Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 23

Yehova Ali Namwe, Simuli Mwekha

Yehova Ali Namwe, Simuli Mwekha

“Yehova ali pafupi ndi onse oitanila pa iye.”—SAL. 145:18.

NYIMBO 28 Kukhala Bwenzi la Yehova

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’cifukwa ciani atumiki a Yehova nthawi zina angaone kuti ali wokha-wokha?

AMBILI a ife timasungulumwa nthawi zina. Ena amakhala osungulumwa kwa nthawi yocepa, pamene ena zimawatengela nthawi yaitali. Tingasungulumwe ngakhale pamene tili pakati pa anthu. Ena zimawavuta kuzoloŵela kukhala mu mpingo watsopano. Ena anacokela m’banja limene anali kucita zinthu zambili capamodzi. Koma amasungulumwa akasamukila kutali na acibale awo. Enanso amayewa kwambili kuceza na wokondedwa wawo amene anamwalila. Ndipo Akhristu ena, maka-maka aja amene anaphunzila coonadi caposacedwa, amaona kuti ali wokha-wokha akakanidwa kapena kuzunzidwa na acibale awo osakhulupilila kapena anzawo akale.

2. Kodi tidzapeza mayankho pa mafunso ati?

2 Yehova amadziŵa komanso kumvetsa zonse zokhudza ife. Iye amadziŵa tikasungulumwa, ndipo amafuna kutithandiza kugonjetsa vutolo. Kodi Yehova amatithandiza bwanji? Tingacite ciani kuti tidzithandize? Nanga tingacite ciani kuti tithandize ena mu mpingo mwathu amene ni osungulumwa? Tiyeni tipeze mayankho pa mafunso amenewa.

YEHOVA AMASAMALA ZA IFE

Yehova anatumiza mngelo kukatsimikizila Eliya kuti sanali yekha (Onani ndime 3)

3. Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti anali kumudela nkhawa Eliya?

3 Yehova amasamala kwambili za alambili ake onse. Iye ali pafupi na aliyense wa ife, ndipo amadziŵa tikakhwethemuka na maganizo olefula. (Sal. 145:18, 19) Onani mmene Yehova anaonetsela kuti anali kumudela nkhawa mneneli Eliya. Munthu wokhulupilika ameneyu anakhalako pa nthawi yovuta m’mbili ya Aisiraeli. Alambili a Yehova anali kuzunzidwa koopsa, ndipo adani amphamvu otsutsa Mulungu anali kufuna kupha Eliya. (1 Maf. 19:1, 2) Mwina cina cimene cinavutitsa maganizo Eliya ni kuona kuti anali atatsala yekha-yekha monga mneneli wotumikila Yehova. (1 Maf. 19:10) Mwamsanga Mulungu anagwapo kuti am’thandize Eliya. Yehova anatumiza mngelo kukam’tsimikizila mneneli wake kuti sanali yekha, koma panalinso Aisiraeli ena ambili oopa Mulungu!—1 Maf. 19:5, 18.

4. Kodi Maliko 10:29, 30 ionetsa bwanji kuti Yehova amaŵadela nkhawa atumiki ake amene mwina angasoŵe cicilikizo ca ena?

4 Yehova amadziŵa kuti tikasankha kum’tumikila, ena a ife tingafunike kudzimana zambili. Izi zingaphatikizepo kusalandilanso cicilikizo kucokela kwa acibale athu osakhulupilila, komanso anzathu akale. Mwina ndiye cifukwa cake mtumwi Petulo anafunsa Yesu mwankhawa kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zonse ndi kukutsatilani, kodi tidzapeza ciani?” (Mat. 19:27) Yesu analimbikitsa ophunzila ake mwa kuwatsimikizila kuti adzakhala m’banja lalikulu lauzimu. (Ŵelengani Maliko 10:29, 30.) Ndipo Yehova Mutu wa banja lathu lauzimu analonjeza kuti adzacilikiza onse amene amafuna kum’tumikila. (Sal. 9:10) Tiyeni tione zinthu zina zothandiza zimene mungacite kuti mulandile thandizo la Yehova polimbana na vuto la kusungulumwa.

ZIMENE MUNGACITE MUKASUNGULUMWA

5. Kodi kuganizila mmene Yehova akukucilikizilani kungakuthandizeni bwanji?

5 Ganizilani mmene Yehova akukucilikizilani. (Sal. 55:22) Izi zidzakuthandizani kukhala na kapenyedwe koyenela pa vuto lanu. Mlongo Carol, * amene ni mbeta ndipo ndiye yekha Mboni m’banja lawo, anati: “Kuyang’ana kumbuyo na kuganizila mmene Yehova wanicilikizila pa mavuto anga onse, kumanithandiza kwambili kuona kuti sinili nekha. Ndipo zimanitsimikizila kuti Yehova adzakhalabe nane nthawi zonse.”

