NKHANI YOPHUNZILA 26
NYIMBO 8 Yehova Ndiye Pothaŵilapo Pathu
Pangani Yehova Kukhala Thanthwe Lanu
“Palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.”—1 SAM. 2:2.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Tidzaphunzila cifukwa cake Yehova amayelekezedwa na thanthwe, komanso mmene tingatsatilile makhalidwe ake amene amamupangitsa kukhala ngati thanthwe.
1. Malinga na Salimo 18:46, kodi Davide anayelekezela Yehova na ciyani?
TIKUKHALA m’dziko limene zinthu zosayembekezeka zingasokoneze umoyo wathu, ngakhale kuusinthilatu. Ndife oyamikila ngako kuti tili na Yehova amene tingathaŵileko tikakumana na mavuto! M’nkhani yapita tinakumbutsidwa kuti Yehova ni Mulungu wamoyo, ndipo nthawi zonse amakhala wokonzeka kutithandiza. Ndipo tinaphunzilanso kuti iye akatithandiza, timazindikila kuti “Yehova ndi wamoyo!” (Ŵelengani Salimo 18:46.) Komabe, Davide atangonena kuti “Yehova ndi wamoyo,” anakambanso kuti Yehova ni “Thanthwe langa.” N’cifukwa ciyani Davide anayelekezela Mulungu wamoyo na thanthwe, lomwe ni cinthu copanda moyo?
2. Tiphunzilenji pa mawu amene Davide ananena akuti Yehova ni “Thanthwe langa”?
2 M’nkhani ino, tikambilane cifukwa cake Yehova amayelekezeledwa na thanthwe, komanso zimene mawu ophiphilitsa amenewa amatiphunzitsa za iye. Tikambilanenso zimene tingacite kuti tizimuona ngati Thanthwe lathu. Cothela, tikambilane njila zimene tingatsatilile makhalidwe a Yehova amene amamupangitsa kukhala ngati thanthwe.
CIFUKWA CAKE YEHOVA AMACHEDWA THANTHWE
3. Ni pa zocitika ziti maka-maka pamene Baibo limaseŵenzetsa liwu lakuti “thanthwe”? (Onani ca pacikuto.)
3 Baibo imaseŵenzetsa mawu ophiphilitsa akuti “thanthwe” potithandiza kudziŵa makhalidwe amene Yehova ali nawo. Nthawi zambili, liwuli limapezeka m’mavesi amene alambili ake anali kum’tamanda kuti ni Mulungu amene alibe wofanana naye. Nthawi yoyamba imene Yehova anayelekezedwa na “Thanthwe” ni pa Deuteronomo 32:4. Komanso pa nthawi ina pomwe Hana anali kupemphela, ananena kuti “palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.” (1 Sam. 2:2) Nayenso Habakuku anacha Yehova kuti “Thanthwe langa.” (Hab. 1:12) Wolemba Salimo 73 anachula Mulungu kuti “thanthwe la mtima wanga.” (Sal. 73:26) Ngakhale Yehova amene, anadziyelekeza na thanthwe. (Yes. 44:8) Tiyeni tikambilane makhalidwe atatu amene amapangitsa Yehova kukhala ngati thanthwe, na kuona zimene tingacite kuti akhale “Thanthwe lathu.”—Deut. 32:31.
4. Kodi Yehova ni malo othaŵilapo a citetezo m’lingalilo lotani? (Salimo 94:22)
4 Yehova ni malo othaŵilapo acitetezo. Munthu angapeze citetezo ku thanthwe pamene wakumana na cimvula ca mphepo. Mofananamo, Yehova amatiteteza m’nthawi zovuta za moyo wathu. (Ŵelengani Salimo 94:22.) Iye amatithandiza kuti titeteze ubwenzi wathu na iye, ndipo amatitsimikizila kuti adzacotsapo mavuto onse amene tikukumana nawo pali pano. Kuwonjezela pamenepo, iye akulonjezanso kuti adzacotsapo zilizonse zimene zimatibweletsela nkhawa, komanso zimene zimaika moyo wathu pa ciopsezo.—Ezek. 34:25, 26.
