NKHANI YOPHUNZILA 27
N’cifukwa Ciyani Tiyenela Kumuopa Yehova?
“Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa.”—SAL. 25:14.
NYIMBO 8 Yehova Ndiye Pothaŵila Pathu
ZIMENE TIKAMBILANE a
1-2. Malinga na Salimo 25:14, kodi tingacite ciyani kuti tikhale pa ubwenzi wathithithi na Yehova?
KODI ni makhalidwe ati amene mumaona kuti ni ofunika kwambili kuti mukhalebe pa ubwenzi wathithithi na anthu ena? Mwina mungayankhe kuti mabwenzi abwino amakondana, komanso kuthandizana. N’kutheka kuti simunaganizileko za mantha kukhala khalidwe lofunika popalana ubwenzi wabwino na ena. Komabe, malinga na lemba la mfundo yaikulu ya nkhani ino, aja amene afuna kukhala pa ubwenzi wolimba na Yehova ayenela ‘kumuopa.’—Ŵelengani Salimo 25:14.
2 Kaya tatumikila Yehova kwa utali wotani, tonsefe tiyenela kupitilizabe kumuopa kwambili. Koma kodi kuopa Mulungu kumatanthauzanji? Nanga tingaphunzile bwanji kumuopa? Kodi tingaphunzile ciyani kwa mtumiki Obadiya, mkulu wa ansembe Yehoyada, na mfumu Yehoasi pa nkhani yoopa Mulungu?
KODI KUOPA MULUNGU KUMATANTHAUZANJI?
3. Fotokozani mmene mantha amatitetezela.
3 Tingacite mantha ngati taona kuti tingadzakumane na zinthu zimene zingativulaze. Mantha otelo ali bwino cifukwa amatithandiza kupanga zisankho zanzelu. Mwacitsanzo, tikamayenda mu msewu umene m’mbali mwake muli cidzenje, timapewa kuyenda m’mbali mwenimweni kuopela kuti tingagwelemo. Mantha oopa kuvulala amatilimbikitsa kuthaŵa zoopsa. Ndipo mantha oopa kuwononga ubwenzi wathu na munthu wina, amatithandiza kupewa kulankhula kapena kucita zinthu zosayenela.
4. Kodi Satana amafuna tikhale na mantha otani kwa Yehova?
4 Satana amafuna kuti anthu aziopa Yehova mosayenela. Iye amalimbikitsa maganizo amene Elifazi anali nawo, akuti Yehova sakhululuka, ndipo ni wamkali moti n’zosatheka kum’kondweletsa. (Yobu 4:18, 19) Satana amafuna kuti tizicita naye mantha Yehova kuti tileke kum’tumikila. Kuti tipewe msampha umenewo, tiyenela kukhala na mantha oyenela oopa Mulungu.
5. Kodi kuopa Mulungu kumatanthauzanji?
5 Munthu amene ali na mantha oyenela amakonda Mulungu, ndipo sangacite ciliconse cimene cingawononge ubwenzi wake na iye. Yesu anali na mantha otelo aumulungu. (Aheb. 5:7) Iye sanali kuopa Yehova mopambanitsa. (Yes. 11:2, 3) M’malo mwake, anali kum’konda kwambili ndiponso anali kumumvela. (Yoh. 14:21,b31) Monga Yesu, nafenso timam’lemekeza kwambili Yehova cifukwa amatikonda, ni wanzelu, wacilungamo, komanso wamphamvu. Cina, timadziŵa kuti Yehova amasamala kwambili za ife, komanso kuti amakhudzika mtima akaona mmene timacitila zinthu pambuyo potiphunzitsa. Zocita zathu zingam’kondweletse Yehova kapena kum’pweteka mtima.—Sal. 78:41; Miy. 27:11.
TINGAPHUNZILE KUOPA MULUNGU
6. N’ciyani cingatithandize kuphunzila kuopa Mulungu? (Salimo 34:11)
6 Kuopa Yehova sitibadwa nako. Timacita kuphunzila. (Ŵelengani Salimo 34:11.) Tingaphunzile kumuopa mwa kuyang’ana zimene analenga. Tikamaona nzelu za Mulungu, mphamvu zake, na cikondi cake cacikulu pa ife “m’zinthu zimene anapanga,” timam’lemekeza kwambili komanso kum’konda ngako. (Aroma 1:20) Mlongo wina dzina lake Adrienne anati: “Nikamaona nzelu za Yehova m’zacilengedwe, nimacita cidwi komanso zimanithandiza kudziŵa kuti iye amanifunila zabwino.” Cifukwa cosinkhasinkha zimenezo, mlongoyo anakambanso kuti: “Sinifuna kucita zinthu zimene zingawononge ubale wanga na Yehova, Gwelo la moyo.” Bwanji osapatulako nthawi mlungu uno kuti musinkhesinkhe cilengedwe ca Yehova? Mukatelo, mudzayamba kum’konda kwambili na kum’lemekeza kwambili.—Sal. 111:2, 3.
