Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 25

Inu Akulu—Tengelani Citsanzo ca Gidiyoni

Inu Akulu—Tengelani Citsanzo ca Gidiyoni

“Nthawi indicepela kuti ndipitilize kufotokoza za Gidiyoni.” —AHEB. 11:32.

NYIMBO 124 Tikhale Okhulupilika Nthawi Zonse

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Malinga na 1 Petulo 5:2, kodi akulu ali na udindo wotani?

 AKULU anapatsidwa udindo wosamalila nkhosa za Yehova zamtengo wapatali. Amuna odzipeleka amenewa amayamikila kwambili kutumikila abale na alongo awo. Ndipo pokhala “abusa,” iwo amagwila nchito yawo molimbika. (Yer. 23:4; ŵelengani 1 Petulo 5:2.) Ndife oyamikila cotani nanga kukhala na amuna amenewo pakati pathu!

2. Kodi akulu angakumane na zovuta zotani?

2 Posamalila maudindo awo, akulu amakumana na zovuta zambili. Paja mudziŵa kuti kusamalila mpingo ni nchito yaikulu. M’bale Tony wa ku America, amene ni mkulu, anaona kuti anafunika kukhala wodzicepetsa kwambili kuti akaneko maudindo ena. Iye anati: “Mlili wa COVID-19 utayamba, n’nali na zocita zambili polinganiza misonkhano na ulaliki. Koma sin’nali kukwanitsa kucita zonse ngakhale niyesetse bwanji. Pothela pake n’nalibe nthawi yoŵelenga Baibo, kucita phunzilo la munthu mwini, na kupemphela.” M’bale Ilir wa ku Kosovo, amene nayenso ni mkulu, anali na vuto lina. Ali m’dela la nkhondo, cinamuvuta kutsatila citsogozo ca gulu. Anati: “Kulimba mtima kwanga kunayesedwa ofesi ya nthambi itanipempha kuti nikathandize abale na alongo okhala m’dela loopsa. N’naopa, ndipo n’naona kuti zimenezo n’zosathandiza.” Kwa m’bale Tim, m’mishonale ku Asia, vuto linali kutangwanika na zocita tsiku lililonse moti anali kulephela kucita zina. Anakamba kuti: “Nthawi zina, nimakhala wolema komanso wopanikizika maganizo.” Nanga n’ciyani cingathandize akulu amene amakumana na zovuta ngati zimenezi?

3. Kodi tonsefe tingaphunzile ciyani kwa Woweluza Gidiyoni?

3 Akulu angaphunzile ku citsanzo ca Woweluza Gidiyoni. (Aheb. 6:12; 11:32) Iye anali kuteteza anthu a Mulungu na kuwaweta monga m’busa. (Ower. 2:16; 1 Mbiri 17:6) Monga Gidiyoni, nawonso akulu anaikidwa kuti azisamalila anthu a Mulungu pa nthawi ino yovuta kwambili. (Mac. 20:28; 2 Tim. 3:1) Tingaphunzile zambili kwa Gidiyoni pa nkhani ya kudzicepetsa na kumvela. Kupilila kwake kunayesedwa pocita utumiki wake. Kaya ndife mkulu kapena ayi, tonsefe tingakulitse ciyamikilo cathu pa akulu. Conco, tiziwacilikiza amuna auzimu amenewa cifukwa amaseŵenza mwakhama.—Aheb. 13:17.

KUDZICEPETSA KWANU KUKAYESEDWA

4. Kodi Gidiyoni anaonetsa bwanji kudzicepetsa?

4 Gidiyoni anali munthu wodzicepetsa. b Mngelo wa Mulungu atauza Gidiyoni kuti wasankhidwa kukapulumutsa Aisiraeli m’manja mwa Amidiyani amphamvu, munthu wodzicepetsayu anati: “Banja lathu ndilo laling’ono zedi m’fuko lonse la Manase, ndipo m’nyumba ya bambo anga, wamng’ono kwambili ndine.” (Ower. 6:15) Gidiyoni anadziona wosayenela utumikiwo. Koma Yehova ndiye anali kum’dziŵa bwino. Mwa thandizo la Yehova, iye anakwanilitsa utumiki wake.

