NKHANI YOPHUNZILA 12
Kodi Nthawi Yoyenela Kukamba ni Iti?
“Ciliconse cili ndi nthawi yake, . . . Nthawi yokhala cete ndi nthawi yolankhula.”—MLALIKI 3:1, 7.
NYIMBO 124 Tikhale Okhulupilika Nthawi Zonse
ZIMENE TIKAMBILANE *
1. Tiphunzilapo ciani pa Mlaliki 3:1, 7?
ENA a ife timakonda kukamba. Koma ena ni a zii. Malinga na lemba limene pazikidwa nkhani ino, pali nthawi yoyenela kukamba na nthawi yoyenela kukhala cete. (Ŵelengani Mlaliki 3:1, 7.) Komabe, abale na alongo ena ni a zii kwambili, ndipo timafuna kuti azimasukako kukamba. Koma ena amakamba-kamba kwambili, ndipo timafuna kuti azikhalako cete nthawi zina.
2. Kodi n’ndani woyenela kutipatsa malangizo ponena za nthawi yoyenela kukamba komanso mmene tiyenela kukambila?
2 Kukamba ni mphatso yocokela kwa Yehova. (Eks. 4:10, 11; Chiv. 4:11) Kupitila m’Mawu ake, Yehova amatithandiza kudziŵa mmene tingaseŵenzetsele bwino mphatso imeneyi. M’nkhani ino, tikambilana zitsanzo za m’Malemba zimene zidzatithandiza kudziŵa nthawi yoyenela kukamba na nthawi yoyenela kukhala cete. Tidzaonanso mmene zokamba zathu kwa ena zimam’khudzila Yehova. Koma coyamba, tiyeni tikambilane za nthawi yoyenela kukamba.
NI NTHAWI ITI PAMENE TIYENELA KUKAMBA?
3. Malinga na Aroma 10:14, ni nthawi iti pamene tiyenela kuuzako ena za Yehova na Ufumu wake?
3 Nthawi zonse, tiyenela kukhala okonzeka kuuzako ena za Yehova na Ufumu wake. (Mat. 24:14; ŵelengani Aroma 10:14.) Tikatelo, ndiye kuti tikutengela citsanzo ca Yesu. Cifukwa cina cacikulu cimene Yesu anabwelela pa dziko lapansi ni kudzaphunzitsa ena coonadi ponena za Atate wake. (Yoh. 18:37) Koma tifunika kukumbukila kuti kudziŵa mokambila bwino uthengawo n’kofunikanso. Conco, pamene tikambilana na ena za Yehova, tifunika kukambilana nawo “ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambili.” Tiyenelanso kuonetsa kuti timawaganizila ndipo timalemekeza zimene amakhulupilila. (1 Pet. 3:15) Tikacita zimenezi, ndiye kuti sitidzangokamba cabe na munthu za Yehova, koma tidzayesetsanso kumuphunzitsa, mwina mpaka kumufika pamtima.
4. Mogwilizana na Miyambo 9:9, kodi kupeleka uphungu kwa ena kungawathandize bwanji?
Miyambo 9:9.) Tifunika kulimba mtima kupeleka uphungu kwa munthu pakakhala pofunikila. N’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika kwambili? Kuti tipeze yankho, tiyeni tikambilane zitsanzo ziŵili zosiyana. M’citsanzo coyamba, mwamuna wina anafunika kupatsa uphungu ana ake. Ndipo m’citsanzo caciŵili, mayi wina analimba mtima kuuza munthu amene anali kudzakhala mfumu kuti wapanga cosankha colakwika.
4 Akulu sayenela kuzengeleza kukamba na m’bale kapena mlongo amene akufunikila uphungu. Koma ayenela kupeza nthawi yabwino yokamba naye kuti asamucititse manyazi. Angafunike kuyembekezela mpata wabwino kuti amupatse uphunguwo ali yekha. Akulu nthawi zonse amayesetsa kukamba mosamala kuti asamucotsele ulemu munthu. Koma sazengeleza kumuuza mfundo za m’Baibo zimene zingam’thandize kucita zinthu mwanzelu. (Ŵelengani5. Ni nthawi iti pamene Mkulu wa Ansembe Eli analephela kupeleka uphungu wamphamvu?
