Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 9

Abale Acinyamata—Kodi Mungacite Ciani Kuti Ena Azikudalilani?

Abale Acinyamata—Kodi Mungacite Ciani Kuti Ena Azikudalilani?

“Gulu la acinyamata amene ali ngati mame a m’bandakuca lili pamodzi ndi iwe.”—SAL. 110:3.

NYIMBO 39 Tipange Dzina Labwino na Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi tinganene ciani za abale acinyamata?

IMWE abale acinyamata, mungacite zambili mumpingo. Ambili a imwe muli na nyonga komanso mphamvu. (Miy. 20:29) Ndimwe ofunika kwambili mumpingo mwanu. Mwina mukuyembekezela mwacidwi nthawi pamene mudzaikidwa kukhala mtumiki wothandiza. Komabe, mwina mungamaganize kuti ena amakuonani kuti ndinu wamng’ono kwambili, kapena simudziŵa zambili moti sangakupatseni nchito zofunika. Ngakhale kuti ndinu wamng’ono, pali zinthu zimene mungacite palipano kuti abale na alongo mumpingo mwanu azikudalilani na kukulemekezani.

2. Kodi tikambilane ciani m’nkhani ino?

2 M’nkhani ino tikambilana zocitika za paumoyo wa Mfumu Davide. Tikambilananso mwacidule zocitika za paumoyo wa mafumu aŵili a Yuda—Asa na Yehosafati. Tikambilana zina mwa zopinga zimene amuna atatu amenewa anakumana nazo, zimene anacita, komanso zimene abale acinyamata angaphunzile pa zitsanzo zawo.

PHUNZILANI KWA MFUMU DAVIDE

3. Ni njila imodzi iti imene acicepele angathandizile acikulile mumpingo?

3 Ali wamng’ono, Davide anaphunzila maluso amene anali othandiza kwa ena. N’zoonekelatu kuti iye anali munthu wauzimu, komanso anakulitsa luso lake loimba, ndipo anaseŵenzetsa luso limenelo pothandiza Sauli mfumu yosankhidwa na Mulungu. (1 Sam. 16:16, 23) Imwe abale acinyamata, kodi muli na maluso amene angakhale othandiza kwa ena mumpingo? Ambili a imwe muli nawo. Mwacitsanzo, acikulile ambili amayamikila kuwaonetsa mmene angaseŵenzetsele matabuleti komanso zipangizo zina pocita phunzilo laumwini na misonkhano. Cidziŵitso canu poseŵenzetsa zipangizo zimenezi cingakhale cothandiza kwambili kwa acikulile.

Davide anali wodalilika posamalila nkhosa za atate ake. Iye anafika ngakhale poteteza nkhosazo ku cimbalangondo (Onani ndime 4)

4. Mofanana na Davide, ni makhalidwe ati amene abale acinyamata afunika kukhala nawo? (Onani cithunzi pacikuto.)

4 Mu umoyo wake wa tsiku na tsiku, Davide anaonetsa kuti anali munthu wodalilika. Mwacitsanzo, ali mnyamata anali kusamalila mwakhama nkhosa za atate ake. Nchito imeneyo inali yoopsa. Patapita nthawi, Davide anafotokozela Mfumu Sauli kuti: “Ine mtumiki wanu ndinakhala m’busa wa nkhosa za bambo anga. Ndiyeno kunabwela mkango komanso cimbalangondo moti ciliconse mwa zilombo zimenezi cinagwila nkhosa ya m’gululo. Pamenepo ine ndinatsatila cilomboco n’kucipha, ndipo ndinapulumutsa nkhosa m’kamwa mwake.” (1 Sam. 17:34, 35) Davide anali kuona kuti ni udindo wake kusamalila nkhosa zimenezo, ndipo molimba mtima anagwebana na zilombo zolusa kuti ateteze nkhosazo. Abale acinyamata angatengele citsanzo ca Davide mwa kugwila molimbika nchito iliyonse imene apatsidwa.

