Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Yehova Watidabwitsa na Kutiphunzitsa Pom’tumikila

Yehova Watidabwitsa na Kutiphunzitsa Pom’tumikila

NILI mwana, n’nali kulakalaka kupita kudziko lina nikangoona ndeke m’mwamba. Koma kwa ine, zinali kuoneka zosatheka.

Makolo anga anacoka ku Estonia kupita ku Germany pa nthawi ya Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse. Ku Germany n’kumene ninabadwila. N’tabadwa, anayamba kukonzekela ulendo wosamukila ku Canada. Nyumba yathu yoyamba ku Canada inali malo osungilamo nkhuku pafupi na mzinda wa Ottawa. Tinali osauka kwadzaoneni. Komabe, tinali kudyako mazila pa cakudya cam’mawa.

Tsiku lina, a Mboni za Yehova anaŵelengela amayi Chivumbulutso 21:3, 4. Lembalo linawakhudza kwambili amayi cakuti anayamba kulila. Mbewu ya coonadi inakula mu mitima ya makolo anga, ndipo patapita nthawi yocepa anabatizika.

Ngakhale kuti makolo anga sanali kucidziŵa bwino Cizungu, anali odzipeleka kwambili pa kutumikila Yehova. Pafupifupi Ciŵelu ciliconse, atate anali kunitenga pamodzi na mlongosi wanga Sylvia kukalalikila. Anali kucita izi ngakhale pambuyo pogwila nchito yosungunula miyala ya nickel ku Ontario mu mzinda wa Sudbury. Ndipo mlungu uliwonse tinali kuphunzila Nsanja ya Mlonda monga banja. Makolo anga ananithandiza kuyamba kukonda Mulungu. Zimenezi zinanilimbikitsa kudzipatulila kwa Yehova nili na zaka 10 mu 1956. Kuona cikondi cacikulu cimene makolo anga anali naco pa Yehova, kwanilimbikitsa pa umoyo wanga wonse.

N’tamaliza maphunzilo a ku sekondale, n’naleka kuika maganizo anga onse pa kutumikila Yehova. N’naganiza kuti nikayamba upainiya sinidzakwanilitsa colinga canga cokwela ndeke na kupita ku maiko osiyanasiyana. Conco, n’nayamba nchito youlutsa nyimbo (DJ) pa nyumba ya wailesi ina m’dela lathu. Nchitoyi n’nali kuikonda kwambili. Cifukwa n’nali kugwila nchito m’madzulo, n’nayamba kuphonya misonkhano ya mpingo, ndipo n’nayambanso kugwilizana na anthu osakonda Mulungu. M’kupita kwa nthawi, cikumbumtima canga cophunzitsidwa Baibo cinanilimbikitsa kupanga masinthidwe.

N’nasamukila ku Ontario mu mzinda wa Oshawa. Kumeneko n’nakumana na m’bale Ray Norman, mlongosi wake Lesli na apainiya ena. Onse ananionetsa cidwi kwambili. Kuona cimwemwe cimene anali naco kunanilimbikitsa kuunikanso zolinga zanga. Iwo ananilimbikitsa kuyamba upainiya ndipo n’nayambadi mu September 1966. N’nali wokondwa ndipo n’nali kuona kuti zinthu zinali kuniyendela bwino kwambili. Koma sin’nadziŵe kuti madalitso amene adzasintha umoyo wanga anali kuniyembekezela.

YEHOVA AKAKUPEMPHANI KUCITA ZINAZAKE, YESANI KUCITA ZIMENEZO

Nili ku sekondale, n’nafunsila utumiki wa pa Beteli mu mzinda wa Toronto ku Canada. Pambuyo pake, nikucita upainiya, n’naitanidwa kukatumikila pa Beteli kwa zaka zinayi. Koma n’nali kum’konda kwambili Lesli, ndipo n’naopa kuti nikavomela utumikiwo sinidzakamuonanso. Koma pambuyo popeleka mapemphelo aatali ocokela pansi pamtima, ninavomela ciitano cokatumikila pa Beteli. Zinali zopweteka kwambili kusanzikana naye Lesli.

N’nali kuseŵenzela ku dipatimenti yocapa zovala, kenako n’nayamba kuseŵenza monga kalembela. Pa nthawiyi, Lesli anakhala mpainiya wapadela mu mzinda wa Gatineau ku Quebec. Nthawi zambili n’nali kudzifunsa kuti akucita ciyani palipano. Ndipo n’nali kukaikila ngati n’napanga cisankho coyenela. Kenako, panacitika cinthu cosangalatsa kwambili cimene sin’nayembekezele. Ray mlongo wa Lesli, anaitanidwa ku Beteli. Ndipo tinayamba kugona cipinda cimodzi! Izi zinacititsa kuti tiyambenso kukambilana na Lesli. Tinakwatilana pa tsiku lothela la utumiki wanga wa pa Beteli wa zaka zinayi pa February 27, 1971.