5 Mkulu wa Ansembe Eli anali ndi ana aŵili aamuna amene anali kuwakonda ngako. Koma anawo sanali kulemekeza Yehova. Iwo anali na udindo waukulu pa cihema, wotumikila monga ansembe. Koma anali kugwilitsila nchito udindo wawo molakwika. Sanali kulemekeza nsembe zopelekedwa kwa Yehova ngakhale pang’ono. Ndiponso anali kucita khalidwe la ciwelewele motailila. (1 Sam. 2:12-17, 22) Malinga na Cilamulo ca Mose, ana a Eli anafunika kuphedwa. Koma Eli anali kungowalekelela, osawadzudzula mwamphamvu. Ndipo anawalola kupitiliza kutumikila pa cihema. (Deut. 21:18-21) Kodi Yehova anamvela bwanji na zimene Eli anacita? Iye anauza Eli kuti: ‘N’cifukwa ciani ukulemekezabe ana ako koposa ine?’ Conco, Yehova anaona kuti amuna aŵili oipawo afunika kuphedwa.—1 Sam. 2:29, 34.
6. Tiphunzilapo ciani pa nkhani ya Eli?
6 Tiphunzilapo mfundo yofunika kwambili pa nkhani ya Eli. Mfundo yake ni yakuti tikadziŵa kuti mnzathu kapena m’bululu wathu waphwanya lamulo linalake la Mulungu, tifunika kukamba naye molimba mtima na kum’kumbutsa zimene malamulo a Yehova amakamba. Ndiyeno, tiyenela kuonetsetsa kuti walandila thandizo lofunikila kwa akulu amene amaimilako Yehova. (Yak. 5:14) Sitingafune olo pang’ono kukhala ngati Eli mwa kulemekeza kwambili mnzathu kapena m’bululu wathu kuposa Yehova. Pamafunika kulimba mtima kuti tikambe na munthu amene akufunikila uphungu. Ndipo kucita zimenezo kungakhale na zotulukapo zabwino. Onani kusiyana pakati pa citsanzo ca Eli ndi ca mayi wina waciisiraeli, dzina lake Abigayeli.
7. N’cifukwa ciani Abigayeli anapita kukakamba na Davide?
7 Abigayeli anali mkazi wa munthu wina wolemela, dzina lake Nabala. Pamene Davide na asilikali ake anali kuthawa Mfumu Sauli, anakhalako kwa kanthawi na abusa a Nabala, ndipo anali kuteteza nkhosa za Nabala kwa acifwamba. Koma kodi Nabala anayamikila thandizo lawo? Iyayi. Davide atatumiza asilikali ake kwa Nabala kuti akapempheko cakudya cocepa na madzi, iye anakwiya na kuyamba kunyoza na kuzazila asilikaliwo. (1 Sam. 25:5-8, 10-12, 14) Davide anakwiya kwambili na zimenezi moti anakonza zakuti akaphe mwamuna aliyense wa m’nyumba ya Nabala. (1 Sam. 25:13, 22) Koma kodi n’ciani cinathandiza kuti zoopsa zimenezi zisacitike? Abigayeli anazindikila kuti imeneyo inali nthawi yoyenela kukamba. Conco, molimba mtima anapita kukakumana na gulu la asilikali 400 onyamula zida, anjala komanso aukali, mpaka anakwanitsa kukamba na Davide.
8. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Abigayeli?
8 Abigayeli atakumana na Davide, anakamba naye molimba mtima, mwaulemu, ndiponso momufika pamtima. Olo kuti si ndiye analakwitsa, anapepesa kwa Davide. Anakamba kuti anali kudziŵa kuti Davide ni munthu wa makhalidwe abwino ndipo adzacita zoyenela. Abigayeli anadalila Yehova kuti am’thandize. (1 Sam. 25:24, 26, 28, 33, 34) Mofanana na Abigayeli, tikaona kuti wina wayamba kuyenda pa njila yolakwika, tifunika kulimba mtima kukamba naye. (Sal. 141:5) Tifunika kukamba naye mwaulemu koma molimba mtima. Ngati tipeleka uphungu mwacikondi kwa munthu wofunikila uphungu, timaonetsa kuti ndife bwenzi leni-leni.—Miy. 27:17.
