Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 11

Pitilizani Kuvala “Umunthu Watsopano” Pambuyo pa Ubatizo

Pitilizani Kuvala “Umunthu Watsopano” Pambuyo pa Ubatizo

“Muvale umunthu watsopano.”—AKOL. 3:10.

NYIMBO 49 Tikondweletse Mtima wa Yehova

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’ciyani cimene kambili cimaumba umunthu wathu?

 KAYA tinabatizika caposacedwa kapena kwa zaka zambili, tonsefe tiyenela kukhala na umunthu umene Yehova amakonda. Kuti tikhale nawo, tiyenela kulamulila kaganizidwe kathu. Cifukwa ciyani? Cifukwa kambili, maganizo athu ndiwo amaumba umunthu wathu. Ngati nthawi zonse timaganizila mmene tingakhutilitsile zolakalaka zathu za kuthupi, tingakambe na kucita zinthu zoipa. (Aef. 4:17-19) Koma ngati tidzaza maganizo athu na zinthu zabwino, tidzakamba na kucita zinthu m’njila imene imakondweletsa Atate wathu, Yehova.—Agal. 5:16.

2. Tikambilane mafunso ati m’nkhani ino?

2 Monga tinaonela m’nkhani yapita, sitingaletseletu maganizo onse oipa kuloŵa mumtima mwathu. Koma tingasankhe kusacita zimene tikuganizazo. Tisanabatizike, tiyenela kuleka kukamba zinthu zimene Yehova amadana nazo, komanso kusazicita. Iyi ndiye sitepu yoyamba ndiponso yofunika kwambili kuti tivule umunthu wakale. Komabe, kuti tim’kondweletse kwambili Yehova, tiyenelanso kumvela lamulo ili lakuti: “Muvale umunthu watsopano.” (Akol. 3:10) M’nkhani ino, tiyankha mafunso aya: Kodi “umunthu watsopano” n’ciyani? Kodi tingavale bwanji umunthu watsopano na kusauvula?

KODI “UMUNTHU WATSOPANO” N’CIYANI?

3. Kodi “umunthu watsopano” n’ciyani? Nanga munthu amauvala bwanji? (Agalatiya 5:22, 23)

3 “Umunthu watsopano,” ni kaganizidwe komanso kacitidwe ka zinthu kotengela citsanzo ca Yehova. Munthu amavala umunthu watsopano mwa kuonetsa makhalidwe amene mzimu woyela wa Mulungu umabala, na kulola mzimuwo kutsogolela maganizo ake, mtima wake, ndiponso zocita zake. (Ŵelengani Agalatiya 5:22, 23.) Mwacitsanzo, iye amakonda Yehova na anthu ake. (Mat. 22:36-39) Amakhalabe wacimwemwe ngakhale pamene akukumana na mayeso. (Yak. 1:2-4) Iye ni wobweletsa mtendele. (Mat. 5:9) Amakhala woleza mtima, komanso wacifundo akamacita zinthu na ena. (Akol. 3:13) Amakonda zabwino na kuzicita. (Luka 6:35) Iye amaonetsa mwa zocita zake kuti ali na cikhulupililo colimba mwa Atate ake wakumwamba. (Yak. 2:18) Cina, amakhalabe wodekha ena akamukhumudwitsa, komanso wodziletsa akayesedwa kucita zosayenela.—1 Akor. 9:25, 27; Tito 3:2.

4. Kuti tivale umunthu watsopano, kodi tiyenela kukhala na makhalidwe ochulidwa pa Agalatiya 5:22, 23 lililonse palokha? Fotokozani.

4 Kuti tivale umunthu watsopano, tiyenela kukhala na makhalidwe onse ochulidwa pa Agalatiya 5:22, 23, ndiponso pa Malemba ena m’Baibo. * Makhalidwe amenewa sali ngati zovala zimene ciliconse timacivala pacokha. Koma makhalidwe amenewa amaloŵana, mbali zake zina zimapezekanso m’makhalidwe anzake. Mwacitsanzo, ngati mnzanu mumam’kondadi, mumamulezelanso mtima komanso kumucitila cifundo. Ndiponso, kuti muonetse ubwino wanu, muyenelanso kukhala wodekha komanso wodziletsa.

