Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

N’cifukwa ciani Akhristu ayenela kukhala osamala poseŵenzetsa njila zotumizilana mauthenga pa intaneti?

Akhristu ena amaseŵenzetsa zipangizo zamakono kuti azikambilana na acibale awo komanso Akhristu anzawo. Koma Mkhristu wokhwima mwauzimu amakumbukila malangizo awa akuti: “Wocenjela amene waona tsoka amabisala. Koma anthu osadziwa zinthu amene amangopitabe amalangidwa.”—Miy. 27:12.

Timadziŵa kuti Yehova amafuna kutiteteza. Conco, timapewa kuyanjana na anthu obweletsa magaŵano, ocotsedwa, kapena obweletsa ziphunzitso zopotoka. (Aroma 16:17; 1 Akor. 5:11; 2 Yoh. 10, 11) Ena amene amayanjana na mpingo angakhale amene satsatila malangizo a m’Baibo. (2 Tim. 2:20, 21) Popanga mabwenzi timakumbukila mfundo imeneyi. Kusankha mabwenzi abwino kungakhale kovuta poseŵenzetsa njila yotumizilana mauthenga pa intaneti.

M’pofunika kusamala kwambili posankha mabwenzi m’gulu lalikulu lotumizilana mauthenga. Akhristu ena amene analoŵapo m’magulu akulu-akulu otumizilana mauthenga anakumana na mavuto. Kodi zingatheke bwanji m’bale kapena mlongo kukhala wosamala ngati gululo lili na anthu mahandiledi kapena masauzande? Cingakhale covuta kuwadziŵa bwino, komanso kudziŵa umoyo wauzimu wa anthu onse m’gululo. Salimo 26:4 imati: “Sindinakhale pansi pamodzi ndi anthu acinyengo. Ndipo sindinayanjane ndi anthu obisa umunthu wawo.” Izi zionetsa kuti tiyenela kuseŵenzetsa njila yotumizilana mauthenga pokambilana na anthu okhawo amene timawadziŵa bwino.

Ngakhale kuti gulu lotumizilana mauthenga lingakhale laling’ono, Mkhristu ayenela kupenda nthawi imene amathela pamacezawo, komanso zimene anthu m’gululo amakambilana. Sitiyenela kukakamizika kuyankha mauthenga amene talandila mosasamala kanthu za zimene akukambilana kapena kuculuka kwa nthawi imene tingathele poyankha mauthengawo. Paulo anacenjeza Timoteyo za anthu “amisece ndi olowelela nkhani za eni.” (1 Tim. 5:13) Zingatheke masiku ano kukhala otelo pa zipangizo zamakono.

Mkhristu wokhwima mwauzimu sangakambe kapena kumvetsela ndemanga zonena Akhristu ena, kapena kuvumbula zinthu za cinsinsi zokhudza Akhristu anzakewo. (Sal. 15:3; Miy. 20:19) Ndipo amapewa nkhani zokokomeza kapena zopanda maumboni. (Aef. 4:25) Timalandila cakudya cauzimu cokwanila na nkhani zodalilika kupitila pa webusaiti yathu ya jw.org, komanso kupitila pa mapulogilamu a pamwezi a JW Broadcasting®

Mboni zina zimaseŵenzetsa njila zotumizilana mauthenga pogulitsa kapena kugula zinthu, na kutsatsa malonda, kapena kulengeza za mwayi wa nchito kwa anthu. Zimenezi ni nkhani zamalonda osati zauzimu. Akhristu amene afuna kukhala umoyo “wosakonda ndalama” saseŵenzetsa abale awo kukhala njila yopezelapo phindu pa zamalonda.—Aheb. 13:5.

Nanga bwanji za kuseŵenzetsa njila zotumizilana mauthenga, popemphetsa ndalama zothandizila okhulupilila ena ofunikila thandizo, kapena okhudzidwa na matsoka a zacilengedwe? Timawakonda abale athu ndipo nthawi zonse timayesetsa kuwathandiza na kuwalimbikitsa. (Yak. 2:15, 16) Koma kuyesa kucita zimenezo kupitila m’magulu akulu-akulu otumizilana mauthenga kungasokoneze makonzedwe abwino olinganizidwa na ofesi ya nthambi kapena mpingo. (1 Tim. 5:3, 4, 9, 10, 16) Ndipo kukamba zoona palibe aliyense wa ife amene angafune kupeleka cithunzi cakuti anapatsidwa utumiki wina wake wapadela wosamalila nkhosa za Mulungu.

Timafunitsitsa kucita zinthu zopeleka ulemelelo kwa Mulungu. (1 Akor. 10:31) Conco mukasankha kuseŵenzetsa njila yotumizilana mauthenga, kapena njila zina, ganizilani ngozi zimene zingakhalepo ndipo khalani wosamala.