Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 11

Mmene Tingapezele Mphamvu m’Malemba

Mmene Tingapezele Mphamvu m’Malemba

“Mulungu . . . amatipatsa mphamvu kuti tithe kupilila.” —AROMA 15:5.

NYIMBO 94 Tiyamikila Mau a Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi anthu a Yehova angakumane na mayeso otani?

KODI mukukumana na ciyeso cacikulu? Mwina wina mumpingo anakukhumudwitsani. (Yak. 3:2) Kapena anzanu a kunchito kapena kusukulu amakunyozani cifukwa cotumikila Yehova. (1 Pet. 4:3, 4) Kapenanso a m’banja lanu amakuletsani kupezeka kumisonkhano, kapena kuuzako ena za cikhulupililo canu. (Mat. 10:35, 36) Ngati ciyeso cakula, mwina mungaganize zoleka kutumikila Yehova. Koma mungakhale na cidalilo cakuti mosasamala kanthu za vuto limene mukukumana nalo, Yehova adzakupatsani nzelu zokuthandizani kulimbana na vutolo, na kukupatsani mphamvu kuti mulipilile.

2. Mogwilizana na Aroma 15:4, kodi kuŵelenga Mawu a Mulungu kungatikhudze bwanji?

2 M’Mawu ake, Yehova anafotokoza bwino-bwino mmene anthu opanda ungwilo anapililila mayeso aakulu. Cifukwa ciani? Kuti tiphunzile kwa iwo. Izi n’zimene Yehova analimbikitsa mtumwi Paulo kulemba. (Ŵelengani Aroma 15:4.) Kuŵelenga nkhani zimenezi, kungatitonthoze na kutipatsa ciyembekezo. Koma kuti tipindule, pali zina zimene tiyenela kucita kuposa kungoŵelenga cabe Baibo. Tifunika kulola Malemba kuumba kaganizidwe kathu na kukhudza mitima yathu. Kodi tingacite ciani ngati tifuna malangizo otithandiza kupilila vuto lina lake? Tingaseŵenzetse njila ya masitepe anayi iyi: (1) Pemphelani, (2) Yelekezani, (3) Sinkha-sinkhani, komanso (4) Seŵenzetsani. Tiyeni tikambilane zofunikila pa sitepe iliyonse. * Ndiyeno tidzaseŵenzetsa njila imeneyi yocitila phunzilo laumwini kuti tiphunzile pa zocitika za mu umoyo wa Mfumu Davide na mtumwi Paulo.

1. PEMPHELANI

Musanayambe kuŵelenga Baibo, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuona zimene mungaphunzilepo (Onani ndime 3)

3. Musanayambe kuŵelenga Baibo, kodi muyenela kucita ciani, ndipo cifukwa ciani?

3 (1) Pemphelani. Musanayambe kuŵelenga Baibo, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuona mmene mungapindulile na zimene mudzaŵelenga. Mwacitsanzo, ngati mufuna malangizo a zimene mungacite kuti mulimbane na vuto lina lake, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kupeza mfundo m’Mawu ake zimene zingakutsogoleleni.—Afil. 4:6, 7; Yak. 1:5.

2. YELEKEZANI

Yelekezani kuti munthu amene mukuŵelenga m’nkhani ya m’Baibo ndinu (Onani ndime 4)

4. N’ciani cingakuthandizeni kuti nkhani ya m’Baibo ikhale yeni-yeni kwa inu?

4 (2) Yelekezani. Yehova anatipatsa luso lapadela lotha kuyelekeza zinthu m’maganizo. Kuti nkhani ya m’Baibo imene mukuŵelenga ikhale yeni-yeni kwa inu, yesani kuyelekeza nkhaniyo m’maganizo ndipo muzidziona kuti munthu amene mukuŵelengayo ndinu. Yesani kuona zinthu zimene munthuyo anali kuona, na kuyesa kumvela mmene anamvelela.