KODI TINGAVALE BWANJI UMUNTHU WATSOPANO

Tikatengela kwambili maganizo a Yesu, m’pamenenso tidzakwanitsa kuonetsa bwino makhalidwe ake (Onani ndime 5, 8, 10, 12, 14)

5. Kodi kukhala na “maganizo a Khristu” kumatanthauza ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani tiyenela kuphunzila umoyo wa Yesu? (1 Akorinto 2:16)

5 Ŵelengani 1 Akorinto 2:16. Kuti tivale umunthu watsopano, tiyenela kukhala na “maganizo a Khristu.” M’mawu ena tingati, tiyenela kuphunzila mmene Yesu amaganizila, na kutengela citsanzo cake. Iye amaonetsa bwino kwambili cipatso ca mzimu wa Mulungu. Monga galasi limene limaonetsa bwino zinthu, iye amaonetsa makhalidwe a Yehova ndendende. (Aheb. 1:3) Tikamaganiza kwambili ngati Yesu, m’pamenenso tidzacita zinthu monga iye, komanso tidzatha kuonetsa bwino makhalidwe ake.—Afil. 2:5.

6. Kodi tiyenela kukumbukila mfundo ziti pamene tikuvala umunthu watsopano?

6 Kodi n’zothekadi kutengela citsanzo ca Yesu? Mwina tingaganize kuti: ‘Yesu ni wangwilo. Siningakwanitse kucita zinthu ndendende mmene anali kucitila.’ Mukakhala na maganizo amenewa, muzikumbukila mfundo izi. Yoyamba, munalengedwa m’njila yakuti muzitha kutengela Yehova na Yesu. Conco, mukasankha kutengela citsanzo cawo mudzakwanitsa kufika pamlingo wina wake. (Gen. 1:26) Yaciŵili, mzimu woyela wa Mulungu ni wamphamvu kwambili m’cilengedwe conse. Ungakuthandizeni kucita zimene simungakwanitse pa inu nokha. Yacitatu, Yehova pali pano, sayembekezela kuti muzionetsa cipatso ca mzimu mwangwilo. Ndiye cifukwa cake, pokhala Tate wathu wacikondi iye anaika zaka 1,000, kuti anthu amene ali na ciyembekezo ca padziko lapansi akafike pokhala angwilo kwathunthu. (Chiv. 20:1-3) Cimene Yehova amafuna kwa ife pali pano, n’cakuti tiyesetse kudalila thandizo lake.

7. Tikambilane ciyani tsopano?

7 Kodi tingatengele citsanzo ca Yesu pa mbali ziti maka-maka? Mwacidule, tiyeni tikambilane makhalidwe anayi amene mzimu wa Mulungu umabala. Pa khalidwe lililonse, tiphunzile zimene Yesu anacita poonetsa khalidwe limenelo. Pamene tikutelo, tidzapenda mafunso amene angatithandize kudzisanthula, kuti tione ngati tikupita patsogolo povala umunthu watsopano.

8. Kodi Yesu anaonetsa bwanji cikondi?

8 Cikondi cacikulu cimene Yesu ali naco pa Yehova, cinamusonkhezela kutumikila Atate wake komanso ife. (Yoh. 14:31; 15:13) Mmene iye anali kucitila zinthu na ŵanthu, zinaonetsa kukula kwa cikondi cake pa iwo. Tsiku lililonse, anali kuonetsa cikondi na cifundo, ngakhale pamene anthu anali kumutsutsa. Ndipo njila yaikulu imene anaonetsela cikondi cake pa anthu, ni kuwaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu. (Luka 4:43, 44) Yesu anaonetsanso cikondi codzimana pa Mulungu komanso anthu, mwa kudzipeleka kuti akavutike komanso kuphedwa na anthu ocimwa. Mwa kutelo, iye anatsegula njila yakuti tonse tikapeze moyo wosatha.

9. Tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu poonetsa cikondi?

9 Tinadzipatulila na kubatizika cifukwa cokonda Atate wathu wakumwamba Yehova. Conco, mofanana na Yesu, tiyenela kuonetsa kuti timakonda Yehova mwa kukonda anthu anzathu. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Amene sakonda m’bale wake amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.” (1 Yoh. 4:20) Tingadzifunse kuti: ‘Kodi nimakonda kwambili anthu? Kodi nimaonetsa cifundo pocita zinthu na ena, ngakhale kuti anicitila zinthu mopanda ulemu? Kodi cikondi cimanilimbikitsa kuseŵenzetsa nthawi yanga, komanso zinthu zanga pothandiza ena kuphunzila za Yehova? Kodi nimapitiliza kucita zimenezi ngakhale pamene anthu ambili sayamikila khama langa, kapena pamene akunitsutsa? Ningacite ciyani kuti nizitaila maola ambili pa nchito yopanga ophunzila?’—Aef. 5:15, 16.

10. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti amakonda mtendele?

