Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 12

Cikondi Cimatithandiza Kupilila Cidani

Cikondi Cimatithandiza Kupilila Cidani

“Ndikukulamulani zinthu izi, kuti muzikondana. Ngati dziko likudana nanu, mukudziŵa kuti linadana ndi ine lisanadane ndi inu.”—YOH. 15:17, 18.

NYIMBO 129 Tidzapilila Mosalekeza

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Malinga na Mateyu 24:9, n’cifukwa ciani sitiyenela kudabwa anthu ena akamatizonda?

YEHOVA anatilenga kuti tizikonda ena komanso tizikondedwa. Conco ngati wina amatizonda, cimatiŵaŵa ndipo mwina tingakhale na mantha. Mwacitsanzo, mlongo wina dzina lake Georgina wa ku Europe anati: “Pamene n’nali na zaka 14, amayi anga anali kunizonda cifukwa cotumikila Yehova. N’namvela kukhala munthu wokanidwa ndipo n’nayamba kukayikila zakuti ndine munthu wabwino.” * M’bale wina dzina lake Danylo analemba kuti: “Asilikali atanimenya, kunitukwana, komanso kuniopseza cifukwa cokhala Mboni ya Yehova, n’nacita mantha ndipo n’nacita manyazi.” Cidani cotelo cimakhala coŵaŵa kwambili, koma izi sizitidabwitsa. Yesu anakambilatu kuti tidzazondewa.—Ŵelengani Mateyu 24:9.

2-3. N’cifukwa ciani otsatila a Yesu amazondewa?

2 Dzikoli limadana na otsatila a Yesu. Cifukwa ciani? Cifukwa mofanana na Yesu ‘sitili mbali ya dzikoli.’ (Yoh. 15:17-19) Ndipo ngakhale kuti timalemekeza maboma a anthu, timakana kuwalambila kapena kulambila zizindikilo zoimila mabomawo. Timalambila Yehova cabe. Timacilikiza Mulungu kuti ndiye woyenela kulamulila anthu, ngakhale kuti Satana na “mbewu yake” amatsutsa mwamphamvu kuti Mulungu ndiye woyenela kulamulila anthu. (Gen. 3:1-5, 15) Timalalikila kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo udzathetsa mavuto a anthu, ndipo Ufumuwo posacedwa udzawononga onse amene amautsutsa. (Dan. 2:44; Chiv. 19:19-21) Umenewu ni uthenga wabwino kwa anthu ofatsa, koma ni uthenga woipa kwa anthu oipa.—Sal. 37:10, 11.

3 Timazondedwanso cifukwa cakuti timayendela mfundo zolungama za Mulungu. Miyezo imeneyi ni yosiyana kwambili na dzikoli pa nkhani ya makhalidwe abwino. Mwacitsanzo, anthu ambili amavomeleza poyela kugonana koipitsitsa kofanana na kumene Mulungu anawonongela nako anthu a ku Sodomu na Gomora. (Yuda 7) Cifukwa cakuti timamamatila miyezo ya m’Baibo ponena za makhalidwe otelo, anthu ambili amatinyoza na kutinena kuti ndife okhwimitsa zinthu!—1 Pet. 4:3, 4.

4. Ni makhalidwe ati amene amatilimbikitsa anthu akamatizonda?

4 N’ciani cingatithandize kupilila anthu akamatizonda na kutinyoza? Tiyenela kukhala na cikhulupililo colimba kuti Yehova adzatithandiza. Mofanana na cishango, cikhulupililo cathu cingathe ‘kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’ (Aef. 6:16) Koma kuwonjezela pa cikhulupililo, palinso cina. Tifunikanso cikondi. Cifukwa ciani? Cifukwa cikondi “sicikwiya.” Cimakwilila komanso kupilila zonse zokhumudwitsa. (1 Akor. 13:4-7, 13) Tsopano tiyeni tione mmene cikondi pa Yehova, pa alambili anzathu, komanso ngakhale pa adani athu cimatithandizila kupilila cidani.