9-10. Kodi akulu ayenela kukumbukila ciani pamene akupatsa ena uphungu?
9 N’kofunika kwambili kuti akulu azilimba mtima kupeleka uphungu kwa abale na alongo mu mpingo amene ayamba kuyenda pa njila yolakwika. Agal. 6:1) Akulu amazindikila kuti nawonso ni opanda ungwilo, ndipo angafunike kupatsidwa uphungu nthawi zina. Koma salola zimenezi kuwalepheletsa kudzudzula anthu amene akufunikila uphungu. (2 Tim. 4:2; Tito 1:9) Popatsa munthu uphungu, akulu amayesetsa kuseŵenzetsa mphatso yawo ya kulankhula kuti alangize munthuyo mwaluso komanso moleza mtima. Iwo amam’konda m’bale wawoyo, ndipo cikondi n’cimene cimawasonkhezela kuti am’thandize. (Miy. 13:24) Koma cacikulu cimene amacitila zimenezi ni kufuna kulemekeza Yehova mwa kucilikiza malamulo ake komanso kuteteza mpingo.—Mac. 20:28.
(10 Pofika pano, takambilana za nthawi pamene tiyenela kukamba. Komabe, nthawi zina timafunika kungokhala cete osakamba ciliconse. Kodi ni zinthu ziti zimene zingapangitse kuti cikhale covuta kukhala cete pa nthawi ngati zimenezo?
NI NTHAWI ITI PAMENE TIYENELA KUKHALA CETE?
11. Kodi Yakobo anaseŵenzetsa fanizo lotani? Nanga n’cifukwa ciani n’loyenela?
11 Nthawi zina, zimakhala zovuta kulamulila lilime lathu. Wolemba Baibo Yakobo anaseŵenzetsa fanizo loyenelela pofotokoza vuto limeneli. Iye anati: “Ngati wina sapunthwa pa mawu, ameneyo ndi munthu wangwilo, ndipo akhoza kulamulilanso thupi lake lonse. Tikamangilila zingwe pakamwa pa mahachi kuti atimvele, timatha kulamulilanso matupi awo onse.” (Yak. 3:2, 3) Zingwe zoyendetsela hosi amazimangilila kumutu kwa hosi ndipo mbali ina yocepa amaikoletsa kukamwa kwake. Poseŵenzetsa zingwezo, woyendetsa hosi amatha kuiwongolela kapena kuiimitsa. Ngati zingwezo zataika m’manja mwake cifukwa cosazigwilitsa, hosiyo ingayambe kuyenda mosalamulilika, ndipo ingadzivulaze komanso kupweteka woyendetsayo. N’cimodzi-modzi na lilime lathu. Tikalephela kulilamulila, likhoza kutibweletsela mavuto ambili. Tiyeni tikambilane zocitika zingapo pamene tiyenela kulamulila lilime lathu na kukhala cete.
12. Ni nthawi iti pamene tiyenela kulamulila lilime lathu na kukhala cete?
12 Kodi mumacita ciani mukadziŵa kuti m’bale kapena mlongo winawake ali na nkhani yacinsinsi? Mwacitsanzo, mukakumana na m’bale kapena mlongo amene akhala ku dziko limene nchito yathu ni yoletsedwa, kodi mumayamba kumufunsa mafunso kuti akuuzeni mmene nchito yathu imacitikila ku dzikolo? Mosakayikila, mungakhale na colinga cabwino pofunsa zimenezo. Timakonda abale athu, ndipo timafuna kudziŵa mavuto amene akukumana nawo. Timafunanso kuchula mavuto awo mwacindunji powapemphelela. Komabe, iyi ni nthawi imene tiyenela kulamulila lilime lathu na kukhala cete. Ngati tikakamiza m’bale kapena mlongo wathu kuti atiuze zinthu zacinsinsi zokhudza nchito yathu m’dziko limene kuli ciletso, timaonetsa kuti sitim’konda munthuyo. Timaonetsanso kuti sitikonda abale na alongo athu okhala m’dzikolo, cifukwa zimene iye angaulule zingawaike m’mavuto. Kukamba zoona, palibe aliyense wa ife amene angafune kuwonjezela mavuto ena pa mavuto amene abale na alongo amakumana nawo ku maiko kumene kuli ciletso. Ndiponso palibe m’bale kapena mlongo wotumikila m’dziko lotelo amene angafune kuulula mmene abale m’dzikolo amagwilila nchito yolalikila, komanso mmene amacitila zinthu zina zauzimu.