5. Kodi kudzicepetsa kwa mkulu kungayesedwe bwanji?

5 Akulu amayesetsa kukhala odzicepetsa m’zinthu zonse. (Mika 6:8; Mac. 20:18, 19) Iwo sadzitama pa zimene amakwanitsa kucita, ndipo sadziona kukhala osayenela cifukwa ca zophophonya zawo. Ngakhale n’telo, kudzicepetsa kwa mkulu kungayesedwe. Mwacitsanzo, mkulu angalandile maudindo oculuka, ndipo zingakhale zovuta kuti awakwanilitse onse. Mwina angalephele kukhala wodzicepetsa anthu akam’tamanda kapena kum’neneza cifukwa ca mmene wacitila zina zake. Kodi akulu angaphunzile ciyani kwa Gidiyoni cimene cingawathandize zaconco zikacitika?

Potengela citsanzo ca Gidiyoni, mkulu wodzicepetsa amapempha thandizo kwa ena, monga polinganiza ulaliki wapoyela (Onani ndime 6)

6. Kodi akulu angaphunzile ciyani kwa Gidiyoni pa nkhani ya kudzicepetsa? (Onaninso cithunzi.)

6 Pemphani thandizo. Munthu wodzicepetsa amadziŵa zimene angakwanitse kucita na zimene sangakwanitse. Gidiyoni anali wodzicepetsa, ndipo anali wofunitsitsa kupempha thandizo kwa ena. (Ower. 6:27, 35; 7:24) Akulu ozindikila amacita cimodzimodzi. M’bale Tony, amene tam’chula uja, anati: “Cifukwa ca mmene n’naleledwela, n’nali kuvomela maudindo ambili kuposa amene nikanakwanitsa kuwasamalila. Conco, n’nasankha kuti tikambilane nkhani ya kudzicepetsa pa kulambila kwa pabanja, na kupempha mkazi wanga kuti anenepo maganizo ake. N’napezanso malangizo othandiza mu vidiyo yakuti, Muziphunzitsa Ena, Kuwakhulupilila, ndi Kuwapatsa Zocita Monga Yesu.” M’bale Tony anayamba kupempha ena kuti azim’thandizila pa maudindo ake. Zotulukapo zake? Mwiniwakeyo anati: “Lomba, nimasamalila bwino nchito za mumpingo, ndipo nili na nthawi yoculuka yolimbitsa ubwenzi wanga na Yehova.”

7. Kodi akulu angatengele bwanji citsanzo ca Gidiyoni akamaimbidwa milandu? (Yakobo 3:13)

7 Muziyankha mofatsa mukamaimbidwa milandu. Kuimbidwa milandu ni ciyeso kwa akulu. Apanso, citsanzo ca Gidiyoni n’cothandiza. Cifukwa codziŵa kuti ni wopanda ungwilo, iye anayankha mofatsa pamene a Efuraimu anamuimba mlandu. (Ower. 8:1-3) Gidiyoni sanayankhe mwaukali. Anaonetsa kudzicepetsa mwa kumvetsela zokamba zawo, ndipo mwaluso anabweza mkwiyo wawo. Akulu anzelu amatengela citsanzo ca Gidiyoni mwa kumvetsela mwachelu, komanso kuyankha mofatsa ena akamawaimba mlandu. (Ŵelengani Yakobo 3:13.) Mwakutelo, iwo amalimbikitsa mtendele mu mpingo.