Titayamba nchito ya m’dela mu 1975

Ine na Lesli tinatumizidwa ku mpingo wa Cifulenci ku Quebec. Patapita zaka zingapo, nili na zaka 28, n’nadabwa n’talandila ciitano coti nikhale woyang’anila dela. N’naona kuti ndine wacicepele, komanso wosadziŵa zambili. Koma mawu apa Yeremiya 1:7, 8 ananilimbikitsa. Komabe, Lesli anapezekapo mu ngozi za galimoto kangapo konse, komanso anali kuvutika kugona. Cotelo, tinaganiza kuti sitingakwanitse kugwila nchito ya m’dela. Ngakhale n’telo, Lesli anakamba kuti, “Yehova akatipempha kucita zinazake, tiyenela kuyesa kucita zimenezo.” Tinavomela utumikiwo, ndipo tinasangalala nawo kwa zaka 17.

Monga woyang’anila dela, n’nali kukhala wotangwanika kwambili, moti sin’nali kukhala na nthawi yokwanila yoceza na Lesli. Apanso n’natengapo phunzilo. Tsiku lina pa Mande m’mawa, n’namva kugogoda pa citseko. N’tatuluka n’nangopeza basiketi, nsalu, zipatso, chizi, mkate, botolo la vinyo, makapu a gilasi na kakhadi komwe sitinadziŵe mlembi wake. Pa kakhadiko panali mawu akuti, “Tengani mkazi wanu mupite kokasangalala,” koma pa citseko panalibe munthu aliyense. Pa tsikulo, dzuŵa linali lowala bwino. N’nauza Lesli kuti sitingapite cifukwa n’nali na nkhani zofunika kukonzekela. Ananimvetsa koma sizinam’sangalatse. N’takhala pampando kuti niyambe kukonzekela nkhani, cikumbumtima cinayamba kunivutitsa. N’naganizila mawu a pa Aefeso 5:25, 28. N’namva ngati Yehova akuseŵenzetsa mavesiwa kuniphunzitsa kuti niyenela kuganizila mmene mkazi wanga akumvela. N’tapemphela n’nauza Lesli kuti, “Tiye tipite.” Izi zinam’sangalatsa kwambili. Tinauyamba ulendo wagalimoto kupita ku nyanja. Kumeneko tinapeza malo abwino kumene tinayala nsalu. Ili ni limodzi mwa masiku osangalatsa kwambili amene tinakhala nawo monga banja. Ndipo, n’napezabe nthawi yokonzekela nkhani.

Tinali kusangalala na mautumiki ambili a m’dela—kucokela ku British Columbia mpaka ku Newfoundland. Tsopano, colinga canga cofuna kupita ku madela ena cinali kukwanilitsika. N’nali n’taganizilapo zopita ku Sukulu ya Giliyadi, koma n’nalibe cikhumbo cotumikila monga mmishonale m’dziko lina. N’nali kuona kuti amishonale anali anthu apadela. Conco, n’nali kuona kuti sindine woyenelela. N’nalinso na nkhawa yakuti angadzatitumize ku dziko la ku Africa lokhudzidwa na matenda komanso nkhondo. N’nali wokhutila kutumikila kumene n’nali.

CIITANO COSAYEMBEKEZELA COKATUMIKILA KU ESTONIA, LATVIA NA KU LITHUANIA

Kuyendela mipingo ku Estonia, Latvia, na ku Lithuania

Mu 1992, Mboni za Yehova zinayambanso kulalikila poyela m’mayiko amene kale anali pansi pa ulamulilo wa Soviet Union. Pa nthawiyo tinafunsidwa ngati tingakonde kukatumikila ku Estonia monga amishonale. Tinadabwa kwambili, koma tinaipemphelela nkhaniyi. Apanso tinaganiza kuti, ‘Yehova akatipempha kucita zinazake, tiyenela kuyesa kucita zimenezo.’ Tinavomela utumikiwo, koma mu mtima n’nati, ‘Zili bwino, malinga si ku Africa.’

Nthawi yomweyo tinayamba kuphunzila ci Estonia. Titakhala m’dzikolo kwa miyezi ingapo, anatipempha kutumikila m’dela. Tinayenela kuyendela mipingo 46 komanso tumagulu ku Estonia, Latvia, Lithuania na ku mzinda wa Kaliningrad, ku Russia. Conco, tinafunika kuphunzila ci Latvia, ci Lithuania, na ci Russia. Sikunali kopepuka. Komabe, abale na alongo anakhudzika kwambili kuona kuti tinali kuyesetsa kuphunzila cinenelo cawo, ndipo anatithandiza. Mu 1999, ofesi ya nthambi inakhazikitsidwa ku Estonia ndipo n’naikidwa kukhala m’komiti ya nthambi pamodzi na Toomas Edur, Lembit Reile, na Tommi Kauko.

