Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 26

Khalanibe Okonzeka Tsiku la Yehova

Khalanibe Okonzeka Tsiku la Yehova

“Tsiku la Yehova lidzabwela ndendende ngati mbala usiku.” —1 ATES. 5:2.

NYIMBO 143 Musaleke Kugwila Nchito, Kuyang’anila, na Kuyembekezela

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Tiyenela kucita ciyani kuti tikapulumuke tsiku la Yehova?

 M’BAIBO, mawu akuti “tsiku la Yehova” amakamba za nthawi pamene Yehova adzawononga adani ake na kupulumutsa anthu ake. Kalelo, Yehova anaonetsapo zakuda mitundu ina. (Yes. 13:1, 6; Ezek. 13:5; Zef. 1:8) M’masiku athu ano, “tsiku la Yehova” lidzayamba na kuukilidwa kwa Babulo Wamkulu, ndipo lidzatha na nkhondo ya Aramagedo. Kuti tikapulumuke pa ‘tsikulo,’ tiyenela kukonzekela palipano. Yesu anati “khalani okonzeka” kaamba ka “cisautso cacikulu.” Izi zitanthauza kuti tiyenela kukhalabe okonzeka.—Mat. 24:21; Luka 12:40.

2. Kodi buku la 1 Atesalonika limatithandiza bwanji?

2 M’kalata yake yoyamba youzilidwa yopita kwa Atesalonika, mtumwi Paulo anagwilitsa nchito mafanizo angapo pothandiza Akhristu kukhalabe okonzeka tsiku lalikulu la Yehova laciweluzo. Paulo anadziŵa kuti tsiku la Yehova silidzafika panthawi imeneyo. (2 Ates. 2:1-3) Ngakhale n’telo, iye analimbikitsa Akhristu anzake kukonzekela tsikulo ngati kuti lidzabwela maŵa. Nafenso tiyenela kuseŵenzetsa uphungu umenewo. Tiyeni tsopano tikambilane mmene anafotokozela zinthu zotsatilazi: (1) mmene tsiku la Yehova lidzafikila, (2) amene sadzapulumuka tsikulo, komanso (3) zimene tingacite kuti tikapumuluke.

KODI TSIKU LA YEHOVA LIDZABWELA MOTANI?

Polemba 1 Atesalonika, mtumwi Paulo anagwilitsa nchito mafanizo amene tingapindule nawo (Onani ndime 3)

3. Kodi tsiku la Yehova lidzabwela ngati mbala motani? (Onaninso cithunzi.)

3 “Ngati mbala usiku.” (1 Ates. 5:2) Ili ni fanizo loyamba pa mafanizo atatu ofotokoza mmene tsiku la Yehova lidzabwelela. Mbala zimafika modzidzimutsa usiku, pamene anthu sakuziyembekezela. Nalonso tsiku la Yehova lidzafika modzidzimutsa, pamene anthu sakuliyembekezela. Ngakhale Akhristu oona angadzadabwe na mmene zinthu zidzasinthila mwadzidzidzi. Koma mosiyana na anthu oipa, ife sitidzawonongedwa.

4. Ni motani mmene tsiku la Yehova lilili monga zoŵaŵa za pobeleka?

4 “Monga zoŵaŵa za pobeleka za mkazi wapakati.” (1 Ates. 5:3) Mayi woyembekezela sangadziŵiletu nthawi yeniyeni imene adzabeleka. Koma amakhala wotsimikiza kuti adzabelekabe. Ndipo nthawiyo imafika mwadzidzidzi, imakhala yoŵaŵa, komanso yosapeweka. Mofananamo, sitidziŵa tsiku na ola limene tsiku la Yehova lidzayamba. Ngakhale n’telo, ndife otsimikiza kuti lidzabweladi, komanso kuti ciweluzo ca Mulungu pa anthu oipa cidzafika mwadzidzidzi, ndipo n’cosapeweka.

5. Ni motani mmene cisautso cacikulu cilili ngati mbandakuca?

5 Ngati mbandakuca. Mawu ofanizila acitatu a Paulo amenewa, akukambanso za mbala zimene zimaba usiku. Koma apa, zikuoneka kuti iye akuyelekezela tsiku la Yehova na mbandakuca. (1 Ates. 5:4) Mbala zimene zikuba usiku zingakhale zotangwanika moti sizingazindikile kuti kwayamba kuca. Kuwala kwa tsiku kungazifikile modzidzimutsa, n’kuvumbula umbava wawo. Mofananamo, cisautso cacikulu cidzavumbula aja amene monga mbala, amakhalabe mumdima n’kumacita zinthu zosakondweletsa Mulungu. Mosiyana na iwo, tiyenela kukhala okonzeka mwa kupewa makhalidwe amene Yehova amadana nawo. M’malo mwake, tizicita “ciliconse cabwino, colungama, ndi coona.” (Aef. 5:8-12) Paulo anaseŵenzetsanso mafanizo aŵili ofanana pofotokoza za anthu omwe sadzapulumuka.