8. Kodi amuna apaudindo ayenela kucita motani akatamandidwa? Fotokozani citsanzo.

8 Lolani citamando cipite kwa Yehova. Gidiyoni atatamandidwa cifukwa cogonjetsa Amidiyani, anapeleka citamandoco kwa Yehova. (Ower. 8:22, 23) Kodi amuna apaudindo angatengele motani citsanzo ca Gidiyoni? Iwo ayenela kupeleka citamando kwa Yehova pa zimene iwowo akwanitsa kucita. (1 Akor. 4:6, 7) Mwacitsanzo, mkulu akayamikilidwa cifukwa ca luso lake la kuphunzitsa, anganene kuti malangizowo acokela m’Mawu a Mulungu, komanso kuti gulu la Yehova n’limene limatiphunzitsa tonsefe. Akulu ayenela kudziunika kuti aone ngati amaphunzitsa m’njila imene imalemekeza Yehova, kapena ngati akudzifunila ulemelelo. Onani citsanzo ici ca mkulu wina dzina lake Timothy. Atangokhala mkulu, anali kukonda kukamba nkhani za anthu onse. Iye anati: “N’nali kukonza mawu oyamba aatali komanso mafanizo ogometsa. Ndipo anthu anali kuniyamikila kwambili. Iwo anayamba kutamanda ine m’malo motamanda Yehova kapena Mawu ake Baibo.” M’kupita kwa nthawi, m’bale Timothy anaona kuti afunika kusintha kaphunzitsidwe kake, kuti apewe kudzifunila ulemelelo. (Miy. 27:21) Kodi panakhala zotulukapo zotani? Iye anati: “Abale na alongo amaniuza mmene nkhani yanga yawathandizila kugonjetsa vuto linalake, kulipilila, kapena kumuyandikila kwambili Yehova. Nikamva ndemangazo, nimakhala wacimwemwe kwambili kuposa cimene n’nali kukhala naco zaka zakumbuyoku anthu akanitamanda.”

KUMVELA KAPENA KULIMBA MTIMA KWANU KUKAYESEDWA

Gidiyoni anamvela pocepetsa ciŵelengelo ca asilikali mwa kusankha amuna 300 amene anaonetsa kuti ni ogalamuka (Onani ndime 9)

9. Kodi kumvela kwa Gidiyoni na kulimba mtima kwake kunayesedwa motani? (Onani cithunzi pacikuto.)

9 Gidiyoni atasankhidwa kukhala woweluza, kumvela na kulimba mtima kwake kunayesedwa. Iye anapatsidwa utumiki wovuta kwambili wakuti akawononge guwa lansembe limene atate ake anali kulambililapo Baala. (Ower. 6:25, 26) Pa nthawi ina, Gidiyoni anasonkhanitsa gulu la asilikali, koma kaŵili konse anauzidwa kuti acepetse ciŵelengelo ca asilikaliwo. (Ower. 7:2-7) Pothela pake, anauzidwa kuti akaukile msasa wa adani pakati pa usiku.—Ower. 7:9-11.

10. Kodi mkulu angayesedwe bwanji pa nkhani ya kumvela?

10 Akulu ayenela kukhala ‘okonzeka kumvela.’ (Yak. 3:17) Mkulu womvela amagonjela mosavuta zimene Malemba amakamba, komanso malangizo a gulu la Mulungu. Mwakutelo, amapeleka citsanzo cabwino kwa ena. Ngakhale n’telo, kumvela kwake kungayesedwe. Mwacitsanzo, malangizo akabwela oculuka m’kanthawi kocepa, cingamuvute kuwatsatila. Nthawi zina, angakayikile ngati malangizo ena alidi othandiza. Kapena angapemphedwe kuti agwile nchito inayake imene ingacititse kuti amangidwe. Kodi akulu angatengele bwanji Gidiyoni pa nkhani ya kumvela ngati zaconco zawacitikila?

11. N’ciyani cingathandize akulu kukhala omvela?

11 Mvetselani malangizo mosamala na kuwatsatila. Mulungu anauza Gidiyoni mowonongela guwa lansembe la atate ake, malo omangilako guwa lansembe la Yehova, komanso nyama yokapeleka nsembe. Gidiyoni sanakayikile malangizowo, anangowatsatila. Lelolino, akulu amalandila malangizo a gulu la Yehova kudzela m’makalata, zilengezo, na zitsogozo zina, kuti tikhale otetezeka kuuzimu na kuthupi. Timawakonda akulu cifukwa amatsatila mokhulupilika malangizo a gulu. Ndipo mpingo umapindula.—Sal. 119:112.

