NKHANI YOPHUNZILA 25
Musapunthwitse “Tianati”
“Musanyoze mmodzi wa tianati.”—MAT. 18:10.
NYIMBO 113 Mtendele Wathu
ZIMENE TIKAMBILANE *
1. Kodi Yehova anacita ciani kwa aliyense wa ife?
YEHOVA anakokela aliyense wa ife kwa iye. (Yoh. 6:44) Ganizilani tanthauzo la zimenezi. Yehova posanthula mosamala mitima ya anthu onse mabiliyoni padzikoli, anaona cina cake camtengo wapatali mwa imwe. Cinthu cimeneco ni mtima wofuna kukulitsa cikondi canu pa iye. (1 Mbiri 28:9) Yehova amakudziŵani, amakumvetsetsani, ndipo amakukondani. Zimenezi n’zolimbikitsa kwambili!
2. Kodi Yesu anapeleka fanizo lotani pomveketsa mfundo yakuti Yehova amasamala za nkhosa yake iliyonse?
2 Yehova amasamala kwambili za imwe, ndipo amasamala kwambili za abale na alongo anu onse acikhristu. Pofuna kumveketsa bwino mfundo imeneyi, Yesu anayelekezela Yehova na m’busa. Ngati nkhosa imodzi pa nkhosa 100 yasocela, kodi m’busa adzacita ciani? Adzasiya “nkhosa 99 zija m’phili ndi kupita kukafunafuna yosocelayo.” M’busa akapeza nkhosayo, sadzaikalipila. Koma adzakondwela. Mfundo yake ni iti? Nkhosa iliyonse ni yofunika kwa Yehova. Yesu anati: “Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.”—Mat. 18:12-14.
3. Tikambilane ciani m’nkhani ino?
3 Mosakayikila, sitingafune kuti m’bale kapena mlongo afooke cifukwa ca ife. Tingapewe bwanji kupunthwitsa ena? Nanga tingacite ciani ngati wina watikhumudwitsa? Mafunso amenewa ayankhidwa m’nkhani ino. Koma coyamba, tiyeni tidziŵe zambili za “tianati” tochulidwa m’Mateyu caputala 18.
KODI “TIANATI” NDANI?
4. Kodi “tianati” ndani?
4 “Tianati” ni ophunzila a Yesu a misinkhu yonse. Mosasamala kanthu za zaka zawo, iwo ali “ngati ana aang’ono” m’lingalilo lakuti ni okonzeka kuphunzitsidwa na Yesu. (Mat. 18:3) Ngakhale kuti amakhala kosiyana, ali na zikhalidwe zosiyana, ndipo amaona zinthu mosiyana, komanso ali na maumunthu osiyana, onse amakhulupilila mwa Khristu. Nayenso Khristu amawakonda kwambili.—Mat. 18:6; Yoh. 1:12.
5. Kodi Yehova amamvela bwanji ngati munthu wina wapunthwitsa, kapena kukhumudwitsa mmodzi wa anthu ake?
5 “Tianati” tonse n’ta mtengo wapatali kwa Yehova. Kuti timvetse mmene iye amamvelela, ganizilani mmene timaonela ana. Ni a mtengo wapatali kwa ife. Timafuna kuwateteza cifukwa alibe mphamvu, cidziŵitso, komanso nzelu monga anthu akulu-akulu. Sitimakondwela ngati munthu wina avutitsidwa, maka-maka ngati wina akuvutitsa mwana, timakwiya kwambili. Mofananamo, Yehova amafuna kutiteteza. Amakwiya ngako ngati munthu wina wapunthwitsa, kapena kukhumudwitsa mmodzi wa anthu ake!—Yes. 63:9; Maliko 9:42.
6. Malinga na 1 Akorinto 1:26-29, kodi dziko limawaona bwanji ophunzila a Yesu?
6 Kodi ophunzila a Yesu ali ngati “tiana” m’njila ina iti? Kodi dziko limaona kuti anthu ofunika ni ati? Aja olemela, ochuka, komanso aulamulilo. Koma ophunzila a Yesu amaoneka ngati “tiana” tosafunika, ndiponso topanda pake. (Ŵelengani 1 Akorinto 1:26-29.) Koma Yehova sawaona mwa njila imeneyi.