CIKONDI PA YEHOVA CIMATITHANDIZA KUPILILA CIDANI

5. Kodi cikondi ca Yesu pa Atate wake cinamulimbikitsa bwanji?

5 Madzulo akuti aphedwa maŵa na adani ake, Yesu anauza otsatila ake okhulupilika kuti: “Ndimakonda Atate, [conco] ndikucita izi kutsatila lamulo limene Atatewo anandipatsa.” (Yoh. 14:31) Cikondi ca Yesu pa Yehova cinamulimbikitsa kupilila mayeso amene anali kudzakumana nawo kutsogolo. Cikondi cathu pa Yehova nafenso cingatithandize mofananamo.

6. Mogwilizana na Aroma 5:3-5, kodi atumiki a Yehova amamvela bwanji kupilila cidani ca dzikoli?

6 Cikondi pa Mulungu cimathandiza atumiki a Yehova nthawi zonse kupilila mazunzo. Mwacitsanzo, atumwi atalamulidwa na khoti lamphamvu komanso lapamwamba la Ayuda kuti aleke kulalikila, cikondi pa Mulungu cinawalimbikitsa “kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.” (Mac. 5:29; 1 Yoh. 5:3) Cikondi cacikulu cotelo cimalimbitsanso abale athu masiku ano, amene ambili a iwo amaima zolimba pa cikhulupililo pamene akuzunzidwa na maboma oipa komanso amphamvu. M’malo molefuka, timauona kukhala mwayi kupilila cidani ca dzikoli.—Mac. 5:41; ŵelengani Aroma 5:3-5.

7. Kodi tiyenela kucita ciani ngati a m’banja lathu amatitsutsa?

7 Ciyeso cikacokela kwa a m’banja lathu, cimakhala cimodzi mwa mayeso ovuta kwambili kuwapilila. Tikayamba kuonetsa cidwi na coonadi, ena mwa a m’banja lathu angaganize kuti tasoceletsedwa. Ena angaganize kuti tacita misala. (Yelekezelani na Maliko 3:21) Angafike ngakhale potitsutsa kwambili. Koma sitiyenela kudabwa na citsutso cimeneci. Yesu anati: “Adani a munthu adzakhala a m’banja lake lenileni.” (Mat. 10:36) Mosasamala kanthu za mmene acibale athu amationela, timapewa kucita nawo zinthu monga adani athu. Mosiyana na zimenezo, pamene cikondi cathu pa Yehova cikula, naconso cikondi cathu pa anthu cimakula. (Mat. 22:37-39) Koma sitidzapeputsa miyezo imene timayendela mwa kunyalanyaza malamulo a m’Baibo na mfundo zake, cabe kuti tikondweletse munthu wina.

Tingavutike kwa kanthawi, koma Yehova nthawi zonse adzakhala nafe kuti atitonthoze na kutilimbikitsa (Onani ndime 8-10)

8-9. N’ciani cinathandiza mlongo wina kuima zolimba ngakhale kuti anali kutsutsidwa kwambili?

8 Mlongo Georgina amene tam’gwila mawu kumayambililo, anakwanitsa kuima zolimba ngakhale kuti anali kutsutsidwa kwambili na amayi ake. Iye anafotokoza kuti: “Ine na amayi tinayambila pamodzi kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova. Koma pambuyo pa miyezi 6 pamene n’nafuna kuyamba kupezeka kumisonkhano, amayi anayamba kunitsutsa kwambili. N’nazindikila kuti anali kukambilana na anthu ampatuko, ndipo anali kuseŵenzetsa zimene anauzidwazo ponitsutsa. Anali kunitukwana, kunidonsa tsitsi, kunikanyanga pakhosi, na kunitayila zofalitsa. N’tafika zaka 15 n’nabatizika. Amayi anayesa kuniletsa kutumikila Yehova mwa kunipeleka kunyumba ina yosungilako acicepele ovuta, amene ena mwa iwo anali kuseŵenzetsa amkolabongo komanso amene anacita milandu. Citsutso cimakhala covuta kwambili kucipilila ngati cacokela kwa munthu amene ayenela kukukonda na kukusamalila.”