12. Kodi akulu angaseŵenzetse bwanji Aheberi 13:17 pakakhala masinthidwe a gulu?

12 Khalani okonzeka kusintha. Kumbukilani kuti atauzidwa na Yehova, Gidiyoni anacepetsa ciŵelengelo ca asilikali mpaka kukhala na ocepa kwambili. (Ower. 7:8) Mwina anadzifunsa kuti, ‘Kodi masinthidwewa ni ofunikiladi? Kodi adzathandizadi?’ Mulimonsemo, Gidiyoni anatsatila zimenezo. Masiku ano, akulu amatengela Gidiyoni mwa kutsatila masinthidwe alionse a gulu. (Ŵelengani Aheberi 13:17.) Mwacitsanzo, mu 2014, Bungwe Lolamulila linasintha mopelekela ndalama zothandiza kumanga Nyumba za Ufumu komanso ma Bwalo a Msonkhano. (2 Akor. 8:12-14) Mipingo inaleka kukhala na nkhongole ya Nyumba za Ufumu. M’malo mwake, gulu limaseŵenzetsa zopeleka zocokela ku mipingo padziko lonse kuti zithandize pa zimango kulikonse kumene zingafunikile, kaya mpingowo uli na ndalama zotani. M’bale José atamva za masinthidwewo, anakayikila ngati zimenezo zingagwile nchito, ndipo mumtima anati: ‘Ngakhale Nyumba ya Ufumu imodzi singamangidwe. Umu si mmene zinthu zimacitikila m’dzikoli.’ N’ciyani cinathandiza José kucilikiza masinthidwewo? Mwiniwakeyo anati: “Mawu a pa Miyambo 3:5,6 ananikumbutsa kuti niyenela kukhulupilila Yehova. Ndipo pakhala zotulukapo zabwino. Nyumba za Ufumu zambili zikumangidwa, ndipo taphunzila kupanga zopeleka m’njila zosiyanasiyana kuti pakhale kufanana.”

Ngakhale pamene nchito yathu ni yotsekedwa, molimba mtima tingathe kulalikila (Onani ndime 13)

13. (a) Kodi Gidiyoni anali wotsimikiza za ciyani? (b) Kodi akulu angatengele bwanji citsanzo ca Gidiyoni? (Onaninso cithunzi.)

13 Citani cifunilo ca Yehova molimba mtima. Olo kuti Gidiyoni anali na mantha komanso anaika moyo wake pa ciwopsezo, iye anamvelabe Yehova. (Ower. 9:17) Atalandila citsimikizo kwa Yehova, anakhala na cidalilo conse kuti adzam’thandiza kuteteza anthu ake. Akulu okhala m’madela mmene nchito yathu ni yoletsedwa amatengela citsanzo ca Gidiyoni. Molimba mtima, iwo amakhala patsogolo kupezeka ku misonkhano na mu ulaliki, mosasamala kanthu za kuopsezedwa kuti adzamangidwa, kufunsidwa mafunso, kucotsedwa nchito, kapena kucitidwa ciwawa. c Pa cisautso cacikulu, akulu adzafunika kukhala olimba mtima kuti akatsatile malangizo amene adzalandila, ngakhale kuti kucita zimenezo kungadzaike moyo wawo pa ciwopsezo. Malangizowo angadzakhale okhudza mmene tingalengezele uthenga wa matalala ophipilitsa, komanso mmene tingapulumukile Gogi wa Magogi akadzatiukila.—Ezek. 38:18; Chiv. 16:21

KUPILILA KWANU KUKAYESEDWA

14. Kodi kupilila kwa Gidiyoni kunayesedwa motani?

14 Utumiki wa Gidiyoni monga woweluza unafuna kulimbika. Pamene Amidiyani anathaŵa usiku pa nkhondo, Gidiyoni anawathamangitsa kucokela ku Cigwa ca Yezereeli, mpaka ku Mtsinje wa Yorodano. N’kutheka kuti delalo linali lozungulidwa na chile. (Ower. 7:22) Ngakhale kuti Gidiyoni na asilikali ake 300 anali otopa, anawolokabe Yorodano na kupitiliza kuthamangitsa adani awo. Pothela pake, iwo anawapeza Amidiyani na kuwagonjetsa.—Ower. 8:4-12.