5. Tingacite ciyani kuti tipange Yehova kukhala thanthwe lathu lothaŵilapo Lacitetezo?
5 Njila imodzi imene tingapangile Yehova kukhala thanthwe lathu lothaŵilapo Lacitetezo ni kupemphela kwa iye. Tikapemphela, Yehova amatipatsa “mtendele” wake umene umateteza mtima wathu na maganizo athu. (Afil. 4:6, 7) Ganizilani cocitika ca m’bale Artem, amene anaponyedwa m’ndende kaamba ka cikhulupililo cake. Ali m’ndende anali kufunsidwa mafunso mobweleza-bweleza na wapolisi wankhanza amene anali kumuvutitsa na kumuopseza. M’bale Artem anati, “N’nali kukhala na nkhawa nthawi zonse nikaitanidwa na wofufuzayo. . . Nthawi zonse n’nali kupemphela kwa Yehova, n’nali kumupempha kuti anipatse mtendele wa mumtima komanso nzelu. Zoyesa-yesa za wonifunsayo sizinaphule kanthu. . . Mwa thandizo la Yehova, zinali ngati naimilila mkati mwa mpanda wa miyala.”
6. N’cifukwa ciyani tiyenela kudalila Yehova? (Yesaya 26:3, 4)
6 Yehova ni wodalilika. Monga thanthwe losasunthika, nayenso Yehova amakhala pafupi kuti atithandize. Tiyenela kumudalila cifukwa iye ni “Thanthwe lamuyaya.” (Ŵelengani Yesaya 26:3, 4.) Yehova adzakhalapo nthawi zonse kuti asunge malonjezo ake, amve mapemphelo athu, komanso kuti atipatse zonse zimene tikufunikila. Tiyenelanso kumudalila cifukwa iye ni wokhulupilika kwa amene amamutumikila. (2 Sam. 22:26) Iye sadzaiŵala zimene timamucitila, ndipo nthawi zonse amatifupa.—Aheb. 6:10; 11:6.
7. Cimacitika n’ciyani tikadalila Yehova? (Onaninso cithunzi.)
7 Timapanga Yehova kukhala Thanthwe lathu tikamamudalila na mtima wathu wonse. Tili na cidalilo cakuti tikamamumvela ngakhale pa nthawi zovuta, tidzapindula. (Yes. 48:17, 18) Tikamaona kuti Yehova akutithandiza, timayamba kum’dalila kwambili. Zikatelo, timakhala okonzeka kum’dalila tikadzakumana na mavuto amene iye yekha ndiye angatithandize kuwapilila. Kaŵili-kaŵili tikakumana na mavuto amene palibe munthu angakwanitse kutithandiza m’pamene timazindikila kuti Yehova ni wodalilika. M’bale Vladimir anati, “Nthawi imene n’nali m’ndende yoyembekezela kuzengedwa mlandu, ni nthawi imene n’namva kuti nili pa ubwenzi wolimba na Yehova. N’naphunzila kudalila kwambili Yehova cifukwa n’nali kwa nekha-nekha, ndipo sinikanasintha zimene zinali kucitikazo.”
8. (a) N’cifukwa ciyani tinganene kuti Yehova sasintha? (b) Timapindula bwanji tikapanga Yehova kukhala Thanthwe lathu? (Salimo 62:6, 7)
8 Yehova sasintha. Yehova ali ngati thanthwe lalikulu lolimba limene silisintha. Makhalidwe ake na colinga cake sizisintha. (Mal. 3:6) Adamu na Hava atapanduka mu Edeni, Yehova sanasinthe colinga cake pa anthu. Monga momwe mtumwi Paulo analembela, Yehova “sangadzikane.” (2 Tim. 2:13) Izi zitanthauza kuti mulimonse mmene zingakhalile, kaya anthu ena acite zotani, Yehova sangasinthe makhalidwe ake, colinga cake, kapena miyeso yake. Popeza timam’dalila Mulungu wathu amene sasintha, tingayang’ane kwa iye kuti atipulumutse na kutithandiza panthawi yovuta.—Ŵelengani Salimo 62:6, 7.
9. Mwaphunzila ciyani pa cocitika ca mlongo Tatyana?
9 Timapanga Yehova kukhala thanthwe lathu mwa kusinkhasinkha mwakuya za umunthu wake, komanso za colinga cake kwa anthu. Kucita zimenezi kudzatithandiza kukhalabe odekha komanso okhulupilika pamene takumana na mavuto. (Sal. 16:8) Izi n’zimene zinacitikila mlongo Tatyana amene anaikidwa pa ukaidi wosacoka pa nyumba cifukwa ca cikhulupililo cake. Iye anati, “N’nali kungokhala nekha-nekha. Zinali zovuta poyamba. Nthawi zambili n’nali kukhala wopsinjika maganizo.” Komabe, iye anayamba kusinkhasinkha za Yehova na colinga cake, ndipo izi zinam’patsa mphamvu zopilila mavuto amene anali kukumana nawo. Iye anati, “Kumvetsa cifukwa cake izi zinali kucitika, kunanithandiza kukumbukila kuti n’nali mu mkhalidwe umenewu cifukwa n’nali kufuna kukondweletsa Yehova. Izi zanithandiza kuleka kuganizila kwambili za ine mwini.”