7. Kodi Yehova amafuna kuti tiziwaona bwanji abale na alongo athu?
7 Yehova amakonda atumiki ake onse, kaya amutumikila kwa zaka zambili kapena ni atsopano m’coonadi. Abale na alongo athu onse ni ofunika kwa Yehova. Conco ayenelanso kukhala ofunika kwa ife. Tiyenela ‘kukonda gulu lonse la abale’ osati cabe ena mwa iwo. (1 Petulo 2:17) Tiyenela kucita zonse zimene tingathe kuti tiwateteze na kuwasamalila. Ngati tazindikila kuti takhumudwitsa munthu wina, sitiyenela kungoinyalanyaza nkhaniyo na kuganiza kuti munthuyo amakwiya msanga, ndipo ayenela kungoiiŵalako nkhaniyo. N’ciani cingapangitse ena kukhumudwa? Mwina cifukwa ca kumene anakulila, abale na alongo ena amadziona kuti ni osafunika. Ena ni acatsopano m’coonadi, ndipo akalibe kudziŵa zimene angacite ena akalakwitsa. Mulimonsemo, tiyenela kucita zonse zotheka kuti tikonze zinthu. Kuwonjezela apo, munthu amene amakonda kukhumudwa na ena, ayenela kukumbukila kuti limeneli ni khalidwe loipa limene afunika kugwililapo nchito. Ayenela kucita izi kuti akhale na mtendele wa maganizo, komanso kuti azikhala mwamtendele na ena.
MUZIONA ENA KUKHALA OKUPOSANI
8. Ni maganizo ofala ati amene anakhudza ophunzila a Yesu?
8 N’ciani cinapangitsa Yesu kukamba za “tianati”? Ophunzila ake anam’funsa funso lakuti: “Ndani kwenikweni amene adzakhala wamkulu kwambili mu Ufumu wakumwamba?” (Mat. 18:1) Pa nthawiyo, Ayuda ambili anali kuona kuti kukhala na udindo n’kofunika kwambili. Katswili wina anati: “Kupatsidwa ulemu na kukhala wochuka zinali zofunika kwambili mu moyo wawo.”
9. Kodi ophunzila a Yesu anayenela kucita ciani?
9 Yesu anali kudziŵa kuti ophunzila ake anayenela kucita khama kuti acotse m’mitima yawo mzimu wa mpikisano, umene unali wozika mizu m’cikhalidwe ca Ayuda. Anawauza kuti: “Amene ali wamkulu kwambili pa Luka 22:26) Timakhala ngati “wamng’ono kwambili” pamene ‘tiona ena kukhala otiposa.’ (Afil. 2:3) Tikakulitsa kwambili khalidwe limeneli, tidzapewa kukhumudwitsa ena.
nonsenu akhale ngati wamng’ono kwambili pa nonsenu, ndipo amene ali mtsogoleli akhale wotumikila.” (10. Ni uphungu wotani wa Paulo umene tiyenela kukumbukila?
10 Abale na alongo athu onse amatiposa m’njila zina. N’cosavuta kuona zimenezi ngati timasumika maganizo athu pa makhalidwe awo abwino. Tiyenela kukumbukila uphungu umene mtumwi Paulo anapeleka kwa Akorinto. Anati: “Kodi akukupangitsa kukhala wosiyana ndi ena ndani? Inde, uli ndi ciani cimene sunacite kulandila? Ndiye ngati unacita kulandila zinthu zimenezo, n’cifukwa ciani ukudzitama ngati kuti sunacite kulandila?” (1 Akor. 4:7) Tiyenela kusamala kwambili kuti tisagwele m’mayeselo odziona kuti ndife apamwamba, kapena kuganiza kuti ndife ofunika kwambili kuposa ena. Ngati m’bale amakamba nkhani zotentha, kapena ngati mlongo ali na mphatso yoyambitsa maphunzilo a Baibo, iwo sayenela kuzengeleza kupeleka citamando kwa Yehova.
