Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 28

Pitilizani Kupindula na Mantha Aumulungu

Pitilizani Kupindula na Mantha Aumulungu

“Munthu woyenda mowongoka mtima amaopa Yehova.” —MIY. 14:2.

NYIMBO 122 Cilimikani, Musasunthike!

ZIMENE TIKAMBILANE a

1-2. Monga Loti, kodi Akhristu amakumana na zovuta zotani masiku ano?

 TIKAMAONA makhalidwe oipa m’dzikoli, timamva monga mmene Loti anamvela. Iye “anavutika mtima kwambili ndi kulowelela kwa anthu ophwanya malamulo mu khalidwe lawo lotayilila,” podziŵa kuti Atate wathu wakumwamba amadana na makhalidwe oipa. (2 Pet. 2:7, 8) Kuopa Mulungu komanso kum’konda kunalimbikitsa Loti kupewa makhalidwe oipa a anthu a m’nthawi yake. Nafenso masiku ano, tili pakati pa anthu amene salemekeza malamulo a Yehova. Ngakhale n’telo, n’zotheka kukhalabe oyela ngati timam’konda Mulungu na kumuopa.—Miy. 14:2.

2 Yehova amatithandiza kucita zimenezo kupyolela m’buku la Miyambo. Akhristu onse—amuna, akazi, ana, komanso okalamba, angapindule na uphungu wanzelu wa m’bukuli.

KUOPA MULUNGU KUMATITETEZA

Kunchito, tizipewa kugwilizana na anthu amene sakonda Yehova na kumuopa, ndipo tisalole akatipempha kucita nawo zinthu zimene zingam’khumudwitse (Onani ndime 3)

3. Malinga n’kunena kwa Miyambo 17:3, n’cifukwa ciyani tiyenela kuteteza mtima wathu? (Onaninso cithunzi.)

3 Cifukwa cacikulu cotetezela mtima wathu wophiphilitsa, n’cakuti Yehova amasanthula mitima yathu. Izi zitanthauza kuti iye amaona umunthu wathu wamkati umene anthu saona. (Ŵelengani Miyambo 17:3.) Iye adzatikonda tikamadzaza mitima yathu na nzelu zake zopatsa moyo. (Yoh. 4:14) Tikatelo, tidzapewa makhalidwe oipa, komanso mabodza a Satana na dziko lake. (1 Yoh. 5:18, 19) Ndipo tikamayandikila kwambili Yehova, tidzayamba kum’konda ngako na kum’lemekeza. Popeza sitifuna kukhumudwitsa Atate wathu, tidzapewa ngakhale maganizo ofuna kucita zoipa. Tikayesedwa kucita zoipa, tidzadzifunsa kuti, ‘Kodi mwadala nim’khumudwitse Mulungu amene amanikonda kwambili conco?’—1 Yoh. 4:9, 10.

4. Kodi kuopa Yehova kunam’thandiza bwanji mlongo wina kusagonja ku mayeselo?

4 Mlongo Marta wa ku Croatia, amene anayesedwa kucita zaciwelewele anati: “Sicinali copepuka kwa ine kuganiza bwino, komanso kugonjetsa cilakolako cofuna kucita zosangalatsa zosakhalitsa zaucimo. Koma kuopa Yehova kunaniteteza.” b Kodi kunam’teteza bwanji? Mlongoyo anati anasinkhasinkha zotsatilapo za cisankho coipa. Nafenso tizicita cimodzimodzi. Tikagonja ku mayeselo, cotsatilapo coipa kwambili n’cakuti tidzakhumudwitsa Yehova, ndipo sitidzakhala pa mzele wokamulambila kwamuyaya.—Gen. 6:5, 6.

5. Kodi muphunzilapo ciyani pa citsanzo ca m’bale Leo?

5 Kuopa Yehova kumatithandiza kupewa kugwilizana na anthu a makhalidwe oipa. M’bale Leo wa ku Congo, anaphunzila nkhwangwa ili m’mutu. Patapita zaka zinayi pambuyo pobatizika, anayamba kugwilizana na anthu ocita zoipa. Anaona kuti zimenezo zilibe vuto cifukwa sanali kucita nawo zoipazo. Koma posakhalitsa, anzakewo anam’sonkhezela kuyamba kumwa moŵa mwaucidakwa komanso kucita zaciwelewele. Pambuyo pake, anayamba kuganizila zimene makolo ake acikhristu anam’phunzitsa, komanso cimwemwe cimene anataya. Zotulukapo n’zakuti anayambanso kucita zoyenela. Mwa thandizo la akulu, anabwelela kwa Yehova. Pano tikamba, ni mkulu komanso mpainiya wapadela.