10. Kodi tingatani kuti tipange Yehova kukhala Thanthwe lathu pali pano?
10 Kutsogoloku, tidzakumana na mayeso amene adzafuna kudalila kwambili Yehova kuposa kale lonse. Ino ndiyo nthawi yofunika kulimbitsa cidalilo cathu mwa iye cakuti adzatipatsa zonse zofunikila kuti tipilile mokhulupilika. Tingacite bwanji zimenezi? Mwa kuŵelenga nkhani za m’Baibo na zocitika pa umoyo wa atumiki a Yehova a masiku ano. Pamene mucita zimenezi, onani mmene Yehova amaseŵenzetsela makhalidwe ake amene amamucititsa kukhala ngati thanthwe pothandiza atumiki ake. Muziziganizila mozama nkhani zimenezi. Kucita zimenezi kudzakuthandizani kupanga Yehova kukhala Thanthwe lanu.
TENGELANI MAKHALIDWE A YEHOVA AMENE AMAMUCITITSA KUKHALA NGATI THANTHWE
11. N’cifukwa ciani tiyenela kutengela makhalidwe a Yehova amene amamucititsa kukhala ngati thanthwe? (Onaninso danga lakuti “ Colinga Cimene Abale Acinyamata Angadziikile.”)
11 Taona makhalidwe amene amacititsa Yehova kukhala ngati thanthwe. Tiyeni tsopano tikambilane mmene tingatsatilile makhalidwe amenewa. Tikamayesetsa kucita zimenezi, tidzakhala okonzeka kulimbikitsa abale na alongo athu mumpingo. Mwa citsanzo, Yesu anapatsa Simoni dzina lakuti Kefa limene kumasulila kwake ni “Petulo.” Dzinali limatanthauza “Cidutswa ca Thanthwe.” (Yoh. 1:42) Izi zinaonetsa kuti Petulo adzalimbikitsa abale na alongo ake mu mpingo. Akulu mu mpingo amafotokozedwa kuti ali ngati “mthunzi wa thanthwe lalikulu.” Izi zionetsa mmene amatetezela abale na alongo mu mpingo. (Yes. 32:2) Komabe, mpingo umapindula ngati abale na alongo onse amatengela makhalidwe a Yehova amene amamucititsa kukhala ngati thanthwe.—Aef. 5:1.
12. Fotokozani zimene tingacite kuti tikhale malo othaŵilapo acitetezo kwa ena.
12 Khalani malo othaŵilapo acitetezo. Nthawi zina tingapeleke malo othaŵilapo kwa abale na alongo athu akakumana na matsoka a cilengedwe, zipolowe, kapena nkhondo. Pomwe zinthu zikuipilaipila ‘m’masiku otsiliza’ ano, mosakaikila tidzakhala na mipata yambili yothandizana wina na mnzake. (2 Tim. 3:1) Tingapelekenso citonthozo kwa abale na kuwalimbitsa kuuzimu. Njila imodzi imene tingacitile zimenezi ni mwa kuwapangitsa kuona kuti ni olandilidwa ku Nyumba ya Ufumu. Mwa kutelo, timathandiza kuti mpingo ukhale malo amene anthu amaonetselana cikondi komanso kulimbikitsana. Tikukhala m’dziko limene anthu ambili ni nkhanza, komanso opanda cikondi. Izi zingacititse abale na alongo athu kukhala na nkhawa komanso kuona ngati palibe amawakonda. Conco abale na alongo athu akapezeka pa misonkhano, tiyenela kuyesetsa kuwaonetsa cikondi na kuwalimbikitsa.
13. Kodi akulu angakhale bwanji malo othaŵilapo acitetezo kwa ena? (Onaninso cithunzi.)
13 Akulu angakhale malo othaŵilapo acitetezo kwa abale na alongo amene akukumana na mavuto akuthupi kapena auzimu. Pakacitika tsoka kapena wina akadwala mwadzidzidzi, akulu ndiwo amakhala patsogolo kupanga makonzedwe opelekela thandizo. Amapelekanso thandizo lauzimu. Cimakhala capafupi kwa abale na alongo kufikila mkulu ngati iye amadziŵika kuti ni wokoma mtima, wacifundo, komanso wokonzeka kuwamvetsela. Makhalidwe amenewa amathandiza ena kumva kuti amakondedwa, ndipo cimakhala cosavuta kwa iwo kutsatila malangizo a m’Baibo amene mkulu angawapatse.—1 Ates. 2:7, 8, 11.
