Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 10

Monga Mpingo, Thandizani Maphunzilo a Baibo Kupita Patsogolo Kuti Akabatizike

Monga Mpingo, Thandizani Maphunzilo a Baibo Kupita Patsogolo Kuti Akabatizike

“Thupi lonselo limakula . . . malinga ndi nchito yoyenelela ya ciwalo ciliconse.”—AEF. 4:16.

NYIMBO 85 Tilandilane Wina Ndi Mnzake

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Ndani angathandize wophunzila Baibo kupita patsogolo kuti akabatizike?

MLONGO Amy wa ku Fiji anati: “N’nali kukonda zimene n’nali kuphunzila pa phunzilo la Baibo. N’nadziŵa kuti cinali coonadi. Koma n’tayamba kuyanjana na abale na alongo, m’pamene n’napanga masinthidwe ofunikila na kupita patsogolo mpaka kukabatizika.” Cocitika ca mlongo Amy cionetsa mfundo yofunika iyi: Wophunzila Baibo amapitabe patsogolo mpaka kukabatizika akamalandila thandizo locokela kwa ena mumpingo.

2 Wofalitsa aliyense angathandize kuti mpingo ukule. (Aef. 4:16) Mlongo mpainiya dzina lake Leilani wa ku Vanuatu anakamba kuti: “Pali mawu akuti kulela mwana n’kwatonse. Niona kuti n’zofanana na nchito yopanga ophunzila. Nthawi zambili zimadalila thandizo la mpingo wonse kuti munthu abwele m’coonadi.” A m’banja, mabwenzi na aziphunzitsi a kusukulu onse amacita mbali yawo pothandiza mwana kuti akule bwino. Amacita zimenezi mwa kulimbikitsa mwanayo na kum’phunzitsa zinthu zofunika. Mofananamo, ofalitsa angapeleke malangizo, cilimbikitso, na kukhala zitsanzo zabwino kwa maphunzilo a Baibo powathandiza kupita patsogolo kuti akabatizike.—Miy. 15:22.

3. Kodi muphunzilapo ciani pa zimene mlongo Ana, m’bale David, komanso mlongo Leilani anakamba?

3 N’cifukwa ciani wofalitsa amene amatsogoza phunzilo la Baibo ayenela kuvomela thandizo limene ofalitsa ena angapeleke kwa wophunzila wake? Onani zimene mlongo Ana, mpainiya wapadela ku Moldova anakamba. Iye ananena kuti: “N’covuta kwambili kuti munthu mmodzi akwanilitse mbali zonse zofunikila kuti wophunzila Baibo apite patsogolo.” M’bale David * mpainiya wapadela amene amatumikila ku dziko limodzi-modzilo anakamba kuti: “Nthawi zambili ofalitsa ena amakamba mfundo inayake imene imamufika pamtima wophunzila, imene sin’naiganizilepo.” Mlongo Leilani anakambanso cifukwa cina. Iye anati: “Cikondi na cidwi cimene wophunzila Baibo angaonetsedwe, cingam’thandize kuzindikila anthu a Yehova.”—Yoh. 13:35.

4. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

4 Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ningam’thandize bwanji wophunzila Baibo kupita patsogolo ngati sindine amene nimam’tsogoza phunzilo?’ Tiyeni tikambilane zimene tingacite tikapemphedwa kuti tikhalepo pa phunzilo la Baibo, na zimene tingacite wophunzila Baibo akayamba kupezeka kumisonkhano. Tidzaonanso mmene akulu angathandizile ophunzila Baibo kupita patsogolo kuti akabatizike.

MUKAPEMPHEDWA KUTI MUKHALEPO PA PHUNZILO LA BAIBO

Ngati mudzakhalapo potsogoza phunzilo la Baibo, konzekelani nkhani imene mudzakambilana (Onani ndime 5-7)

5. Kodi udindo wanu ni wotani mukapemphedwa kukhalapo pa phunzilo la Baibo?

5 Pa phunzilo la Baibo, mphunzitsi ndiye amakhala na udindo waukulu wothandiza wophunzilayo kumvetsa Mawu a Mulungu. Ngati mphunzitsiyo wakupemphani kuti mupite naye ku phunzilo, muzidziona kuti ndimwe wothandiza wake. Udindo wanu ni kum’cilikiza. (Mlal. 4:9, 10) Kodi mungacite ciani maka-maka kuti mukhale wothandiza wabwino pa phunzilo la Baibo?