5. Malinga na Salimo 25:14, kodi cinthu cofunika kwambili cimene abale acinyamata angacite n’ciani?

5 Wacicepele Davide, anakhala pa ubale wolimba na Yehova. Ubale umenewo unali wofunika kwambili kwa Davide kuposa kulimba mtima kapena luso lake poseŵenzetsa coimbila ca zingwe. Yehova sanali cabe Mulungu wa Davide koma analinso bwenzi lake, inde bwenzi lake lapamtima. (Ŵelengani Salimo 25:14.) Abale acinyamata, cinthu cofunika kwambili cimene mungacite ni kulimbitsa ubale wanu na Atate wanu wakumwamba. Ndipo kucita zimenezo kungakuthandizeni kuti mulandile mautumiki owonjezeleka.

6. Kodi anthu ena anali kumuona motani Davide?

6 Davide anafunika kupilila vuto loonedwa kuti ni wamng’ono kwambili komanso wosadalilika. Mwacitsanzo, pamene Davide anadzipeleka kuti amenyane na Goliyati, Mfumu Sauli inamuletsa mwa kumuuza kuti: “Ndiwe mwana.” (1 Sam. 17:31-33) Poyamba, m’bale wake weni-weni wa Davide anamupatsa mlandu wakuti anali wosadalilika. (1 Sam. 17:26-30) Komabe, Yehova sanaone Davide kuti anali wamng’ono kwambili kapena wosadalilika. Anali kum’dziŵa bwino mnyamatayo. Ndipo mwa kudalila Yehova bwenzi lake kuti amupatse mphamvu, Davide anakantha Goliyati.—1 Sam. 17:45, 48-51

7. Mungaphunzile ciani pa zimene zinacitikila Davide panthawi ina?

7 Mungaphunzile ciani pa zimene zinacitikila Davide? Mungaphunzilepo kuti mufunika kukhala oleza mtima. Anthu amene anakudziŵani kucokela muli mwana, zingawatengele nthawi kuti ayambe kukuonani kuti mwakula tsopano. Komabe, khalani otsimikiza kuti Yehova saona cabe maonekedwe anu akunja. Amakudziŵani bwino, ndipo amadziŵanso zimene mungakwanitse kucita. (1 Sam. 16:7) Limbitsani ubale wanu na Mulungu. Davide anacita zimenezo mwa kuyang’anitsitsa zinthu zimene Yehova analenga. Davide anaganizilapo mozama pa zinthu zimenezo na kuona zimene angaphunzilepo ponena za Mlengi. (Sal. 8:3, 4; 139:14; Aroma 1:20) Cina cimene mungacite ni kuyang’ana kwa Yehova kuti akupatseni mphamvu. Mwacitsanzo, kodi anzanu ena kusukulu, amakusekani cifukwa cakuti ndinu wa Mboni za Yehova? Ngati n’conco, pemphelani kwa Yehova kuti akuthandizeni kupilila vuto limeneli. Komanso seŵenzetsani malangizo othandiza opezeka m’Mawu ake ndiponso m’mabuku ophunzitsa Baibo na mavidiyo. Nthawi zonse mukaona kuti Yehova wakuthandizani kugonjetsa copinga, cidalilo canu mwa iye cimakula. Kuwonjezela apo, pamene ena aona kuti mumadalila Yehova, adzayamba kukudalilani.

Abale acinyamata modzicepetsa angathandize ena m’njila zambili (Onani ndime 8-9)

8-9. N’ciani cinathandiza Davide kuyembekezela moleza mtima kufikila nthawi imene anayamba kulamulila monga mfumu? Nanga kodi abale acinyamata angaphunzilepo ciani pa citsanzo cake?

8 Onani copinga cina cimene Davide anakumana naco. Pambuyo pakuti wadzozedwa monga mfumu, Davide anafunika kuyembekezela kwa zaka zambili kuti ayambe kulamulila monga mfumu ya Yuda. (1 Sam. 16:13; 2 Sam. 2:3, 4) Kodi n’ciani cinamuthandiza kuyembekezela moleza mtima panthawi yonseyo? M’malo molefuka, Davide anasumika maganizo pa zimene akanakwanitsa kucita. Mwacitsanzo, pamene Davide anali kukhala umoyo wothaŵa-thaŵa m’dziko la Afilisiti, anaseŵenzetsa nthawiyo kumenyana na adani a Isiraeli. Mwa kucita zimenezo, Davide anateteza malile a ufumu wa Yuda.—1 Sam. 27:1-12.

