Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
N’cifukwa ciyani 2 Samueli 21:7-9 imati Davide ‘anamvelela cisoni Mefiboseti,’ koma pambuyo pake anapeleka Mefiboseti kuti akaphedwe?
Ena amene anaŵelengapo nkhaniyi, anadzifunsapo funso limeneli. Koma m’mavesi amenewa, akuchula amuna aŵili amene anali na dzina lofanana lakuti Mefiboseti. Ndipo tingaphunzilepo kanthu mwa kupenda zimene zinacitika.
Sauli mfumu ya Isiraeli anali na ana aamuna 7, komanso aakazi aŵili. Mwana woyamba wa Sauli anali Yonatani. Pambuyo pake, anabelekanso mwana wina kwa mdzakazi wake Rizipa, dzina lake Mefiboseti. N’zocititsa cidwi kuti nayenso Yonatani anali na mwana dzina lake Mefiboseti. Conco, Mfumu Sauli anali na mwana dzina lake Mefiboseti, komanso mdzukulu wa dzina limodzi-modzili.
Pa nthawi ina, Mfumu Sauli anaukila Agibeoni amene anali kukhala pakati pa Aisiraeli, ndipo anafuna kuwaseselatu onse. Ambili a iwo anaphedwa. Kucita zimenezo kunali kulakwa. Cifukwa ciyani? Cifukwa kalelo m’masiku a Yoswa, atsogoleli aciisiraeli anacita pangano lamtendele na Agibeoni.—Yos. 9:3-27.
Pangano limenelo linali kugwilabe nchito m’nthawi ya Mfumu Sauli. Koma mfumuyi inapha Agibeoni zimene zinali zosemphana na panganolo. Izi zinapangitsa kuti ‘Sauli pamodzi na a m’nyumba yake akhale na mlandu wa magazi.’ (2 Sam. 21:1) Potsilizila pake, Davide anakhala mfumu. Agibeoni opulumuka, anauza Davide zoipa zimene Sauli anacita. Iye anawafunsa zimene angacite kuti aphimbe chimo la Sauli, zimene zikanapangitsa kuti Yehova adalitse dziko la Isiraeli. M’malo mopempha ndalama, Agibeoni anapempha ana 7 aamuna a ‘munthu amene anakonza ciwembu cowaononga,’ kuti awapeleke m’manja mwawo kuti akawaphe. (Num. 35:30, 31) Davide anacita zimene iwo anapempha.—2 Sam. 21:2-6.
Pa nthawiyo, Sauli na Yonatani anali ataphedwa pa nkhondo. Koma Mefiboseti mwana wa Yonatani anali akali moyo. Iye anali wolemala kucokela ali mwana cifukwa ca ngozi inacitika, ndipo sanatengeko mbali pamene ambuye ake anali kupha Agibeoni. Davide anali atacita pangano la ubwenzi na Yonatani, limene linali kudzapindulitsa mbadwa za Yonatani, kuphatikizapo mwana wake Mefiboseti. (1 Sam. 18:1; 20:42) Nkhaniyo imati: “Mfumu [Davide] inamvela cisoni Mefiboseti mwana wamwamuna wa Yonatani, mwana wa Sauli, cifukwa ca lumbilo limene Davideyo ndi Yonatani . . . anacita pakati pawo pamaso pa Yehova.”—2 Sam. 21:7.
Ngakhale n’conco, Davide anamvela pempho la Agibeoni. Iye anapeleka ana aamuna aŵili a Sauli, ndipo Mefiboseti anali mmodzi wa iwo. Anapelekanso adzukulu asanu a Sauli. (2 Sam. 21:8, 9) Zimene Davide anacitazi zinathetsa mlandu wa magazi m’dzikolo.
Zocitika zimenezi sizinangokhala cabe mbili yakale ayi. Lamulo la Mulungu linakamba momveka bwino kuti: “Ana asaphedwe cifukwa ca macimo a abambo.” (Deut. 24:16) Ngati ana aamuna aŵili a Sauli komanso adzukulu ake asanu analibe mlandu, Yehova sakanalola kuti iwo aphedwe. Lamulo limenelo linakambanso kuti: “Aliyense aziphedwa cifukwa ca chimo lake.” Zioneka kuti mbadwa 7 za Sauli zimene zinaphedwa, zinatengako mbali pamene Sauliyo anali kupha Agibeoni. Pa cifukwa cimeneci, amuna 7 amenewo anaphedwa cifukwa ca chimo lawo.
Nkhaniyi ionetsa kuti munthu sangapeleke cifukwa codzikhululukila pa colakwa cake, pokamba kuti anali kungotsatila zimene anauzidwa. Mwambi wina umati: “Salaza njila ya phazi lako, ndipo njila zako zonse zikhazikike.”—Miy. 4:24-27; Aef. 5:15.