3. SINKHA-SINKHANI

Ganizilani mosamala zimene mukuŵelenga, na kuona mmene nkhaniyo ikukhudzilani (Onani ndime 5)

5. Kodi kusinkha-sinkha kumatanthauza ciani, nanga mungasinkhe-sinkhe bwanji?

5 (3) Sinkha-sinkhani. Kusinkha-sinkha kumatanthauza kuganizila mosamala zimene mukuŵelenga, komanso mmene nkhaniyo ikukhudzilani. Kumathandiza munthu kugwilizanitsa mfundo na kumvetsetsa mozama nkhaniyo. Kuŵelenga Baibo popanda kusinkha-sinkha kuli monga kungoyang’ana nchelwa cabe, osazitenga kuti umange nyumba. Kusinkha-sinkha kuli monga kuyala nchelwa kuti zilumikizane bwino-bwino pomanga kuti nyumba yonse ithe. Pokuthandizani kusinkha-sinkha mungayese kupeza mayankho pa mafunso awa: ‘Kodi munthu amene nikuŵelenga m’nkhaniyi anacita ciani kuti athetse vuto limene anakumana nalo? Kodi Yehova anam’thandiza bwanji? Kodi ningaseŵenzetse bwanji zimene naphunzila kuti zinithandize kupilila mayeso?’

4. SEŴENZETSANI

Seŵenzetsani zimene mwaphunzila kuti mupange zosankha zabwino, mupeze mtendele woculuka, komanso mulimbitse cikhulupililo canu (Onani ndime 6)

6. N’cifukwa ciani tifunika kuseŵenzetsa zimene timaphunzila?

6 (4) Seŵenzetsani. Yesu anakamba kuti ngati sitiseŵenzetsa zimene timaphunzila, tili monga munthu amene wamanga nyumba yake pamcenga. Iye amagwila nchito molimbika koma amangowononga mphamvu zake. Cifukwa ciani? Cifukwa cimphepo na madzi zikawomba, nyumbayo imagwa. (Mat. 7:24-27) Mofananamo, ngati tipemphela, kuyelekezela zinthu m’maganizo, na kusinkha-sinkha koma sitiseŵenzetsa zimene tinaphunzila, ndiye kuti tinangotaya cabe nthawi yathu. Ndipo cikhulupililo cathu cikayesedwa na mavuto kapena cizunzo, sicidzalimba. Koma tikaphunzila na kuseŵenzetsa zimene taphunzilazo, timapanga zosankha zabwino, timakhala na mtendele woculuka, komanso cikhulupililo cathu cimalimba. (Yes. 48:17, 18) Mwa kuseŵenzetsa masitepe anayi amene tangokambilana kumene, tiyeni tione zimene tingaphunzile pa cocitika ca mu umoyo wa Mfumu Davide.

KODI TINGAPHUNZILE CIANI KWA MFUMU DAVIDE?

7. Kodi tsopano tikambilane cocitika citi ca m’Baibo?

7 Kodi mnzanu kapena wa m’banja lanu anakucitilani zinthu zokukhumudwitsani? Ngati n’conco, mudzapindula kuona zimene zinathandiza Mfumu Davide, pamene mwana wake Abisalomu anamuukila na kuyesa kum’landa ufumu.—2 Sam. 15:5-14, 31; 18:6-14.

8. Kodi mungacite ciani kuti Yehova akuthandizeni?

8 (1) Pemphelani. Muli na nkhaniyi m’maganizo, muuzeni Yehova mmene mumvelela pa zoipa zimene ena anakucitilani. (Sal. 6:6-9) Muuzeni zonse mwacindunji. Ndiyeno pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuona mfundo zimene zingakutsogoleleni pamene muyesa kupilila vuto lalikulu limene mwakumana nalo.

9. N’ciani cinacitika pakati pa Davide na Abisalomu?

9 (2) Yelekezani. Ganizilani zocitika za m’nkhaniyi, na kuyelekezela m’maganizo mwanu mmene Mfumu Davide anamvelela. Kwa zaka zambili, Abisalomu mwana wa Davide, wakhala akucita zonse zotheka kuti anthu amukonde. (2 Sam. 15:7) Pamene Abisalomu akuona kuti nthawi tsopano yakwana, iye atumiza akazitape m’dziko lonse la Isiraeli kukonzekeletsa anthu kuti amulandile monga mfumu yawo yatsopano. Iye akopa ngakhale Ahitofeli mmodzi wa anzake a Davide apamtima, amenenso anali mmodzi wa alangizi ake kuti am’cilikize pa ciwembu cake. Ndiyeno Abisalomu akudziika yekha kukhala mfumu, kenako ayesa kugwila Davide kuti amuphe, amene zioneka kuti anali wodwala kwambili panthawiyo. (Sal. 41:1-9) Davide wadziŵa za ciwembuco, ndipo athaŵa kucoka ku Yerusalemu. Pothela pake, gulu la asilikali a Abisalomu lithilana nkhondo na gulu la asilikali okhulupilika kwa Davide. Gulu la asilikali opandukawo ligonjetsedwa, ndipo Abisalomu mwana wa Davide aphedwa.

