Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mudziŵa?

Kodi Mudziŵa?

Kodi anthu m’nthawi ya Yesu anali kukhoma misonkho yotani?

KUCOKELA kale-kale, Aisiraeli nthawi zonse anali kupeleka ndalama zocilikizila kulambila koona. Koma nkhani yokhometsa misonkho inadzakhala yocolowana kwambili, komanso kukhala mtolo kwa Ayuda m’nthawi ya Yesu.

Pocilikiza kulambila ku cihema, komanso pambuyo pake ku kacisi, Ayuda onse akulu-akulu aamuna anali kupeleka hafu ya sekeli imodzi (madalakima aŵili). M’zaka za zana loyamba, ndalamazo zinali kuseŵenzetsedwa pogula nsembe zopelekedwa pa kacisi, komanso kusamalila kacisiyo amene anamangidwa na Herode. Ayuda ena anafunsa Petulo za mmene Yesu anali kuonela nkhaniyo. Khristu sananene kuti kupeleka msonkho n’kulakwa. Ndipo iye anauza Petulo kumene akanapeza khobili lokhomela msonkho umenewo.—Mat. 17:24-27.

Cina, kumbuyoko anthu a Mulungu anali atauzidwa kupeleka cakhumi. Izi zinatanthauza kupeleka gawo limodzi mwa magawo khumi a mbewu zawo, kapena pa ndalama zimene apeza pa zimene agulitsa. (Lev. 27:30-32; Num. 18:26-28) Atsogoleli acipembedzo anali kukakamiza anthu kupeleka cakhumi cimeneci pa ndiwo zamasamba zilizonse, ngakhale pa “timbewu ta minti, dilili, ndi citowe.” Yesu sanakambe kuti kupeleka cakhumi n’kulakwa, koma anavumbula cinyengo ca alembi na Afarisi.—Mat. 23:23.

Pa nthawiyo Aroma ndiwo anali kulamulila, ndipo anali kufuna kuti Ayuda aziwapatsa misonkho yambili. Mwacitsanzo, panali msonkho umene anthu okhala na malo anafunika kupeleka, ndipo akanakhoma msonkhowo mwa kupeleka ndalama kapena zinthu. Ngati munthu wakolola matumba anayi pa malowo, anafunika kupeleka pafupi-fupi thumba limodzi kwa Aroma monga msonkho. Komanso, panali msonkho umene Myuda aliyense anayenela kupeleka. Msonkho umenewo ni umene Afarisi anafunsa Yesu ngati panali poyenela kuupeleka. Iye anaonetsa mmene tiyenela kuonela nkhani yopeleka misonkho pamene anakamba kuti: “Pelekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.”—Mat. 22:15-22.

Panalinso msonkho wina umene unali kupelekedwa katundu ukaloŵa m’cigawo cina, kapena potuluka m’cigawo cina. Msonkho umenewo unali kutengedwela pa madoko, maulalo, mphambano za njila, kapena poloŵela m’matauni, kapenanso m’misika.

Kukhoma misonkho kunali mtolo wolemetsa kwambili pansi pa ulamulilo wa Aroma. Malinga na wolemba mbili yakale waciroma dzina lake Tacitus, pa nthawi ya ulamulilo wa mfumu Tiberiyo, “anthu ku Siriya komanso ku Yudeya anapempha kuti awacepetseleko misonkho, cifukwa zinali zovuta kwambili kwa iwo kupeleka misonkho imeneyo.”

Mmene misonkho inali kukhomedwela, zinapangitsa umoyo wa anthu kukhala wovuta kwambili. Nchito yokhoma misonkho inali kupelekedwa kwa munthu amene wagula nchitoyo na ndalama zambili. Kenako munthuyo anali kulemba nchito anthu ena kuti azikhometsa misonkhoyo. Ndipo onse anali kufuna kupezelapo phindu. Zioneka kuti Zakeyu anali na anchito otelo okhometsa misonkho. (Luka 19:1, 2) M’pomveka kuti anthu anali okhumudwa na misonkhoyo, ndipo anali kuzonda anthu okhometsa misonkho imeneyo.