Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 10

N’zotheka ‘Kuvula Umunthu Wakale’

N’zotheka ‘Kuvula Umunthu Wakale’

“Vulani umunthu wakale pamodzi ndi nchito zake.”—AKOL. 3:9.

NYIMBO 29 Tikhala Monga mwa Dzina Lathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi umoyo wanu unali bwanji musanayambe kuphunzila Baibo?

 KODI umoyo wanu unali bwanji musanayambe kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova? Ambili a ife sitingakonde n’komwe kuganizila mmene unalili. Mwacionekele, miyezo ya m’dzikoli ya cabwino na coipa, ni imene inali kuumba maganizo athu na umunthu wathu. Ngati ni mmene zinalili, ndiye kuti ‘tinalibe ciyembekezo, komanso Mulungu m’dzikoli.’ (Aef. 2:12) Koma tinasintha umunthu wathu cifukwa cophunzila Baibo.

2. Kodi munadziŵa zotani mutayamba kuphunzila Baibo?

2 Mutayamba kuphunzila Baibo, munadziŵa kuti muli na Atate wanu wakumwamba amene amakukondani kwambili. Munazindikila kuti, kuti mukondweletse Yehova na kukhala m’banja la alambili ake, muyenela kusintha kwambili khalidwe lanu, mmene mumaonela zinthu, komanso kaganizidwe kanu. Kenako, munayenela kuphunzila kutsatila miyezo yake yapamwamba.—Aef. 5:3-5.

3. Malinga n’kunena kwa Akolose 3:9, 10, kodi Yehova amafuna kuti ticite ciyani? Nanga tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 Mlengi wathu komanso Atate wathu wakumwamba Yehova, ali na ufulu woika miyezo ya makhalidwe abwino imene a m’banja lake ayenela kutsatila. Ndipo iye amafuna kuti tisanabatizike, tiyesetse ‘kuvula umunthu wakale pamodzi na nchito zake.’ * (Ŵelengani Akolose 3:9, 10.) Nkhani ino, ithandize aja amene akufuna kukabatizika kuyankha mafunso atatu aya: (1) Kodi “umunthu wakale” n’ciyani? (2) N’cifukwa ciyani Yehova amatilamula kuvula umunthu wakale? (3) Tingavule bwanji umunthu wakale? Ife amene tinabatizika kale, nkhani ino itithandize kuti tisayambenso makhalidwe oipa a umunthu wakale.

KODI “UMUNTHU WAKALE” N’CIYANI?

4. Kodi munthu amene ali na “umunthu wakale” amakhala na makhalidwe otani?

4 Munthu amene ali na “umunthu wakale,” kaganizidwe kake, komanso kacitidwe kake ka zinthu, kamakhala m’njila ya ucimo. Iye angakhale wodzikonda, wa mtima wapacala, wosayamika, komanso wonyada. Angamakonde kupenyelela zamalisece, komanso mafilimu oipa. N’zoona kuti iye angakhale na makhalidwe abwino, ndipo angamadziimbe mlandu pa zoipa zimene amacita kapena kukamba. Koma alibe mtima uja wofunitsitsa kusintha kaganizidwe kake na khalidwe lake.—Agal. 5:19-21; 2 Tim. 3:2-5.

Tikavula “umunthu wakale,” sitimalolanso makhalidwe akuthupi kutilamulila (Onani ndime 5) *

5. N’cifukwa ciyani tiyenela kuona zinthu moyenelela pa nkhani yovula umunthu wakale? (Machitidwe 3:19)

5 Popeza ndife opanda ungwilo, sitingathetseletu maganizo onse osayenela, komanso zilakolako zoipa mumtima mwathu. Nthawi zina, tidzakamba mawu kapena kucita zinthu zimene tingadziimbe mlandu pambuyo pake. (Yer. 17:9; Yak. 3:2) Koma tikavula umunthu wakale, sitimalolanso makhalidwe akuthupi kutilamulila. Timasintha n’kukhala munthu wa khalidwe labwino.—Yes. 55:7; ŵelengani Machitidwe 3:19.

6. N’cifukwa ciyani Yehova amatilimbikitsa kuthetsa maganizo oipa komanso zizolowezi zoipa za umunthu wakale?

6 Yehova amatilimbikitsa kuthetsa maganizo oipa na zizolowezi zoipa cifukwa amatikonda kwambili, ndipo amafuna kuti tizikondwela na moyo. (Yes. 48:17, 18) Iye amadziŵa kuti anthu amene amagonja ku zilakolako zoipa amadzipweteka okha, komanso kupweteka ena. Cimamuŵaŵa akaona kuti tadzipweteka tokha na kupweteka ena.