6. Kodi 1 Petulo 5:9, 10 ingawalimbikitse bwanji aja amene ali na vuto la kusungulumwa?

6 Ganizilani mmene Yehova akuthandizila alambili anzanu amene amasungulumwa. (Ŵelengani 1 Petulo 5:9, 10.) M’bale Hiroshi, amene kwa zaka zambili wakhala yekha Mboni ya Yehova m’banja lawo, anati: “Mu mpingo, n’cosavuta kuona kuti aliyense zinthu zili bwino mu umoyo wake. Kudziŵa kuti tonse tikucita zimene tingathe potumikila Yehova, kungalimbikitse ena a ife amene tili tekha m’coonadi m’banja lathu.”

7. Kodi pemphelo limakuthandizani bwanji?

7 Khalani na pulogilamu yabwino yocita zauzimu. Izi ziphatikizapo kuuza Yehova momasuka mmene mumvelela. (1 Pet. 5:7) Mlongo Massiel anati: “Cimodzi mwa zinthu zofunika kwambili zimene zinanithandiza kugonjetsa vuto langa la kusungulumwa, cinali kupemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima.” Mlongo wacitsikana ameneyu atasankha kutumikila Yehova, anali kukhala wosungulumwa cifukwa a m’banja lake sanali kutumikila Yehova. Mlongoyo anapitiliza kuti: “Yehova anali Tate wanga weni-weni, ndipo n’nali kupemphela kwa iye tsiku lililonse maulendo ambili patsiku, kumuuza mmene n’nali kumvelela.”

Kumvetsela kuŵelengedwa kwa Baibo komanso zofalitsa zofotokozela Baibo zojambulidwa, kungathandize amene ali okha kucepetsa vuto la kusungulumwa (Onani ndime 8) *

8. Kodi kuŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkha-sinkha kumakuthandizani bwanji?

8 Ŵelengani Mawu a Mulungu nthawi zonse, ndipo sinkha-sinkhani pa nkhani zoonetsa kuti Yehova amakukondani. Mlongo Bianca amene amalefulidwa na a m’banja lake, anafotokoza kuti: “Kuŵelenga na kusinkha-sinkha pa nkhani za m’Baibo, komanso mbili za atumiki a Yehova amene anakumanapo na mavuto ofanana na anga kumanithandiza kwambili.” Akhristu ena amaloŵeza pa mtima Malemba otonthoza monga Salimo 27:10 na Yesaya 41:10. Ena amaona kuti kumvetsela nkhani zojambulidwa zimene zidzaphunzilidwa, kumawathandiza kusakhala osungulumwa pokonzekela misonkhano, kapena poŵelenga Baibo.

9. Kodi kupezeka ku misonkhano kumakupindulitsani bwanji?

9 Muziyesetsa kusonkhana mokhazikika. Mudzapindula na pulogilamu yolimbikitsa, ndipo mungaŵadziŵe bwino abale na alongo anu. (Aheb. 10:24, 25) Mlongo Massiel amene tam’gwila mawu kuciyambi anati: “Ngakhale kuti n’nali wamanyazi, n’nali kuyesetsa kupezeka ku misonkhano yonse ya mpingo na kupelekapo ndemanga. Izi zinanithandiza kumvela kuti nanenso ndine ciwalo ca mpingowo.”

10. N’cifukwa ciani kupalana ubwenzi na Akhristu okhulupilika n’kofunika?

10 Palanani ubwenzi na Akhristu okhulupilika. Palanani ubwenzi na anthu amene mungaphunzileko zina kwa iwo, ngakhale amene musiyana nawo zaka kapena cikhalidwe. Baibo imatikumbutsa kuti “okalamba . . . amakhala ndi nzelu.” (Yobu 12:12) Nawonso acikulile angaphunzile zambili kwa acicepele okhulupilika. Davide anali wamng’ono kwambili poyelekezela na Yonatani. Koma zimenezo sizinawalepheletse kukhala pa ubwenzi wolimba. (1 Sam. 18:1) Davide na Yonatani anali kuthandizana potumikila Yehova ngakhale pa mavuto aakulu. (1 Sam. 23:16-18) Mlongo Irina amene palipano ndiye yekha Mboni m’banja mwawo, ananena kuti: “Abale na alongo athu angakhaledi makolo athu a kuuzimu, kapena azikulu athu na azing’ono athu. Yehova angawaseŵenzetse kukhala banja lathu limene tifunikila.”