KHULULUKANI NA “MTIMA WONSE”
11. Kodi Yesu anatiphunzitsa mfundo yanji pa fanizo la mfumu na kapolo wake?
11 Pambuyo pakuti Yesu wacenjeza otsatila ake kuti asamakhumudwitse ena, anapeleka fanizo lonena za mfumu na kapolo wake. Mfumuyo inakhululukila kapolo wake pa nkhongole yaikulu imene sakanatha kuibweza. Pambuyo pake, kapolo mmodzimodziyo anakana kukhululukila kapolo mnzake nkhongole yaing’ono imene anali nayo kwa iye. Pamapeto pake, mfumuyo inaponya m’ndende kapolo wopanda cifundoyo. Kodi pali phunzilo lanji pamenepa? Yesu anati: “Atate wanga wakumwamba adzathana ndi inu ngati aliyense wa inu sakhululukila m’bale wake ndi mtima wonse.”—Mat. 18:21-35.
12. Kodi timawakhumudwitsa bwanji ena ngati takana kukhululuka?
12 Zocita za kapolo woipayo sizinavulaze iye yekha, koma zinavulazanso ena. Coyamba, iye mopanda cifundo anavulaza kapolo mnzakeyo mwa “kukam’peleka kundende mpaka pamene adzabweze ngongoleyo.” Caciŵili, kapolo woipayo anakhumudwitsa akapolo ena amene anaona zimene iye anacita. “Akapolo anzake ataona zimene zinacitikazo, anamva cisoni kwambili.” Mofananamo, zocita zathu zimakhudza ena. N’ciani cingacitike ngati munthu wina watilakwila ndipo takana kum’khululukila? Coyamba, timam’khumudwitsa mwa kukana kum’khululukila, kusamumvetsela, ndiponso kusamuonetsa cikondi. Caciŵili, timapangitsa ena mu mpingo kukhala osamasuka akadziŵa kuti sitigwilizana na munthu wina.
13. Mwaphunzilapo ciani pa cocitika ca mlongo wina amene ni mpainiya?
13 Tikamakhululukila abale na alongo athu, timapindula ife eni ndiponso timapindulitsanso ena. Izi n’zimene zinacitikila mpainiya wina amene tam’patsa dzina lakuti Crystal. Mlongoyu anakhumudwitsidwa na mlongo wina mu mpingo. Mlongo Crystal anati: “Mawu ake okhadzula anali kunilasa monga mpeni. Popita mu ulaliki sin’nali kufuna ngakhale kuyendela naye pamodzi. Cangu canga cinayamba kucepa ndipo n’nataya cimwemwe.” Mlongo Crystal anali kuona kuti ali na cifukwa comveka cokhalila wokhumudwa. Koma sanasunge mkwiyo kapena kudzimvela cisoni. Modzicepetsa anaseŵenzetsa uphungu wa m’Malemba wopezeka m’nkhani yakuti “Khululukani Kucokela mu Mtima” mu
Nsanja ya Mlonda ya October 15, 1999. Anakhululukila mlongo wake. Mlongo Crystal ananena kuti: “Tsopano nadziŵa kuti tonsefe tikuyesetsa kuvala umunthu watsopano, ndipo Yehova amatikhululukila tsiku lililonse. Nimvela monga kuti natula pansi cinthu colema kwambili. Nakhalanso wacimwemwe.”14. Malinga na Mateyu 18:21, 22, kodi zioneka kuti mtumwi Petulo anali kuvutika kucita ciani? Nanga tingaphunzile ciani pa yankho la Yesu?
14 Timadziŵa kuti tiyenela kukhululukila ena. Ndipo ndiye cinthu coyenela kucita. Koma tingamavutike kucita zimenezi. Nthawi zina mtumwi Petulo ayenela kuti anali kumvela mwa njila imeneyi. (Ŵelengani Mateyu 18:21, 22.) Ndiye n’ciani cingatithandize? Coyamba, tiyenela kusinkha-sinkha za kuculuka kwa zimene Yehova watikhululukila. (Mat. 18:32, 33) Si ndife oyenela cikhululukilo cake, koma amatikhululukila na mtima wonse. (Sal. 103:8-10) Pa nthawi imodzimodzi “ifenso tiyenela kukondana.” Conco, kukhululuka si nkhani yocita kusankha kuti tikhululuke kapena ayi. Tiyenela kuwakhululukila abale na alongo athu. (1 Yoh. 4:11) Caciŵili, tiyenela kuganizila zotulukapo zabwino zimene zingakhalepo tikakhululuka. Tingathandize munthu amene watilakwila, kugwilizanitsa mpingo, kuteteza ubale wathu na Yehova, ndiponso kumva kukhala omasuka. (2 Akor. 2:7; Akol. 3:14) Cothela, tiyenela kupemphela kwa amene amafuna kuti tizikhululuka. Tisalole kuti Satana asokoneze mtendele umene tili nawo na alambili anzathu. (Aef. 4:26, 27) Timafunikila thandizo la Yehova kuti tipewe kugwela mu msampha wa Satana.