6. Tikambilane za akazi aŵili ati ophiphilitsa?

6 Tiyeni lomba tikambilane Miyambo caputala 9, imene imachula za akazi aŵili ophiphilitsa. Mmodzi aimila nzelu, wina aimila kupusa. (Yelekezelani na Aroma 5:14; Agalatiya 4:24.) Pamene tikukambilana, kumbukilani kuti zaciwelewele komanso zamalisece zili paliponse m’dziko la Satanali. (Aef. 4:19) Conco, m’pofunika kukhalabe na mantha aumulungu na kupatuka pa coipa. (Miy. 16:6) Ndipo tonsefe, kaya ndife mwamuna kapena mkazi, tingapindule na mfundo za m’caputalaci. Akazi aŵiliwo akufotokozedwa kuti akupeleka ciitano kwa anthu osadziŵa zinthu, inde ‘opanda nzelu.’ Akazi onse aŵiliwo akuitana kuti, ‘Bwelani mudzadye cakudya m’nyumba mwanga,’ titelo kunena kwake. (Miy. 9:1, 5, 6, 13, 16, 17) Koma pali zotsatilapo zosiyana kwa aja amene akuvomela ciitano ca akaziwo.

KANANI CIITANO CA MKAZI WOPUSA

Ciitano ca “mkazi wopusa” cimakhala na zotsatilapo zoipa (Onani ndime 7)

7. Malinga na Miyambo 9:13-18, n’ciyani cimacitikila anthu ovomela ciitano ca mkazi wopusa? (Onaninso cithunzi.)

7 Mvani ciitano ici ca “mkazi wopusa.” (Ŵelengani Miyambo 9:13-18.) Mopanda manyazi akuitana opanda nzelu kuti, ‘Patukilani kuno’ mudzadye cakudya. Kodi zotsatilapo zake n’zotani? “Amene amaitanidwa ndi mkaziyu ali kumalo otsika a ku Manda.” Mungakumbukile mawu ophiphilitsa ofanana na amenewa m’macaputala oyambilila m’buku la Miyambo. Timacenjezedwa za “mkazi wacilendo” komanso “waciwelewele.” (Miy. 2:11-19 Buku Lopatulika.) Ndipo Miyambo 5:3-10 imaticenjeza za mkazi winanso “wacilendo” amene “mapazi ake amatsikila ku imfa.”

8. Kodi tingafunike kupanga cisankho cotani?

8 Amene amamva ciitano ca “mkazi wopusa,” amafunika kusankha kaya kulabadila ciitanoco kapena ayi. Nafenso tingafunike kupanga cisankho ngati cimeneci. Tikayesedwa kuti ticite zaciwelewele kapena kuonelela zamalisece, kodi tidzacitanji?

9-10. Tiyenela kupewa khalidwe laciwelewele pa zifukwa zotani?

9 Tili na zifukwa zomveka zopewela khalidwe laciwelewele. Pa lembalo, “mkazi wopusa” akunena kuti: “Madzi akuba amatsekemela.” Kodi “madzi akuba” n’ciyani? Baibo imayelekezela kugonana pakati pa mwamuna na mkazi wake na madzi otsitsimula. (Miy. 5:15-18) Kugonana kumasangalatsa ngati kucitika pakati pa mwamuna na mkazi okwatilana mwalamulo. Komabe, izi n’zosiyana kutalitali na “madzi akuba,” omwe angatanthauze ciwelewele. Nthawi zambili, ciwelewele cimacitika usiku, monga mbala imene kambili imaba usiku. “Madzi akuba” angaoneke otsekemela maka-maka ngati ocita ciwelewele cimeneco amaona kuti palibe adzadziŵa. Ati kudzinamiza kwake ŵati! Yehova amaona zonse. Ndipo palibe coŵaŵa kwambili kuposa kutaya ciyanjo cake. Conco, palibenso ‘cotsekemela’ ngakhale pang’ono. (1 Akor. 6:9, 10) Koma palinso zifukwa zina zopewela khalidwe laciwelewele.