10 Yesu anali munthu wokonda mtendele. Anthu akamucitila zoipa, iye sanali kubwezela. Koma anacita zoposa pamenepa. Anali kuyamba ndiye kukhazikitsa mtendele, ndipo anali kulimbikitsa ena kuthetsa kusamvana pakati pawo. Mwacitsanzo, anaphunzitsa anthu kuti ayenela kukhazikitsa mtendele na m’bale wawo, ngati afuna kuti Yehova alandile kulambila kwawo. (Mat. 5:9, 23, 24) Ndipo mobweleza-bweleza, anathandiza atumwi kuthetsa mkangano pa nkhani yakuti ndani anali wamkulu pakati pawo.—Luka 9:46-48; 22:24-27.

11. Tingacite ciyani kuti tikhale anthu obweletsa mtendele?

11 Kuti tikhale munthu wobweletsa mtendele, pali cina cimene tiyenela kucita kuposa cabe kungopewa kuyambitsa mikangano. Tiyenela kuyamba ndife kukhazikitsa mtendele na ena, komanso kulimbikitsa abale na alongo athu kuthetsa kusamvana pakati pawo. (Afil. 4:2, 3; Yak. 3:17, 18) Tingadzifunse mafunso aya: ‘Kodi ndine wokonzeka kudzimana zinthu zina kuti nikhazikitse mtendele na ena? M’bale kapena mlongo akanikhumudwitsa, kodi nimasunga cakukhosi? Kodi nimayembekezela kuti wina abwele kudzakhazikitsa mtendele, kapena nimayamba ndine kucita zimenezo, olo pamene iye akuoneka kuti ndiye wolakwa? Ngati m’poyenela, kodi nimalimbikitsa aja amene anasemphana maganizo kuti akhazikitse mtendele pakati pawo?’

12. Kodi Yesu anaonetsa motani kukoma mtima?

12 Yesu anali wokoma mtima. (Mat. 11:28-30) Iye anaonetsa kukoma mtima mwa kukhala wololela, komanso wodekha ngakhale m’mikhalidwe yovuta. Mwacitsanzo, pamene mayi wa ku Foinike anam’pempha kuti amucilitsile mwana wake, poyamba Yesu anakana pempho lake. Koma mayiyo ataonetsa cikhulupililo cacikulu, iye mokoma mtima anamucilitsila mwana wake. (Mat. 15:22-28) Ngakhale kuti Yesu anali wokoma mtima, sanaleke kupeleka uphungu pakafunika kutelo. Nthawi zina, anali kuonetsa kukoma mtima mwa kuwongolela anthu amene anali kuwakonda. Mwacitsanzo, Petulo atayesa kumulefula kuti asacite cifunilo ca Yehova, Yesu anamudzudzula pamaso pa atumwi ake ena. (Maliko 8:32, 33) Iye anacita izi, osati kuti acititse Petulo manyazi, koma kuti amuphunzitse na kumucenjeza pamodzi na atumwi ena kupewa kudzikuza. N’kutheka kuti Petulo anacita manyazi, koma anapindula na uphunguwo.

13. Kodi tingaonetse bwanji kukoma mtima?

13 Kuti tionetse kukoma mtima kwa anthu amene timawakonda, nthawi zina tingafunike kukamba nawo mosapita m’mbali. Mukafuna kucita zimenezo, tengelani citsanzo ca Yesu mwa kuzika uphungu wanu pa mfundo za m’Mawu a Mulungu. Khalani wodekha. Khalani na cikhulupililo cakuti iwo amafuna kucita zoyenela, podziŵa kuti anthu amene amakonda Yehova ndiponso imwe, adzalabadila uphungu wanu wacikondi. Dzifunseni mafunso akuti: ‘Kodi nimalimba mtima kupeleka uphungu kwa munthu amene nimam’konda, nikaona kuti akucita cina cake cosayenela? Nikafuna kupeleka uphungu, kodi nimalankhula mokoma mtima, kapena mwaukali? Kodi colinga canga copelekela uphungu n’ciyani? Kodi nimapeleka uphunguwo cifukwa cokhumudwa na zocita zake, kapena nimaupeleka kuti nimuthandize?’

14. Kodi Yesu amaonetsa bwanji khalidwe la ubwino?

14 Yesu samangodziŵa cabe zabwino, koma amazicita. Cifukwa cokonda Atate wake, nthawi zonse iye amacita coyenela na colinga cabwino. Munthu wabwino, nthawi zonse amafuna-funa mipata yothandizila ena na kuwacitila zabwino. Kungodziŵa zabwino zoyenela kucita si kokwanila. Tiyenela kucita zabwinozo, ndipo tizicite na colinga cabwino. Wina angafunse kuti, ‘Kodi zingatheke munthu kucita cabwino na colinga colakwika?’ Inde, zingatheke. Mwacitsanzo, Yesu anakamba za anthu amene anali kuthandiza osauka modzionetsela kuti anthu awaone n’kuwatamanda. Ngakhale kuti zimene anacitazo zinali zabwino, Yehova sanakondwele nawo.—Mat. 6:1-4.

