Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ubwino—Kodi tingalikulitse bwanji khalidwe limeneli?

Ubwino—Kodi tingalikulitse bwanji khalidwe limeneli?

MWACIBADWA, aliyense wa ife amafuna kuti anthu ena azimuona kuti ni munthu wabwino. Komabe, kukhala munthu wabwino masiku ano n’kovuta. Zili conco cifukwa anthu ambili amene tikhala nawo ni “osakonda zabwino.” (2 Tim. 3:3) Iwo amakana kutsatila miyezo ya Yehova ya cabwino na coipa. Koma adzipangila miyezo yawo, moti amaona kuti: “Cabwino n’coipa ndipo coipa n’cabwino.” (Yes. 5:20) Cinanso, zingakhale zovuta kukhala munthu wabwino cifukwa ndife opanda ungwilo, komanso mwina cifukwa ca mmene umoyo wathu unalili kumbuyoku. Conco, tingamvele monga mmene mlongo Anne * anamvelela. Olo kuti watumikila Yehova kwa zaka zambili, iye anati: “Nimakayikila zoti ndine munthu wabwino.”

Koma cokondweletsa n’cakuti, tonse tingathe kukulitsa khalidwe la ubwino, cifukwa ni limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyela wa Mulungu umabala. Ndipo mzimu umenewu ni wamphamvu kwambili, cakuti ungagonjetse zopinga zilizonse zimene zingatilepheletse kukulitsa khalidweli. Lomba tiyeni tikambilane zambili zokhudza khalidweli, komanso mmene tingalionetsele mokulilapo.

KODI UBWINO N’CIANI?

Kukamba mwacidule, ubwino umatanthauza kukhala wabwino, wopanda coipa ciliconse. Munthu wabwino amakhala na makhalidwe abwino, komanso amacita zinthu zoyenela. Nthawi zonse, iye amayesetsa kuthandiza ena na kuwacitila zinthu zabwino.

Mwacionekele, mumaona kuti anthu ena amakonda kucitila zabwino anthu a m’banja lawo komanso mabwenzi awo. Koma kukhala munthu wabwino kumaphatikizapo zambili kuposa pamenepa. Kukamba zoona, sitingakwanitse kucita zabwino nthawi zonse. Ndiye cifukwa cake Baibo imati: “Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amacita zabwino zokhazokha osacimwa.” (Mlal. 7:20) Komanso, mtumwi Paulo anakamba moona mtima kuti: “Ndikudziwa kuti mwa ine, ndikunenatu za m’thupi langa, simukhala kanthu kabwino.” (Aroma 7:18) Conco, kuti tikulitse khalidwe la ubwino, n’zoonekelatu kuti tifunika kuphunzila kwa Yehova, amene ndiye Gwelo la khalidweli.

‘YEHOVA NI WABWINO’

Yehova Mulungu ndiye amaika miyezo ya cabwino. Ponena za iye, Baibo imati: “Inu ndinu wabwino ndipo mukucita zabwino. Ndiphunzitseni malamulo anu.” (Sal. 119:68) Tsopano tiyeni tikambilane mfundo ziŵili zokhudza ubwino wa Yehova zimene zachulidwa m’vesili.

Yehova ni wabwino. Yehova ni wabwino kwambili, ndipo makhalidwe ake onse ni abwino. Ganizilani zimene zinacitika pamene iye anauza Mose kuti: “Ineyo ndidzakuonetsa ubwino wanga wonse.” Pamene Yehova anaonetsa Mose ulemelelo wake, komanso ubwino wake, Mose anamva mawu akuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi coonadi. Wosungila mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukila zolakwa ndi macimo, koma wosalekelela konse wolakwa osam’langa.” (Eks. 33:19; 34:6, 7) Mawu amenewa aonetsa kuti Yehova ni wabwino pa ciliconse, komanso m’makhalidwe ake onse. Ngakhale kuti pa anthu onse, Yesu anali wa khalidwe labwino kwambili, iye anati: “Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.”—Luka 18:19.