9 Kodi n’ciani cinathandiza mlongo Georgina kupilila? Iye anati: “Pa tsiku limene amayi anayamba kunitsutsa n’nali n’tatsiliza kumene kuŵelenga Baibo yonse. N’nali na cikhulupililo conse kuti tsopano napezadi coonadi, ndipo n’naona kuti nayandikilana kwambili na Yehova. N’nali kupemphela kaŵili-kaŵili kwa iye, ndipo anali kuniyankha. Pamene n’nali kunyumba ija imene amayi ananipelekako, mlongo wina anali kunipempha kuyenda kunyumba kwake, ndipo tinali kukambilana mfundo za m’Baibo capamodzi. Panthawi yonseyo, abale na alongo anali kunilimbikitsa. Ananipangitsa kumvela kuti ndine wa m’banja lawo. N’nadzionela nekha kuti Yehova ni wamphamvu kuposa otitsutsa kaya akhale otani.”

10. Kodi tingakhale na cidalilo cotani mwa Yehova Mulungu wathu?

10 Mtumwi Paulo analemba kuti palibe cimene cingathe “kutilekanitsa ndi cikondi ca Mulungu cimene cili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 8:38, 39) Ngakhale kuti tingavutike kwa kanthawi, Yehova nthawi zonse adzakhala kumbali yathu kutitonthoza na kutilimbikitsa. Ndipo monga mmene cocitika ca mlongo Georgina cionetsela, Yehova amatithandizanso kupitila m’banja lathu lauzimu.

CIKONDI PA ALAMBILI ANZATHU CIMATITHANDIZA KUPILILA CIDANI

11. Kodi cikondi cimene Yesu anafotokoza pa Yohane 15:12, 13, cinawathandiza bwanji ophunzila ake? Fotokozani citsanzo.

11 Usiku wakuti aphedwa maŵa, Yesu anakumbutsa ophunzila ake kuti azikondana. (Ŵelengani Yohane 15:12, 13.) Iye anadziŵa kuti cikondi codzimana, cidzawathandiza kukhalabe ogwilizana komanso kupilila cidani ca dzikoli. Ganizilani citsanzo ca mpingo wa ku Tesalonika. Kucokela pamene unakhazikitsidwa, abale na alongo mumpingowo anali kuzunzidwa. Ngakhale n’telo, iwo anakhala zitsanzo zabwino pa nkhani ya kukhulupilika na cikondi. (1 Ates. 1:3, 6, 7) Paulo anawalimbikitsa kupitiliza kuonetsa cikondi “mowonjezeleka.” (1 Ates. 4:9, 10) Cikondi cinali kuwasonkhezela kulimbikitsa anthu opsinjika maganizo komanso kucilikiza ofooka. (1 Ates. 5:14) Iwo anatsatila malangizo a Paulo, cifukwa m’kalata yake yaciŵili imene analemba patapita pafupi-fupi caka cimodzi, Paulo ponena za iwo anati: “Cikondi ca aliyense wa inu kwa mnzake cikuwilikiza.” (2 Ates. 1:3-5) Cikondi cawo cinawathandiza kupilila mazunzo na mavuto ena.

Cikondi cacikhristu cingatithandize kupilila cidani (Onani ndime 12) *

12. Panthawi ya nkhondo m’dziko lina, kodi abale na alongo anaonetsana bwanji cikondi?

12 Ganizilani cocitika ca m’bale Danylo amene tamuchula kuciyambi, na mkazi wake. M’tauni imene anali kukhala mutabuka nkhondo, iwo anapitiliza kupezeka kumisonkhano, kulalikila mmene angathele, komanso kugaŵana zakudya zimene anali nazo na abale na alongo awo. Ndiyeno tsiku lina, asilikali a mfuti m’manja anabwela kunyumba kwa m’bale Danylo. M’bale Danylo anati: “Iwo ananilamula kuti nisiye cikhulupililo canga. N’takana, ananimenya na kuyelekeza kuniwombela, akuphulitsa zipolopolo pamwamba pa mutu wanga. Asanacoke, anaopseza kuti akabwelanso adzagwilila mkazi wanga. Koma mwamsanga, abale athu anatikwezeketsa sitima kuti tipite ku tauni ina. Sinidzaiŵala cikondi ca abale amenewa. Ndipo titafika ku tauni yatsopanoyo, abale kumeneko anatipatsa zakudya na kutithandiza kupeza nchito na nyumba! Cotulukapo cake n’cakuti tinakwanitsa kupezelako malo Mboni za Yehova zina zimene zinali kuthaŵa kucoka kumadela ankhondo.” Zocitika zimenezi zionetsa kuti cikondi cacikhristu cingatithandize kupilila cidani.