6. Mukapemphedwa kuti mukakhalepo pa phunzilo la Baibo, kodi mungaseŵenzetse bwanji mfundo ya pa Miyambo 20:18?

6 Konzekelani phunzilo la Baibo. Coyamba, pemphani mphunzitsi kuti akuuzenkoni zina zokhudza wophunzilayo. (Ŵelengani Miyambo 20:18.) Mungamufunse kuti: “Mudziŵako zotani zokhudza wophunzilayo? Kodi mudzaphunzila naye mutu ciani? Mudzafuna kugogomeza mfundo yanji pa mutu umenewu? Kodi pali zina zimene niyenela kucita kapena kusacita kapenanso kusakamba pamene tikuphunzila naye? Ningacite ciani kuti nilimbikitse wophunzilayo kupita patsogolo?” Mwacionekele, mphunzitsi sangakuuzeni zacinsinsi zokhudza wophunzilayo. Koma zina zimene angakuuzenkoni zingakuthandizeni. Mmishonale wina dzina lake Joy amakambilana zimenezi na wofalitsa amene wapita naye ku phunzilo lake. Iye ananena kuti: “Kukambilana zimenezi kumathandiza amene napita naye ku phunzilo kuonetsa cidwi kwa wophunzila na kudziŵa zimene angakambe pa phunzilolo.”

7. N’cifukwa ciani imwe monga wothandiza muyenela kukonzekela phunzilo?

7 Ngati mwapemphedwa kuti mukakhalepo pa phunzilo, zingakhale bwino kukonzekela phunzilo limenelo. (Ezara 7:10) M’bale David amene tam’gwila mawu kuciyambi anakamba kuti: “Nimayamikila ngati munthu amene napita naye ku phunzilo wakonzekela, cifukwa amatha kupelekapo ndemanga zothandiza.” Kuwonjezela apo, wophunzila adzaona kuti nonse aŵili mwakonzekela bwino ndipo izi zidzam’patsa citsanzo cabwino. Ngakhale kuti simungakonzekele mwacikwane-kwane nkhaniyo, pezani ndithu nthawi yoona mfundo zikulu-zikulu na kuzisunga m’maganizo.

8. Mungacite ciani kuti pemphelo lanu lizikhala lopindulitsa pa phunzilo la Baibo?

8 Pemphelo ni lofunika kwambili pa phunzilo la Baibo. Conco, ganizilani pasadakhale zimene mungakambe ngati mungapemphedwe kupeleka pemphelo. Mukatelo, pemphelo lanu lidzakhala lopindulitsa. (Sal. 141:2) Mlongo Hanae wa ku Japan, amakumbukilabe mapemphelo amene mlongo wina, amene anali kubwela na mphunzitsi wake wa Baibo anali kupeleka. Iye ananena kuti: “N’naona kuti iye anali paubwenzi wolimba na Yehova, ndipo nanenso n’nafuna kukhala monga iye. N’naonanso kuti anali kunikonda cifukwa anali kuchula dzina langa m’mapemphelo ake.”

9. Malinga na Yakobo 1:19, mungacite ciani kuti mukhale wothandiza pa phunzilo la Baibo?

9 Cilikizani mphunzitsi pa phunzilo. Mlongo Omamuyovbi, mpainiya wapadela ku Nigeria ananena kuti: “Mnzako wothandiza amamvetsela mwachelu pa phunzilo. Mnzakoyo amapelekapo ndemanga zabwino, koma sakambapo kwambili podziŵa kuti mphunzitsi ndiye akutsogoza phunzilo.” Mungadziŵe bwanji nthawi yoyenela kukambapo pa phunzilo na zimene mungakambe? (Miy. 25:11) Mvetselani mwachelu pamene mphunzitsi na wophunzila akukambilana. (Ŵelengani Yakobo 1:19.) Mukacita zimenezi mudzakhala wokonzeka kupeleka thandizo pakafunikila kutelo. Komabe, mufunika kukhala wozindikila. Mwacitsanzo, simungafunike kukambapo kwambili, kudula mawu mphunzitsi, kapena kubweletsapo nkhani ina. Koma na ndemanga yacidule, fanizo, kapena funso, mungathandize kumveketsa mfundo imene ikuphunzitsidwa. Nthawi zina mungaone kuti mulibe zambili zokambapo pankhaniyo. Koma ngati mumuyamikila wophunzilayo na kumuonetsa cidwi, mudzam’thandiza kwambili kupita patsogolo.