Kulamanja: Nikukamba nkhani pa msonkhano wacigawo ku Lithuania

Kumanzele: Komiti ya Nthambi ku Estonia, imene inakhazikitsidwa mu 1999

Tinadziŵana na Mboni zambili zimene zinali zitatumizidwapo kundende ku Siberia. Ngakhale kuti anali kucitidwa nkhanza ku ndendeko komanso anali atalekanitsidwa na mabanja awo, sanasunge cakukhosi kapena kukwiya. Anakhalabe acimwemwe komanso okangalika pa utumiki. Citsanzo cawo cinatithandiza kuona kuti nafenso tingathe kupilila komanso kukhala acimwemwe pa nthawi zovuta.

Tinali kuseŵenza mwakhama kwa zaka zambili, ndipo sitinali kupumula mokwanila. Conco, Lesli anayamba kumva kutopa kwambili. Sitinazindikile nthawi yomweyo kuti kutopako kunali cifukwa ca matenda ochedwa fibromyalgia. Cotelo tinaganiza zobwelela ku Canada. Titaitanidwa kuti tikalandile maphunzilo owonjezela ku Patterson, New York, U.S.A, tinakayikila ngati tingakwanitse. Pambuyo popemphela mocokela pansi pa mtima, tinavomela. Ndipo Yehova anadalitsa cisankho cathu. Tili ku sukulu imeneyo, m’pamene Lesli analandila cithandizo cimene anali kufunikila. Conco, tinayambanso kugwila nchito yathu monga kale.

DALITSO LINA LOSAYEMBEKEZELA —KUKATUMIKILA KU CIGAWO CINA CA DZIKO

Tsiku lina madzulo mu 2008 ku Estonia, a ku likulu ananitumila foni n’kunifunsa ngati tingavomele kukatumikila ku Congo. N’nadabwa kwambili. N’nali kufunika kupeleka yankho tsiku lotsatila. Poyamba, sin’namchulile Lesli cifukwa n’nadziŵa kuti angasoŵe tulo. M’malo mwake, ine ndiye n’nasoŵa tulo. N’nacezela kupemphela kwa Yehova pa zimene zinali kunidetsa nkhawa ku Africa.

Tsiku lotsatila n’tamuuza Lesli, tinati, “Yehova akutipempha kupita ku Africa. Tidziŵa bwanji kuti sitingakwanitse komanso kuti sitingasangalale, ngati sitinapiteko?” Conco, pambuyo potumikila zaka 16 ku Estonia, tinapita ku Kinshasa, ku Congo. Ofesi ya nthambi kumeneko, inali na malo okongola kwambili komanso abata. Cimodzi mwa zinthu zoyamba zimene Lesli anaika m’cipinda cathu, cinali khadi limene anasunga cicokeleni ku Canada. Pa khadilo panali mawu akuti, “Sangalala na utumiki umene uli nawo.” Pambuyo podziŵana na abale, kutsogoza maphunzilo a Baibo, na kumva kukoma kwa umishonale, cimwemwe cathu cinawonjezeka. M’kupita kwa nthawi, tinakhala na mwayi woyendela maofesi anthambi a mu Africa okwanila 13. Maulendowa anatipatsa mwayi woona mitundu ya anthu osiyanasiyana ocititsa cidwi. Nkhawa zanga zinathelatu, ndipo tinam’yamikila Yehova potitumiza ku Africa.

Ku Congo, anali kutipatsa zakudya zamitundu-mitundu monga tudoyo, zimene n’naona kuti sitingakwanitse kudya. Koma poona kuti abale anali kuzikonda, tinalaŵako ndipo nafenso tinazikonda.

Kum’mawa kwa dzikolo, magulu azigawenga anali kuukila anthu a m’midzi ndiponso kuvulaza azimayi na ana. Conco, tinapitako kukathandiza abale na alongo kuthupi na kuuzimu. Ambili a iwo anali osaukila. Ngakhale n’telo, ciyembekezo cawo colimba ca ciukitso, cikondi cawo pa Yehova, na kukhulupilika kwawo ku gulu lake kunatikhudza mtima kwambili. Citsanzo cawo cinatisonkhezela kudziunikanso na kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa Yehova. Nyumba na zam’munda za abale ena zinawonogeka. Zocitikazi zinanikumbutsa mfundo yakuti tingatayikilidwe zinthu zakuthupi mosavuta koma ubwenzi wathu na Yehova ndiwo cinthu cofunika koposa. Ngakhale kuti anali pa mavuto adzaoneni, abale sanali kukhalila kudandaula. Kaonedwe kawo ka zinthu kanatilimbikitsa kuyang’anizana na mavuto athu molimba mtima kuphatikizapo okhudza thanzi lathu.