13. Malinga na mfundo ya pa Miyambo 11:13, kodi akulu afunika kucita ciani? Nanga cifukwa ciani?
13 Akulu maka-maka ni amene afunika kukhala patsogolo potsatila mfundo ya m’Baibo ya pa Miyambo 11:13. Ayenela kuyesetsa kusunga cinsinsi. (Ŵelengani.) Izi zingakhale zovuta, maka-maka ngati mkulu ni wokwatila. Mwamuna na mkazi wake amayesetsa kulimbitsa cikondi pakati pawo mwa kukambilana kaŵili-kaŵili, komanso kufotokozelana zakukhosi, mmene amvelela, na nkhawa zawo. Koma mkulu amazindikila kuti sayenela kuulula “zinsinsi” za abale kapena alongo mu mpingo. Ngati angacite zimenezi, angadziwonongele mbili ndipo abale na alongo angaleke kum’dalila. Abale amene amaikidwa pa udindo mu mpingo ayenela kukhala “osanena pawili.” (1 Tim. 3:8) Izi zitanthauza kuti sayenela kucitila ena cinyengo kapena kuwajeda. Mkulu amene amakonda mkazi wake, sangamuuze nkhani zimene safunika kudziŵa.
14. Kodi mlongo amene mwamuna wake ni mkulu angathandize bwanji kuteteza mbili yabwino ya mwamuna wakeyo?
14 Mlongo angathandize kuteteza mbili ya mwamuna wake mwa kupewa kum’kakamiza kuti amuuze nkhani zacinsinsi. Ngati mlongo apewa kucita zimenezi, ndiye kuti akucilikiza mwamuna wake, ndiponso amaonetsa kuti amalemekeza anthu amene anauza mwamuna wakeyo nkhani zacinsinsi. Ndipo koposa zonse, Yehova amakondwela naye mlongo wotelo, cifukwa zocita zake zimathandiza kuti mu mpingo mukhale mtendele na mgwilizano.—Aroma 14:19.
KODI ZIMENE TIMAKAMBA ZIMAM’KHUDZA BWANJI YEHOVA?
15. Kodi Yehova anamvela bwanji na zimene anzake atatu a Yobu anakamba? Nanga cifukwa ciani?
15 Tingaphunzile zambili m’buku la m’Baibo la Yobu pa nkhani ya kakambidwe koyenela komanso nthawi yoyenela kukamba. Yobu atakumana na mavuto aakulu motsatizana-tsatizana, amuna anayi anabwela kudzam’tonthoza na kudzam’patsa uphungu. Amuna amenewo anakhala cete kwa nthawi yaitali. Atatu mwa amunawo anali Elifazi, Bilidadi, na Zofari. Malinga na zimene amuna atatuwa anakamba pambuyo pake, n’zoonekelatu kuti panthawi imene anali cete, sanali kuganizila za mmene akanathandizila Yobu. M’malomwake, anali kungoganizila zimene akanakamba pofuna kupeleka umboni wakuti Yobu anacita colakwa cina-cake. Zina zimene anakamba zinali zoona. Koma zambili zimene anakamba ponena za Yobu na Yehova zinali zoipa ndiponso zabodza. Iwo anamunena Yobu kuti anali munthu woipa. (Yobu 32:1-3) Kodi Yehova anamvela bwanji? Anawakwiyila kwambili amuna atatuwo. Anakamba kuti iwo anali opusa, ndipo anawauza kuti akapemphe Yobu kuti awapemphelele.—Yobu 42:7-9.