10. Kodi zikanatheka Mfumu Davide kucita ciani?

10 Ndiyeno yelekezani m’maganizo mmene Davide anamvelela pamene zonsezi zinali kum’citikila. Iye anali kum’konda Abisalomu ndipo anali kukhulupilila Ahitofeli. Ngakhale n’telo, onse aŵiliwa anamupandukila. Iwo anam’khumudwitsa kwambili ndipo anafuna ngakhale kumupha. Davide akanaleka kukhulupilila mabwenzi ake ena, powaganizila kuti nawonso anagwilizana na Abisalomu. Iye akanayamba kungoganizila za iye yekha, ndipo akanafuna kuthaŵa yekha m’dzikolo. Kapena akanafooka kwambili. Koma Davide sanacite zimenezo. M’malomwake, iye anagonjetsa vuto lalikulu limenelo. Kodi cinam’thandiza n’ciani?

11. Kodi Davide anacita ciani panthawi yovuta imeneyi?

11 (3) Sinkha-sinkhani. Kodi ni mfundo zotani zimene mwaphunzilapo pa cocitika cimeneci? Yankhani funso lakuti, “Kodi Davide anacita ciani kuti athetse vuto limene anakumana nalo?” Davide sanataye mtima na kupanga zosankha mopupuluma kapena mopanda nzelu. Komanso sanazengeleze kucitapo kanthu cifukwa ca mantha. M’malomwake, anapemphela kwa Yehova kuti amuthandize. Anapemphanso mabwenzi ake kuti amuthandize. Ndipo anacitapo kanthu mwamsanga pa zimene anasankha kucita. Ngakhale kuti ena anam’khumudwitsa kwambili, Davide sanakhalebe wokhumudwa. Iye anapitlizabe kudalila Yehova komanso mabwenzi ake.

12. Kodi Yehova anacita ciani pothandiza Davide?

12 Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Davide? Mwa kufufuza, mudzadziŵa kuti Yehova anapatsa mphamvu Davide zofunikila kuti apilile vuto limeneli. (Sal. 3:1-8; tumawu twapamwamba) Yehova anadalitsa zosankha zimene Davide anapanga. Ndipo anateteza anzake okhulupilika a Davide pamene anali kumenya nkhondo yoteteza mfumu yawo.

13. Kodi mungatengele bwanji citsanzo ca Davide ngati wina wakukhumudwitsani kwambili? (Mat. 18:15-17)

13 (4) Seŵenzetsani. Dzifunseni kuti, ‘kodi ningatengele bwanji citsanzo ca Davide?’ Mungafunike kucitapo kanthu mwamsanga kuti muthetse vuto limene mwakumana nalo. Malinga na mmene zinthu zilili, mungatsatile mwacindunji masitepe amene Yesu anafotokoza m’Mateyu caputala 18, kapena mungaseŵenzetse mfundo za m’malangizowo mwa njila ina. (Ŵelengani Mateyu 18:15-17.) Koma simuyenela kucita zinthu mopupuluma cifukwa ca mmene mumvelela. Muyenela kupempha Yehova kuti akupatseni mtima wodekha na nzelu zofunikila kuti mulimbane na vutolo. Musaleke kuwadalila mabwenzi anu. M’malomwake, khalani okonzeka kulandila thandizo limene angakupatseni. (Miy. 17:17) Ndipo koposa zonse, tsatilani malangizo amene Yehova amapeleka m’Mawu ake.—Miy. 3:5, 6.

KODI TINGAPHUNZILE CIANI KWA PAULO?

