Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

N’cifukwa ciyani ena amaganiza kuti mawu akuti “mudzawayang’anila” a pa Salimo 12:7 amanena za “Mawu a Yehova” ochulidwa mu vesi 6, pomwe Baibulo la Dziko Latsopano limaonetsa kuti mawuwa akunena za anthu “ovutika” ochulidwa mu vesi 5?

Nkhani yonse ionetsa kuti vesiyi ikunena za anthu.

Pa Salimo 12:​1-4, timaŵelengapo kuti “anthu okhulupilika athelatu pakati pa anthu.” Tiyeni tsopano tiunike mawu a pa Salimo 12:​5-7, mavesi amene akugwilizana na nkhaniyi.

“Yehova wanena kuti ‘cifukwa cakuti ovutika akupondelezedwa

Cifukwa ca kuusa moyo kwa anthu osauka,

Ndidzanyamuka ndi kucitapo kanthu,

‘Ndidzawapulumutsa kwa anthu amene akuwanyoza.’

Mawu a Yehova ndi oyela.

Ali ngati siliva woyengedwa mung’anjo yadothi nthawi zokwanila 7.

Inu Yehova mudzawayang’anila.

Aliyense wa iwo mudzamuteteza ku m’badwo uwu mpaka kalekale.”

Vesi 5 imanena kuti Mulungu adzapulumutsa anthu ovutika.

Vesi 6 imawonjezela kuti, “Mawu a Yehova ndi oyela. Ali ngati siliva woyengedwa.” Umu ni mmene Akhristu odzipeleka amaonela mawu a Mulungu.—Sal. 18:30; 119:140.

Tsopano ganizilani zimene Salimo 12:7 imanena. Imati, “Inu Yehova mudzawayang’anila, aliyense wa iwo mudzamuteteza ku m’badwo uwu mpaka kalekale.” Kodi mawuwa akunena za ndani?

Popeza kuti vesi 6 inena za “Mawu a Yehova,” ena angaganize kuti vesi 7 imatanthauza kuti Mulungu ‘adzateteza’ Mawu ake. Ndipo tidziŵa kuti Mulungu waiteteza Baibo ngakhale kuti anthu otsutsa ayesetsa kuti aiwononge komanso kuletsa kuti isafalitsidwe.—Yes. 40:8; 1 Pet. 1:25.

Komabe Yehova wakhala akutetezanso anthu ochulidwa mu vesi 5. Yehova wakhala akuthandiza anthu “ovutika” komanso amene “akupondelezedwa.” Ndipo adzapitiliza kutelo.—Yobu 36:15; Sal. 6:4; 31:​1, 2; 54:7; 145:20.

Ndiye, kodi mawu a mu vesi 7 amanena za ndani?

Mfundo ya pa Salimoli ionetsa kuti mawuwa amanena za anthu.

Kumayambililo kwa Salimo 12:​1, Davide anachula “anthu okhulupilika” amene ananamizidwa na anthu oipa. Ndiyeno m’mavesi otsatila timapeza mawu oonetsa kuti Yehova adzalanga anthu amene amaseŵenzetsa milomo yawo molakwika. Salimo limeneli limatitsimikizila kuti tiyenela kukhulupilila kuti Mulungu adzapulumutsa anthu ake cifukwa mawu ake ni oyela.

Conco vesi 7 imanena kuti Yehova ‘adzawayang’anila’ na ‘kuwateteza’ kutanthauza anthu amene akuvutitsidwa na anthu oipa.

Makope a Malemba a Ciheberi odalilika ya Amasoreti yamatsimikizilanso mfundo imeneyi. Pomasulila vesili, Baibo ya Cigiriki ya Septuagint inaseŵenzetsa mawu akuti mudzatiyang’anila komanso mudzatiteteza. Izi zionetsa kuti mawu amenewa amanena za anthu okhulupilika amene akuvutika komanso kupondelezedwa. Pomalizila, vesi 7 imanena kuti “aliyense wa” anthu okhulupilika adzatetezedwa “ku m’badwo uwu” wa anthu amene amalimbikitsa makhalidwe oipa. (Sal. 12:​7, 8) Baibo ya Ciaramu ya Tagamu, inamasulila mbali yoyambilila ya vesi 7 kuti, “Inu Ambuye, mudzayang’anila anthu olungama na kuwateteza ku m’badwo woipawu mpaka kalekale.” Izi zimangowonjezela umboni wakuti Salimo 12:7 simakamba za Mawu a Mulungu.

Pa cifukwa cimeneci, vesili limapatsa ciyembekezo “anthu okhulupilika” cakuti Mulungu adzacitapo kanthu.