10. Kodi kufotokozako zocitika za pa umoyo wanu kungam’thandize bwanji wophunzila Baibo?

10 Fotokozankoni zocitika za mu umoyo wanu. Ngati m’poyenela, fotokozelani wophunzilayo mmene munaphunzilila coonadi, mmene munagonjetsela copinga cina cake kapena mmene Yehova wakuthandizilani mu umoyo wanu. (Sal. 78:4, 7) Mwina izi n’zimene wophunzilayo angafunikile kumva. Zimenezi zingalimbitse cikhulupililo cake, kapena kum’limbikitsa kupita patsogolo mpaka kukabatizika. Ndipo mwina zingam’thandizenso kuona mmene angagonjetsele ciyeso cimene akukumana naco. (1 Pet. 5:9) M’bale Gabriel wa ku Brazil amene tsopano akutumikila monga mpainiya, amakumbukila zimene zinam’thandiza pamene anali kuphunzila Baibo. Iye anafotokoza kuti: “N’tamvela zocitika za pa umoyo wa abale, n’nadziŵa kuti Yehova amaona mavuto amene timakumana nawo. N’nadziŵanso kuti na ine ningapilile ngati iwo anatha kuwapilila.”

WOPHUNZILA BAIBO AKAYAMBA KUPEZEKA KUMISONKHANO

Tonsefe tingalimbikitse wophunzila kupitiliza kupezeka kumisonkhano (Onani ndime 11)

11-12. N’cifukwa ciani tiyenela kumulandila mwacimwemwe wophunzila Baibo amene amafika kumisonkhano?

11 Kuti wophunzila Baibo apite patsogolo mpaka kukabatizika, afunika kumapezeka kumisonkhano yampingo na kupindula na misonkhanoyo. (Aheb. 10:24, 25) Nthawi zambili mphunzitsi ndiye amaitanila wophunzila kumsonkhano woyamba. Akabwela kumisonkhano, tonsefe tingam’limbikitse kupitilizabe kubwela ku Nyumba ya Ufumu. Kodi tingacite bwanji zimenezo?

12 Landilani wophunzilayo mwacimwemwe. (Aroma 15:7) Ngati wophunzila alandilidwa bwino kumisonkhano, nthawi zambili amapitilizabe kubwela ku Nyumba ya Ufumu. M’thandizeni kukhala womasuka ndipo m’patseni moni mwacimwemwe na kum’dziŵikitsa kwa ena. Pewani kuganiza kuti pali wina amene akumusamalila. Mwina mphunzitsi wake angacedwe kufika kumisonkhano, kapena angatangwanike na zocitika zina. Mvetselani mwachelu pamene wophunzilayo akulankhula ndipo muonetseni cidwi. Kodi pangakhale zotulukapo zotani mukam’landilani mwacimwemwe wophunzila? Onani citsanzo ca m’bale Dmitrii amene anabatizika zaka zingapo zapitazo, ndipo tsopano akutumikila monga mtumiki wothandiza. Pokamba za msonkhano woyamba umene anapitako, m’baleyo anakamba kuti: “Nili womangika panja pa Nyumba ya Ufumu, m’bale wina ananiona ndipo mokoma mtima ananitenga kupita nane mkati. Ambili anabwela kudzanipatsa moni. N’nadabwa kwambili. N’nakondwela ngako cakuti n’nafuna kuti tizisonkhana tsiku lililonse mlungu uliwonse. N’nali n’sanaonepo zimenezi kwina kulikonse.”

13. Kodi khalidwe lanu lingam’khudze bwanji wophunzila Baibo?

13 Khalani citsanzo cabwino. Khalidwe lanu lingam’thandize wophunzila Baibo kutsimikiza kuti wapezadi coonadi. (Mat. 5:16) M’bale Vitalii amene tsopano ni mpainiya ku Moldova anafotokoza kuti: “N’naona mmene ena mumpingo anali kukhalila, kuganizila, komanso mmene anali kucitila zinthu. Izi zinanitsimikizila kuti Mboni za Yehova zimayendadi na Mulungu.”