14. Kodi 2 Timoteyo 1:12-16; 4:6-11, 17-22, ingakulimbikitseni m’mikhalidwe yotani?

14 Kodi a m’banja lanu amakutsutsani? Kapena mumakhala m’dziko limene nchito ya anthu a Yehova ni yoletsedwa kwambili, kapena m’dziko limene mulibe ufulu wokwanila wa kulambila? Ngati n’telo, mungalimbikitsidwe mwa kuŵelenga 2 Timoteyo 1:12-16 na ; 4:6-11, 17-22. * Paulo analemba mavesi amenewa ali mu ndende.

15. Kodi mungam’pemphe ciani Yehova?

15 (1) Pemphelani. Musanaŵelenge mavesiwo, muuzeni Yehova za vuto lanu na mmene mukumvelela cifukwa ca vutolo. Mufotokozeleni mosapita m’mbali. Ndiyeno pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuzindikila mfundo za m’nkhani yokhudza mayeso amene Paulo anakumana nawo, zimene zingakuthandizeni kudziŵa zoyenela kucita pa ciyeso cimene mukukumana naco.

16. N’ciani cinacitika kwa Paulo?

16 (2) Yelekezani. Yelekezani kuti ndimwe Paulo. Iye ni womangidwa m’maunyolo m’ndende ku Roma. Anamangidwapo kale kumbuyoko, koma tsopano sakukayikila zakuti adzaphedwa. Ena mwa mabwenzi ake amusiya, ndipo akuoneka wofooka kwambili.—2 Tim. 1:15.

17. Kodi zikanatheka Paulo kucita ciani?

17 Zikanatheka Paulo kusumika maganizo ake pa zakumbuyo, na kuganiza kuti ngati sakanasankha kukhala Mkhristu wokangalika motelo, mwina sakanamangidwa. Iye akanakwiyila amuna a m’cigawo ca Asia amene anamusiya, ndipo akanaleka kudalila mabwenzi ake ena. Koma Paulo sanacite zimenezo. N’ciani cinam’thandiza kupitilizabe kudalila mabwenzi ake komanso kukhala wotsimikiza kuti Yehova adzamupatsa mphoto?

18. Kodi Paulo anacita ciani pa vuto lalikulu limene anakumana nalo?

18 (3) Sinkha-sinkhani. Yankhani funso lakuti, “Kodi Paulo anacita ciani kuti adzithandize pa vuto lake?” Ngakhale kuti Paulo anali kudziŵa kuti posacedwa adzaphedwa, iye anasumikabe maganizo pa nkhani yaikulu, imene ni kubweletsa ulemelelo kwa Yehova. Ndipo anapitiliza kuganizila mmene angalimbikitsile ena. Iye anadalila Yehova mwa kupemphela nthawi zonse. (2 Tim. 1:3) M’malo mosumika maganizo ake pa aja amene anamusiya, anayamikila mocokela pansi pamtima thandizo limene anzake okhulupilika anam’patsa. Kuwonjezela apo, Paulo anapitilizabe kuŵelenga Mawu a Mulungu. (2 Tim. 3:16, 17; 4:13) Ndipo koposa zonse, iye anali na cidalilo conse kuti Yehova na Yesu amamukonda. Iwo sanamusiye, ndipo anali kudzam’patsa mphoto pa kukhulupilika kwake.

19. Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Paulo?

19 Yehova anali atacenjezelatu Paulo kuti anali kufunika kupilila mazunzo cifukwa cokhala Mkhristu. (Mac. 21:11-13) Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Paulo? Iye anayankha mapemphelo a Paulo, ndipo m’kupita kwa nthawi anam’patsa mphamvu. (2 Tim. 4:17) Mulungu anam’tsimikizila Paulo kuti adzalandila ndithu mphoto imene anaigwilila nchito molimbika. Iye anaseŵenzetsanso anzake a Paulo okhulupilika kum’patsa thandizo lofunikila.

20. Tili na Aroma 8:38, 39 m’maganizo, kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo?

20 (4) Seŵenzetsani. Dzifunseni kuti, ‘kodi ningatengele bwanji citsanzo ca Paulo?’ Mofanana na Paulo, tiyenela kuyembekezela kuzunzidwa kaamba ka cikhulupililo cathu. (Maliko 10:29, 30) Kuti tisungebe umphumphu wathu pa mayeselo, tiyenela kudalila Yehova mwa kum’fikila m’pemphelo na kukhalabe na pulogilamu yabwino yophunzila Baibo. Ndipo nthawi zonse tifunika kukumbukila kuti cimodzi mwa zinthu zofunika kwambili zimene tingacite ni kupeleka ulemelelo kwa Yehova. Tingakhale wotsimikiza kuti Yehova sadzatisiya konse ndipo palibe cimene wina aliyense angacite coletsa kuti Yehova atikonde.—Ŵelengani Aroma 8:38, 39; Aheb. 13:5, 6.

