MAWU A M’BAIBO
Kodi Muli na Cikhulupililo?
Kuti tikondweletse Yehova tiyenela kukhala na cikhulupililo. Koma Baibo imati “si anthu onse amene ali ndi cikhulupililo.” (2 Ates. 3:2) Ponena mawu amenewa, mtumwi Paulo anali kunena za “anthu oipa kwambili” amene anali kumuzunza, ndipo anali kufuna kuti apulumutsidwe kwa iwo. Koma mfundo imene anakamba pa nkhani ya cikhulupililo ingagwilenso nchito kwa anthu onse. Anthu ena amanyalanyaza umboni wosatsutsika wakuti kuli Mulungu amene ni Mlengi wa zinthu zonse. (Aroma 1:20) Anthu ena anganene kuti ali na cikhulupililo cifukwa amakhulupilila cinthu cina cake, kapena munthu wina wake wamphamvu zapadela. Koma ici si cikhulupililo ceniceni.
Sitiyenela kukayikila kuti Yehova alikodi, komanso kuti amapeleka mphoto kwa anthu amene ali na cikhulupililo colimba mwa iye. (Aheb. 11:6) Cikhulupililo ni cimodzi mwa zipatso zimene mzimu wake woyela umabala. Kupemphela kwa Yehova kungatithandize kuti tilandile mzimu woyela. (Luka 11:9, 10, 13) Njila ina yapadela imene tingalandilile mzimu woyela ni kuŵelenga Mawu ake ouzilidwa. Ndiyeno tizisinkhasinkha zimene taŵelenga na kuzigwilitsa nchito. Tikatelo, mzimu wa Yehova udzatithandiza kukhala na cikhulupililo cimene cimam’kondweletsa.