7. Kodi pemphelo lingatithandize bwanji kuopa Yehova?
7 Cina cingatithandize kumuopa Mulungu, ni kupemphela nthawi zonse. Tikamapemphela kaŵili-kaŵili, Yehova adzakhala weniweni kwa ife. Nthawi zonse tikam’pempha mphamvu kuti tipilile mayeso, timakumbukila kuti iye ni Mulungu wa mphamvu zonse. Tikamamuyamikila cifukwa ca mphatso ya Mwana wake, timakumbukila kuti Yehova amatikonda. Ndipo tikam’condelela Yehova kuti atithandize pa vuto lathu, timakumbukila kuti iye ni wanzelu kwambili. Mapemphelo ngati amenewa amatithandiza kumuopa Yehova. Komanso amatithandiza kupewa kucita ciliconse cimene cingaononge ubwenzi wathu na iye.
8. Kodi tingatani kuti tikhalebe na mantha oopa Mulungu?
8 Tingakhalebe na mantha oopa Mulungu mwa kuŵelenga Baibo kuti titengepo phunzilo pa zitsanzo zabwino komanso zoipa. Tiyeni tikambilane za atumiki a Yehova aŵili okhulupilika—Obadiya, amene anali kugwila nchito m’nyumba yacifumu ya Ahabu, komanso Mkulu wa Ansembe Yehoyada. Kenaka, tikambilane zimene tingaphunzile kwa Yehoasi Mfumu ya Yuda, amene anayamba bwino koma anam’siya Yehova.
KHALANI OLIMBA MTIMA MONGA OBADIYA
9. Kodi kuopa Yehova kunam’thandiza bwanji Obadiya? (1 Mafumu 18:3, 12)
9 Pochula za Obadiya b, Baibo imayamba na mawu akuti: “Obadiya anali atasonyeza kuti anali munthu woopa Yehova kwambili.” (Ŵelengani 1 Mafumu 18:3, 12.) Kodi mantha oyenela amenewa anam’thandiza bwanji Obadiya? Anam’thandiza kukhala woona mtima komanso wokhulupilika. Conco, Mfumu inamuika kuti aziyang’anila za m’nyumba yake yacifumu. (Yelekezelani na Nehemiya 7:2.) Anam’thandizanso kukhala wolimba mtima, khalidwe limene anali kufunikila. Anakhalako m’nthawi ya Mfumu Ahabu, amene “anacita zoipa pamaso pa Yehova kuposa onse amene anakhalapo iye asanakhale.” (1 Maf. 16:30) Cina, mkazi wa Ahabu Yezebeli amene anali kulambila Baala, anali kudana naye Yehova kwambili cakuti anafuna kuseselatu kulambila koona mu ufumu wa kumpoto wa Isiraeli. Anaphanso aneneli ambili a Yehova. (1 Maf. 18:4) Mosakayikila, Obadiya anali kulambila Yehova pa nthawi yovuta.
10. Kodi Obadiya anaonetsa bwanji kulimba mtima?
10 Kodi Obadiya anaonetsa bwanji kulimba mtima? Pamene Yezebeli anali kufuna-funa aneneli a Mulungu kuti awaphe, Obadiya anabisa aneneli 100, ‘m’magulu aŵili a aneneli 50 gulu lililonse ndipo anali kuwapatsa mkate ndi madzi.’ (1 Maf. 18:13, 14) Akanam’tulukila, munthu wolimba mtima Obadiya akanaphedwa. N’kutheka kuti Obadiya anacita mantha. Koma anali kukonda kwambili Yehova na atumiki ake, kuposa mmene anali kukondela moyo wake.
11. Kodi atumiki a Yehova amakono amafanana bwanji na Obadiya? (Onaninso cithunzi.)
11 Masiku ano, pali atumiki ambili a Yehova omwe ali m’maiko amene nchito yathu inatsekedwa. Amapeleka ulemu woyenelela kwa olamulila. Koma monga Obadiya, abale na alongo amenewa amadzipeleka kwa Yehova yekha basi. (Mat. 22:21) Amaonetsa kuti amaopa Mulungu yekha pomumvela m’malo momvela anthu. (Mac. 5:29) Amatelo mwa kupitiliza kulalikila uthenga wabwino na kupitiliza kusonkhana mwakabisila. (Mat. 10:16, 28) Iwo amaonetsetsa kuti abale na alongo awo ali na cakudya cauzimu cokwanila. Onani citsanzo ici ca m’bale Henri wa mu Africa. M’dziko limene akhala nchito yathu inali yotsekedwa kwa kanthawi. Pa nthawi ya ciletso, iye anadzipeleka kuti azigaŵila cakudya cauzimu Mboni zinzake. Iye anati: “Mwacibadwa, ndine wamanyazi. Conco, sinikayikila kuti kuopa kwambili Yehova n’kumene kunanithandiza kukhala wolimba mtima.” Kodi inunso ndinu wolimba mtima monga Henri? Ngati muopa Mulungu moyenela, mudzakhaladi wolimba mtima.
