Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Yesu atabadwa, n’cifukwa ciyani Yosefe na Mariya anakhalabe ku Betelehemu m’malo mobwelela kwawo ku Nazareti?

Baibo siikambapo ciliconse. Koma imafotokoza mbali zina zocititsa cidwi zimene mwina zinapangitsa kuti asabwelele ku Nazareti pa nthawiyo.

Mngelo anauza Mariya kuti adzakhala na pakati n’kubeleka mwana. Pamene uthengawu unafika, Mariya na Yosefe anali kukhala ku Galileya m’tauni ya Nazareti, kwawo kwa Yosefe. (Luka 1:26-31; 2:4) Patapita nthawi, iwo atabwelako ku Iguputo m’pamene anabwelela ku Nazareti. Yesu anakulila kumeneko, ndipo anakhala Mnazareti. (Mat. 2:19-23) N’cifukwa cake tikamakamba za Yesu, Yosefe, komanso Mariya, timaganizila za Nazareti.

Mariya anali na wacibale dzina lake Elizabeti amene anali kukhala ku Yuda. Elizabeti anali mkazi wa wansembe Zekariya, ndipo anakhala mayi wa Yohane M’batizi. (Luka 1:5, 9, 13, 36) Tsiku lina, Mariya anapita ku Yuda kukacezela Elizabeti, ndipo anakhalako miyezi itatu. Kenako, iye anabwelela ku Nazareti. (Luka 1:39, 40, 56) Conco, Mariya anali kulidziŵa bwino dela la Yuda.

Patapita nthawi, Yosefe anacoka ku Nazareti kupita ku Betelehemu “kumzinda wa Davide,” pomvela lamulo lakuti aliyense ‘akalembetse’ ku “mzinda wakwawo.” Betelehemu unali mzinda umene munali kudzabadwila Mesiya, malinga na ulosi. (Luka 2:3, 4; 1 Sam. 17:15; 20:6; Mika. 5:2) Pambuyo pakuti Mariya wabeleka Yesu, Yosefe sanafune kuti apange ulendo wautali wobwelela ku Nazareti na mwana wawo wakhanda. Iwo anakhalabe ku Betelehemu komweko, umene unali pa mtunda wa makilomita ngati 9 kucokela ku Yerusalemu. Conco, cinali cosavuta kupita na mwana wawo wakhanda ku kacisi kuti akapeleke nsembe.—Lev. 12:2, 6-8; Luka 2:22-24.

Mngelo wa Mulungu anali atauza Mariya kuti mwana wake adzam’patsa “mpando wacifumu wa Davide, komanso kuti “adzalamulila monga Mfumu.” Kodi n’kutheka kuti Yosefe na Mariya anaona kuti n’kofunika kwambili kuti Yesu akabadwile ku mzinda wa Davide? (Luka 1:32, 33; 2:11, 17) Mwina iwo anaona kuti ni bwino kukhalabe komweko, poyembekezela kuti Mulungu awauze zotsatila zofunika kucita.

Sitidziŵa kuti ku Betelehemu anakhalako nthawi yaitali motani openda nyenyezi asanafike. Komabe, pa nthawiyo iwo anali kukhala m’nyumba, ndipo mwana wawoyo sanalinso khanda ayi. (Mat. 2:11) Cioneka kuti m’malo mobwelela ku Nazareti, iwo anakhalabe ku Betelehemu kwa nthawi yaitali ndithu.

Herode analamula kuti “ana onse aamuna m’Betelehemu . . . kuyambila azaka ziŵili kutsika m’munsi,” aphedwe. (Mat. 2:16) Mngelo wa Mulungu atauza Yosefe za lamulo la mfumu limenelo, iye na Mariya pamodzi na Yesu anathaŵila ku Iguputo. Anakhalabe kumeneko mpaka Herode atamwalila. Patapita nthawi, Yosefe anatenga banja lake kupita nalo ku Nazareti. Koma iwo sanabwelele ku Betelehemu. Cifukwa ciyani? Pofuna kupewa Arikelao wopondeleza—mwana wa Herode—amene anali kukhala ku Yudeya, komanso pofuna kumvela cenjezo la Mulungu. Ku Nazareti n’kumene Yosefe akanalelela Yesu motetezeka kuti akhale mtumiki woona wa Mulungu.—Mat. 2:19-22; 13:55; Luka 2:39, 52.

Zioneka kuti Yosefe anamwalila Yesu asanatsegule khomo la moyo wakumwamba. Conco, Yosefe adzaukitsidwa n’kukhala na moyo pano padziko lapansi. Iye adzatifotokozela zambili zokhudza cifukwa cake anasankha kukhalabe ku Betelehemu Yesu atabadwa.