14. Kodi citsanzo canu cingathandize bwanji wina kupitabe patsogolo?

14 Kuti wophunzilayo ayenelele ubatizo, afunika kuseŵenzetsa zimene amaphunzila. Kucita izi nthawi zina kumakhala kovuta. Koma wophunzilayo akaona mmene inu mukupindulila cifukwa coseŵenzetsa mfundo za m’Baibo, nayenso angalimbikitsidwe kutengela citsanzo canu. (1 Akor. 11:1) Ganizilani citsanzo ca mlongo Hanae amene tam’chula kumayambililo. Iye anakamba kuti: “Abale na alongo anali citsanzo cabwino kwa ine, cifukwa anali atayamba kale kuseŵenzetsa zimene ine n’nali kuphunzila. N’naona mmene ningakhalile wolimbikitsa, wokhululuka, komanso mmene ningaonetsele cikondi. Iwo nthawi zonse anali kukamba zabwino za ena, ndipo n’nali kufuna kutengela citsanzo cawo.”

15. Kodi Miyambo 27:17 itithandiza bwanji kuona cifukwa cake tiyenela kukhala bwenzi la wophunzila Baibo pamene akupitiliza kupezeka kumisonkhano?

15 Pangani ubwenzi na wophunzilayo. Pamene wophunzilayo apitiliza kubwela kumisonkhano, pitilizani kumuonetsa cidwi. (Afil. 2:4) Bwanji osaceza naye kuti mudziŵane bwino? Popanda kuloŵelela nkhani zake zaumwini, mungamuyamikile pa masinthidwe amene wapanga, na kumufunsa za mmene phunzilo la Baibo likuyendela, za banja lake komanso nchito yake. Kukambilana zimenezi kudzakuthandizani kuti muyambe kugwilizana kwambili. Ngati mwakhala bwenzi la wophunzilayo, mudzam’thandiza kupita patsogolo kuti akabatizike. (Ŵelengani Miyambo 27:17.) Mlongo Hanae lomba ni mpainiya wanthawi zonse. Pokamba za nthawi yoyamba pamene anayamba kupezeka kumisonkhano, iye anati: “Pamene n’napanga mabwenzi mumpingo n’nali kuyembekezela mwacidwi kupita kumisonkhano, ndipo n’nali kupezekapo ngakhale pamene n’nali wolema. N’nali kusangalala kukhala na mabwenzi atsopano, ndipo izi zinanithandiza kuthetsa ubwenzi na anthu amene sanali kukhulupilila zimene n’nali kuphunzila. N’nali kufuna kumuyandikila Yehova komanso kugwilizana na abale na alongo. Conco n’nasankha kubatizika.”

16. N’ciani cina cimene mungacite kuti muthandize wophunzila Baibo kukhala womasuka mumpingo?

16 Pamene wophunzila apita patsogolo na kupanga masinthidwe, m’thandizeni kumva kuti ni wofunika mumpingo. Mungacite zimenezi mwa kukhala woceleza. (Aheb. 13:2) Ponena za nthawi pamene anali kuphunzila Baibo, m’bale Denis amene akutumikila ku Moldova anati: “Nthawi zambili abale anali kuniitanila kumaceza pamodzi na mkazi wanga. Abalewo anatiuza mmene Yehova anali kuwathandizila. Zimenezo zinatilimbikitsa. Macezawo anatithandiza kukhala otsimikiza kufuna kutumikila Yehova komanso kuti tidzakhala na tsogolo labwino tikasankha kutelo.” Wophunzila Baibo akayenelela kukhala wofalitsa, mungam’pemphe kupita naye mu ulaliki. M’bale Diego wa ku Brazil anakamba kuti: “Abale ambili anali kunipempha kuti nipite nawo mu ulaliki. Imeneyi inali njila yabwino yakuti niŵadziwe bwino. Pamene n’naŵadziŵa bwino, n’naphunzila zambili, ndipo n’namvela kuti nili pafupi kwambili na Yehova na Yesu.”

KODI AKULU ANGATHANDIZE BWANJI?