KHALANI WOKHULUPILIKA MONGA MKULU WA ANSEMBE YEHOYADA
12. Kodi Mkulu wa Ansembe Yehoyada na mkazi wake anaonetsa bwanji kuti anali okhulupilika ngako kwa Yehova?
12 Mkulu wa Ansembe Yehoyada anali kuopa Yehova. Ndipo mantha amenewo anam’limbikitsa kukhala wokhulupilika, na kulimbikitsa kulambila koona. Izi zinaonekela bwino pamene Ataliya, mwana wa mkazi wa Yezebeli, anadzilonga ufumu mu Yuda. Anthu anali kumuopa kwambili Ataliya, cifukwa anali wankhanza komanso anali kufunitsitsa ulamulilo. Ndipo anapha pafupifupi adzukulu ake onse pofuna kufafaniza mzele wa banja lacifumu. (2 Mbiri 22:10, 11) Koma mmodzi wa adzukuluwo, Yehoasi, sanaphedwe cifukwa Yehosabati mkazi wa Yehoyada anam’pulumutsa. Iye na mwamuna wake anabisa mwanayo na kum’samalila bwino. Mwakutelo, Yehoyada na Yehosabati anathandiza kuteteza mzele wa mafumu a m’banja la Davide. Yehoyada anali wokhulupilika kwa Yehova, ndipo sanaope Ataliya.—Miy. 29:25.
13. Yehoasi atakwanitsa zaka 7, kodi Yehoyada anaonetsanso motani kukhulupilika kwake kwa Yehova?
13 Yehoasi atakwanitsa zaka 7, Yehoyada anaonetsanso kukhulupilika kwake kwa Yehova. Iye anapanga pulani. Pulaniyo ikanayenda bwino, Yehoasi mbadwa ya Davide anali kudzakhala mfumu. Koma ikanalephela, Yehoyada akanaphedwa. Mwa thandizo la Yehova, pulaniyo inayenda bwino. Yehoyada pamodzi na atsogoleli komanso Alevi, analonga Yehoasi ufumu, ndipo analamula kuti Ataliya aphedwe. (2 Mbiri 23:1-5, 11, 12, 15; 24:1) Kenako, Yehoyada “anacita pangano pakati pa Yehova, mfumu, ndi anthu, kuti anthuwo azisonyeza kuti ndi anthu a Yehova.” (2 Maf. 11:17) Cina, “anaika alonda a pazipata pafupi ndi zipata za nyumba ya Yehova kuti aliyense wodetsedwa mwa njila ina iliyonse asaloŵe.”—2 Mbiri 23:19.
14. Kodi Yehoyada analemekezedwa motani cifukwa colemekeza Yehova?
14 Kalelo, Yehova anakamba kuti:“Amene akundilemekeza ndiwalemekeza.” Izi n’zimene anacita kwa Yehoyada. (1 Sam. 2:30) Mwacitsanzo, analola kuti nkhani ya mkulu wa ansembeyo ilembedwe m’Baibo kuti tiphunzilepo kanthu. (Aroma 15:4) Ndipo Yehoyada atamwalila, analemekezedwa mwapadela poikidwa “m’manda a mafumu mu Mzinda wa Davide, cifukwa anacita zabwino mu Isiraeli ndiponso kwa Mulungu woona ndi nyumba Yake.”—2 Mbiri 24:15, 16.
15. Kodi tingaphunzile ciyani kwa Yehoyada? (Onaninso cithunzi.)
15 Nkhani ya Yehoyada ingatithandize tonsefe kumaopa Mulungu. Akulu angatengele Yehoyada mwa kukhalabe chelu, komanso kuteteza nkhosa za Mulungu. (Mac. 20:28) Okalamba angaphunzile kwa Yehoyada kuti akamaopa Yehova na kukhalabe okhulupilika kwa iye, angawagwilitse nchito kucita cifunilo cake. Ndipo sangaŵasiye. Acicepele naonso angaganizile mmene Yehova anali kucitila naye Yehoyada, na kutengela citsanzo cake mwa kulemekeza acikulile, maka-maka aja amene atumikila Yehova mokhulupilika kwa zaka zambili. (Miy. 16:31) Ndipo tonsefe, tingaphunzile kwa atsogoleli, komanso Alevi amene anathandiza Yehoyada. Tiyeni tizithandiza “amene akutsogolela” mwa kuwamvela.—Aheb. 13:17.