Timaona ubwino wa Yehova m’zinthu zimene analenga

Yehova amacita zabwino. Zonse zimene Mulungu amacita zimaonetsa kuti ni wabwino. Baibo imati: “Yehova amakomela mtima aliyense, ndipo nchito zake zonse amazicitila cifundo.” (Sal. 145:9) Popeza kuti Yehova ni wabwino komanso wopanda tsankho, amapatsa anthu moyo na zinthu zocilikiza moyo wawo. (Mac. 14:17) Iye amaonetsanso kuti ni wabwino, mwa kutikhululukila zolakwa zathu. Wamasalimo analemba kuti: “Inu Yehova ndinu Mulungu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.” (Sal. 86:5) Conco, ndife otsimikiza kuti: “Yehova samana anthu oyenda mosalakwa cinthu ciliconse cabwino.”—Sal. 84:11.

“PHUNZILANI KUCITA ZABWINO”

Popeza tinalengedwa m’cifanizilo ca Mulungu, n’zotheka kukhala anthu abwino komanso kucita zabwino. (Gen. 1:27) Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti: “Phunzilani kucita zabwino.” (Yes. 1:17) Koma kodi tingacite ciani kuti tiphunzile kucita zabwino? Tiyeni tikambilane njila zitatu zimene tingacitile zimenezi.

Yoyamba, tizipempha mzimu woyela, umene udzatithandiza kukhala anthu abwino monga mmene Mulungu amafunila. (Agal. 5:22) Inde, mzimu wa Mulungu ungatithandize kuyamba kukonda zabwino na kuzonda zoipa. (Aroma 12:9) Ndipo Baibo imakamba kuti Yehova ‘angatilimbitse mu nchito yabwino iliyonse ndiponso m’mawu.’—2 Ates. 2:16, 17.

Yaciŵili, tiyenela kumaŵelenga Mawu a Mulungu ouzilidwa. Tikatelo, Yehova adzatiphunzitsa “njila yonse ya zinthu zabwino,” na kutikonzekeletsa kugwila “nchito iliyonse yabwino.” (Miy.  2:9; 2 Tim. 3:17) Tikamaŵelenga Baibo na kusinkha-sinkha zimene taŵelenga, ndiye kuti tikuika m’mitima yathu zinthu zabwino zokhudza Yehova na cifunilo cake. Mwakutelo, timawonjezela cuma camtengo wapatali m’nkhokwe yathu ya cidziŵitso, cimene tingakaciseŵenzetse kutsogolo—Luka 6:45; Aef. 5:9.

Yacitatu, tiyenela kuyesetsa ‘kutsanzila zabwino.’ (3 Yoh. 11) M’Baibo, muli zitsanzo zimene tingatengele pa nkhani imeneyi. Citsanzo cabwino kwambili ni ca Yehova na Yesu. Koma mulinso anthu ena amene anali kudziŵika kuti anali abwino. Mwina tingaganizileko za Tabita na Baranaba. (Mac. 9:36; 11:22-24) Tingapindule na citsanzo cawo cabwino mwa kuŵelenga Baibo kuti tiwadziŵe bwino, komanso kuti tidziŵe zimene anacita pothandiza ena. Ndiyeno, ganizilani zimene imwe mungacite kuti muthandize ena m’banja mwanu kapena mumpingo. Mungacite bwino kuganizilanso mapindu amene Tabita na Baranaba anapeza cifukwa cocitila anthu ena zabwino. Ndipo na ife tingapindule ngati titengela citsanzo cawo.

Palinso zitsanzo za Akhristu amakono amene amacita zabwino. Mwacitsanzo, ganizilani za akulu akhama mumpingo, amene ni anthu ‘okonda zabwino.’ Ganizilaninso za alongo okhulupilika, amene mwa zocita na zokamba zawo, amaonetsa kuti ni “aphunzitsi a zinthu zabwino.” (Tito 1:8; 2:3) Mlongo wina, dzina lake Roslyn, anati: “Mnzanga amayesetsa kuthandiza anthu mumpingo na kuwalimbikitsa. Amaganizila mmene zinthu zilili mu umoyo wawo, ndipo nthawi zambili amawapatsako mphatso, kapena kuwathandiza m’njila zina. Nimaona kuti iye ni munthu wabwino kwambili.”

Yehova amatilimbikitsa kuti tiyenela ‘kuyesetsa kucita zabwino.’ (Amosi 5:14) Kucita zimenezi kudzatisonkhezela kukonda miyezo yake, komanso kupitiliza kucita zabwino.