11. Kodi tiyenela kucita ciani kuti tilimbitse ubwenzi na ena?

11 Kupanga mabwenzi atsopano kungakhale kovuta maka-maka ngati ndimwe wamanyazi. Mlongo Ratna amene ni wamanyazi, ndipo anaphunzila coonadi ngakhale kuti anali kutsutsidwa ananena kuti: “N’nafunika kuvomeleza kuti n’nali kufunikila thandizo na cicilikizo cocokela ku banja langa lauzimu.” Cingakhale covuta kufotokoza mmene umvelela. Koma kukambilana momasuka na wina kumakhala maziko a ubwenzi wolimba. Mabwenzi anu amafuna kukulimbikitsani na kukucilikizani. Ngakhale n’conco, mufunika kucita kuwauza kuti adziŵe mmene angakuthandizileni.

12. Kodi ulaliki ungakuthandizeni bwanji kupanga mabwenzi abwino?

12 Imodzi mwa njila zothandiza kwambili popanga mabwenzi, ni mwa kulalikila pamodzi na Akhristu anzathu. Mlongo Carol amene tam’gwila mawu kuciyambi anakamba kuti: “Napeza mabwenzi ambili abwino mwa kulalikila pamodzi na alongo, komanso kucita nawo zinthu zina zauzimu. Kwa zaka zambili, Yehova wakhala akunithandiza kupitila mwa mabwenzi amenewa. M’pake kulimbikila kupalana ubwenzi na Akhristu okhulupilika. Yehova amaseŵenzetsa mabwenzi otelo pokuthandizani kulimbana na maganizo olefula monga kusungulumwa.—Miy. 17:17.

THANDIZANI ENA KUMVELA KUTI ALI M’BANJA LA MPINGO WANU

13. Kodi onse mu mpingo ali na udindo wanji?

13 Onse mu mpingo ali na udindo wothandiza kuti mu mpingomo mukhale cikondi na mtendele, kuti pasapezeke aliyense woona kuti ali yekha-yekha. (Yoh. 13:35) Zimene timakamba na kucita zingakhale zothandiza zedi! Mvelani zimene mlongo wina anakamba. Iye anati: “N’taphunzila coonadi, mpingo unakhala banja langa. Popanda thandizo lawo, sinikanakhala wa Mboni za Yehova.” Kodi mungacite ciani kuti muthandize aja amene m’banja mwawo iwo okha ndiwo Mboni, kuti nawonso azimvela kuti ni ziwalo za mpingo?

14. Mungacite ciani kuti mukhale pa ubwenzi na anthu amene asamukila mu mpingo mwanu?

14 Khalani patsogolo kupanga ena kukhala mabwenzi anu. Tingayambe mwa kulandila mwansangala anthu amene asamukila mu mpingo mwathu. (Aroma 15:7) Komabe, siziyenela kuthela cabe pa kuwapatsa moni mwaubwenzi. M’malo mwake, tiyenela kukhala nawo pa ubwenzi wolimba m’kupita kwa nthawi. Conco, muzikhala na cidwi ceni-ceni kwa amene asamukila mu mpingo mwanu. Mosaloŵelela nkhani zawo zaumwini, yesani kumvetsa mavuto amene akupitamo. Ena zimaŵavuta kufotokoza mmene akumvelela. Conco samalani kuti musawakakamize kukamba. Koma mokoma mtima afunseni mafunso mosamala kuti afotokoze za mu mtima mwawo. Ndipo amvetseleni moleza mtima akamayankha. Mwacitsanzo, mungaŵafunse mmene anaphunzilila coonadi.

15. Kodi Akhristu okhwima kuuzimu angathandize bwanji ena mu mpingo?

15 Onse mu mpingo adzakula kuuzimu ngati Akhristu okhwima, maka-maka akulu awaonetsa cidwi. Mlongo Melissa amene anaphunzitsidwa coonadi na amayi ake ananena kuti: “Nimacita kusoŵa mawu oyamikila abale amene kwa zaka zambili akhala monga atate anga a kuuzimu. Nthawi zonse nikafuna wokamba naye, iwo amanimvetsela.” M’bale wacicepele Mauricio amene anadzimva wotaika mphunzitsi wake wa Baibo ataleka coonadi anati: “Akulu ananionetsa cidwi ceni-ceni, ndipo zimenezo zinanithandiza kwambili. Anali kukambilana nane nthawi zambili. Anali kulalikila nane, kuniuzako cuma cauzimu cimene anapeza pa phunzilo lawo laumwini, ngakhale kucita nane maseŵela olimbitsa thupi.” Onse aŵili mlongo Melissa na Mauricio, anafika poyamba utumiki wanthawi zonse.

Kodi mudziŵako wina wake mu mpingo mwanu amene angayamikile kwambili kuceza naye komanso kumuonetsa kukoma mtima? (Onani ndime 16-19) *

16-17. Kodi tingathandize ena m’njila ziti?