MUSAKHALE MONGA MFUMU YEHOASI
16. N’ciyani cionetsa kuti Mfumu Yehoasi anali wofooka kuuzimu?
16 Yehoyada anathandiza mfumu Yehoasi kukhala munthu wabwino. (2 Maf. 12:2) Cotelo, pamene anali wacicepele, mfumu Yehoasi anali kufuna kukondweletsa Yehova. Koma Yehoyada atamwalila, Yehoasi anamvetsela malangizo a akalonga opanduka. Zotulukapo n’zakuti iye na anthu ake ‘anayamba kutumikila mizati yopatulika ndiponso mafano.’ (2 Mbiri 24:4, 17, 18) Ngakhale kuti izi zinamupweteka mtima Yehova, “anapitiliza kutumiza aneneli pakati pawo kuti awabwezele kwa iye . . ., koma sanamvele.” Sanamvelenso Zekariya mwana wa Yehoyada, olo kuti anali mneneli, wansembe, komanso msuweni wa Yehoasi. Mfumu Yehoasi anafika ngakhale pa kupha Zekariya, amene makolo ake anapulumutsa moyo wake.—2 Mbiri 22:11; 24:19-22.
17. Kodi zinthu zinam’thela bwanji Yehoasi?
17 Yehoasi sanapitilize kuopa Yehova moyenela, ndipo sizinamuyendele bwino. Yehova anali atanena kuti: “Amene akundinyoza ndi opanda pake kwa ine.” (1 Sam. 2:30) Patapita nthawi, kagulu ka asilikali ocepa a Siriya kanagonjetsa “gulu lankhondo lalikulu kwambili” la Yehoasi, ndipo “anamusiya akuvutika kwambili.” Asiriya atacoka, Yehoasi anaphedwa na atumiki ake cifukwa anapha Zekariya. Anthu anaona kuti mfumu yoipa imeneyo siinali yoyenela kuikidwa m’manda a mafumu.—2 Mbiri 24:23-25.
18. Malinga na Yeremiya 17:7, 8, tingacite ciani kuti tisakhale monga Yehoasi?
18 Kodi tiphunzila ciyani kwa Yehoasi? Iye anali ngati mtengo umene mizu yake sinazikike pansi kwambili, ndipo unali kudalila mzati kuti usagwe. Koma pamene mzatiwo—Yehoyada—unacoka ndiponso cimphepo campatuko cinawomba, iye anagwa. Nkhaniyi itiphunzitsa kuti kuopa kwathu Mulungu, sikuyenela kudalila kwambili Akhristu anzathu, ngakhalenso a m’banja mwathu. Kuti tikhalebe olimba mwauzimu, tiyenela kukulitsa cikondi komanso mantha athu pa iye, mwa kuphunzila Baibo nthawi zonse, kusinkhasinkha, na kupemphela.—Ŵelengani Yeremiya 17:7, 8; Akol. 2:6, 7.
19. Kodi Yehova amafunanji kwa ife?
19 Yehova sayembekezela zambili kwa ife. Zimene amafuna kwa ife zinafotokozedwa pa Mlaliki 12:13 imene imati: “Opa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake cifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenela kucita.” Tikamaopa Mulungu, tidzatha kuima nji poyang’anizana na mayeso alionse m’tsogolomu, monga anacitila Obadiya na Yehoyada. Palibe cimene cidzatha kuwononga ubale wathu na Yehova.
NYIMBO 3 Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu
a M’Baibo, liwu lakuti “kuopa” lili na matanthauzo ambili. Malinga na nkhani yake, lingatanthauze kucita mantha kwambili, kupeleka ulemu, kapena kucita nthumanzi. M’nkhani ino, tikambilane mantha amene angatithandize kukhala olimba mtima, komanso okhulupilika potumikila Atate wathu wakumwamba.
b Obadiya amene tikunena pano si mneneli Obadiya amene anadzakhalako zaka zambili pambuyo pake, amenenso analemba buku la m’Baibo lochedwa na dzina lake.
c MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’citsanzo ici, m’bale akugaŵila cakudya cauzimu panthawi ya ciletso.
d MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo wacicepele akuphunzila mocitila ulaliki wa pafoni kwa mlongo wacikulile. M’bale wacikulile akuonetsa kulimba mtima mwa kulalikila poyela. M’bale waluso akuphunzitsa ena mmene angasamalile Nyumba ya Ufumu.