PHUNZILANI KWA ANTHU ENA OCHULIDWA M’BAIBO

21. N’ciani cinathandiza mlongo Aya na m’bale Hector kugonjetsa zopinga zimene anakumana nazo?

21 Mosasamala kanthu za vuto limene tili nalo, tingapeze mphamvu kucokela ku zitsanzo zochulidwa m’Baibo. Mwacitsanzo, mlongo Aya mpainiya ku Japan, anakamba kuti nkhani ya Yona inamuthandiza kuthetsa mantha amene anali nawo pocita ulaliki wa poyela. M’bale Hector, mnyamata wa ku Indonesia amene makolo ake satumikila Yehova, analimbikitsidwa na citsanzo ca Rute kuti aphunzile za Yehova na kumutumikila.

22. Kodi mungacite ciani kuti muzipindula kwambili na maseŵelo a m’Baibo kapena nkhani zakuti “Tsanzilani Cikhulupililo Cawo”?

22 Kodi mungapeze kuti zitsanzo za m’Baibo zimene zingakulimbikitseni? Mavidiyo athu na maseŵelo ongomvetsela komanso nkhani zakuti, “Tsanzilani Cikhulupililo Cawo,” zimathandiza kumvetsetsa zocitika za m’Baibo. * Musanayambe kutamba, kumvetsela, kapena kuŵelenga nkhani zofufuzidwa bwino zimenezi, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kupeza mfundo zimene mungaseŵenzetse. Yelekezani kuti munthu amene mukuŵelenga m’nkhaniyo ndinu. Sinkha-sinkhani zimene atumiki a Yehova amenewo anacita, na kuona mmene iye anawathandizila kugonjetsa mavuto amenewa. Ndiyeno seŵenzetsani zimene mwaphunzilazo pocita na vuto limene mwakumana nalo. Yamikilani Yehova pa thandizo limene wapeleka kale. Ndipo onetsani kuti mwayamikila thandizo limenelo mwa kupeza mipata yolimbikitsila ena na kuwacilikiza.

23. Malinga na Yesaya 41:10, 13, kodi Yehova anatilonjeza ciani?

23 Umoyo m’dziko lolamulidwa na Satanali, ungakhale wovuta kucita nawo ndipo nthawi zina tingasoŵe cocita. (2 Tim. 3:1) Koma tisade nkhawa kapena kucita mantha. Yehova adziŵa mavuto amene tipitamo. Tikagwa, iye analonjeza kuti adzatigwila mwamphamvu na dzanja lake lamanja. (Ŵelengani Yesaya 41:10, 13.) Tili na cidalilo conse cakuti adzaticilikiza, tingapeze mphamvu m’Malemba na kupilila vuto lililonse limene tingakumane nalo.

NYIMBO 96 Buku Lake la Mulungu ni Cuma

^ ndime 5 Nkhani zambili m’Baibo zimaonetsa kuti Yehova amakonda atumiki ake ndipo adzawathandiza pa mayeso awo onse. Nkhani ino idzafotokoza mmene tingacitile phunzilo la Baibo laumwini limene lingatithandize kupindula kwambili na nkhani zimene tiŵelenga.

^ ndime 2 Njila ya kaphunzilidwe imene taipeleka monga lingalilo pano, ni imodzi mwa njila zina zimene tingaseŵenzetse pophunzila. Malingalilo ena a mophunzilila Baibo mungawapeze mwa kuyang’ana mu Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova pansi pa mutu wakuti, “Baibo” pa kamutu kakuti “Kuŵelenga na kumvetsetsa Baibo.”

^ ndime 14 Musaŵelenge mavesi amenewa phunzilo la Nsanja ya Mlonda ili mkati.

^ ndime 22 Onani nkhani zakuti “Tsanzilani Cikhulupililo Cawo—Amuna ndi akazi ochulidwa m’Baibo” pa jw.org. (Pitani ku Chichewa pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUKHULUPILILA MULUNGU.)