Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 13

Gwilitsani Nchito Zacilengedwe Pophunzitsa Ana Anu za Yehova

Gwilitsani Nchito Zacilengedwe Pophunzitsa Ana Anu za Yehova

“Kodi ndani amene analenga zinthu zimenezo?”—YES. 40: 26

NYIMBO 11 Cilengedwe Citamanda Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi makolo amakhumba ciyani ponena za ana awo?

 INU MAKOLO, tidziŵa kuti mumafuna kuthandiza ana anu kudziŵa Yehova na kum’konda. Koma Mulungu saoneka. Ndiye kodi mungawathandize bwanji ana anu kumuona monga munthu weniweni na kumuyandikila?—Yak. 4:8

2. Kodi makolo angawaphunzitse bwanji ana awo za makhalidwe a Yehova?

2 Njila yaikulu imene mungathandizile ana anu kumuyandikila Yehova ni kuphunzila nawo Baibo.(2 Tim. 3:14-17) Ngakhale n’telo, Baibo imafotokoza njila ina imene ana angaphunzilile za Yehova. Mwacionekele, tate winawake m’buku la Miyambo, anakumbutsa mwana wake kusaiŵala makhalidwe a Yehova amene amaonekela m’zacilengedwe. (Miy. 3:19-21) Tiyeni tsopano tikambilane zina mwa njila zimene makolo angaseŵenzetse pothandiza ana awo kuphunzila za Yehova pogwilitsa nchito zacilengedwe.

MMENE MUNGAGWILITSILE NCHITO ZACILENGEDWE POPHUNZITSA ANA ANU

3. Kodi makolo ayenela kuwathandiza kucita ciyani ana awo?

3 Baibo imakamba kuti ‘cilengedwele dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekela bwino m’zinthu zimene anapanga.’ (Aroma 1: 20) Inu makolo, mwina mumakonda kuceza na ana anu acicepele muli panja. Gwilitsani nchito mpata umenewu kuthandiza ana anu kuona kugwilizana kumene kulipo pakati pa ‘zimene Yehova anapanga’ na makhalidwe ake opatsa cidwi. Lomba, tiyeni tione zimene makolo angaphunzile pa citsanzo ca Yesu.

4. Kodi Yesu anagwilitsa nchito bwanji zacilengedwe pophunzitsa ophunzila ake? (Luka 12:24, 27-30)

4 Onani mmene Yesu anagwilitsila nchito cilengedwe pophunzitsa anthu. Pa nthawi ina, iye anauza ophunzila ake kuti ayang’anitsitse akwangwala komanso maluŵa. (Ŵelengani Luka 12:24, 27-30.) Yesu akanachula nyama iliyonse kapena comela ciliconse. M’malo mwake, iye anachula mbalame na maluŵa zimene ophunzila ake anali kuzidziŵa bwino. N’kutheka kuti ophunzilawo anali kuona akwangwala komanso maluŵa akuphukila. Taganizilani Yesu akuloza zinthuzo pokamba nawo. Nanga kodi anacita ciyani atachula zinthu zimenezi? Iye anaphunzitsa ophunzila ake mfundo yofunika kwambili yokhudza kukoma mtima, komanso kuwolowa manja kwa Atate wawo wakumwamba. Mfundoyo ni yakuti: Yehova adzasamalila atumiki ake okhulupilika powapatsa cakudya na zovala, monga mmene amasamalila akwangwala na maluŵa.

5. Ni zinthu ziti zacilengedwe zimene makolo angagwilitse nchito pophunzitsa mwana wawo za Yehova?

5 Inu makolo, kodi mungatengele bwanji citsanzo ca Yesu pophunzitsa ana anu? Njila imodzi, mungauzeko mwana wanu colengedwa cimene mumacita nazo cidwi kwambili, monga nyama kapena comela. Pamene mukutelo, m’fotokozeleni mwanayo kuti cinthuco citiphunzitsa ciyani za Yehova. Kenako, m’funseni nyama imene amaikonda kapena comela. Mwanayo adzayamba kumvetsela mwachelu pom’phunzitsa za makhalidwe a Yehova, mukamagwilitsa nchito zinthu zimene nayenso amacita nazo cidwi.

