Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Yehova Amaona Kuti “Ameni” Wanu ni Wofunika

Yehova Amaona Kuti “Ameni” Wanu ni Wofunika

YEHOVA amaona kuti kulambila kwathu n’kofunika. Iye ‘amachela khutu ndi kumvetsela’ atumiki ake akamakamba. Ndipo amayamikila zilizonse zimene timacita pom’tamanda, ngakhale zooneka ngati zazing’ono. (Mal. 3:16) Mwacitsanzo, ganizilani za liwu limene timalikamba kaŵili-kaŵili. Liwu lake ni lakuti “ameni.” Kodi Yehova amaonadi kuti kukamba “ameni” pambuyo pa pemphelo n’kofunika? Inde, amaona conco! Kuti tidziŵe cifukwa cake, tiyeni tikambilane zimene mawuwa amatanthauza, komanso mmene amaseŵenzetsedwela m’Baibo.

“ANTHU ONSE AYANKHE KUTI, ‘ZIKHALE MOMWEMO!’”

Liwu la cizungu lakuti “ameni” limatanthauza “zikhale momwemo” kapena kuti “ndithudi.” Liwu limeneli linacokela ku liwu la Ciheberi limene limatanthauza “khala wokhulupilika” kapena “khala wodalilika.” Ndipo nthawi zina, linali kugwilitsidwa nchito poweluza milandu. Mwacitsanzo, munthu akapanga lumbilo linalake, anali kukamba kuti “ameni,” pofuna kuonetsa kuti zimene wakamba ni zoona. Zinali kuonetsanso kuti anali wokonzeka kukumana na zilizonse zimene zingacitike cifukwa ca zimene wakamba. (Num. 5:22) Kukamba mawu amenewa pagulu, kunali kum’limbikitsa kusunga lonjezo lake.—Neh. 5:13.

Citsanzo cocititsa cidwi ca mmene liwu lakuti “ameni” linagwilitsidwila nchito, cili pa Deuteronomo caputa 27. Aisiraeli ataloŵa M’dziko Lolonjezedwa, anasonkhana pakati pa Phili la Ebala na Phili la Gerizimu kuti amvetsele pamene Cilamulo cinali kuŵelengedwa. Kuwonjezela pa kumvetsela, anafunikanso kuvomeleza zolembedwa m’Cilamuloco. Anacita izi mwa kukamba mawu akuti “Zikhale momwemo!” kapena kuti “Ameni!” pambuyo pakuti zotulukapo za kusamvela Cilamulo zaŵelengedwa. (Deut. 27:15-26) Ganizilani cabe mmene zinalili panthawiyo pamene cikhamu ca amuna, akazi, ndi ana cinali kuyankhila pamodzi mokweza kuti “Ameni!” (Yos. 8:30-35) Mwacionekele, iwo sanaiŵale mawu amene anakamba pa tsikulo. Ndipo anasungadi lonjezo lawo, cifukwa Baibo imati: “Aisiraeli anapitiliza kutumikila Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akulu amene anapitiliza kukhalabe ndi moyo Yoswa atamwalila, omwe ankadziwa nchito zonse zimene Yehova anacitila Aisiraeli.”—Yos. 24:31.

Nayenso Yesu anali kuseŵenzetsa mawu akuti “ameni” pofuna kutsimikizila kuti zimene wakamba n’zoona. Koma anali kucita izi mosiyanako. M’malo moseŵenzetsa liwu lakuti “ameni” poyankha zimene zakambidwa kale, Yesu anali kukamba liwu lakuti “ameni” (lomasulidwa kuti “ndithu” m’Cinyanja), poyamba kukamba mfundo ya coonadi. Nthawi zina, iye anali kubweleza liwuli, amvekele “ameni ameni,” ndipo mawuwa ndiwo anamasulidwa kuti “ndithu” kapena “ndithudi” m’Cinyanja. (Mat. 5:18; Yoh. 1:51) Pokamba mwanjila imeneyi, Yesu anali kutsimikizila omvetsela ake kuti zimene anali kukamba ni coonadi ceni-ceni. Iye anali kukamba motsimikiza conco cifukwa anapatsidwa udindo wokwanilitsa malonjezo onse a Mulungu.—2 Akor. 1:20; Chiv. 3:14.