9 Kodi abale acinyamata angaphunzilepo ciani pa citsanzo ca Davide? Seŵenzetsani mipata imene muli nayo potumikila abale anu. Ganizilani zimene zinacitika kwa m’bale wina dzina lake Ricardo. * Kwa nthawi yaitali anali kulakalaka kutumikila monga mpainiya wanthawi zonse. Koma akulu anamuuza kuti ayembekeze. M’malo molefuka kapena kukalipa, m’bale Ricardo anali kuthela nthawi yaitali mu nchito yolalikila. Iye anati: “Nikayang’ana kumbuyo, nimaona kuti n’nacita bwino kupitabe patsogolo. N’naika maganizo pa kubwelelako kwa munthu aliyense amene anaonetsa cidwi na kupanga maulendo obwelelako opindulitsa. Panthawiyo, n’nakhala na phunzilo langa la Baibo loyamba na kulitsogoza. Kuthela nthawi yoculuka mu ulaliki, kunanithandiza kucepetsa mantha amene n’nali nawo.” M’bale Ricardo tsopano ni mpainiya wanthawi zonse waluso komanso ni mtumiki wothandiza.

10. Kodi Davide panthawi ina anacita ciani asanapange cosankha cofunika?

10 Ganizilaninso cocitika cina pa umoyo wa Davide. Panthawi imene iye na asilikali ake anali kukhala othaŵa-thaŵa, anasiya mabanja awo n’kupita kukamenya nkhondo. Pamene asilikaliwo anali kunkhondo, adani anafunkha zinthu m’nyumba zawo na kutenga mabanja awo n’kupita nawo. Pokhala kuti Davide anali katswili pa nkhondo, akanaganiza kuti angapeze njila yabwino kwambili yopulumutsila anthu amene anagwidwawo. Koma Davide anayang’ana kwa Yehova kuti amutsogolele. Mothandizidwa na wansembe Abiyatara, Davide anafunsila kwa Yehova kuti: “Kodi ndithamangitse gulu la acifwambali?” Yehova anauza Davide kuti acite zimenezo ndipo anamutsimikizila kuti adzapambana. (1 Sam. 30:7-10) Kodi mungaphunzilepo ciani pa cocitika cimeneci?

Abale acinyamata ayenela kufunsila malangizo kwa akulu (Onani ndime 11)

11. Kodi mungacite ciani musanapange zosankha?

11 Funsilani malangizo kwa ena musanapange zosankha. Funsilani kwa makolo anu. Mungapezenso malangizo abwino mwa kukambilana na akulu amene ni aciyambakale. Yehova amawadalila amuna oikidwa amenewa, ndipo inunso mungawadalile. Yehova amawaona kuti ni “mphatso” mumpingo. (Aef. 4:8) Mukamatengela cikhulupililo cawo na kumvela malangizo anzelu amene iwo angapeleke, mudzapindula kwambili. Tsopano tiyeni tione zimene tingaphunzile kwa Mfumu Asa.

