Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 23

NYIMBO 28 Kukhala Bwenzi la Mulungu

Ciitano Capadela ca Yehova Cokhala Alendo Ake

Ciitano Capadela ca Yehova Cokhala Alendo Ake

“Tenti yanga idzakhala pakati pawo. Ine ndidzakhala Mulungu wawo.”EZEK. 37:27.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Kutithandiza kuyamikila kwambili mwayi woitanidwa na Yehova kuti tikhale alendo m’tenti yake yophiphilitsa. Kutithandizanso kuyamikila mmene amatisamalila monga alendo ake.

1-2. Ni ciitano cotani cimene Yehova akupeleka kwa alambili ake okhulupilika?

 MUNGAYANKHE bwanji munthu wina atakufunsani kuti, ‘Kodi Yehova ni ndani wanu?’ Mwina mungayankhe kuti, ‘Yehova ni Atate wanga, Mulungu wanga, komanso Bwenzi langa.’ Palinso maina ena audindo a Yehova omwe mungachule. Koma kodi mumaonanso kuti mungakhale mlendo m’tenti yake?

2 Mfumu Davide anayelekezela Yehova na mwininyumba, ndipo alambili ake okhulupilika anawayelekezela na alendo m’nyumba yake. Anafunsa kuti: “Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo m’tenti yanu? Ndi ndani amene angakhale mʼphili lanu lopatulika?” (Sal. 15:1) Mawu ouzilidwa amenewa amatiphunzitsa kuti n’zotheka kukhala alendo a Yehova, kutanthauza kukhala mabwenzi ake. Ici ni ciitano capadela zedi cocokela kwa Yehova!

YEHOVA AFUNA KUTI TIKHALE ALENDO AKE

3. Kodi mlendo woyamba m’tenti ya Yehova anali ndani? Nanga kodi Yehova na mlendo wakeyo anali kumva bwanji?

3 Yehova anali yekha asanalenge ciliconse. Koma pa nthawi ina analenga Mwana wake woyamba na kumulandila m’tenti yake. Conco anakhala ngati Mwininyumba yemwe analandila mlendo wake woyamba, ndipo anali wokondwela kucita zimenezo. Baibo imanena kuti Yehova “ankasangalala kwambili” na Mwana wake. Mwana wakeyo nayenso anali kukhala “wosangalala pamaso pa [Yehova] nthawi zonse.”—Miy. 8:30.

4. Ndaninso ena amene anakhala alendo m’tenti ya Yehova?

4 Pambuyo pake, Yehova analenga angelo, ndipo nawonso anakhala alendo ake. Angelowo amachedwa “ana. . .a Mulungu” ndipo Baibo imaonetsa kuti amasangalala kukhala na Yehova. (Yobu 38:7; Dan. 7:10) Kwa zaka zambili-mbili, mabwenzi a Mulungu anali cabe zolengedwa zauzimu zimene zinali kukhala naye kumwamba. Pambuyo pake, Yehova analenga anthu, ndipo nawonso anapatsidwa mwayi wokhala alendo ake. M’kupita kwa nthawi, ena mwa alendowo anadzaphatikizapo Inoki, Nowa, Abulahamu, na Yobu. Alambili oona amenewo anafotokozedwa kuti anali mabwenzi a Mulungu, kapena amene “anayenda ndi Mulungu woona.”—Gen. 5:24; 6:9; Yobu 29:4; Yes. 41:8.

5. Tiphunzila ciyani pa ulosi wa pa Ezekieli 37:​26, 27?

5 Kwa zaka mahandiledi ambili, Yehova wakhala akuitana mabwenzi ake kuti akhale alendo m’tenti yake. (Ŵelengani Ezekieli 37:​26, 27.) Mwa citsanzo, ulosi wa Ezekieli umatiphunzitsa kuti Mulungu amafunitsitsa kuti alambili ake okhulupilika akhale naye pa ubwenzi wolimba. Analonjeza kuti adzacita “nawo pangano la mtendele.” Ulosi umenewu unali kunena za nthawi pamene alambili a Yehova amene ali na ciyembekezo cokakhala kumwamba, na amene ali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi, adzakhala “gulu limodzi” m’tenti yake yophiphilitsa. (Yoh. 10:16) Ulosi umenewu ukukwanilitsika masiku ano.

MULUNGU AMASAMALA ZA IFE KULIKONSE KUMENE TINGAKHALE

6. Kodi munthu ayenela kutani kuti akhale mlendo m’tenti ya Yehova? Nanga tenti imeneyi imapezeka kuti?

6 M’nthawi zochulidwa m’Baibo, tenti inali malo amene anthu anali kugonamo, ndipo inali kuteteza munthu ku dzuŵa na mphepo. Mlendo anali kuyembekezela kusamalidwa bwino na mwini tentiyo. Tikadzipatulila kuti tikhale pa ubale na Yehova, timakhala alendo m’tenti yake yophiphilitsa. (Sal. 61:4) Timakhala na cakudya cauzimu coculuka, ndipo timasangalalanso kukhala pa ubwenzi wabwino na anthu ena, amenenso ni alendo a Yehova. Tenti Yake yophiphilitsa siipezeka kumalo amodzi okha. Mwina munapezekako pa msonkhano wa cigawo wapadela ku dziko lina, ndipo munapezanso anthu ena amene ni osangalala kukhala m’tenti ya Mulungu. Tenti imeneyi imapezeka kulikonse kumene kuli alambili ake okhulupilika.—Chiv. 21:3.