6. Kodi tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca amayi ake a m’bale Christopher?

6 Kodi makolo ayenela kucita kuthela nthawi yoculuka kufufuza za nyama inayake kapena comela, komanso zimene cinthuco cikutiphunzitsa ponena za Yehova? Osati kwenikweni. Yesu sanacite kufotokoza zambili zokhudza cakudya cimene akwangwala amadya kapena mmene maluŵa amakulila. Ngakhale kuti mwana wanu amasangalala mukamamufotokozela zambili zokhudza cilengedwe, nthawi zina ndemanga yacidule kapena funso lingakhale lokwanila kumveketsa mfundo. M’bale wina dzina lake Christopher akukumbukilabe zimene makolo ake anali kucita iye ali mwana. Anati: “Amayi anali kufotokoza ndemanga zacidule pofuna kutithandiza anafe kuyamikila zacilengedwe zotizungulila. Mwacitsanzo, tikakhala kufupi na mapili anali kunena kuti, ‘Taonani mapili awa ni aakulu komanso okongola. Yehova ni wamkulu, si conco?’ Ndipo tikakhala kunyanja anali kunena kuti, ‘Taonani mphamvu za mafunde. Mulungu ni wamphamvu, si telo kodi?’” M’bale Christopher anatinso: “Ndemanga zacidule komanso zotithandiza kuganiza zimenezo, zinali kutilimbikitsa kwambili.”

7. Kodi mungawaphunzitse bwanji ana anu kumaganizila zacilengedwe?

7 Pamene ana anu akusinkhuka mungawaphunzitse kuti aziganizila kwambili zacilengedwe, na kuzindikila makhalidwe a Yehova. Mungachuleko cinthu cimodzi cimene Mulungu analenga na kufunsa ana anu kuti, ‘Kodi cinthuci citiphunzitsa ciyani za Yehova?’ Mungacite cidwi na zimene ana anu angayankhe.—Mat. 21:16.

NI PANTHAWI ZITI PAMENE MUNGAGWILITSE NCHITO ZACILENGEDWE POPHUNZITSA ANA ANU?

8. Ni mwayi wotani umene makolo aciisiraeli anali kukhala nawo akamayenda “pamsewu”?

8 Makolo aciisiraeli analimbikitsidwa kuphunzitsa ana awo mawu a m’cilamulo ca Yehova akamayenda “pamsewu.” (Deut. 11:19) M’misewu ya kumadela a kumidzi ku Isiraeli, anthu anali kutha kuona nyama zosiyanasiyana, mbalame, na maluŵa. Pamene mabanja aciisiraeli anali kuyenda m’misewu imeneyo, makolo anali na mwayi wokulitsa cidwi ca ana awo pa zinthu zimene Yehova analenga. Mwina inunso monga makolo muli na mipata yofananako yogwilitsa nchito zacilengedwe pophunzitsa ana anu. Onani mmene makolo ena acitila zimenezi.

9. Kodi mwaphunzila ciyani kwa mlongo Punitha na Katya?

9 Mayi wina dzina lake Punitha wokhala mu mzinda waukulu ku India anati: “Tikapita kukacezela acibale kumudzi, timatengelapo mwayi wophunzitsa ana athu za cilengedwe cokongola ca Yehova. Nimaona kuti ana anga amamvetsa bwino zinthu zacilengedwe tikakhala kumadela akumidzi.” Dziŵani kuti ana anu sadzaiŵala nthawi yosangalatsa imene mumakhala nawo mukapita kumalo okongola. Katya mlongo wa ku Moldova anati: “Sinimaiŵala nthawi yosangalatsa imene tinali kukhala nayo tikapita na makolo anga kumudzi. Nimawayamikila kwambili kuti ananiphunzitsa kuyang’anitsitsa zinthu zimene Yehova analenga, na kuphunzila za makhalidwe ake ku zinthuzo.”

Ngakhale m’matauni, n’zotheka kupeza zinthu zacilengedwe zimene mungagwilitse nchito pophunzitsa ana anu za Yehova (Onani ndime 10)

10. Kodi makolo angacite ciyani ngati n’zowavuta kupita ku madela akumidzi? (Onani kabokosi kakuti “ Thandizo kwa Makolo.”)

10 Bwanji ngati n’zosatheka kwa inu kupita ku madela akumidzi? M’bale Amol amene nayenso akhala ku India anati: “Kumene nikhala makolo amagwila nchito maola ambili. Komanso ulendo wopita kumudzi umalila ndalama zambili. Komabe, n’zotheka kuona zinthu zacilengedwe na kuphunzila makhalidwe a Yehova mukapita ku paki kapena mukakhala pamtenje.” Mukayang’anitsitsa mosamala mudzaona kuti pa khomo panu pomwepo, pali zinthu zambili zacilengedwe zimene mungaonetse ana anu. (Sal. 104:24) Mwina mungathe kuona mbalame, tudoyo, zomela, na zina zotelo. Mlongo Karina wa ku Germany anati: “Amayi amakonda maluŵa. Conco, nili wacicepele anali kukonda kunionetsa maluŵa okongola nthawi zonse tikapita kwina kwake.” Makolonu, mungaphunzitse ana anu pogwilitsanso nchito mavidiyo ambili komanso zofalitsa pa zacilengedwe zimene gulu lathu latulutsa. Inde, mosasamala kanthu za mikhalidwe yanu, mungathandize ana anu kuyang’anitsitsa zinthu zimene Mulungu analenga. Lomba, tiyeni tikambilane ena mwa makhalidwe a Yehova amene mungafotokozele ana anu.