AMENE SADZAPULUMUKA TSIKU LA YEHOVA

6. Kodi anthu ambili ali mtulo m’lingalilo lotani? (1 Atesalonika 5:6, 7)

6 “Ogona.” (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:6, 7.) Paulo anayelekezela anthu amene sadzapulumuka tsiku la Yehova na anthu amene ali mtulo. Iwo sadziŵa zimene zikucitika kapena mmene nthawi ikupitila. Conco, saona zocitika zikulu-zikulu zimene zikucitika ndipo sacitapo kanthu. Anthu ambili masiku ano ali m’tulo twauzimu. (Aroma 11:8) Iwo sakhulupilila maumboni oonetsa kuti tikukhala “m’masiku otsiliza,” komanso kuti cisautso cacikulu cifika posacedwa. Zocitika zikulu-zikulu padzikoli zingadzutse ena ku tulo twawo twauzimu, na kuwasonkhezela kumvetsela uthenga wabwino wa Ufumu. Koma ambili amagonanso mwauzimu m’malo mokhalabe maso. Ngakhale aja amene amakhulupilila tsiku laciweluzo la Yehova amaganiza kuti tsikulo likali kutali. (2 Pet. 3:3, 4) Komabe, tsiku lililonse likamadutsa, m’pofunika kwambili kutsatila uphungu wouzilidwa wakuti tikhalebe maso.

7. Kodi amene adzawonongedwa na Mulungu ali ngati anthu oledzela m’lingalilo lotani?

7 “Amene amaledzela.” Mtumwi Paulo anayelekezela aja amene adzawonongedwa na anthu oledzela. Anthu oledzela amacedwa kucitapo kanthu pa zimene zikucitika, ndipo amalephela kupanga zisankho zanzelu. Mofananamo, anthu oipa sacitapo kanthu pa macenjezo a Mulungu. Amasankha njila imene imawatsogolela ku ciwonongeko. Koma Akhristu amalimbikitsidwa kukhala oganiza bwino. (1 Ates. 5:6) Katswili wina wa Baibo, anati kuganiza bwino kumeneku ndiko “kukhala na maganizo odekha komanso osasunthika, osinkhasinkha bwino zinthu, ndipo maganizowo amathandiza munthu kupanga zisankho zabwino.” N’cifukwa ciyani tiyenela kukhala odekha komanso osasunthika? Kuti tisatengeke na zandale kapena zocitika zina za m’dzikoli. Pamene tsiku la Yehova likuyandikila, tingakakamizike kwambili kutengako mbali m’zinthu zimenezi. Koma sitiyenela kuda nkhawa na mmene tikacitile. Pa nthawiyo, mzimu wa Mulungu udzatithandiza kukhala odekha komanso osasunthika, kuti tipange zisankho zabwino.—Luka 12:11, 12.

ZIMENE TINGACITE KUTI TIKAPULUMUKE TSIKU LA YEHOVA

Anthu ambili amanyalanyaza kubwela kwa tsiku la Yehova. Koma ife timakhalabe okonzeka mwa kuvala codzitetezela pacifuwa cacikhulupililo na cikondi, komanso cisoti cimene n’ciyembekezo (Onani ndime 8, 12)

8. Malinga na 1 Atesalonika 5:8, n’ziti zingatithandize kukhalabe maso komanso oganiza bwino? (Onaninso cithunzi.)

8 “Tivale codzitetezela pacifuwa . . . ndi . . . cisoti.” Paulo anatiyelekezela na asilikali amene ali chelu komanso okonzeka kumenya nkhondo. (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:8.) Msilikali amene ali pa nchito amakhala wokonzeka nthawi iliyonse kumenya nkhondo. Nafenso n’cimodzimodzi. Timakhalabe okonzeka tsiku la Yehova mwa kuvala codzitetezela pacifuwa cacikhulupililo na cikondi, komanso cisoti cimene n’ciyembekezo. Zinthu zimenezi n’zothandiza kwambili.