7. N’cifukwa ciyani tinganene kuti anthu okhulupilika amene anamwalila akali alendo m’tenti ya Yehova? (Onaninso cithunzi.)

7 Nanga bwanji za anthu okhulupilika amene anamwalila? Kodi m’pomveka kunena kuti akali alendo m’tenti ya Yehova? Inde! Tikutelo cifukwa ciyani? Cifukwa Yehova amawakumbukila bwino ngako. Zili ngati ali moyo kwa iye. Yesu anafotokoza kuti: “Koma zakuti akufa amaukitsidwa ngakhalenso Mose anafotokoza mu nkhani ya citsamba ca minga, pamene ananena kuti Yehova ndi ‘Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.’ Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, cifukwa kwa iye onsewa ndi amoyo.”—Luka 20:​37, 38.

Ngakhale anthu okhulupilika amene anamwalila akali alendo m’tenti ya Mulungu (Onani ndime 7)


MAPINDU NA MAUDINDO OKHALA M’TENTI YA YEHOVA

8. Kodi alendo a Yehova amapindula motani cifukwa cokhala m’tenti yake?

8 Tenti imakhala malo ogonamo komanso acitetezo ku mvula na mphepo. Mofananamo, tenti ya Yehova imateteza alendo ake kuuzimu, ndipo imawapatsa ciyembekezo. Tikakhalabe oyandikana na Yehova, Satana sangacite ciliconse cimene cingativulaze mpaka kale-kale. (Sal. 31:23; 1 Yoh. 3:8) M’dziko latsopano, Yehova adzapitiliza kuteteza mabwenzi ake okhulupilika ku imfa, komanso ku zinthu zimene zingawavulaze kuuzimu.—Chiv. 21:4.

9. Kodi Yehova amafuna kuti alendo ake azicita ciyani?

9 Ni mwayi wapadela zedi kukhala mlendo m’tenti ya Yehova, kutanthauza kusangalala na ubale wabwino na iye umene udzakhalapo mpaka kale-kale. Tiyenela kucita ciyani kuti tipitilize kukhala alendo ake? Mukaitanidwa ku nyumba ya munthu winawake, mungafune kudziŵa zimene iye afuna kuti mucite. Mwa citsanzo, iye angafune kuti muvule nsapato musanaloŵe m’nyumba, ndipo mungacite zimenezo mosanyinyilika. Mofananamo, nafenso tiyenela kudziŵa zimene Yehova amafuna kuti tizicita kuti tikhalabe alendo m’tenti yake. Cikondi pa Yehova cimatisonkhezela kucita zonse zotheka kuti ‘tizimusangalatsa pa ciliconse.’ (Akol. 1:10) N’zoona kuti Yehova ni Bwenzi lathu, koma timadziŵanso kuti iye ni Mulungu wathu, komanso Atate wathu, ndipo tiyenela kum’patsa ulemu. (Sal. 25:14) Sitiyenela kuiŵala mfundo imeneyi, ndipo nthawi zonse tiyenela kum’patsa ulemu waukulu. Mantha amenewa adzatithandiza kupewa makhalidwe amene angamukhumudwitse. Ndife ofunitsitsa kuyenda “modzicepetsa” na Mulungu wathu.—Mika 6:8.

MMENE ANAONETSELA KUTI ALIBE TSANKHO M’CIPULULU

10-11. Kodi mmene Yehova anacitila zinthu na Aisiraeli m’cipululu ca Sinai zinaonetsa bwanji kuti alibe tsankho?

10 Yehova amacita zinthu mopanda tsankho kwa alendo ake onse. (Aroma 2:11) Timamvetsa bwino mfundoyi tikaona mmene anacitila zinthu na Aisiraeli m’cipululu ca Sinai.

11 Yehova atapulumutsa anthu ake mu ukapolo ku Iguputo, anasankha ansembe kuti azitumikila pa cihema. Anasankhanso Alevi kuti azigwila nchito zina zopatulika za pa cihema. Koma kodi amene anali kutumikila pa cihema, kapena amene anali kukhala pafupi naco, anali kusamalidwa mwapadela? Ayi! Yehova alibe tsankho.

12. Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti ni wopanda tsankho pocita zinthu na mtundu wake watsopano? (Ekisodo 40:38) (Onaninso cithunzi.)