PHUNZILANI KWA MFUMU ASA

12. Kodi Mfumu Asa anali na makhalidwe otani pamene anayamba kulamulila?

12 Ali wacinyamata, Mfumu Asa anali wodzicepetsa komanso wolimba mtima. Mwacitsanzo, iye ataloŵa m’malo atate ake, Abiya, anayamba kugwila nchito yocotsa mafano m’dziko lake lonse. Cina, iye anauza Ayuda kuti “afunefune Yehova Mulungu wa makolo awo ndi kutsatila cilamulo.” (2 Mbiri 14:1-7) Ndipo pamene Zera Mwiitiyopiya anaukila Ayuda pamodzi na asilikali 1,000,000, Asa mwanzelu anatembenukila kwa Yehova kuti amuthandize. Iye anati: “Inu Yehova mukafuna kuthandiza, zilibe kanthu kuti anthuwo ndi ambili kapena ndi opanda mphamvu. Tithandizeni Yehova Mulungu wathu cifukwa tikudalila inu.” Mawu amenewa aonetsa kuti Asa anali na cidalilo cakuti Yehova adzamupulumutsa pamodzi na anthu ake. Asa anadalila Atate wake wakumwamba ndipo “Yehova anagonjetsa Aitiyopiyawo.”—2 Mbiri 14:8-12.

13. Kodi n’ciani cinacitika kwa Asa m’kupita kwa nthawi? Nanga n’cifukwa ciani?

13 Mosakayikila, mungavomeleze kuti kuyang’anizana na gulu la asilikali 1,000,000 kunali koopsa kwambili. Koma cifukwa cakuti Asa anadalila Yehova, anapambana. Komabe, n’zomvetsa cisoni kuti pamene Asa anayang’anizana na gulu lankhondo locepa sanadalile Yehova. Ataopsezedwa na Baasa Mfumu yoipa ya Isiraeli, Asa anapita kwa mfumu ya Siriya kukapempha thandizo. Cosankha cimeneco cinakhala na zotulukapo zoipa. Kupitila mwa mneneli Hanani, Yehova anauza Asa kuti: “Cifukwa cakuti munadalila mfumu ya Siriya, osadalila Yehova Mulungu wanu, gulu lankhondo la mfumu ya Siriya lathawa m’manja mwanu.” Kungoyambila panthawi imeneyo, anthu anali kucita naye nkhondo Asa. (2 Mbiri 16:7, 9; 1 Maf. 15:32) Kodi pali phunzilo lanji pamenepa?

14. Mungaonetse bwanji kuti mumadalila Yehova, ndipo malinga na 1 Timoteyo 4:12, kodi mudzapeza mapindu otani mukacita zimenezi?

14 Khalanibe odzicepetsa ndipo pitilizani kudalila Yehova. Pamene munali kubatizika, munaonetsa kuti muli na cikhulupililo cacikulu mwa Yehova ndipo mumam’dalila. Ndipo Yehova mokondwela anakupatsani mwayi wokhala m’banja lake. Koma cofunika kwambili tsopano ni kupitilizabe kudalila Yehova. Kudalila Yehova kungakhale kosavuta popanga zosankha zikulu-zikulu mu umoyo. Koma bwanji pa zosankha zina? M’pofunika kwambili kuti muzidalila Yehova popanga zosankha kuphatikizapo zija zokhudzana na zosangalatsa, nchito yakuthupi, komanso zolinga zimene mudzadziikila mu umoyo. Musadalile nzelu zanu. M’malomwake, fufuzani mfundo za m’Baibo zimene zingakuthandizeni popanga zosankha, ndipo citani zinthu mogwilizana na mfundo zimene mwapeza. (Miy. 3:5, 6) Mukacita zimenezi, mudzakondweletsa Yehova, ndipo abale na alongo mumpingo adzayamba kukulemekezani.—Ŵelengani 1 Timoteyo 4:12.

PHUNZILANI KWA MFUMU YEHOSAFATI

15. Mogwilizana na 2 Mbiri 18:1-3; 19:2, kodi Mfumu Yehosafati analakwitsa ciani?

15 N’zoona kuti monga tonsefe, ndinu opanda ungwilo ndipo nthawi zina mungalakwitse zinthu. Komabe, izi siziyenela kukulepheletsani kucita zonse zimene mungathe potumikila Yehova. Ganizilani citsanzo ca Mfumu Yehosafati. Iye anali na makhalidwe ambili abwino. Ali mnyamata, “iye anafunafuna Mulungu wa bambo ake ndipo anayenda motsatila cilamulo cake.” Iye anatuma akalonga m’mizinda yonse ya Yuda kuti aziphunzitsa anthu za Yehova. (2 Mbiri 17:4, 7) Ngakhale kuti Yehosafati anali munthu woona mtima, nthawi zina anali kupanga zosankha zoipa. Ndipo panthawi ina atapanga cosankha coipa, Yehosafati anadzudzulidwa na mmodzi wa aneneli a Yehova. (Ŵelengani 2 Mbiri 18:1-3; 19:2.) Kodi mungaphunzilepo ciani pa nkhani imeneyi?