Akulu, cikondi canu cingathandize ophunzila Baibo kupita patsogolo (Onani ndime 17)

17. Kodi akulu angawathandize bwanji ophunzila Baibo?

17 Pezani nthawi yokambilana na ophunzila Baibo. Akulu, cikondi canu cingathandize wophunzila kupita patsogolo na kukabatizika. Kodi mungamakambilaneko na ophunzila Baibo kumisonkhano? Iwo adzaona kuti muli nawo cidwi mukamakumbukila maina awo, makamaka akayamba kupelekapo ndemanga. Kodi mungakonzenso ndandanda yanu ya zocita kuti muziyenda kaŵili-kaŵili na wofalitsa wina pokatsogoza phunzilo lake la Baibo? Mungam’thandize kwambili wophunzila Baibo, kuposa mmene mungaganizile. Mlongo mpainiya wa ku Nigeria dzina lake Jackie ananena kuti: “Ophunzila ambili amadabwa akadziŵa kuti m’bale amene n’napita naye pokaphunzila nawo ni mkulu. Wophunzila Baibo wina anakamba kuti: ‘M’busa wa ku chalichi kwathu sangacite zimenezo. Iye amangoyendela cabe anthu olemela ndipo amatelo kokha ngati amulipila.’” Wophunzilayo tsopano amapezeka kumisonkhano.

18. Kodi akulu angakwanilitse bwanji udindo umene anapatsidwa malinga na Machitidwe 20:28?

18 Thandizani aphunzitsi a Baibo na kuwalimbikitsa. Akulu muli na udindo waukulu wothandiza ofalitsa kukhala aluso mu ulaliki, kuphatikizapo kuwathandiza pa nchito yawo yophunzitsa anthu Baibo. (Ŵelengani Machitidwe 20:28.) Ngati wina acita manyazi kutsogoza phunzilo la Baibo imwe mulipo, dzipelekeni kuti mutsogoze ndinu. Mlongo Jackie amene tam’gwila mawu kuciyambi anafotokoza kuti: “Nthawi zambili akulu amanifunsa za maphunzilo anga a Baibo. Nikakumana na zovuta zina pa nchito yotsogoza maphunzilo a Baibo, iwo amapeleka malangizo othandiza.” Akulu angacite zambili pothandiza aphunzitsi a Baibo na kuwalimbikitsa kupitilizabe kugwila nchito yawo. (1 Ates. 5:11) Mlongo Jackie anawonjezela kuti: “Nimamvela bwino akulu akanilimbikitsa na kuniuza kuti amayamikila nchito imene nimagwila molimbika. Mawu awo olimbikitsa amanitsitsimula monga madzi ozizila kukatentha. Cilimbikitso cawo cimakulitsa cidalilo canga na kuwonjezela cimwemwe canga pa nchito yotsogoza maphunzilo a Baibo.”—Miy. 25:25.

19. N’ciani cingatibweletsele cimwemwe tonsefe?

19 Ngakhale kuti palipano sitikutsogoza phunzilo la Baibo, tingathandizebe wina wake kukula mwauzimu. Popanda kukambapo kwambili, tingacilikize mphunzitsi pa phunzilo na ndemanga zathu zokonzekela bwino. Tingapange ophunzila kukhala mabwenzi athu akabwela ku Nyumba ya Ufumu, komanso tingakhale zitsanzo zabwino kwa iwo. Ndipo akulu angalimbikitse ophunzila mwa kupatula nthawi yoceza nawo, komanso angalimbikitse aphunzitsi mwa kuwathandiza na kuwayamikila. Kukamba zoona, palibe cina cosangalatsa kuposa kudziŵa kuti tinacitako ngakhale kagawo kocepa pothandiza wina kukonda Atate wathu Yehova na kum’tumikila!

NYIMBO 79 Aphunzitseni Kucilimika

^ ndime 5 Ena a ife tilibe mwayi wotsogoza phunzilo la Baibo palipano. Ngakhale n’telo, aliyense wa ife angathe kuthandiza wina kupita patsogolo kuti akabatizike. M’nkhani ino, tione mmene aliyense wa ife angathandizile wophunzila Baibo kukwanilitsa colinga cimeneco.

^ ndime 3 Maina ena asinthidwa.