9. Kodi cikhulupililo cimatiteteza motani?

9 Codzitetezela pacifuwa cinali kuteteza mtima wa msilikali. Mofananamo, cikhulupililo na cikondi zimateteza mtima wathu wophiphilitsa. Zimatithandiza kupitiliza kutumikila Mulungu na kutsatila Yesu. Cikhulupililo cimatitsimikizila kuti Yehova amapeleka mphoto kwa anthu omufuna-funa na mtima wonse. (Aheb. 11:6) Ndipo cimatilimbikitsa kukhalabe okhulupilika kwa Mtsogoleli wathu Yesu, ngakhale tikumane na mavuto. Cikhulupililo cathu cimeneco tingacilimbitse mwa kuphunzila ku zitsanzo zamakono za anthu amene akhalabe okhulupilika, mosasamala kanthu za mazunzo kapena mavuto azacuma. Ndipo tingapewe msampha wokonda zinthu zakuthupi mwa kutengela aja amene anasankha kukhala umoyo wosalila zambili kuti aike zinthu za Ufumu patsogolo. b

10. Kodi kukonda Mulungu komanso anthu kumatithandiza bwanji kupilila?

10 Cikondi naconso n’cofunika kwambili kuti tikhalebe maso komanso oganiza bwino. (Mat. 22:37-39) Kukonda Mulungu kumatithandiza kupilila mavuto amene tingakumane nawo tikamalalikila. (2 Tim. 1:7, 8) Popeza timakondanso anthu amene satumikila Mulungu, timapitilizabe kulalikila m’gawo, komanso kulalikila pafoni na m’makalata. Timakhala na ciyembekezo cakuti tsiku lina, iwo adzasintha umoyo wawo na kuyamba kucita zabwino.—Ezek. 18:27, 28.

11. Kodi kukonda Akhristu anzathu kumatithandiza bwanji? (1 Atesalonika 5:11)

11 Timakondanso Akhristu anzathu. Ndipo timaonetsana cikondi cimeneco mwa “kutonthozana ndi kulimbikitsana.” (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:11.) Monga asilikali amene amaseŵenzela pamodzi pa nkhondo, timalimbikitsana. N’zoona kuti nthawi zina msilikali angavulaze msilikali wa kumbali yake mwangozi nkhondo ili mkati. Koma sangacite zimenezo mwadala. Mofananamo, sitingakhumudwitse abale na alongo athu mwadala, kapena kubwezela coipa pa coipa. (1 Ates. 5:13, 15) Timaonetsanso cikondi cathu polemekeza abale amene akutsogolela mu mpingo. (1 Ates. 5:12) Pamene mtumwi Paulo analemba kalatayi, mpingo wa Tesalonika unali usanakwanitse caka. N’kutheka kuti amuna apaudindo mumpingowo anali acatsopano, ndipo anali kulakwitsa zina. Ngakhale n’telo, anayenela kulemekezedwa. Pamene cisautso cacikulu cikuyandikila, tidzafunika kudalila kwambili citsogozo ca akulu kuposa kale lonse. Nthawi zina sizingatheke kulandila malangizo ocokela ku likulu lathu kapena ku ofesi ya nthambi. Conco, m’pofunika kwambili palipano kuphunzila kuwakonda akulu na kuwalemekeza. Kaya pacitike zotani, tiyeni tikhalebe oganiza bwino, na kupewa kuyang’ana zophophonya zawo. M’malo mwake, tiziika maganizo athu pa mfundo yakuti Yehova kudzela mwa Khristu, akutsogolela amuna okhulupilika amenewa.

12. Kodi ciyembekezo cimateteza bwanji maganizo athu?

12 Monga mmene cisoti cimatetezela mutu wa msilikali, naconso ciyembekezo cathu cacipulumutso cimateteza maganizo athu. Tikakhala na ciyembekezo colimba, timaona kuti zimene dzikoli limapeleka n’zopanda phindu. (Afil. 3:8) Cimatithandizanso kukhala odekha komanso osasunthika. Citsanzo ni m’bale Wallace na mkazi wake Laurinda, amene akutumikila mu Africa. M’milungu itatu, aliyense wa iwo anataikilidwa kholo mu imfa. Cifukwa ca mlili wa COVID-19, cinali covuta kubwelela kwawo kuti akalile nawo malilo. M’bale Wallace anati: “Ciyembekezo ca ciukitso cimanithandiza kuganizila mmene iwo adzakhalile m’dziko latsopano akadzaukitsidwa, osati mmene analili atatsala pang’ono kumwalila. Cimanithandizanso kumvako bwino nikakhala na cisoni.”

13. Kodi tingatani kuti tilandile mzimu woyela?

13 “Musazimitse moto wa mzimu.” (1 Ates. 5:19) Paulo anayelekezela mzimu woyela na moto. Tikakhala na mzimu wa Mulungu, timakhala acangu, ofunitsitsa kucita zoyenela, komanso kutumikila Yehova. (Aroma 12:11) Kodi tingatani kuti tilandile mzimu woyela? Mwa kuupempha, kuŵelenga Mawu a Mulungu ouzilidwa, komanso kugwilizana na gulu limene amalitsogolela na mzimu wake. Tikatelo, timakhala na “makhalidwe amene mzimu woyela umatulutsa.”—Agal. 5:22 23.