Abale acinyamata amene ni olimbika panchito komanso odalilika amakhala na mbili yabwino (Onani ndime 16)

16. Kodi mungaphunzile ciani pa citsanzo ca m’bale Rajeev?

16 Landilani uphungu na kuuseŵenzetsa. Mofanana na acinyamata ambili, mwina zimakuvutani kuika zofunika patsogolo. Koma musafooke. Ganizilani zimene zinacitika kwa m’bale wina wacinyamata dzina lake Rajeev. Ponena za nthawi pamene anali wacicepele, iye anati: “Nthawi zina sin’nali kudziŵa kuti nidzauseŵenzetsa motani umoyo wanga. Mofanana na acicepele ena ambili, n’nali kukonda ngako maseŵela olimbitsa thupi na zosangalatsa zina kuposa kupita ku misonkhano kapena mu ulaliki.” N’ciani cinathandiza m’bale Rajeev? Mkulu wina wacikondi anamupatsa uphungu. M’bale Rajeev anati: “Iye ananithandiza kuganizila mfundo ya pa 1 Timoteyo 4:8.” M’bale Rajeev anamvela uphunguwo modzicepetsa, ndipo anapendanso kuti ni zinthu ziti zofunika kwambili mu umoyo wake. Iye anati: “N’nasankha kuika zolinga zauzimu patsogolo.” Kodi panakhala zotulukapo zotani? M’bale Rajeev anafotokoza kuti: “Patapita zaka zocepa kucoka pamene n’nalandila uphunguwo, n’nayenelela kukhala mtumiki wothandiza.”

KONDWELETSANI ATATE WANU WAKUMWAMBA

17. Kodi acikulile amawaona motani abale acinyamata amene amatumikila Yehova?

17 Acikulile amakuyamikilani kwambili imwe acinyamata amene mumatumikila nawo Yehova limodzi “mogwilizana”! (Zef. 3:9) Iwo amakondwela kuona kuti mumagwila mokangalika, molimbika, komanso mwacangu nchito imene mwapatsidwa. Amakukondani kwambili.—1 Yoh. 2:14.

18. Malinga na Miyambo 27:11, kodi Yehova amamvela bwanji akaona acinyamata amene amamutumikila?

18 Imwe abale acinyamata, kumbukilani kuti Yehova amakukondani komanso amakudalilani. Iye anakambilatu kuti m’masiku otsiliza, padzakhala gulu la anyamata amene adzadzipeleka mofunitsitsa. (Sal. 110:1-3) Amadziŵa kuti mumam’konda, ndipo mumafuna kum’tumikila mmene mungathele. Conco khalani oleza mtima kwa ena, ngakhalenso kwa inu mwini pa zimene mukufuna. Mukalakwitsa zinthu, phunzilamponi kanthu na kulandila cilango cimene mwapatsidwa, ndipo onani cilangoco kuti cacokela kwa Yehova. (Aheb. 12:6) Gwilani mwakhama nchito iliyonse imene mwapatsidwa. Ndipo cofunika kwambili, m’zocita zanu zonse muzikondweletsa Atate wanu wakumwamba.—Ŵelengani Miyambo 27:⁠11.

NYIMBO 135 Yehova Alangiza Mwacikondi Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzelu”

^ ndime 5 Pamene abale acinyamata akukula kuuzimu, amafuna kutumikila Yehova m’njila zambili. Kuti iwo ayenelele kukhala atumiki othandiza, amafunika kukhala odalilika mumpingo. Kodi abale acinyamata angacite ciani kuti abale na alongo mumpingo aziwadalila?

^ ndime 9 Maina ena asinthidwa.