7. Malinga na Aroma 12:1, 2, n’cisankho citi cimene tiyenela kupanga?

7 Mabwenzi athu ena kapena acibale, poyamba angatinyoze pamene tikusintha umunthu wathu. (1 Pet. 4:3, 4) Iwo angatiuze kuti tili na ufulu wocita ciliconse cimene tifuna, komanso kuti sitiyenela kulola ena kutiuza zocita. Koma anthu amene amakana miyezo ya Yehova sikuti amadziimila pawokha. M’ceniceni, iwo amalola dziko lolamulidwa na Satana kuwaumba. (Ŵelengani Aroma 12:1, 2.) Motelo, tonsefe tiyenela kupanga cisankho: Kaya kuvalabe umunthu wathu wakale, wotsogoleledwa na ucimo komanso dziko la Satana, kapena kulola Yehova kusintha umunthu wathu kuti tikhale munthu wabwino amene tiyenela kukhala.—Yes. 64:8.

KODI ‘MUNGAVULE’ BWANJI UMUNTHU WAKALE?

8. N’ciyani cingatithandize kuthetsa maganizo olakwika na zizolowezi zoipa?

8 Yehova amadziŵa kuti zimafuna nthawi komanso khama, kuti tithetse maganizo olakwika na zizolowezi zoipa. (Sal. 103:13, 14) Koma kupitila m’Mawu ake, mzimu wake, na gulu lake, Yehova amatipatsa nzelu, mphamvu, na thandizo kuti tisinthe umunthu wathu. Mosakayikila iye wakuthandizani kale. Tsopano, tiyeni tikambilane zimene mungacite kuti mupitilize kuvula umunthu wanu wakale, n’colinga cakuti muyenelele ubatizo.

9. Kodi Mawu a Mulungu angakuthandizeni bwanji?

9 Gwilitsilani nchito Baibo kuti mudzisanthule mofikapo. Mawu a Mulungu ali ngati galasi. Angakuthandizeni kusanthula maganizo anu, zokamba zanu, na zocita zanu. (Yak. 1:22-25) Mphunzitsi wanu wa Baibo, kapena Akhristu ena ofikapo kuuzimu angakupatseni malangizo othandiza. Mwacitsanzo, angaseŵenzetse Malemba pokuthandizani kuona mbali zimene mumacita bwino, komanso zimene simucita bwino. Iwo angakuonetseni mopezela mfundo za m’Baibo zimene zingakuthandizeni kuthetsa zizolowezi zoipa. Ndipo nthawi zonse Yehova ni wokonzeka kukuthandizani. Iye angakuthandizeni bwino kwambili, cifukwa amadziŵa za mumtima mwanu. (Miy. 14:10; 15:11) Conco, muzipemphela kwa iye nthawi zonse, na kuŵelenga Mawu ake tsiku lililonse.

10. Kodi mwaphunzila ciyani pa citsanzo ca Elie?

10 Khulupililani kuti miyezo ya Yehova ni yabwino koposa. Zonse zimene Yehova amatiuza kucita zimakhala zopindulitsa. Aja amene amatsatila miyezo yake amadzipezela ulemu, amakhala na umoyo waphindu, ndiponso amakhala na cimwemwe ceniceni. (Sal. 19:7-11) Koma aja amene amanyalanyaza miyezo ya Yehova, amakumana na mavuto obwela cifukwa cocita nchito za thupi. Pa nkhani yonyalanyaza miyezo ya Mulungu, onani zinacitikila mwamuna wina dzina lake Elie. Iye analeledwa na makolo okonda Yehova. Koma atafika zaka zaunyamata, anayamba kugwilizana na anzake oipa. Anayamba makhalidwe oipa monga kumwa mankhwala osokoneza bongo, ciwelewele, na kuba. Elie anakamba kuti izi zinapangitsa kuti akhale waukali kwambili, komanso waciwawa. Iye anati: “Mwacidule ningati n’nali kucita zonse zimene n’naphunzila kuti Mkhristu sayenela kucita.” Ngakhale n’telo, iye sanaiŵale zimene anaphunzila ali wacicepele. Pothela pake, anayambanso kuphunzila Baibo. Anacita khama kuti athetse zizolowezi zake zoipa, ndipo mu 2000 anabatizika. Kodi anapindula bwanji cifukwa cotsatila miyezo ya Yehova? Elie anati: “Tsopano nili na mtendele wa maganizo komanso cikumbumtima coyela.” * Citsanzo ici, cionetsa kuti anthu amene amakana miyezo ya Yehova amadzipweteka okha. Ngakhale n’conco, Yehova ni wofunitsitsa kuwathandiza kuti asinthe.