MUSALOLE KUTI WINA AKUPUNTHWITSENI
15. Mogwilizana na Akolose 3:13, tingacite ciani ngati tikuvutika maganizo na zimene m’bale kapena mlongo anaticitila?
15 Bwanji ngati Mkhristu mnzanu wacita zinthu zimene zikukuvutitsani maganizo Luka 6:28) Ngati simungathe kuiŵalako zimene m’bale wanu wakucitilani, ganizilani njila yabwino ya mmene mungakambile naye. Nthawi zonse ni bwino kuganizila kuti m’baleyo sanacitile dala kuti akukhumudwitseni. (Mat. 5:23, 24; 1 Akor. 13:7) Pokambilana naye muziona kuti ali na zolinga zabwino. Nanga bwanji ngati iye safuna kubweletsa mtendele? ‘Pitilizani kumulolela.’ Musaleme naye m’bale wanu. (Ŵelengani Akolose 3:13.) Cofunika kwambili, musasunge cakukhosi, cifukwa kucita zimenezo kungawononge ubwenzi wanu na Yehova. Musalole ciliconse kukupunthwitsani. Mwa kucita zimenezi, mudzaonetsa kuti mumakonda Yehova kuposa cina ciliconse.—Sal. 119:165.
kwambili? Kodi muyenela kucita ciani? Citani zonse zotheka kuti mukhazikitse mtendele. Tembenukilani kwa Yehova mwa kupemphela mocokela pansi pa mtima. M’pempheni kuti athandize munthu amene wakulakwilaniyo, komanso kuti akuthandizeni kuona makhalidwe abwino mwa munthuyo—inde, makhalidwe a munthuyo amene Yehova amakonda. (16. Kodi aliyense wa ife ali na udindo wotani?
16 Timayamikila mwayi umene tili nawo wotumikila Yehova mogwilizana monga “gulu limodzi” pansi pa “m’busa mmodzi”! (Yoh. 10:16) Buku lakuti Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova, tsamba 165 limati: “Popindula na umodzi umenewo, tilinso na udindo wa kuulimbitsa.” Conco, tiyenela ‘kuzolowela kuona abale na alongo athu mmene Yehova amawaonela.’ Kwa Yehova, tonse ndife “tiana” ta mtengo wapatali. Kodi umu ni mmene mumaonela abale na alongo anu? Yehova amaona ndipo amayamikila zonse zimene mumacita powathandiza na kuwasamalila.—Mat. 10:42.
17. Kodi ndife otsimikiza mtima kucita ciani?
17 Timawakonda alambili anzathu. Conco, ndife ‘otsimikiza mtima kusaikila m’bale wathu cokhumudwitsa kapena copunthwitsa.’ (Aroma 14:13) Timaona abale na alongo athu kukhala otiposa, ndipo timafuna kuwakhululukila mocokela pansi pa mtima. Tisalole kuti ena atipunthwitse. M’malo mwake, “tiyeni titsatile zinthu zobweletsa mtendele ndiponso zolimbikitsana.”—Aroma 14:19.
NYIMBO 130 Khalani Wokhululuka
^ ndime 5 Cifukwa ca kupanda ungwilo, tingakambe kapena kucita zinthu zimene zingakhumudwitse abale na alongo athu. Kodi zaconco zikacitika timacita ciani? Kodi timayesetsa kukonzanso ubale wathu? Kodi timapepesa mwamsanga? Kapena mumakhala na maganizo akuti ‘ilo ni vuto lawo osati langa?’ Kapena timakhumudwa msanga na zimene ena angakambe kapena kucita? Kodi timadzilungamitsa pa zimene tacita mwa kukamba kuti ndiye mmene tilili, n’cibadwa cathu? Kapena timaona zimene tacita monga cifooko cimene tiyenela kugwililapo nchito?
^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Mlongo wakwiyila mlongo wina mu mpingo. Pambuyo pokambilana mwamseli, iwo aiŵalako nkhaniyo ndipo akutumikila pamodzi mwacimwemwe.