10 Zaciwelewele zingapangitse kuti tizicita manyazi, kudziona wacabe-cabe, kutenga mimba zapathengo, komanso zingawononge mabanja. Conco, n’cinthu canzelu kupewa “nyumba” ya mkazi wopusa komanso cakudya cake. Kuwonjezela pa kumwalila mwauzimu, anthu ambili ocita zaciwelewele amatenga matenda omwe angadukize moyo wawo weniweniwo. (Miy. 7:23, 26) Mawu othela pa vesi 18 ya caputala 9 akuti: “Amene amaitanidwa ndi mkaziyu ali kumalo otsika a ku Manda.” Nanga n’cifukwa ciyani anthu oculuka amavomela ciitano ca mkaziyo cimene cimawabweletsela tsoka?—Miy. 9:13-18.

11. N’cifukwa ciyani kuonelela zamalisece n’koopsa kwambili?

11 Msampha wofala ni zamalisece. Ena amaona kuti kuonelela zamalisece kulibe vuto. Koma zoona n’zakuti kumavulaza, kumacotsela munthu ulemu, komanso n’kovuta kuti munthu aleke. Zithunzi zamalisece zimazika mizu m’maganizo mwa munthu, ndipo n’kovuta kuzicotsa. Paja amati caona maso mtima suiŵala. Cina, zamalisece zimangodzutsa zilakolako zoipa osati kuzipha ayi. (Akol. 3:5; Yak. 1:14, 15) Ndipo anthu ambili amene amaonelela zamalisece amacita zaciwelewele.

12. Kodi tingacite ciyani kuti tipewe zithunzi zodzutsa cilakolako ca kugonana?

12 Pokhala Akhristu kodi tiyenela kucita ciyani zithunzi zamalisece zikaonekela pa cipangizo cathu? Tisaziyang’ane ngakhale pang’ono! Cingatithandize kutelo ni kukumbukila kuti ubale wathu na Yehova ni wamtengo wapatali. Ndipo ngakhale zithunzi zimene si zamalisece kwenikweni zingadzutse cilakolako ca kugonana. N’cifukwa ciyani nazonso tiyenela kuzipewa? Cifukwa sitifuna ngakhale pang’ono kuganizila zocita zaciwelewele. (Mat. 5:28, 29) Mkulu wina ku Thailand dzina lake David anati: “Nimadzifunsa kuti: ‘Olo kuti zithunzi zimenezi si zamalisece kwenikweni, kodi Yehova angakondwele nikapitiliza kuziyang’ana?’ Funso ngati limeneli limanithandiza kucita mwanzelu.”

13. N’ciyani cimatithandiza kucita mwanzelu?

13 Mantha oyenela oopa kukhumudwitsa Yehova, amatithandiza kucita mwanzelu. Mantha aumulungu otelo ndiwo “ciyambi ca nzelu.” (Miy. 9:10) Izi zafotokozedwa bwino m’mavesi oyambilila a Miyambo caputala 9, mmene akuchula mkazi wina wophiphilitsa, amene akuimila “nzelu yeniyeni.”

LABADILANI CIITANO CA MKAZI WANZELU

14. Kodi pa Miyambo 9:1-6, timaŵelengapo za ciitano cotani?

14 Ŵelengani Miyambo 9:1-6. Pa lembali, tipezapo ciitano cocokela kwa Yehova, Mlengi wathu komanso Gwelo la nzelu zenizeni. (Miy. 2:6; Aroma 16:27) Mophiphilitsa akuchula za nyumba yaikulu yokhala na zipilala 7. Izi zitanthauza kuti Yehova ni wowolowa manja, komanso kuti amalandila aliyense wofuna kugwilitsa nchito nzelu zake.

15. Kodi Mulungu akutipempha kucita ciyani?

15 Pa citsanzo ca mkazi amene aimila “nzelu yeniyeni,” tiphunzilapo kuti Yehova ni woolowa manja, ndipo amatipatsa zinthu zambili zabwino. Miyambo caputala 9 imafotokoza kuti mkazi wophiphilitsa ameneyo waphika bwino nyama yake, wasakaniza bwino vinyo, komanso wayala pathebulo m’nyumba mwake. (Miy. 9:2) Cinanso, malinga na vesi 4 na 5, kwa aliyense wopanda nzelu mumtima mwake, mkaziyo [nzelu yeniyeni] akunena kuti: “Bwelani mudzadye cakudya canga.” N’cifukwa ciyani tiyenela kubwela kunyumba kwa nzelu yeniyeni na kudya cakudya cake? Cifukwa Yehova afuna kuti ana ake akhale anzelu komanso otetezeka. Safuna kuti tikaphunzile nkhwangwa ili m’mutu ayi. Ndiye cifukwa cake, kwa “anthu owongoka mtima, iye amawasungila nzelu zopindulitsa.” (Miy. 2:7) Tikakhala na mantha oyenela pa Yehova, tidzacita zinthu zom’kondweletsa. Tidzamvela uphungu wake wanzelu na kuugwilitsa nchito.—Yak. 1:25.