15. Kodi tingaonetse bwanji khalidwe la ubwino mocokela pansi pamtima?

15 Tingaonetse khalidwe la ubwino, kokha ngati timacita zabwinozo osati na zolinga zadyela. Conco, dzifunseni kuti: ‘Kodi nimadziŵa zabwino zimene niyenela kucita na kuyesetsa kuzicita? Kodi colinga canga pocita zabwinozo n’ciyani?’

KODI UMUNTHU WATHU WATSOPANO TINGAUTETEZE BWANJI?

16. Kodi tiyenela kucita ciyani tsiku lililonse? Nanga cifukwa ciyani?

16 Tisakhale na maganizo akuti kuvala umunthu watsopano kumathela pa ubatizo. Umunthu watsopano uli monga “covala catsopano” cimene tiyenela kupitiliza kucivala. Njila imodzi imene tingacitile zimenezo, ni kufuna-funa mipata tsiku lililonse kuti tionetse makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umabala. Cifukwa ciyani? Cifukwa Yehova amaseŵenzetsa mzimu wake kuti agwile nchito zosiyana-siyana. (Gen. 1:2) Conco, khalidwe lililonse limene mzimu umabala liyenela kutipangitsa kuonetsa nchito yake. Mwacitsanzo, wophunzila Yakobo analemba kuti: “Cikhulupililo copanda nchito zake ndi cakufa.” (Yak. 2:26) N’cimodzimodzinso na makhalidwe ena amene mzimu wa Mulungu umabala. Nthawi iliyonse tikaonetsa khalidwe limenelo, timapeleka umboni wakuti mzimu wa Mulungu ukugwila nchito mwa ife.

17. Tiyenela kucita ciyani tikalephela kuonetsa makhalidwe amene mzimu woyela umabala?

17 Ngakhale Akhristu amene anabatizika zaka zambili kumbuyoku, nthawi zina amalephela kuonetsa makhalidwe amene mzimu woyela umabala. Komabe, cofunika kwambili ni kupitiliza kuonetsa makhalidwe amenewa. Ganizilani citsanzo ici. Ngati mwang’amba covala cimene mumakonda kwambili, kodi mungacitaye nthawi yomweyo? Ayi. Mosakaikila mudzasoka covalaco mosamala ngati n’zotheka. Komanso, mudzakhala wosamala kwambili kuti cisakang’ambikenso. Mofananamo, ngati nthawi zina muona kuti mwalephela kuonetsa wina cifundo, kuleza mtima, kapena cikondi, musalefuke. Mankhwala ake ni kupepesa mocokela pansi pa mtima. Kuli ngati kusoka ubale wanu umene wang’ambika, titelo kukamba kwake, n’colinga cakuti mukhalenso pa ubale wabwino na iye. Mukatelo, yesetsani kukhala wosamala m’tsogolo.

18. Kodi tingakhale otsimikiza za ciyani?

18 Tiyamikila ngako kuti tili na citsanzo ca Yesu cimene tingatengele! Tikamatengela kwambili maganizo ake na zocita zake, m’pamenenso cidzakhala copepuka kwa ife kucita zinthu monga iye. Komanso, tikamacita zinthu motengela kwambili citsanzo ca Yesu, m’pamenenso tidzakwanitsa kuvala bwino umunthu watsopano. M’nkhani ino, takambilana cabe makhalidwe anayi amene mzimu wa Mulungu umabala. Bwanji osapatula nthawi yophunzila makhalidwe enanso amene mzimuwu umabala, na kuwasinkhasinkha kuti muone mmene mukuwaonetsela? Mudzapeza nkhani zokamba pa makhalidwe amenewa mu Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova, pansi pa mutu wakuti “Umoyo Wacikhristu,” kenako “Cipatso ca mzimu.” Mungakhale otsimikiza kuti mukacita mbali yanu, Yehova adzakuthandizani kuvala umunthu watsopano na kusauvula.

NYIMBO 127 Mtundu wa Munthu Amene Niyenela Kukhala

^ Kaya cikhalidwe cathu cotani, n’zotheka kuvala “umunthu watsopano.” Kuti ticite zimenezi, tiyenela kupitiliza kusintha kaganizidwe kathu na kuyesetsa kukhala monga Yesu. M’nkhani ino, tikambilane maganizo a Yesu komanso zocita zake. Tikambilanenso mmene tingapitilizile kutengela citsanzo cake pambuyo pa ubatizo.

^ Lemba la Agalatiya 5:22, 23, silichula makhalidwe onse amene mzimu wa Mulungu umatithandiza kukhala nawo. Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani yakuti: “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga,” mu Nsanja ya Mlonda ya June 2020.