12 Mwisiraeli aliyense anali na mwayi wokhala pa ubwenzi wabwino na Yehova, mosasamala kanthu kuti anali kutumikila pa cihema, kapena anali kukhala kutali na cihemaco. Mwa citsanzo, Yehova anaonetsetsa kuti mtundu wonse wa Isiraeli unali kutha kuona cipilala ca mtambo, komanso cipilala ca moto zomwe zinali kukhala pamwamba pa cihema. (Ŵelengani Ekisodo 40:38.) Mtambo ukayamba kuyenda, ngakhale amene anali kukhala kutali na cihema anali kutha kuuona, ndipo anali kusonkhanitsa katundu wawo, kupasula matenti awo, na kuyendela pamodzi na mtundu wonse wa Isiraeli. (Num. 9:​15-23) Onse anali kumva kulila kosiyana kwa malipenga aŵili asiliva opeleka cizindikilo cakuti ayambe kuyenda. (Num. 10:2) Izi zionetsa kuti kukhala pafupi na cihema pakokha sikunali cizindikilo cakuti munthu ali pa ubwenzi wabwino na Yehova. M’malo mwake, munthu aliyense mu mtundu wa Yehova watsopanowo anali na mwayi wokhala mlendo Wake, na kudalila citsogozo komanso citetezo Cake. N’cimodzi-modzinso masiku ano, mosasamala kanthu za kumene timakhala, Yehova akhoza kutisamalila na kutiteteza.

Makonzedwe a Mulungu a cihema anaonetsa kuti iye alibe tsankho (Onani ndime 12)


MMENE YEHOVA AMAONETSELA KUPANDA TSANKHO MASIKU ANO

13. Kodi Yehova amaonetsa bwanji kuti alibe tsankho masiku ano?

13 Ena mwa anthu a Mulungu amakhala pafupi na likulu lathu, kapena pafupi na ofesi ya nthambi. Ndipo ena amatumikila pa maofesi amenewa. Conco, iwo amatengako mbali m’nchito zambili zimene zimacitika pa maofesi amenewa. Ndipo amakhala na mwayi woseŵenza na abale otsogolela. Pomwe ena akutumikila monga oyang’anila madela kapena m’mautumiki ena a padela. Ngakhale kuti simucitako mautumiki apadela amenewa, musakaikile zakuti Yehova amatikonda tonsefe, ndipo amatilandila monga alendo ake. Iye amatisamalila aliyense payekha-payekha. (1 Pet. 5:7) Atumiki onse a Yehova amalandila cakudya cauzimu, citsogozo, komanso citetezo cimene amafunikila.

14. Ni njila ina iti imene Yehova amaonetsela kuti ni wopanda tsankho?

14 Njila ina imene Yehova amaonetsela kuti alibe tsankho monga wotisamalila m’tenti yake, ni yakuti amaonetsetsa kuti Baibo ikupezeka kwa anthu onse kuzungulila dziko lonse lapansi. Malemba Opatulika analembedwa koyamba m’zinenelo zitatu: Ciheberi, Ciaramu, na Cigiriki. Kodi amene amakwanitsa kuŵelenga Baibo m’zinenelo zimenezi ali pa ubale wolimba na Yehova kuposa amene sakwanitsa kutelo? Ayi.—Mat. 11:25.

15. N’ciyani cimatsimikizila kuti Yehova alibe tsankho? (Onaninso cithunzi.)

15 Kukhala wovomelezeka kwa Yehova sikudalila maphunzilo amene tinapata kapena zinenelo zimene tidziŵa. Iye amapeleka nzelu zake kwa munthu aliyense padziko lapansi, kaya ni wophunzila kwambili kapena ayi. Baibo, Mawu ake ouzilidwa, yamasulidwa m’zinenelo masauzande. Conco, anthu kulikonse padziko lapansi angapindule na ziphunzitso zake, ndiponso angaphunzile kukhala mabwenzi ake.—2 Tim. 3:​16, 17.

Kodi kumasulidwa kwa Baibo m’zinenelo zambili kumaonetsa bwanji kuti Mulungu alibe tsankho? (Onani ndime 15)


KHALANIBE “WOVOMELEZEKA” KWA YEHOVA

16. Malinga na Machitidwe 10:​34, 35, tingatani kuti tikhalebe ovomelezeka kwa Yehova?

16 Ni mwayi wapadela zedi kulandilidwa monga mlendo m’tenti ya Yehova yophiphilitsa. Iye ni Mwininyumba wabwino kuposa wina aliyense, cifukwa ni wokoma mtima kopambana, wacikondi cacikulu, komanso woceleza ngako. Kuwonjezela apo, ni wopanda tsankho. Amalandila munthu aliyense monga mlendo wake mosasamala kanthu za kumene amakhala, kumene anakulila, kaya ni mwamuna kapena mkazi, maphunzilo ake, mtundu, fuko, kapena zaka zake. Ngakhale n’telo, iye amalandila anthu okhawo amene amatsatila miyeso yake.—Ŵelengani Machitidwe 10:​34, 35.

17. Tidzakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?

17 Monga ionetsela Salimo 15:​1, Davide anafunsa kuti: “Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo m’tenti yanu? Ndi ndani amene angakhale mʼphili lanu lopatulika?” Mouzilidwa na Yehova, Davide anayankha mafunso amenewa. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana zina mwa zinthu zimene tiyenela kucita kuti tikhalebe m’tenti ya Yehova.

NYIMBO 32 Ima Kumbali ya Yehova!