IKULU-IKULU

Yehova akafuna kuti “khamu lonse” la Aisiraeli likasonkhane pa khomo la kum’maŵa kwa cihema, ansembe anali kuliza malipenga onse aŵili. (Num. 10:3) Popeza kuti mafuko onse a Aisiraeli anali kumanga misasa mozungulila cihema, ansembe akaliza malipenga, Aisiraeli onse anali kukwanitsa kumvela kulila kwa malipengawo. Mafuko amene anali kukhala capafupi na khomo la cihema, mwacionekele anali kufika mwamsanga pakhomolo. Ena anali kukhala kutali, ndipo anali kufunikila nthawi yokwanila komanso khama kuti akapezekepo. Kaya anali kukhala pafupi kapena kutali, Yehova anali kufuna kuti Aisiraeli onse akasonkhane pa khomo lacihema kuti akalandile malangizo ake.

Masiku ano, sitisonkhana pa cihema, koma timaitanidwa kuti tikapezeke ku misonkhano ya anthu a Mulungu. Misonkhanoyi iphatikizapo misonkhano yacigawo na misonkhano ina yapadela kumene timaphunzitsidwa na kulandila malangizo ofunikila. M’maiko osiyana-siyana kuzungulila dziko lonse, anthu a Yehova amalandila malangizo ofanana pa misonkhano. Conco, onse amene amalabadila ciitano cakuti akapezeke ku misonkhanoyi, ali mbali ya gulu limodzi lacimwemwe. Ena amafunika kuyenda msenga wautali kuti akapezekepo, koma ena sayenda msenga wautali. Zilibe kanthu kuti timayenda msenga wautali kapena waufupi, tonse timaona kuti kupezekapo n’kofunika kwambili.

Nanga bwanji za ofalitsa a m’tumagulu twakutali amene sakwanitsa kupezeka pa misonkhano ikulu-ikulu? Cifukwa ca zipangizo zamakono, ofalitsa ambili amene amakhala kutali, nawonso amapindula na misonkhano imeneyi, ndipo amafika podzimva kuti ali mbali ya gulu la abale na alongo amene apezeka pa misonkhanoyo. Mwacitsanzo, pa kucezela kwina kwa woimila likulu lathu, ofesi ya nthambi ku Benin inalumikiza msonkhano wapadela ku tauni ina yochedwa Arlit ku Niger. Iyi ni tauni ya migodi m’Cipululu ca Sahara. Abale na alongo pamodzi ndi anthu ena acidwi amene anasonkhana analipo 21. Olo kuti anali kumalo akutali, iwo anadzimva kuti anali mbali ya gulu la abale na alongo okwana 44,131 amene anapezeka pa msonkhanowo. M’bale wina anati: “Tiyamikila mocokela pansi pa mtima potilumikiza ku pulogilamu yapadela imeneyi. Izi zaonetsanso kuti mumatikonda kwambili.”

KULILA KWA LIPENGA KOITANILA AKULU

Wansembe waciisiraeli akaliza lipenga limodzi, “akuluakulu amene ndi atsogoleli a masauzande” ndiwo okha anali kufunika kukapezeka ku cihema cokumanako. (Num. 10:4) Kumeneko, anali kulandila malangizo komanso kuphunzitsidwa na Mose. Zimene anali kuphunzilazo zinali kuwathandiza kusamalila bwino maudindo awo m’mafuko awo. Mukanakhala mmodzi wa akulu-akuluwo, kodi simukanacita zonse zotheka kuti mukapezeke ku msonkhanowo n’colinga cakuti mukalandile nawo malangizo?

Masiku ano, akulu mumpingo si “atsogoleli,” komanso sacita ufumu pa gulu la nkhosa za Mulungu limene iye analisiya m’manja mwawo. (1 Pet. 5:1-3) Olo n’telo, iwo amacita zonse zimene angathe poŵeta nkhosazo. Ndiye cifukwa cake amalabadila na mtima wonse akaitanidwa kuti akalandile malangizo owonjezeleka, mwacitsanzo kupitila m’Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Pa sukulu imeneyi, akulu amaphunzitsidwa mmene angasamalile bwino mipingo. Zotulukapo zake n’zakuti onse m’mipingo amakhala olimba mwauzimu. Olo kuti simunaloŵepo sukulu imeneyi, mwacionekele mukupindula na maphunzilo amene akulu omwe analoŵapo sukuluyi analandila.