16. Kodi kuopa Mulungu kunam’thandiza bwanji m’bale Alain? Nanga panakhala zotulukapo zotani?

16 Onani mmene kuopa Mulungu kunathandizila m’bale Alain, amene ni mkulu komanso wogwila nchito yauphunzitsi, kupanga cisankho cabwino. Iye anati: “Anzanga ambili a kunchito anali kuti mafilimu a zamalisece ni maphunzilo a zakugonana.” Koma m’bale Alain sakhulupilila zimenezo. Iye anakamba kuti: “Cifukwa coopa Mulungu, n’nakana kupenyelela nawo mafilimu amenewo. Ndipo n’nawafotokozela anzangawo cifukwa cake.” M’baleyu amatsatila ulangizi wa “nzelu yeniyeni” wakuti: “Yendani mowongoka m’njila yomvetsa zinthu.” (Miy. 9:6) Poona khalidwe labwino la m’bale Alain, ena mwa aphunzitsi anzake amaphunzila Baibo na kupezeka ku misonkhano.

Kulabadila ciitano ca “nzelu yeniyeni” kumatsogolela ku moyo (Onani ndime 17-18)

17-18. Kodi anthu amene amalabadila ciitano ca “nzelu yeniyeni” amapeza madalitso otani? Nanga ali na ciyembekezo cotani? (Onaninso cithunzi.)

17 Pogwilitsa nchito akazi aŵili ophiphilitsa, Yehova akutiphunzitsa mokhalila na tsogolo labwino. Aja amene amalabadila ciitano ca “mkazi wopusa,” amafuna kupeza cisangalalo m’zaciwelewele. Kukamba zoona, iwo amangokhalila za lelo basi, ndipo sadziŵa kuti zocita zawo mapeto ake ni “Manda.”—Miy. 9:13, 17, 18.

18 Izi n’zosiyana na anthu amene amalabadila ciitano ca “nzelu yeniyeni.” Iwo amasangalala na cakudya cauzimu cokonzedwa bwino komanso copatsa thanzi, inde phwando lauzimu. (Yes. 65:13) Kudzela mwa mneneli Yesaya, Yehova anati: “Chelani khutu kwa ine kuti mudye zabwino, ndiponso kuti moyo wanu usangalale kwambili ndi zakudya zamafuta.” (Yes. 55:1, 2) Tikuphunzila kukonda zimene Yehova amakonda, komanso kudana na zimene amadana nazo. (Sal. 97:10) Ndipo timakhala acimwemwe tikamaitana ena kuti apindule na “nzelu yeniyeni.” Zili monga kuti ‘tapita pamwamba pa zitunda za m’mudzi na kuitanila anthu kuti: “Aliyense wosadziŵa zinthu apatukile kuno.’” Mapindu amene ife komanso iwo amapeza si a palipano cabe. Koma ni amuyaya, ndipo tidzakhalabe na “moyo” kwamuyaya malinga ‘tiyenda mowongoka m’njila yomvetsa zinthu.’—Miy. 9:3, 4, 6.

19. Malinga na Mlaliki 12:13, 14, kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciyani? (Onaninso kabokosi kakuti “ Mapindu a Kuopa Mulungu.”)

19 Ŵelengani Mlaliki 12:13, 14. Tiyeni tipitilize kulola mantha aumulungu kuteteza mitima yathu, na kutithandiza kukhala oyela m’makhalidwe komanso kukhala pa ubale wolimba na Yehova m’masiku ano otsiliza oipa. Ndipo mantha amenewo adzatilimbikitsa kuti tisaleke kuitana anthu ambili mmene tingathele, kuti afunefune “nzelu yeniyeni” na kupindula nayo.

NYIMBO 127 Mtundu wa Munthu Amene Niyenela Kukhala

a Akhristu ayenela kukulitsa mantha oyenela pa Mulungu. Mantha otelo angateteze mitima yathu, na kutithandiza kupewa zaciwelewele komanso zamalisece. M’nkhani ino, tikambilane Miyambo caputala 9, imene imachula za akazi aŵili ophiphilitsa, poonetsa kusiyana pakati pa nzelu komanso kupusa. Mfundo za m’caputalaci zingatipindulile masiku ano mpaka muyaya.

b Maina ena asinthidwa.