14. Tingaonetse bwanji kuti ndife odalilika?
14 Khalani odalilika. Timafuna kuti ena azitidalila maka-maka pa nthawi zovuta. (Miy. 17:17) Tingatani kuti tizidziŵika kuti ndife odalilika? Tiyenela kuyesetsa mmene tingathele kutengela citsanzo ca Yehova. Mwa citsanzo, tiyenela kumasunga malonjezo athu, na kusunga nthawi. (Mat. 5:37) Kuwonjezela apo, tizipelekanso thandizo kwa ena pamene akufunikila thandizo. Cina, tizionetsetsa kuti takwanilitsa mbali imene tapatsidwa mumpingo mogwilizana na malangizo ake.
15. Kodi mpingo umapindula bwanji akulu akakhala odalilika?
15 Akulu odalilika ni dalitso ku mpingo. Motani? Ofalitsa amaona kuti ni otetezeka ngati nthawi iliyonse amakhala na ufulu wokamba na akulu, kuphatikizapo woyang’anila kagulu kawo ka ulaliki. Ofalitsa amaona kuti amakondedwa akadziŵa kuti akulu amakhala okonzeka kuwathandiza. Ndipo akulu akamapeleka uphungu wozikika m’Baibo komanso m’zofalitsa za kapolo wokhulupilika, m’malo mongokamba maganizo awo, alambili anzawo amawakhulupilila ngako. Abale na alongo amakhulupililanso akulu amene sauzako ena nkhani zaumwini zimene awauza, komanso amene amasunga malonjezo.
16. Timapindula bwanji tikakhala osasunthika? Nanga ena amapindula bwanji tikakhala osasunthika?
16 Khalani osasunthika. Tingakhale citsanzo cabwino kwa ena ngati timakhala osasunthika pocita zoyenela, na kupanga zisankho mogwilizana na mfundo za m’Baibo. Tikamalimbitsa cikhulupililo cathu na kuwonjezela cidziŵitso cathu, timakhala olimba kwambili m’coonadi. Ndipo sitikhala osakhazikika kapena otengeka-tengeka na ziphunzitso zabodza komanso kaganizidwe ka anthu a m’dzikoli. (Aef. 4:14; Yak. 1:6-8) Cifukwa cakuti timakhulupilila Yehova na malonjezo ake, timakhalabe odekha tikalandila uthenga woipa. (Sal. 112:7, 8) Timathanso kuthandiza amene akukumana na mavuto.—1 Ates. 3:2, 3.
17. Kodi akulu angathandize bwanji ena kukhala odekha?
17 Akulu ayenela kukhala oganiza bwino, adongosolo, ololela, komanso osacita zinthu mopitilila malile. Akulu amenewa amathandiza ena kukhala odekha, komanso kukhala na cikhulupililo colimba mwa Yehova, mwa ‘kugwila mwamphamvu mawu okhulupilika.’ (Tito 1:9; 1 Tim. 3:1-3) Mwa citsanzo cawo komanso mwa kucita maulendo aubusa, akulu amathandiza kuti ofalitsa azipezeka pa misonkhano nthawi zonse, azilalikila, komanso kuti azicita phunzilo la munthu mwini. Abale na alongo akakumana na mavuto, akulu angacite bwino kuwalimbikitsa kudalila Yehova na kuganizila za colinga cake.
18. N’cifukwa ciyani timafuna kutamanda Yehova na kupitiliza kumuyandikila? (Onaninso mbali yakuti “ Zimene Zingakuthandizeni Kuyandikila Yehova.”)
18 Pambuyo pokambilana makhalidwe ocititsa cidwi a Yehova m’nkhani ino, tinganene monga Mfumu Davide anakambila kuti: “Atamandike Yehova Thanthwe langa.” (Sal. 144:1) Yehova ni Mulungu amene tingadalile nthawi zonse. Pa umoyo wathu wonse, ngakhale titakalamba, tili na cifukwa cokambila kuti: “Iye ndi Thanthwe langa.” Tinganene zimenezi tili na cidalilo cakuti Yehova nthawi zonse adzatithandiza kukhalabe pa ubale wolimba na iye.—Sal. 92:14, 15.
NYIMBO 150 Funani Cipulumutso ca Mulungu
a MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo akufikila akulu momasuka pomwe ali m’Nyumba ya Ufumu.