Dzifunseni kuti, ‘Kodi zocita zanga zimaonetsa kuti nimafuna kuti Mulungu apitilize kunipatsa mzimu wake?’ (Onani ndime 14)

14. Kodi tiyenela kupewa ciyani kuti tipitilize kulandila mzimu wa Mulungu? (Onaninso cithunzi.)

14 Mulungu akatipatsa mzimu wake woyela, tiyenela kukhala osamala kuti ‘tisazimitse moto wa mzimuwo.’ Mulungu amapatsa mzimu wake anthu okhawo oganiza bwino, komanso a khalidwe loyela. Iye sangapitilize kutipatsa mzimu woyela ngati tikhalabe na maganizo oipa. (1 Ates. 4:7, 8) Kuti tizilandilabe mzimu woyela, tiyenela kupewa ‘kunyoza mawu aulosi.’ (1 Ates. 5:20) Pa lembali, liwu lakuti ‘ulosi’ litanthauza mauthenga ouzilidwa na mzimu wa Mulungu. Aphatikizapo onena za tsiku la Yehova komanso masiku athu ano. Sitikankhila tsikulo kutsogolo, poganiza kuti Aramagedo sidzabwela pamene tili moyo. M’malo mwake, nthawi zonse timakhala ngati kuti tsikulo libwela maŵa, mwa kukhalabe na makhalidwe abwino, komanso kutangwanika na ‘nchito zosonyeza kuti ndife odzipeleka kwa Mulungu.’—2 Pet. 3:11, 12.

“TSIMIKIZILANI ZINTHU ZONSE”

15. Kodi tingapewe bwanji kuputsitsidwa na mauthenga abodza a ziŵanda? (1 Atesalonika 5:21)

15 Posacedwa, adani a Mulungu adzalengeza kuti: “Bata ndi mtendele!” (1 Ates. 5:3) Mauthenga ouzilidwa na ziŵanda adzafalikila paliponse, na kusocoletsa anthu ambili. (Chiv. 16:13, 14) Koma ife mauthengawo sadzatiputsitsa ngati ‘timatsimikizila zinthu zonse.’ (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:21.) Liwu la Cigiriki limene analimasulila kuti “tsimikizilani,” analigwilitsa nchito pofotokoza mmene anthu amayesela miyala yamtengo wapatali kuti adziŵe ngati ni yeniyeni. Conco, tiyenela kuyesa kapena kuti kutsimikizila zimene timamva kapena kuŵelenga, kuti tidziŵe ngati n’zenizeni. Kucita zimenezi kunali kofunika kwambili kwa Atesalonika, ndipo kudzakhala kofunika ngako kwa ife pamene cisautso cacikulu cikuyandikila. M’malo mokhulupilila m’cimbulimbuli zimene ena amakamba, timagwilitsa nchito luso la kuzindikila kuti tiyelekezele ngati zimene timaŵelenga komanso kumva, n’zogwilizana na zimene Baibo ndiponso gulu la Yehova limakamba. Tikatelo, sitidzaputsitsidwa na mauthenga abodza a ziŵanda.—Miy. 14:15; 1 Tim. 4:1.

16. Kodi ndife otsimikiza za ciyani? Nanga tidzayesetsa kucita ciyani?

16 Monga gulu, atumiki a Mulungu adzapulumuka cisautso cacikulu. Koma aliyense payekha amadziŵa kuti cakudza siciimba ng’oma. (Yak. 4:14) Kaya tidzapyola amoyo cisautso cacikulu kapena tidzamwalila cisanafike, tidzalandila mphoto ya moyo wosatha tikakhalabe okhulupilika. Odzozedwa adzakhala na Khristu kumwamba. Koma a nkhosa zina adzakhala m’paradaiso padziko lapansi. Conco, tiyeni tonse tiziganizila kwambili za ciyembekezo cathu cimeneci, ndipo tikhalebe okonzeka tsiku la Yehova.

NYIMBO 150 Funani Cipulumutso ca Mulungu

a Mu 1 Atesalonika caputala 5 muli mafanizo angapo otiphunzitsa za tsiku la Yehova la kutsogolo. Kodi “tsiku” limenelo n’ciyani? Nanga lidzafika motani? Ndani adzapulumuke pa tsikulo? Nanga ndani amene sadzapulumuka? Kodi tingalikonzekele bwanji? Tipeza mayankho pa mafunsowa pokambilana mawu a mtumwi Paulo.

b Onani nkhani zakuti “Anadzipeleka na Mtima Wonse.”