MAKHALIDWE A YEHOVA “OSAONEKA NDI MASO AKUONEKELA BWINO”

11. Kodi makolo angathandize motani ana awo kuona cikondi ca Yehova?

11 Pofuna kuthandiza ana anu kuona cikondi ca Yehova, mungawafotokozele mmene nyama zambili zimasamalila ana awo mwacikondi. (Mat. 23:37) Mungawafotokozelenso zinthu zacilengedwe za mitundu yosiyana-siyana zimene timasangalala nazo. Mlongo Karina amene tam’chula uja anati: “Tikapita kokayenda, amayi anali kunilimbikitsa kuima na kuyang’anitsitsa mmene duŵa lililonse analipangila mwapadela, komanso mmene kukongola kwake kumaonetsela cikondi ca Yehova. Kucokela nthawiyo mpaka pano, nimayang’anitsitsa maluŵa mwacidwi, mmene anawapangila, mtundu wake, komanso mmene lililonse limasiyanilana na linzake. Maluŵa amenewo amanikumbutsabe kuti Yehova amatikonda kwambili.”

Mungafotokoze mmene matupi athu anawapangila modabwitsa pophunzitsa ana anu nzelu za Mulungu (Onani ndime 12)

12. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuona nzelu za Mulungu? (Salimo 139:14) (Onaninso cithunzi.)

12 Thandizani ana anu kuona nzelu za Mulungu. Yehova ndiye wanzelu koposa m’cilengedwe conse. (Aroma 11:33) Mwacitsanzo, mungamufotokozele mwana wanu mmene madzi amakwelela kumwamba kukapanga mitambo. Komanso mmene mitambo imeneyo imayendela na kugwetsa mvula kumalo osiyana-siyana. (Yobu 38:36, 37) Mungamufotokozelenso mmene thupi la munthu analipangila modabwitsa. (Ŵelengani Salimo 139:14.) Izi n’zimene tate wina dzina lake Vladimir anacita. Iye anati: “Tsiku lina, mwana wathu anagwa pa njinga n’kudzipweteka. Patangopita masiku ocepa, cilondaco cinapola. Ndiyeno ine na mkazi wanga tinafotokozela mwanayo kuti Yehova anakonza matupi athu kuti azitha kudzikonza okha. Tinamuuza kuti zinthu zimene anthu amapanga sizimakwanitsa kudzikonza zokha. Mwacitsanzo, motoka ikawonongeka pa ngozi, siingathe kudzikonza yokha. Cocitika cimeneci cinathandiza mwana wathu kumvetsa nzelu za Yehova.”

13. Kodi makolo angawathandize bwanji ana awo kuona mphamvu za Mulungu? (Yesaya 40:26)

13 Yehova akutipempha kuti tiziyang’ana kumwamba na kuganizila mmene mphamvu zake zimathandizila kuti zinthu za kuthambo zisamacoke pamalo ake. (Ŵelengani Yesaya 40:26.) Mungawalimbikitse ana anu kuyang’ana kumwamba na kusinkhasinkha zimene akuona. Onani zimene mlongo wina dzina lake Tingting wa ku Taiwan anali kucita ali mwana. Iye anati: “Tsiku lina amayi anapita nane kokayenda, ndipo usiku tinayang’ana kumwamba kowala bwino na nyenyezi cifukwa sitinali m’tauni mmene munali magetsi. Panthawi imeneyo, n’nali kudela nkhawa ngati n’dzakwanitsa kutumikila Yehova mokhulupilika, cifukwa anzanga a m’kalasi anali kunituntha kuti niyambe makhalidwe oipa. Amayi ananilimbikitsa kuganizila mphamvu zimene Yehova anagwilitsa nchito polenga nyenyezi zonsezo, komanso kuti iye adzagwilitsa nchito mphamvu zomwezo ponithandiza kugonjetsa mayeso alionse. Pambuyo poona cilengedwe pa ulendo umenewo, zinanithandiza kum’dziŵa bwino Yehova. Komanso n’nakulitsa cifuno canga com’tumikila.”

14. Kodi makolo angagwilitse nchito bwanji zinthu zacilengedwe pothandiza ana awo kuona kuti Yehova ni Mulungu wacimwemwe?