11. Ni zinthu ziti zimene Yehova amadana nazo?

11 Phunzilani kudana na zimene Yehova amadana nazo. (Sal. 97:10) Baibo imati Yehova amadana na “maso odzikweza, lilime lonama, [komanso] manja okhetsa magazi a anthu osalakwa.” (Miy. 6:16, 17) Iye amadananso na “munthu wacinyengo.” (Sal. 5:6) Yehova amadana nawo kwambili makhalidwe amenewa moti m’nthawi ya Nowa, anaseselatu anthu oipa cifukwa anali atadzadza dziko lonse na ciwawa. (Gen. 6:13) Ganizilaninso citsanzo ici. Kupitila mwa mneneli Malaki, Yehova anakamba kuti amadana na anthu amene amasemela akazi awo mlandu wabodza n’colinga cakuti asudzulane. Mulungu salandila kulambila kwawo, ndipo adzawaweluza pa khalidwe lawo loipalo.—Mal. 2:13-16; Aheb. 13:4.

Tiyenela kunyansidwa na cinthu cimene Yehova amati n’coipa, monga mmene tinganyansidwile na cakudya coola (Onani ndime 11-12)

12. Kodi ‘kunyansidwa na coipa’ kumatanthauza ciyani?

12 Yehova amafuna kuti ‘tizinyansidwa na coipa.’ (Aroma 12:9) Mawu akuti ‘kunyansidwa’ naco cinthu, amatanthauza kudana naco kwambili, ngakhalenso kucita naco mselu. Tangoganizilani mmene mungamvelele atakuuzani kuti mudye cakudya coola. Kungomva cabe zimenezo, kungakudwalitseni. Mofananamo, nafenso tiyenela kunyansidwa na maganizo ofuna kucita cimene Yehova amati n’coipa.

13. N’cifukwa ciyani tiyenela kuteteza maganizo athu?

13 Tetezani maganizo anu. Maganizo ndiwo amasonkhezela zocita zathu. Ndiye cifukwa cake, Yesu anatiphunzitsa kuti tiyenela kukaniza maganizo amene angatitsogolele kucita chimo lalikulu. (Mat. 5:21, 22, 28, 29) Timafuna kukondweletsa Atate wathu wakumwamba, si conco kodi? Motelo, n’kofunika kwambili kucotsa mwamsanga maganizo oipa amene angabwele mumtima mwathu.

14. Kodi mawu athu amavumbula ciyani? Nanga tiyenela kuyankha mafunso ati?

14 Samalani na zimene mumakamba. Yesu anati: “Zotuluka m’kamwa zimacokela mumtima.” (Mat. 15:18) Inde, zokamba zathu zimavumbula umunthu wathu wamkati. Conco, dzifunseni mafunso aya: ‘Kodi nimapewa kunama, ngakhale pamene naona kuti kukamba zoona kunganiloŵetse m’mavuto? Pokhala munthu ali pa banja, kodi nimapewa kuceza mokopana na munthu amene si mkazi kapena mwamuna wanga? Kodi nimapewelatu kukamba mawu oipa? Kodi nimayankha modekha wina akanikhumudwitsa?’ Kuganizila mafunso amenewa kudzakuthandizani kwambili. Mawu anu tingawayelekezele na mabatani a pa covala. Mukamasula mabatani, m’posavuta kuvula covala. Mofananamo, mukayesetsa kusiya kukamba mawu acipongwe, kunama, kapena kutukwana, cidzakhala cosavuta kwa inu kuvula umunthu wakale.

15. Kodi kupacika umunthu wathu wakale “pamtengo” kumatanthauza ciyani?

15 Yesetsani kucitapo kanthu mwamsanga. Mtumwi Paulo, anafotokoza citsanzo cogwila mtima cotithandiza kuona kufunika kopanga masinthidwe ofunikila pa umoyo wathu. Iye analemba kuti tiyenela kupacika umunthu wathu wakale “pamtengo.” (Aroma 6:6) M’mawu ena, tingati tiyenela kutengela citsanzo ca Khristu. Izi zitanthauza kuti tiyenela kupha maganizo osayenela na makhalidwe oipa amene Yehova amadana nawo. Tikatelo, m’pamene tidzakhala na cikumbumtima coyela, ndiponso ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya. (Yoh. 17:3; 1 Pet. 3:21) Kumbukilani kuti Yehova sadzasintha miyezo yake kuti igwilizane na khalidwe lathu. M’malo mwake, ndife tiyenela kusintha na kutsatila miyezo yake.—Yes. 1:16-18; 55:9.