KULILA KWA LIPENGA KOTIPEMPHA KUPANGA MASINTHIDWE

Mtambo ukayamba kuyenda kucoka pa cihema, ansembe aciisiraeli anali kuliza lipenga lolila mosintha-sintha. Ici cinali cizindikilo cakuti Yehova afuna kuti Aisiraeli onse asamuke. (Num. 10:5, 6) Posamuka, Aisiraeli anali kucita zinthu mwadongosolo kwambili. Koma kusamuka inali nchito yaikulu kwa iwo. Ndipo n’kutheka kuti ena nthawi zina anali kuwaya-waya kusamuka. Cifukwa ciani?

Mwina ena anali kuona kuti anali kuuzidwa kaŵili-kaŵili kuti asamuke, komanso mosayembekezeleka. Baibo imakamba kuti nthawi zina mtambo wotsogolela Aisiraeli m’cipululu “unali kukhalapo kucokela madzulo kufika m’mawa.” Koma nthawi zina, unali kukhalapo “masiku awili, mwezi, kapena masiku ambili.” (Num. 9:21, 22) Kodi Aisiraeli anasamuka kangati? Numeri caputa 33 imakamba kuti iwo anasamuka kucoka pamalo ena na kupita kumalo ena maulendo pafupi-fupi 40.

Nthawi zina, Aisiraeli ena anali kumanga msasa pamalo amene panali mthunzi. Kukhala pa malo a mthunzi kuyenela kuti kunali kokondweletsa ngako cifukwa cipululu cimene anali kuyendamo cinali “cacikulu ndi cocititsa mantha.” (Deut. 1:19) Conco, n’kutheka kuti cinali covuta kwa Aisiraeli ena kusamuka pa malo otelo, podela nkhawa kuti akasamuka sadzapezanso malo abwino ngati amenewo.

Aisiraeli akayamba kusamuka, ciyenela kuti cinali covuta kwa ena kuyembekezela nthawi yawo yosamuka. Lipenga lolila mosintha-sintha likalila, onse anali kumvela, koma sikuti onse anali kusamuka pa nthawi imodzi. Lipengalo likalila koyamba, cinali cizindikilo cakuti mafuko amene anamanga misasa yawo kum’maŵa anyamuke. Mafuko amenewo anali a Yuda, Isakara, na Zebuloni. (Num. 2:3-7; 10:5, 6) Amenewa akanyamuka, ansembe anali kulizanso lipengalo kaciŵili kupeleka cizindikilo cakuti mafuko atatu amene anamanga misasa yawo kum’mwela anyamuke. Ansembe anali kupitiliza kucita zimenezi mpaka Aisiraeli onse atasamuka.

Mwina nthawi ina munavutikapo kutsatila masinthidwe enaake amene gulu linapanga. N’kutheka kuti munali kuona kuti zinthu zimene zasintha zaculuka kwambili. Kapena munali kukondwela na mmene zinthu zinali kuyendela kale, ndipo simunali kufuna kuti zisinthe. Mosasamala kanthu za cifukwa cimene munali naco, zinali zovuta kwa imwe kujaila masinthidwewo moleza mtima, ndipo n’kutheka kuti zinakutengelani nthawi. Koma tikayesetsa kutsatila masinthidwe amene apangidwa, mwacionekele tidzaona kuti Mulungu akutidalitsa.

M’nthawi ya Mose, Yehova anatsogolela Aisiraeli mamiliyoni kudutsa m’cipululu. Pakati pawo panali amuna, akazi, ndi ana. Iwo sakanakhala na moyo ngati Mulungu sanali kuwasamalila komanso kuwatsogolela. M’masiku otsiliza ano, timakhalabe olimba kuuzimu cifukwa Yehova amatitsogolela. Conco, tiyeni tonse tiyesetse kukhala omvela monga mmene Aisiraeli okhulupilika anali kucitila polabadila kulila kwa malipenga!