16. Kodi tiphunzilapo ciani pa citsanzo coipa ca Elifazi, Bilidadi, na Zofari?
16 Tiphunzilapo mfundo zingapo pa citsanzo coipa ca Elifazi, Bilidadi, na Zofari. Mfundo yoyamba ni yakuti sitiyenela kuweluza abale athu. (Mat. 7:1-5) M’malomwake, tiyenela kuwamvetsela mosamala tisanakambe ciliconse. Tikatelo, m’pamene tingamvetsetse mavuto awo. (1 Pet. 3:8) Yaciŵili, pamene tikamba nawo, tifunika kuyesetsa kukamba mokoma mtima komanso tizikamba zoona. (Aef. 4:25) Ndipo yacitatu, Yehova amamvetsela mwachelu zimene timakamba kwa wina na mnzake.
17. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Elihu?
17 Munthu wacinayi amene anakamba na Yobu anali Elihu, m’bululu wake wa Abulahamu. Iye anali kumvetsela pamene Yobu na amuna atatuwo anali kulankhula. Mwacionekele, pa nthawiyo Elihu anali kumvetsela mwachelu. Takamba conco cifukwa pambuyo pake, iye anakwanitsa kupatsa Yobu uphungu mwacikondi koma mosapita m’mbali. Uphunguwo unathandiza Yobu kuwongolela maganizo ake. (Yobu 33:1, 6, 17) Colinga cacikulu ca Elihu cinali kulemekeza Yehova, osati kudzilemekeza iye mwini kapena wina aliyense. (Yobu 32:21, 22; 37:23, 24) Pa citsanzo ca Elihu tiphunzilapo kuti pali nthawi yoyenela kukhala cete na nthawi yoyenela kukamba. (Yak. 1:19) Tiphunzilaponso kuti pamene tipatsa ena uphungu, colinga cathu cacikulu ciyenela kukhala kulemekeza Yehova osati kudzipezela ulemu.
18. Tingaonetse bwanji kuti timayamikila mphatso ya kulankhula imene Mulungu anatipatsa?
18 Tingaonetse kuti timayamikila mphatso ya kulankhula mwa kutsatila malangizo a m’Baibo onena za nthawi yoyenela kukamba na nthawi yoyenela kukhala cete. Mfumu ya nzelu Solomo anauzilidwa kulemba kuti: “Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenela ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.” (Miy. 25:11) Ngati timvetsela mwachelu pamene ena akamba, komanso kuganizilapo tisanayankhe, mawu athu adzakhala monga zipatso za maapozi agolide. Adzakhala abwino komanso opindulitsa. Mwa kutelo, zokamba zathu kaya zikhale zocepa kapena zambili, zidzakhala zolimbikitsa kwa ena, ndiponso tidzakondweletsa Yehova. (Miy. 23:15; Aef. 4:29) Ndithudi, iyi ni njila yabwino kwambili yoonetsela kuti timayamikila mphatso yocokela kwa Mulungu imeneyi ya kulankhula!
NYIMBO 82 “Onetsani Kuwala Kwanu”
^ ndime 5 M’Mawu a Mulungu muli mfundo zimene zingatithandize kudziŵa nthawi yoyenela kukamba na nthawi yokhala cete. Tikadziŵa mfundo zimenezo na kuziseŵenzetsa, zokamba zathu zidzakhala zokondweletsa Yehova.
^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo akupeleka malangizo anzelu kwa mlongo mnzake pamene kuli koyenela.
^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale apeleka malangizo othandiza kwa m’bale wina pa nkhani ya ukhondo.
^ ndime 66 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pa nthawi yoyenela, Abigayeli anacondelela Davide, ndipo panakhala zotulukapo zabwino.
^ ndime 68 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale na mkazi wake apewa kuulula mmene nchito yathu imacitikila ku dziko limene kuli ciletso.
^ ndime 70 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI:Mkulu akucita zinthu mosamala kuti wina aliyense asamveleko nkhani yacinsinsi ya mu mpingo imene akukambilana na ena pa foni.