14 Zinthu zimene Yehova analenga zimaonetsa kuti iye ni wacimwemwe, komanso kuti amafuna kuti ifenso tikhale acimwemwe. Asayansi apeza kuti nyama zambili nazonso zimaseŵela, kuphatikizapo mbalame na nsomba. (Yobu 40:20) Kodi ana anu amaseka akamaona nyama zikuseŵela? Mwina ana anu anaonapo cona akuthamangitsa kampila, kapena ana a galu akugwebana. Tsiku lina mukadzaona ana anu akuseka poona nyama ikucita zoseketsa, bwanji osatengelapo mwayi wowakumbutsa kuti timatumikila Mulungu wacimwemwe?—1 Tim. 1:11.

MUZISANGALALA NA CILENGEDWE CA YEHOVA MONGA BANJA

Pamene ana anu akusangalala na zacilengedwe pamodzi nanu, iwo angamasuke kukuuzani mmene akumvela (Onani ndime 15)

15. N’ciyani cingathandize makolo kudziŵa za mumtima mwa ana awo? (Miyambo 20:5) (Onaninso cithunzi.)

15 Nthawi zina, makolo angaone kuti n’covuta kumasula ana awo kuti aziwauza mavuto amene amakumana nawo. Ngati zili conco kwa inunso, yesetsani kudziŵa za mumtima mwa ana anu. (Ŵelengani Miyambo 20:5.) Makolo ena amaona kuti mpata wabwino wocitila zimenezi, m’pamene akusangalala na zacilengedwe pamodzi na ana awo. Cifukwa ciyani? Cifukwa cimodzi n’cakuti sipakhala zosokoneza zambili kwa ana komanso makolo. Tate wina wa ku Taiwan dzina lake Masahiko anachula cifukwa cina. Iye anati: “Tikapita kokayenda na ana athu, monga kukakwela phili kapena kukaona nyanja, iwo amakhala omasuka kwambili. Izi zimatithandiza kukambilana nawo momasuka, kuti tidziŵe za mumtima mwawo.” Mlongo Katya amene tam’chula uja anati: “Nthawi zambili amayi anali kupita nane kupaki. Tikakhala kumalo abata amenewo, n’nali kumasuka kuwafotokozela zinanicitikila kusukulu na nkhawa zimene n’nali nazo.”

16. Kodi mabanja angacite ciyani kuti azisangalala poyang’ana cilengedwe ca Yehova?

16 Mabanja akamapatula nthawi yosangalala na cilengedwe ca Yehova, amalimbitsa cikondi pa wina na mnzake. Baibo imati pali “nthawi yoseka” na “nthawi yodumphadumpha mosangalala.” (Mlal. 3: 1, 4) Kudzela m’nchito ya manja ake, Yehova anatipatsa malo oculuka ocitilako zinthu zimene timasangalala nazo. Mabanja ambili amakonda kupita kumalo monga kumapaki, kumalo akumidzi, kumapili, komanso kunyanja. Ndipo ana ambili amasangalala akamanyaya na kuona zinyama zosiyanasiyana. Inde, tili na mipata yambili yosangalala na zinthu zotizungulila zimene Yehova analenga.

17. N’cifukwa ciyani makolo ayenela kuthandiza ana awo kusangalala na zinthu zimene Mulungu analenga?

17 M’dziko latsopano la Mulungu, makolo komanso ana adzasangalala na cilengedwe ca Yehova kuposa kale lonse. Mosiyana na masiku ano, panthawiyo tidzakhala pa mtendele na nyama. (Yes. 11:6-9) Tidzasangalala na cilengedwe ca Yehova kosatha. (Sal. 22:26) Koma inu makolo, musacite kuyembekeza mpaka nthawi imeneyo kuti mudzayambe kuthandiza ana anu kusangalala na zinthu zacilengedwe. Mukamagwilitsa nchito zacilengedwe pophunzitsa ana anu za Yehova, iwo angafike povomeleza zimene Mfumu Davide ananena. Iye anati: “Inu Yehova . . . palibe nchito zilizonse zofanana ndi nchito zanu.”—Sal. 86:8.

NYIMBO 134 Ana ni Mphatso Zimene Mulungu Amaikiza kwa Makolo

a Abale na alongo ambili amakumbukila nthawi yosangalatsa imene anali kuyang’ana cilengedwe na makolo awo. Iwo sanaiŵale mmene makolo awo anaseŵenzetsela nthawiyo powaphunzitsa za makhalidwe a Yehova. Ngati muli na ana, kodi mungasewenzetse bwanji cilengedwe powaphunzitsa za makhalidwe a Mulungu? Nkhani ino iyankha funso limeneli.