CIKONDI PA ADANI ATHU CIMATITHANDIZA KUPILILA CIDANI

13. Kodi mzimu woyela umatithandiza bwanji kupilila potumikila Yehova ngakhale pamene anthu atizonda?

13 Yesu anauza otsatila ake kukonda adani awo. (Mat. 5:44, 45) Kodi kucita zimenezi n’kopepuka? Kutalitali! Koma n’zotheka na thandizo la mzimu woyela wa Mulungu. Makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umabala ndiwo cikondi, komanso kuleza mtima, ubwino, kufatsa, komanso kudziletsa. (Agal. 5:22, 23) Makhalidwe amenewa amatithandiza kupilila cidani. Anthu ambili amene anali otsutsa anasintha mitima yawo cifukwa cakuti mwamuna, mkazi, mwana, kapena munthu wokhala naye pafupi anaonetsa makhalidwe aumulungu amenewa. Ambili a iwo akhala abale na alongo athu. Conco ngati zimakuvutani kukonda anthu amene amakuzondani, cabe cifukwa cakuti mumatumikila Yehova, pemphani mzimu woyela. (Luka 11:13) Ndipo khalani na cikhulupililo cakuti kumvela Mulungu, nthawi zonse kumakhala kopindulitsa.—Miy. 3:5-7.

14-15. Kodi Aroma 12:17-21, inamuthandiza bwanji mlongo Yasmeen poonetsa cikondi kwa mwamuna wake ngakhale kuti anali kum’tsutsa kwambili?

14 Ganizilani citsanzo ca mlongo Yasmeen wa ku Middle East. Atakhala Mboni ya Yehova, mwamuna wake anaganiza kuti wasoceletsedwa, ndipo anayesa kumuletsa kutumikila Mulungu. Anali kumutukwana, ndipo analimbikitsa acibale, m’busa wacipembedzo, komanso wamatsenga kuti amuopseze na kum’patsa mlandu wofuna kupasula banja lake. Mwamuna wa mlongoyo anafika ngakhale ponyoza abale misonkhano ya mpingo ili mkati! Mlongo Yasmeen nthawi zambili anali kukhalila kulila cifukwa sanali kucitilidwa zinthu mwacikondi.

15 Ku Nyumba ya Ufumu, banja lauzimu la mlongo Yasmeen linali kumutonthoza na kumulimbikitsa. Akulu analimbikitsa mlongoyo kuseŵenzetsa malangizo a pa Aroma 12:17-21 (Ŵelengani.) Mlongo Yasmeen anati: “Zinali zovuta. Koma n’napempha Yehova kuti anithandize, ndipo n’nacita zonse zotheka kuti niseŵenzetse zimene Baibo imakamba. Conco mwamuna wanga akadetsela dala m’khichini, n’nali kuyeletsa. Akanitukwana, n’nali kuyankha modekha. Ndipo pamene anadwala n’namusamalila bwino.”

Tikamaonetsa cikondi anthu otizunza, tingafewetse mitima yawo (Onani ndime 16-17) *

16-17. Kodi muphunzilapo ciani pa citsanzo ca mlongo Yasmeen?

16 Mlongo Yasmeen anadalitsidwa cifukwa coonetsa cikondi kwa mwamuna wake. Iye anati: “Mwamuna wanga anayamba kunidalila kwambili cifukwa anali kudziŵa kuti nthawi zonse nimakamba zoona. Iye anayamba kunimvetsela mwaulemu tikamakambilana zacipembedzo, ndipo anavomela kubweletsa mtendele panyumba. Tsopano amanilimbikitsa kuyenda kumisonkhano ya mpingo. Umoyo wathu wa banja wakhala wabwino kwambili, ndipo timasangalala kukhala mwamtendele. Ciyembekezo canga n’cakuti mwamuna wanga akatsegule mtima wake ku coonadi na kutumikila nane Yehova.”