Timayesetsa kukhala anthu abwino na kucitila ena zabwino

Kukhala munthu wabwino, sikulila kucitila ena zinthu zazikulu, kapena kuwapatsa mphatso zodula. Mwacitsanzo, kuti mbewu ikule bwino sitimaithilila cabe kamodzi na vimadzi vambili-mbili. Koma timaithilila kaŵili-kaŵili na madzi asaizi. Mofananamo, ngati kaŵili-kaŵili timacitila anthu ena zinthu zooneka ngati zazing’ono koma zothandiza, tidzaonetsa kuti ndife anthu abwino.

Baibo imatilimbikitsa kukhala ‘okonzeka’ kucitila ena zabwino. (2 Tim. 2:21; Tito 3:1) Ngati timakhala chelu kuona mmene zinthu zilili mu umoyo wa ena, tidzapeza njila yowacitila ‘zabwino zowalimbikitsa.’ (Aroma 15:2) Izi zingaphatikizepo kuwapatsako zinthu zimene tili nazo. (Miy. 3:27) Mwacitsanzo, tingaitanile ena ku cakudya cosalila zambili kapena ku maceza olimbikitsa. Ngati tamvela kuti winawake wadwala, tingapite kukamuona, kumulembela kalata, kapena kumutumila foni. Inde, pali mipata yambili yokambila mawu “alionse olimbikitsa monga mmene kungafunikile, kuti asangalatse owamva.”—Aef. 4:29.

Mofanana na Yehova, timayesetsa kucitila anthu onse zabwino. Timapewa tsankho. Njila yabwino yoonetsela kuti tilibe tsankho, ni mwa kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu kwa anthu onse. Monga mmene Yesu analamulila, timayesetsa kucita zabwino ngakhale kwa anthu amene amatizonda. (Luka 6:27) Tifunika kukomela mtima anthu ena komanso kuwacitila zinthu zabwino, cifukwa “palibe lamulo loletsa zinthu zotelezi.” (Agal. 5:22, 23) Ngati tiyesetsa kucitila anthu zabwino ngakhale pamene tikuvutika kapena kutsutsidwa, tingasonkhezele ena kuphunzila coonadi na kulemekeza Mulungu.—1 Pet. 3:16, 17.

TIMAPEZA MAPINDU NGATI TICITILA ENA ZABWINO

Baibo imati: “Munthu wabwino adzakhutila ndi zotsatila za zocita zake.” (Miy. 14:14) Kodi ni mapindu ena ati amene timapeza ngati ticitila ena zabwino? Nthawi zambili anthu tikawacitila zabwino, nawonso amaticitila zabwino. (Miy. 14:22) Ngakhale asaticitile zabwino, ife tiyenela kupitiliza kuwacitila zabwino. Izi zingathandize kuti asinthe maganizo awo na kuyamba kuticitila zabwino.—Aroma 12:20.

Cinanso, munthu akaleka kucita zoipa na kuyamba kucita zabwino, amapindula. Abale na alongo ambili angacitile umboni mfundo imeneyi. Mwacitsanzo, ganizilani za mlongo wina dzina lake Nancy. Iye anati: “Pamene n’nali kukula n’nali munthu wopupuluma, waciwelewele, komanso wopanda ulemu. Koma pamene n’naphunzila miyezo ya Mulungu ya cabwino na coipa na kuyamba kuiseŵenzetsa, n’nakhala wacimwemwe. Tsopano nimadziona kuti ndine munthu wolongosoka.”

Cifukwa cacikulu cimene tiyenela kukulitsila khalidwe la ubwino n’cakuti, khalidweli limakondweletsa Yehova. Ngakhale anthu ambili asaone zimene timacita, Yehova amaona. Iye amaona zabwino zonse zimene timacita komanso zimene timaganiza. (Aef. 6:7, 8) Kodi zotulukapo zake zimakhala zotani? Baibo imati: “Munthu wabwino Yehova amakondwela naye.” (Miy. 12:2) Conco, tiyeni tipitilize kukulitsa khalidwe la ubwino. Yehova walonjeza kuti: “Aliyense wocita zabwino . . . adzalandila ulemelelo, ulemu ndi mtendele.”—Aroma 2:10.

^ ndime 2 Maina ena asinthidwa.