Kulamanja Nikupeleka cilimbikitso kwa anthu othaŵa kwawo

Kumanzele: Kupeleka zinthu zofunikila komanso mankhwala ku mzinda wa Dungu ku Congo

UTUMIKI WATSOPANO KU ASIA

Tinalandilanso dalitso lina lomwe sitinayembekezele. Anatipempha kukatumikila ku nthambi ya ku Hong Kong. Sitinaganizilepo zokhala ku Asia! Koma poona mmene Yehova wakhala akutithandizila mwacikondi m’mautumiki athu onse, tinavomela utumikiwo. Mu 2013, tinakwinyilila kusiya abale athu okondedwa, komanso cigawo cokongola ca Africa. Sitinadziŵe kuti tidzakumana na zotani ku Asia.

Kukhala mumzinda wa Hong Kong wokhala na anthu ambili kunali masinthidwe aakulu kwa ife. Tinavutikanso kuphunzila cinenelo ca ci Chinese. Koma abale anatilandila bwino, ndipo tinasangalala na zakudya za ku dzikolo. Nchito yolalikila inali kupita patsogolo mofulumila. Ndipo ofesi ya nthambi inali kufuna malo owonjezela. Koma mitengo ya malo inali yokwela kwambili. Conco Bungwe Lolamulila linaganiza zosamutsila nchito zina kwina, na kugulitsa zimango zina pa nthambipo. Posakhalitsa, mu 2015 anatitumiza ku South Korea kumene tikutumikila palipano. Kumeneko tinakumananso na vuto la cinenelo. Koma abale amatilimbikitsa potiuza kuti tikupita patsogolo kuphunzila ci Korea.

Kulamanja: Kuyamba umoyo watsopano ku Hong Kong

Kumanzele: Ofesi ya nthambi ya ku Korea

ZIMENE TAPHUNZILA

Si copepuka kupanga mabwenzi atsopano. Koma tapeza kuti tikamaonetsa mzimu woceleza, timapanga mabwenzi mosavuta. Taona kuti abale athu amafanana m’zinthu zambili, komanso kuti Yehova anatilenga m’njila yakuti tizifutukula mtima wathu, na kuonetsa cikondi mabwenzi athu ambili.—2 Akor. 6:11.

Taphunzila kufunika koona anthu mmene Yehova amawaonela, komanso kuona umboni wakuti Yehova amatikonda na kutitsogolela pa umoyo wathu. Tikalefuka kapena tikayamba kukaikila ngati ena amatikonda, timaŵelenganso makadi kapena makalata ocokela kwa mabwenzi athu. Taona mmene Yehova amayankhila mapemphelo athu, kutilimbikitsa, na kutipatsa mphamvu.

Pa zaka zonsezi, ine na mkazi wanga taphunzila kufunika kopatula nthawi yoceza aŵili-aŵili, ngakhale kuti timatangwanika. Taphunzilanso kudziseka tikalakwitsa zinthu, maka-maka pophunzila cinenelo catsopano. Ndipo usiku uliwonse, timaganizila zinthu zosangalatsa zimene Yehova waticitila, na kumuyamikila.

Kukamba zoona, sin’naganizileko kuti ningakhale m’mishonale kapena kutumikila ku maiko ena. Komabe, naphunzila kuti na thandizo la Yehova, zinthu zonse zimatheka. Nimakumbukila mawu a mneneli Yeremiya akuti: “Mwandidabwitsa inu Yehova.” (Yer. 20:7) Ndithudi, iye watipatsa madalitso ambili amene sitinali kuyembekezela, kuphatikizapo kukwanilitsa colinga canga cokwela ndeke. Tapita m’maiko ambili kuposa amene n’nali kuganizila nili mwana, kuyendela nthambi m’zigawo zisanu za dzikoli. Nimayamikilanso mkazi wanga Lesli, pokhala wofunitsitsa kunithandiza pa mautumiki onsewa.

Nthawi zonse timakumbukila kuti timacita zimenezi cifukwa timakonda Yehova. Madalitso amene tikusangalala nawo pali pano, ni kadyonkho cabe ka moyo wosatha, pamene Yehova ‘adzatambasula dzanja lake ndi kukhutilitsa zokhumba za camoyo ciliconse’.—Sal. 145:16.