17 Citsanzo ca mlongo Yasmeen cionetsa kuti cikondi “cimakwilila zinthu zonse, . . . cimayembekezela zinthu zonse, cimapilila zinthu zonse.” (1 Akor. 13:4, 7) Cidani cingakhale cacikulu komanso coŵaŵa, koma cikondi n’camphamvu koposa. Cimakopa mtima. Komanso cimakondweletsa mtima wa Yehova. Koma ngakhale otsutsa apitilize kutizonda, tingakhalebe acimwemwe. Motani?

KHALANI ACIMWEMWE ENA AKAMAKUZONDANI

18. N’cifukwa ciani tingakhale acimwemwe tikamazondewa?

18 Yesu anati: “Ndinu odala (acimwemwe) anthu akamadana nanu.” (Luka 6:22) Siticita kusankha kuti anthu azitizonda. Sitisangalala kuzunzidwa kaamba ka cikhulupililo cathu. Nanga n’cifukwa ciani tingakhale acimwemwe pamene ena atizonda? Onani zifukwa zitatu izi. Coyamba, tikapilila timayanjidwa na Mulungu. (1 Pet. 4:13, 14) Caciŵili, cikhulupililo cathu cimayengedwa ndipo cimalimba. (1 Pet. 1:7) Ndipo cacitatu, tidzalandila mphoto ya mtengo wapatali, moyo wosatha.—Aroma 2:6, 7.

19. N’cifukwa ciani atumwi anali acimwemwe pambuyo pokwapulidwa?

19 Patapita nthawi yocepa Yesu atangoukitsidwa, atumwi anapeza cimwemwe cimene iye anafotokoza. Atakwapulidwa na kulamulidwa kuti aleke kulalikila, iwo anakondwela. Cifukwa ciani? “Cifukwa cakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenela kucitilidwa cipongwe cifukwa ca dzina la Yesu.” (Mac. 5:40-42) Cikondi cawo pa Mbuye wawo cinali cacikulu kuposa mantha oopa adani awo. Ndipo anaonetsa cikondi cawo mwa kupitiliza kulengeza uthenga wabwino “mwakhama.” Abale athu ambili masiku ano akupitiliza kutumikila mokhulupilika olo kuti akumana na zovuta. Iwo amadziŵa kuti Yehova sadzaiŵala nchito yawo na cikondi cawo cimene anaonetsa pa dzina lake.—Aheb. 6:10.

20. Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

20 Dzikoli lidzapitiliza kudana nafe malinga ngati dongosolo lino la zinthu likalipo. (Yoh. 15:19) Koma sitiyenela kucita mantha. Monga tidzaonela m’nkhani yotsatila, Yehova ‘adzalimbitsa na kuteteza’ okhulupilika ake. (2 Ates. 3:3) Conco tiyeni tipitilize kukonda Yehova, abale na alongo athu, komanso ngakhale kukonda adani athu. Tikatsatila malangizo amenewa, tidzakhalabe ogwilizana komanso olimba mwauzimu. Cina, tidzapeleka ulemu kwa Yehova, ndipo tidzaonetsa kuti cikondi n’camphamvu kwambili kuposa cidani.

NYIMBO 106 Kukulitsa Mkhalidwe wa Cikondi

^ ndime 5 M’nkhani ino, tikambilane mmene cikondi pa Yehova, pa alambili anzathu, komanso ngakhale pa adani athu cimatithandizila kugonjetsa cidani ca dziko. Tionenso cifukwa cake Yesu anakamba kuti tingakhalebe acimwemwe ngakhale pamene tizondewa.

^ ndime 1 Maina ena asinthidwa.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Asilikali ataopseza m’bale Danylo, abale anamuthandiza pamodzi na mkazi wake kusamukila kudela lina, ndipo kumeneko analandilidwa bwino.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo Yasmeen anali kutsutsidwa na mwamuna wake, koma akulu anamupatsa malangizo abwino. Iye anaonetsa kuti anali mkazi wabwino, ndipo anasamalila mwamuna wake pamene anali kudwala.