Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Kodi mtumwi Paulo anatanthauza ciani pamene anakamba kuti: “Mwa cilamulo, ine ndinafa ku cilamulo”?—Agal. 2:19.

Paulo analemba kuti: “Mwa cilamulo, ine ndinafa ku cilamulo, moti sindingacitsatilenso, kuti ndikhale wamoyo kwa Mulungu.”—Agal. 2:19.

Zimene Paulo analemba zinali zogwilizana na mfundo yaikulu, imene anali kumveketsa ku mipingo ya ku cigawo ca Roma ku Galatiya. Akhristu ena kumeneko, anali kutengela maganizo a aphunzitsi onyenga. Aphunzitsiwo anali kuphunzitsa kuti ngati munthu afuna kukapeza cipulumutso ayenela kusunga zonse za m’Cilamulo ca Mose, maka-maka kucita mdulidwe. Koma Paulo anadziŵa kuti tsopano Mulungu sanali kufunanso kuti Mkhristu aliyense mpaka acite mdulidwe. Mwa kufotokoza mokhutilitsa, iye anatsutsa ziphunzitso zabodza, ndipo analimbitsa cikhulupililo ca abale mu nsembe ya dipo la Yesu Khristu.—Agal. 2:4; 5:2.

Baibo imakamba momveka bwino kuti munthu akangomwalila, sadziŵa ciliconse ndipo sakhudzidwa na zimene zikucitika. (Mlal. 9:5) Pamene Paulo anakamba kuti: “Ndinafa ku cilamulo,” anatanthauza kuti sanalinso womangidwa na Cilamulo ca Mose. M’malo mwake, Paulo anali wotsimikiza kuti mwa cikhulupililo cake anakhala “wamoyo kwa Mulungu.”

“Mwa cilamulo,” zinthu zinasintha kwa Paulo. Motani? Iye anafotokoza “kuti munthu amayesedwa wolungama mwa kukhulupilila Khristu Yesu, osati cifukwa ca nchito za cilamulo.” (Agal. 2:16) Cilamuloco, cinakwanilitsa mbali ina yake yofunika. Paulo anafotokozela Agalatiya kuti: “[Cilamulo] anaciwonjezelapo kuti macimo aonekele, mpaka amene ali mbewuyo atafika, amene anapatsidwa lonjezolo.” (Agal. 3:19) Inde, Cilamulo cinaonetsa bwino kuti anthu opanda ungwilo, sangasunge Cilamulo mwangwilo, ndipo anafunikila nsembe yangwilo yopelekedwa kothela. Conco Cilamuloco cinatsogolela anthu ku “mbewuyo,” Khristu. Mwa kukhulupilila mwa Yesu Khristu, munthu angaonedwe wolungama kwa Mulungu. (Agal. 3:24) Paulo anafika pa mfundo imeneyo cifukwa mwa Cilamulo analandila Yesu na kukhulupilila mwa iye. Pa nthawi imeneyo Paulo ‘anafa ku cilamulo,’ ndipo anakhala “wamoyo kwa Mulungu.” Cilamuloco cinalibenso mphamvu pa iye, koma Mulungu.

Paulo anakambanso mfundo yofanana na imeneyi m’kalata yake yopita kwa Aroma. Iye anati: “Abale anga, thupi la Khristu linakupangani kukhala akufa ku Cilamulo . . . Tamasulidwa ku Cilamulo, cifukwa tafa ku Cilamulo cimene cinali kutimanga cija.” (Aroma 7:4, 6) Pa lembali komanso pa Agalatiya 2:19, paonetsa kuti Paulo sanali kukamba za kufa monga munthu wocimwa pansi pa Cilamulo. M’malo mwake, anali kufotokoza momveka bwino za kumasulidwa. Paulo mofanana na Akhristu ena monga iye, sanali omangidwa na Cilamuloco. Iwo anali atamasulidwa mwa kukhulupilila dipo la Khristu.