16. N’cifukwa ciyani muyenela kupitiliza kukaniza zilakolako zoipa?

16 Pitilizani kukaniza zilakolako zoipa. Ngakhale pambuyo pa ubatizo, mudzafunika kupitiliza kukaniza zilakolako zoipa. Ganizilani citsanzo ici ca mwamuna wina dzina lake Maurício. Ali wacinyamata, anayamba kugonana na amuna anzake. Koma potsilizila pake, anayamba kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova. Atapanga masinthidwe ofunikila, anabatizika mu 2002. Ngakhale kuti watumikila Yehova kwa zaka zambili, Maurício anati: “Nthawi zina nimalimbana na maganizo olakalaka zoipa.” Koma samalola zimenezo kumulefula. Iye anati: “ Nimalimbikitsidwa kudziŵa kuti nikasankha kusacita zoipazo, nimakondweletsa Yehova.” *

17. N’ciyani colimbikitsa cimene mwapeza pa citsanzo ca Nabiha?

17 Pemphani Yehova kuti akuthandizeni, ndipo dalilani mzimu wake osati mphamvu zanu. (Agal. 5:22; Afil. 4:6) Tiyenela kucita khama kuti tivule umunthu wakale na kusauvalanso. Ganizilani citsanzo ici ca mayi wina dzina lake Nabiha. Atate ake anacoka panyumba pamene iye anali na zaka 6. Anati: “Atate atacoka, n’napsinjika maganizo kwambili.” Pamene Nabiha anali kukula, anakhala waukali kwambili, komanso wa mtima wapacala. Atayamba kugulitsa mankhwala osokoneza bongo anamangidwa, ndipo anakhala m’ndende kwa zaka ndithu. Mboni zimene zinali kulalikila ku ndendeko, zinayamba kuphunzila naye Baibo. Nabiha anayamba kupanga masinthidwe aakulu. Iye anati: “Sin’navutike kuleka makhalidwe ena oipa. Koma cinali covuta kwambili kwa ine ni kuleka kupepa fwaka.” Nabiha analimbana na vutoli kwa caka na miyezi, koma pamapeto pake anakwanitsa kuleka fwaka. Kodi anakwanitsa bwanji? Iye anati: “Kupemphela kwa Yehova nthawi zonse n’kumene kunanithandiza kwambili kuti nileke.” Iye amauza ena kuti: “Sinikaikila kuti ngati ine n’nakwanitsa kusintha kuti nitumikile Yehova, n’zotheka aliyense kusintha!” *

MUNGAYENELELE UBATIZO!

18. Malinga na 1 Akorinto 6:9-11, kodi atumiki a Mulungu ambili akwanitsa kucita ciyani?

18 M’nthawi ya atumwi, amuna na akazi ena amene Yehova anasankha kuti akalamulile na Khristu, anali na makhalidwe oipa asanakhale Akhristu. Mwacitsanzo, ena anali acigololo, amathanyula, komanso akawalala. Komabe, mzimu woyela wa Mulungu unawathandiza kusintha umunthu wawo. (Ŵelengani 1 Akorinto 6:9-11.) Mofananamo, Baibo yathandiza anthu ofika mamiliyoni kusintha umoyo wawo. * Iwo afika poleka makhalidwe oipa amene anali ozika mizu mwa iwo. Citsanzo cawo ni umboni wakuti inunso mungasinthe umunthu wanu, na kuthetsa zizolowezi zoipa kuti muyenelele ubatizo.

19. Tidzakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?

19 Kuwonjezela pa kuvula umunthu wawo wakale, anthu amene akufuna kukabatizika ayenelanso kucita khama kuti avale umunthu watsopano. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene tingacitile zimenezo, komanso mmene ena angatithandizile.

NYIMBO 41 Mvelani Pemphelo Langa Conde

^ Kuti tiyenelele ubatizo, tiyenela kuyesetsa kusintha umunthu wathu. Nkhani ino, itithandiza kudziŵa makhalidwe amene amapanga umunthu wakale, cifukwa cake tiyenela kuvula umunthu wakale umenewo, komanso mmene tingacitile zimenezo. Nkhani yotsatila, idzafotokoza mmene tingapitilizile kuvala umunthu watsopano, ngakhale pambuyo pa ubatizo.

^ KUFOTOKOZELA MAWU ENA: ‘Kuvula umunthu wakale,’ kumatanthauza kuleka makhalidwe oipa, komanso zizolowezi zimene Yehova sakondwela nazo. Ndipo tiyenela kucita izi tisanabatizike.—Aef. 4:22.

^ Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani yakuti “Baibulo Limasintha Anthu—‘Ndinazindikila Kuti Ndiyenela Kubwelela kwa Yehova,’” mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 2012.

^ Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani yakuti Baibulo Limasintha Anthu—‘Anandikomela Mtima Kwambili,’” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2012.

^ Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani yakuti “Baibulo Limasintha Anthu—‘Ndinali Munthu Waukali, Komanso Wosacedwa Kupsa Mtima,’” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2012.

^ Onani bokosi lakuti “ Baibo Imasintha Anthu.”

^ MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Kuthetsa makhalidwe osayenela na zizolowezi zoipa, kuli monga kutaya covala cakale.