16 Pelekani thandizo lofunikila. (Agal. 6:10) M’bale Leo amene akutumikila monga mmishonale ku dziko lakutali na kwawo anakamba kuti: “Kambili cimene munthu angafunikile ni kungomuonetsa kukoma mtima pa nthawi yoyenela. Nikumbukila tsiku lina n’nacita ngozi na motoka. Pamene n’nali kufika ku nyumba, n’nali wopsinjika maganizo. Koma banja lina linaniitanila ku nyumba kwawo ku cakudya. Sinikumbukila zimene tinadya, koma nikumbukila kuti pamapeto pake mtima wanga unakhala m’malo!”

17 Tonsefe timakondwela na mapulogilamu auzimu monga misonkhano yadela komanso yacigawo, cifukwa imakhalanso nthawi yabwino yoceza na ena. Ndiponso, timakambilana mfundo zokhudza pulogilamu imeneyo. Ngakhale n’telo, mlongo Carol amene tam’gwila mawu kumayambililo anati: “Nimakhala wosungulumwa ngako pa misonkhano yadela komanso yacigawo.” Cifukwa ciani? Iye ananena kuti: “Olo kuti ningakhale pakati pa abale na alongo mahandiledi kapena masauzande, nthawi zambili onse amakhala na mabanja awo. Nikaŵaona nimasungulumwa kwambili.” Ena cimaŵavuta kupezeka ku msonkhano wacigawo kapena wadela kwa nthawi yoyamba pambuyo potaikilidwa mnzawo wa m’cikwati. Kodi mudziŵako wina amene ali na zopinga ngati zimenezi? Ngati n’telo, bwanji osam’pempha kuti pa msonkhano wotsatila mukakhalile naye pamodzi na banja lanu?

18. Kodi tingaiseŵenzetse bwanji 2 Akorinto 6:11-13 pa nkhani ya kuceleza?

18 Cezani nawo. Pamaceza anu, phatikizamponi abale na alongo osiyana-siyana, maka-maka aja amene amasungulumwa. Timafuna ‘kufutukula mitima yathu’ maka-maka kwa anthu otelo. (Ŵelengani 2 Akorinto 6:11-13.) Mlongo Melissa amene tam’gwila mawu kumayambililo ananena kuti: “Nthawi zonse tinali kukondwela mabwenzi akatiitanila kukaceza ku nyumba kwawo pamodzi na mabanja awo, kapena kupita nawo pa maulendo okasangalala.” Kodi mu mpingo mwanu muli wina wake amene mungamuceleze?

19. Ni pa nthawi monga ziti pamene kuceza na Akhristu anzathu kungakhale kothandiza kwambili?

19 Akhristu anzathu angayamikile kwambili kuceza nawo maka-maka pa nthawi zina. Ena cingaŵavute kukhala na acibale awo osakhulupilila pa maholide azikondwelelo. Enanso angakhale acisoni kwambili maka-maka pa masiku ena monga, pa tsiku limene mnzawo wa m’cikwati anamwalila. Tikadzipeleka kuceza na abale na alongo amene ali na zopinga ngati zimenezi, timawaonetsa kuti ‘timasamaladi za iwo.’—Afil. 2:20.

20. Kodi mawu a Yesu a pa Mateyu 12:48-50 angatithandize bwanji tikasungulumwa?

20 Pali zifukwa zambili zimene zingapangitse Mkhristu kusungulumwa nthawi zina. Komabe, tisaiŵale kuti Yehova amadziŵa bwino mmene timamvelela tikasungulumwa. Nthawi zambili amatipatsa zimene timafunikila kupitila mwa Akhristu anzathu. (Ŵelengani Mateyu 12:48-50.) Nafenso timaonetsa ciyamikilo cathu kwa Yehova pa makonzedwe ake acikondi, mwa kucita zonse zotheka pa kucilikiza banja lathu lauzimu. Mosasamala kanthu za mmene timamvelela nthawi zina, sitili tekha, cifukwa Yehova nthawi zonse ali nafe!

NYIMBO 46 Tikuyamikani Yehova

^ ndime 5 Kodi nthawi zina mumasungulumwa? Ngati n’conco, khalani wotsimikiza kuti Yehova amadziŵa mmene mumamvelela, ndipo amafuna kukuthandizani. M’nkhani ino, tikambilane zimene mungacite polimbana na vuto la kusungulumwa. Tiphunzilenso zimene tingacite polimbikitsa alambili anzathu amene amasungulumwa.

^ ndime 5 Maina ena asinthidwa.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale amene mkazi wake anamwalila, akupindula kumvetsela kuŵelengedwa kwa Baibo kojambulidwa, na nkhani imene idzaphunzilidwa.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale na mwana wake wapita kukacezela m’bale wokalamba wa mu mpingo mwawo, ndipo akumucitila zinthu zoonetsa kukoma mtima