15. Kodi kupilila kwa mkulu kungayesedwe motani?

15 Nthawi zina, mkulu angatope kwambili cifukwa cosamalila maudindo mumpingo, komanso banja lake. Zikakhala conco, kodi akulu angatengele bwanji citsanzo ca Gidiyoni?

Akulu acikondi alimbikitsapo anthu ambili ofunikila thandizo (Onani ndime 16-17)

16-17. N’ciyani cinathandiza Gidiyoni kupilila? Nanga akulu ayenela kukhala na cidalilo cotani? (Yesaya 40:28-31) (Onaninso cithunzi.)

16 Khalani na cidalilo cakuti Yehova adzakulimbitsani. Gidiyoni anali na cidalilo cakuti Yehova adzam’limbitsa, ndipo sanagwilitsidwe mwala. (Ower. 6:14, 34) Iye na asilikali ake anathamangitsa mafumu aŵili acimidiyani wapansi, pamene mwina mafumuwo anali atakwela pa ngamila. (Ower. 8:12, 21) Koma mwa thandizo la Yehova, anagwila mafumuwo ndipo anapambana nkhondoyo. Mofananamo, akulu ayenela kudalila Yehova amene “satopa kapena kufooka.” Iye adzawapatsa mphamvu pamene zikufunikila.—Ŵelengani Yesaya 40:28-31.

17 Onani cocitika ici ca mbale Matthew, wa m’Komiti Yokambilana ndi Acipatala. N’ciyani cimam’thandiza kupilila? Iye anati: “Naona kukwanilitsidwa kwa Afilipi 4:13 pa ine. Nikakhala wotopa moti nilibenso mphamvu, nimapemphela kwambili kwa Mulungu, kum’condelela kuti anipatse mphamvu zofunikila kuti nithandize abale anga. Nikatelo, nimacita kumva kuti mzimu wa Yehova wanipatsa mphamvu kuti nipilile.” Monga Gidiyoni, akulu athu odzipeleka angakumane na zovuta pamene akuweta nkhosa. Motelo, ayenela kukhala odzicepetsa, komanso kuzindikila kuti sangakwanitse kucita zonse zimene akufuna. Ngakhale n’conco, ayenelanso kukhala na cidalilo cakuti Yehova amamva mapemphelo awo, ndipo adzawathandiza kupilila.—Sal. 116:1; Afil. 2:13.

18. Malinga na zimene takambilana, kodi akulu angatengele motani citsanzo ca Gidiyoni?

18 Akulu angaphunzile zambili pa citsanzo ca Gidiyoni. Iwo ayenela kuonetsa kudzicepetsa akapatsidwa maudindo ena, akatamandidwa kapena kuimbidwa milandu. Cina, ayenela kukhala omvela komanso olimba mtima, maka-maka pamene mapeto a dzikoli akuyandikila. Ndipo ayenelanso kukhala na cidalilo cakuti Mulungu adzawalimbitsa zivute zitani. Zoonadi, timawayamikila kwambili abusa ogwila nchito mwakhama amenewa, ndipo ‘tiziwalemekeza kwambili.’—Afil. 2:29.

NYIMBO 120 Tengelani Kufatsa kwa Khristu

a Yehova anasankha Gidiyoni kuti atsogolele na kuteteza anthu a Mulungu panthawi yovuta kwambili m’mbili ya Aisiraeli. Gidiyoni anagwila nchitoyi mokhulupilika kwa zaka ngati 40. Ngakhale n’telo, anakumanabe na zovuta. M’nkhani ino, tikambilane mmene citsanzo cake cingathandizile akulu akakumana na mayeso.

b Ngati ndife odzicepetsa, timapewa kuganizila kwambili za ife eni, ndipo timavomeleza kuti pali nchito zina zimene sitingakwanitse kucita. Kuwonjezela apo, timalemekeza ena na kuwaona kukhala otiposa.—Afil. 2:3.

c Onani nkhani yakuti, “Musaleke Kulambila Yehova pa Nthawi ya Ciletso.” Nkhaniyi ili mu Nsanja ya Mlonda ya July 2019, masa. 10-11, ndime 10-13.