“ANTHU ONSE ANANENA KUTI, ‘AMENI!’ N’KUTAMANDA YEHOVA”

Aisiraeli anali kugwilitsilanso nchito liwu lakuti “ameni” popemphela kwa Yehova na kum’tamanda. (Neh. 8:6; Sal. 41:13) Mwa kukamba mawuwa pambuyo pomvetsela pemphelo, iwo anali kuonetsa kuti agwilizana na zimene zakambidwa m’pemphelolo. Mwanjila imeneyi, onse opezekapo anali kukhala na mwayi wotengako mbali pa kulambila Yehova, ndipo izi zinali kuwathandiza kukhala acimwemwe. Zotele n’zimene zinacitika pamene Mfumu Davide anabweletsa Likasa la Yehova ku Yerusalemu. Panthawiyo, Aisiraeli anacita cikondwelelo. Pa cikondweleloco, Davide anapeleka pemphelo lokhudza mtima lokonzedwa monga nyimbo. Pemphelolo linalembedwa pa 1 Mbiri 16:8-36. Anthu amene analipo, anakhudzidwa kwambili na mawu a m’pemphelolo cakuti “anthu onse ananena kuti, “Ame!” n’kutamanda Yehova.” Inde, iwo anakondwela kulambila Yehova pamodzi.

Nawonso Akhristu a m’nthawi ya atumwi anali kukamba mawu akuti “ameni” potamanda Yehova. Ndipo olemba Baibo, nthawi zambili anali kuseŵenzetsa mawuwa polemba makalata opita ku mipingo. (Aroma 1:25; 16:27; 1 Pet. 4:11) Buku la Chivumbulutso limakamba kuti zolengedwa zauzimu kumwamba zimapeleka ulemelelo kwa Yehova mwa kukamba kuti: “Ame! Tamandani Ya!” (Chiv. 19:1, 4) Komanso Akhristu a m’nthawi ya atumwi, pa misonkhano yawo anali kukonda kukamba kuti “Ameni” pambuyo pa pemphelo. (1 Akor. 14:16) Komabe, sanali kukamba mawu amenewa mwamwambo cabe.

CIFUKWA CAKE KUKAMBA KUTI “AMENI” N’KOFUNIKA

Pamene takambilana mmene atumiki a Yehova anali kuseŵenzetsela mawu akuti “ameni”, tingathe kuona cifukwa cake kukamba mawu amenewa kumapeto kwa pemphelo n’kofunika. Tikakamba mawuwa kumapeto kwa pemphelo laumwini, timaonetsa kuti tatsimikizila kuti zimene takamba n’zimenedi tinafuna kukamba. Ndipo tikayankha kuti “ameni” pambuyo pa pemphelo la pagulu, ngakhale ca mumtima cabe, timaonetsa kuti tagwilizana na zimene zakambidwa. Tiyeni tikambilane zifukwa zina zimene tiyenela kukambila “ameni” pambuyo pa pemphelo.

Timaonetsa kuti tili chelu polambila Yehova. Pemphelo likamapelekedwa, timaonetsa kuti tikulambila Yehova mwa kukamba “ameni” komanso mwa kuonetsa khalidwe laulemu. Timafuna kuti “ameni” wathu akhale watanthauzo. Conco, timayesetsa kumvetsela mwachelu pamene pemphelo likupelekedwa komanso kuonetsa khalidwe laulemu.

Timakhala ogwilizana pa kulambila kwathu. Zimene zimakambidwa m’pemphelo la pagulu, zimakhala zokhudza mpingo wonse. (Mac. 1:14; 12:5) Conco, tikayankhila pamodzi ndi abale na alongo athu kuti “ameni”, zimaonetsa kuti ndife ogwilizana kwambili. Kaya tikambe “ameni” mokweza mawu kapena ca mumtima,” Yehova amakhala na cifukwa cabwino cocitila zinthu mogwilizana na mapemphelo athu.

Tikakamba kuti “ameni,” Yehova amatamandika

Timatamanda Yehova. Yehova amaona zilizonse zimene timacita pom’lambila, olo zikhale zocepa. (Luka 21:2, 3) Amaona zimene zili mumtima mwathu komanso zolinga zathu. Ngakhale pamene timvetsela misonkhano kupitila pa foni, tiyenela kukhala otsimikiza kuti ngati takamba kuti “ameni,” Yehova amamvela ndiponso amayamikila. Tikakamba mawuwa, ndiye kuti tikutamanda Yehova mogwilizana ndi abale athu amene ali ku misonkhano.

Inde, kukamba “ameni” pambuyo pa pemphelo, kungaoneke monga kosafunikila kweni-kweni. Koma n’kofunika kwambili. Buku lina lokamba za Baibo linati: “Mwa kukamba liwu limodzi limeneli” pambuyo pa pemphelo, atumiki a Mulungu amaonetsa kuti ‘akutsimikizila zimene zakambidwa, kugwilizana nazo, komanso kuti ali na ciyembekezo codalilika’ cakuti zidzayankhidwa. Lekani kuti “ameni” wathu akhale wokondweletsa kwa Yehova nthawi zonse.—Sal. 19:14.